Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso. Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo Atate amakhala mwa Ine? Mau amene ndimakuuzani sachokera kwa Ine ndekha ai, koma Atate amene amakhala mwa Ine, ndiwo amagwira ntchito yao. Mundikhulupirire kuti Ine ndimakhala mwa Atate ndipo Atate amakhala mwa Ine. Kupanda apo, khulupiriranitu chifukwa cha ntchito zanga zomwezo. Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.” “Ngati mundikonda, muzidzatsata malamulo anga. Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu. Sindidzakusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ndidzabweranso kwa inu. Kwangotsala kanthaŵi pang'ono, ndipo anthu ongokonda zapansipano sadzandiwonanso, koma inu mudzandiwona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. M'nyumba mwa Atate anga muli malo ambiri okhalamo. Kukadakhala kuti mulibe malo, ndikadakuuzani. Ndikupita kukakukonzerani malo. Tsiku limenelo mudzadziŵa kuti Ine ndimakhala mwa Atate, ndipo inu mumakhala mwa Ine, monga Ine ndimakhala mwa inu. “Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.” Yudasi, osati Iskariote uja ai, adamufunsa kuti, “Ambuye zatani kuti muziti mudzadziwonetsa kwa ife, koma osati kwa anthu onse?” Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye. Munthu amene sandikonda, satsata zimene ndanena Ine. Mau amene mulikumvaŵa si angatu ai, koma ndi a Atate amene adandituma. “Zimenezi ndakuuzani ndikadali nanu. Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani. “Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa. Mwandimva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita, koma ndidzabweranso kwa inu.’ Mukadandikonda, bwenzi mutakondwera kuti ndikupita kwa Atate, chifukwa Atate ngoposa Ine. Ndakuuziranitu zimenezi tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika, mudzakhulupirire. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti inunso mukakhale kumene kuli Ine.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Abale, tifuna kuti mudziŵeko za anthu amene adamwalira, kuti chisoni chanu chisakhale ngati cha anthu ena amene alibe chiyembekezo. Paja ife timakhulupirira kuti Yesu adaamwalira naukanso. Motero timakhulupiriranso kuti anthu amene adamwalira akukhulupirira Yesu, iwonso Mulungu adzaŵaukitsa nkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo.
Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu?
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Chikondi chanu chosasinthika chindisangalatse ine mtumiki wanu, monga momwe mudalonjezera.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Munditsogolere m'choona chanu ndi kundilangiza, pakuti Inu ndinu Mulungu Mpulumutsi wanga, ndimadalira Inu masiku onse.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Zimenezi zikukondweretseni, ngakhale tsopano mumve zoŵaŵa poyesedwa mosiyanasiyana pa kanthaŵi. Monga golide, ngakhale ndi wotha kuwonongeka, amayesedwa ndi moto, momwemonso chikhulupiriro chanu, chimene nchoposa golide kutali, chimayesedwa, kuti chitsimikizike kuti nchenicheni. Apo ndiye mudzalandire chiyamiko, ulemerero ndi ulemu pamene Yesu Khristu adzaoneka.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Motero musadere nkhaŵa zamaŵa. Zamaŵa nzamaŵa. Tsiku lililonse lili ndi zovuta zake zokwanira.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
“Iwe imfa, kupambana kwako kuli kuti? Iwe imfa, ululu wako uli kuti?” Ululu wake wa imfa ndi uchimo, ndipo chimene chimapatsa uchimo mphamvu, ndi Malamulo. Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku. Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo. Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.
Nkhaŵa ya munthu imakhala ngati katundu wolemera mumtima mwake, koma mau abwino amamsangalatsa.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo. Munthu wongodalira zilakolako zake zokha, chimene adzakolole ndi imfa. Koma munthu wodalira Mzimu Woyera, chimene adzakolole ndi moyo wosatha. Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta. Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake. Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu. Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao. Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake. Maso anga akuyang'ana kwa Chauta nthaŵi zonse, pakuti adzaonjola mapazi anga mu ukonde. Inu Chauta yang'aneni ine, ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha, ndipo ndazunzika kwambiri. Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga, ndipo munditulutse m'masautso anga. Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga, ndipo mundikhululukire machimo anga onse. Onani m'mene adani anga ankhalwe achulukira ndi m'mene chidani chao ndi ine chakulira. Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
“Atonthozeni mtima, atonthozeni mtima anthu anga,” akutero Mulungu wanu. Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake. Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa. Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo? Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake? Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu? Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi. Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha. Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake. Kodi Mulungu mungathe kumuyerekeza ndi yani? Kodi mungamufanizire ndi chiyani? Likakhala fano, ndi munthu waluso amene amalipanga, kenaka mmisiri wa golide amalikuta ndi golide, nalipangira ukufu wasiliva. “Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”
Chiyembekezo cha wokhulupirira chimapezetsa chimwemwe, koma zimene woipa amayembekezera, zimafera m'mazira.
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake. Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Usamadziwona ngati wanzeru. Uziwopa Chauta, ndipo uleke zoipa. Kuchita choncho kudzapatsa thupi lako moyo, kudzalimbitsa mafupa ako.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.” Chauta akuti, “Koma simudapemphere kwa Ine, inu am'banja la Yakobe, mudatopa nane, inu Aisraele. Simudadzatule kwa Ine nkhosa kuti zikhale zopereka zopsereza, simudandilemekeze ndi nsembe zanu. Sindidakulemetseni pomakupemphani zopereka zanu, sindidakutopetseni pomakupemphani lubani. Simudandigulire bango lonunkhira, simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu, mwandilemetsa ndi zolakwa zanu. “Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu. Mundikumbutse zakale, titsutsane. Mufotokoze mlandu wanu kuwonetsa kuti simudalakwe. Atate anu oyamba adachimwa, atsogoleri anu aja adandilakwira. Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.” Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako. Ndine Woyera uja wa Israele, Mpulumutsi wako. Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe. Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Chauta adzathetsa imfa mpaka muyaya, adzapukuta misozi m'maso mwa aliyense, ndipo adzachotsa manyazi a anthu ake pa dziko lonse lapansi. Watero Chauta.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
“Ndidaona m'mene ankachitira, komabe ndidzaŵachiritsa. Ndidzaŵatsogolera ndi kuŵatonthoza. Anthu olira nao adzandiyamika ndi milomo yao. Anthu onse akutali ndi apafupi, ndidzaŵapatsa mtendere. Ndidzachiritsa anthu anga.
Namondwe akaomba, oipa amachotsedwa, koma anthu ochita chilungamo amakhazikika mpaka muyaya.
“Ndithu ngati mukhululukira anthu machimo ao, Atate anu akumwamba adzakukhululukirani inunso. Koma ngati simukhululukira anthu machimo ao, Atate anunso sadzakukhululukirani machimo anu.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika. Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe.
Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya. Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.