Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.
Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu. Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani. Musamadzinyenga pakungomva chabe mau a Mulungu, koma muzichita zimene mauwo anena. Paja munthu amene amangomva chabe mau, osachita zimene wamvazo, ali ngati munthu woyang'anira nkhope yake yachibadwa m'galasi. Tsono amati akadzipenya, amachokapo, posachedwa nkuiŵalako m'mene akuwonekera. Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse. Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga. Chipembedzo choona ndi changwiro pamaso pa Mulungu amene ali Atate, ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto ao, ndiponso kudzisunga bwino, kuwopa kudetsedwa ndi zoipa za m'dziko lapansi. Paja mukudziŵa kuti mukamayesedwa m'chikhulupiriro chanu, mumasanduka olimbika. Koma kulimbika kumeneku kuzigwira ntchito yake kotheratu, kuti mukhale angwiro, opanda chilema ndi osapereŵera pa kanthu kalikonse.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Tsono abale, khazikani mtima pansi mpaka Ambuye adzabwere. Onani m'mene amachitira mlimi. Amadikira kuti zipatso zokoma ziwoneke m'munda mwake. Amangoyembekeza mokhazika mtima kuti zilandire mvula yachizimalupsa ndi yachikokololansanu. Inunso khazikani mtima. Limbani mtima, pakuti Ambuye ali pafupi kubwera.
Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama. Limbitsani tsono manja anu ofooka ndiponso maondo anu agooka. Muziyenda m'njira zoongoka, kuti miyendo yopunduka isagweduke, koma ichiritsidwe. Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako. Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale wadama, kapena wonyoza zauzimu, monga Esau, amene adaagulitsa ukulu wake ndi chakudya cha kamodzi kokha. Paja mukudziŵa kuti, pambuyo pake adaafuna kulandira madalitso a atate ake, koma zidakanika, chifukwa sadathenso kusintha maganizo, ngakhale adaalakalaka kutero molira mizozi. Inu simudachite monga Aisraele aja, amene adaafika ku chinthu chimene adaatha kuchikhudza, ndiye kuti ku Phiri la Sinai, lija linali loyaka moto, lamdima wa bii, la mphepo yamkuntho; limene panali kulira kwa lipenga, ndiponso kumveka kwa mau. Anthu atamva mauwo, adaapempha kuti asaŵamvenso konse, Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu. Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chauta ndi wabwino kwa amene amamudalira, kwa onse amene amafuna kuchita zimene Iye afuna. Nkwabwino kumdikira Chauta mopirira kuti aonetse chipulumutso chake.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.
Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika.
Munthu wosapsa mtima msanga amapambana wankhondo, amene amadzigwira mtima amapambana msilikali wogonjetsa mzinda.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Ngati tilimbika, tidzakhala mafumu pamodzi naye. Ngati ife timkana, Iyenso adzatikana.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
Nchifukwa chake Abrahamu adaayembekeza molimbikira, nalandira zimene Mulungu adaamlonjeza.
Paja Iye adakupatsani mwai, osati wakungokhulupirira Khristu ai, komanso wakumva zoŵaŵa chifukwa cha Iye. Ndimayamika Mulungu wanga nthaŵi zonse ndikamakukumbukirani. Inunso mukumenya nkhondo yomwe ija imene mudandiwona ine ndikuimenya, yomwenso ndikumenyabe tsopano, monga mukumveramu.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika,
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu,
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri, koma wofulumira kupsa mtima amaonetsa uchitsiru wake.
Pamene ndinali m'mavuto ndidapemphera kwa Chauta, ndipo Iye adandichotsera mavutowo. Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani?
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Tsono musataye kulimba mtima kwanu, pakuti kumabweretsa mphotho yaikulu. Pafunikadi kupirira, kuti muchite zimene Mulungu akufuna, kuti motero mukalandire zimene adalonjeza.
