Mulungu ali nafe nthawi zonse. Ndikudziwa kuti pa moyo timakumana ndi mavuto ambiri omwe amatitengera mtendere wathu ndi kutidzaza ndi nkhawa. Koma tiyeni tikumbukire kuti Mulungu amatipatsa mphamvu kudzera m’Mawu ake m’nthawi zovuta zimenezi.
“Musadandaule konse; koma pa chilichonse, ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” Afilipi 4:6. Landirani mtendere wa Khristu mumtima mwanu ndipo khulupirirani chowonadi chake.
Chifukwa chomwe chili chofunika kwambiri si zimene vuto lanu likunena za inu, koma zimene Atate wathu wakumwamba wakukonzerani kumwamba. Zinthu zikhoza kuoneka zovuta pano padziko, koma tiyeni tikhale olimba m’chikhulupiriro chathu. Mulungu ali nafe.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto.
Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga.
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Inu Mulungu, imvani kulira kwanga, mverani pemphero langa. Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola, komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Mtima wa munthu umatha kupirira matenda, koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso?
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Wokondedwa, ndimapemphera kuti zako zonse zikuyendere bwino, ndipo kuti moyo wako wathupi ukhale wolimba, monga momwe uliri moyo wako wauzimu.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha? Ngakhale bambo wanga ndi mai wanga andisiye ndekha, Inu Chauta mudzandisamala. Mundiwonetse njira zanu zachifundo, Inu Chauta, munditsogolere m'njira yosalala, chifukwa ndili ndi adani ambiri. Musandipereke m'manja mwa adani angawo. Mboni zonama zandiwukira, ndipo zimandiwopseza. Ndikhulupirira kuti ndidzaona ubwino wake wa Chauta m'dziko la amoyo. Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta. Pamene adani ndi amaliwongo anga andiputa kuti andiphe, adzaphunthwa ndipo adzagwa. Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,