Pajatu ndi chinthu chabwino ngati munthu, chifukwa chokumbukira Mulungu, apirira zoŵaŵa zosamuyenera. Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso, Kodi pali chiyani choti nkukuyamikirani ngati mupirira pamene akumenyani chifukwa choti mwachimwa? Koma mukapirira zoŵaŵa mutachita zabwino, apo mwachita chinthu chovomerezedwa ndi Mulungu.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Musalole zophunzitsa zosiyanasiyana ndiponso zachilendo kuti zikusokeretseni. Choyenera kutilimbitsa mtima ndi kukoma mtima kwa Mulungu, osati malamulo onena za chakudya ai. Malamulo ameneŵa sadaŵapindulitsepo anthu amene ankaŵatsata.
Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Muziganiza za Iye amene adapirira udani waukulu chotere wochokera kwa anthu ochimwa, kuti musafookere ndi kutaya mtima.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.
Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo. Pakuti munthu akafa, ndiye kuti wamasuka ku mphamvu ya uchimo.
Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako.
Kukhala wosauka ndimakudziŵa, kukhala wolemera ndimakudziŵanso. Pa zonse ndidaphunzira chinsinsi chake cha kukhala wokhutitsidwa, pamene ndapeza chakudya kapena ndili ndi njala, pamene ndili ndi zambiri kapena ndili wosoŵeratu. Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.
Wolungama wanga adzakhala ndi moyo pakukhulupirira. Koma akamachita mantha nkubwerera m'mbuyo, Ine sindikondwera naye.”
Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika.
Nchifukwa chake anthu amene amamva zoŵaŵa monga Mulungu afunira, adzipereke m'manja mwa Mlengi wao wokhulupirika, ndi kumachitabe ntchito zabwino.
Ngwodala munthu amene amaganizirako za amphaŵi, popeza kuti Chauta adzapulumutsa munthu wotere pa tsiku lamavuto. Koma Inu Chauta, mundikomere mtima, mundichiritse kuti ndiŵalange anthuwo. Mukatero ndidzadziŵa kuti mumakondwera nane, chifukwa mdani wanga sadandipambane. Inu mwandichirikiza chifukwa cha kukhulupirika kwanga, mwandikhazika pamaso panu mpaka muyaya. Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Inde momwemo. Inde momwemo. Chauta adzamteteza ndi kumsunga ndi moyo. Adzatchedwa wodala pa dziko. Chauta sadzampereka kwa adani ake, kuti amchite zimene iwo akufuna.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Ife amene tili ndi chikhulupiriro champhamvu, tiziŵalezera mtima anthu ofooka, osamangodzikondweretsa tokha. Akutinso, “Inu anthu a mitundu ina, kondwani pamodzi ndi anthu ake a Mulungu.” Ndiponso akuti, “Inu nonse a mitundu ina, tamandani Ambuye, anthu a mitundu yonse amtamande.” Nayenso mneneri Yesaya akuti, “Mmodzi mwa zidzukulu za Yese adzabwera. Iye adzadzambatuka kuti alamule anthu a mitundu ina, ndipo iwo adzaika chikhulupiriro chao pa Iyeyo.” Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana. Komabe m'kalata ino zina ndakulemberani mopanda mantha konse, kuti ndikukumbutseni zimenezo. Ndalemba motere popeza kuti Mulungu adandikomera mtima pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera. Tsono pokhala ndine wake wa Khristu Yesu, ndikunyadira ntchito imene ndikugwirira Mulungu. Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko. Aliyense mwa ife azikondweretsa mnzake, ndi kumchitira zabwino, kuti alimbikitse chikhulupiriro chake.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri. Ngati tikuzunzika, nkuti inu mupeze chokulimbitsani mtima ndiponso chipulumutso. Ngati ife atilimbitsa mtima, nkuti inunso mulimbitsidwe mtima ndi kulandira mphamvu za kupirira pamene mulikumva zoŵaŵa zomwezo zimene ifenso timamva.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Chauta akadapanda kundithandiza, bwenzi posachedwa nditapita ku dziko lazii. Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza.
“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.