Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


61 Mau a m'Baibulo Munthawi Yovuta

61 Mau a m'Baibulo Munthawi Yovuta

M'kati mwa zonsezi, Mulungu ndi wokhulupirika nthawi zonse, ndipo Mawu ake amatikumbutsa za kukhulupirika kwake m'nthawi yovuta. Amaona chisoni changa ndipo sachinyoza, koma amanditsimikizira kuti sizatha zonse.

Ndiyenera kumvetsa kuti chisoni ndi chinthu chachibadwa chifukwa cha ululu ndi kutayika, ndipo palibe cholakwika ndi kumva chisoni. Ndimadziwanso kuti nthawi zachisoni zili ndi cholinga, chifukwa Iye amachititsa kuti zonse zigwirizane ndi cholinga chake kwa onse amene adawaitana.

Salmo 46:10 amatikumbutsa kuti tikhale chete ndikupumula podziwa kuti Iye ndi Mulungu. “Khalani chete, mudziwe kuti Ine ndine Mulungu; Ine ndidzakwezedwa pakati pa amitundu; Ine ndidzakwezedwa pa dziko lapansi.”

Usaiwale kuti chimwemwe cha Ambuye ndi mphamvu yako, ndipo ukhoza kuchita zonse mwa Khristu amene amakulimbitsa. Choncho limbika mtima, vuto limeneli silidzatha ndi iwe; koma ndi mwayi woti uyandikire kwa Ambuye ndi kuti muzimveka kulambira kwabwino kochokera mumtima mwako.




Masalimo 119:50

Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:11

Atatha mazunzo akewo, adzaona phindu lake, ndipo adzakhutira. Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzasenza machimo a anthu onse kuti iwo ambiri a iwo asadzapezekenso kuti ndiopalamula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:92

Malamulo anu akadapanda kundisangalatsa, bwenzi nditafa ndi mazunzo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:19

Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:13

Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:5

Pakuti monga tikumva zoŵaŵa kwambiri pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatilimbitsa mtima kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:18

Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:18

Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga, ndipo mundikhululukire machimo anga onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:5

Koma iwe, uzikhala maso pa zonse, pirira pa zoŵaŵa, gwira ntchito yolalika Uthenga Wabwino. Kwaniritsa udindo wako mosamala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nahumu 1:7

Chauta ndi wabwino, ndiye kothaŵira pa nthaŵi yamavuto. Amasamala onse amene amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:6

Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:10

Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva, ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 26:24

Monga ndakusungirani moyo wanu leromu, momwemonso Chauta ateteze moyo wanga, ndipo andipulumutse m'mavuto anga onse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:6

Munthu wosaukayu adalira, ndipo Chauta adamumva, nampulumutsa m'mavuto ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 42:11

Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:24

Khalani amphamvu ndipo mulimbe mtima, inu nonse okhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:12

Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-2

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 31:6

Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 61:2

Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:3

Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:15

Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:1-2

Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:3-4

Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Maliro 3:22-23

Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 11:18

Udzalimba mtima poti chikhulupiriro chilipo. Mulungu adzakutchinjiriza, ndipo udzapumula mwamtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:5

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:15-16

Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:19

Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:15

Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:9

Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6-7

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:12

Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:7

Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:4

Ngodala anthu amene akumva chisoni, pakuti Mulungu adzaŵasangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:28

Ndafookeratu ndi chisoni. Limbitseni monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:1-2

Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya. Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:5-6

Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:143

Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:16-18

Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 38:15

Koma tsono ndimayembekezera Inu Chauta, Ndinu Chauta, Mulungu wanga amene mudzayankha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1-2

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:8-9

Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse. Nchifukwa chake mtima wanga ukukondwa, ndipo m'katikati mwangamu ndikusangalala. Thupi langanso lidzakhala pabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Yesu wabwino Atate wanga wachikondi, mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chitsirizo. Mzimu Woyera wokondedwa wanga, m'nthawi ino yovuta ndikupemphani mundilimbitse, mundithandize tsiku lililonse kuyenda m'chikhulupiriro osati m'kuona, kumvetsa kuti ngakhale lero zinthu zonse zikuoneka zoipa, mawa zidzakhala bwino, kuti ngati lero zonse zikuoneka zamdima, mawa kuwala kudzawala. Pa nthawi yovutayi ndithandizeni kukhazikitsa maso anga pa kukula ndi mphamvu zanu osati pamavuko. Mawu anu amati: «Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi kuti adzakumane nanu. Koma ataona mphepo yamphamvu, anaopa; ndipo anayamba kumira, nalira, nati: Ambuye, ndipulumutseni!» Atate, ndithandizeni kuti ndisapatuke kutsatira zokhumba ndi zilakolako za dziko lino kuti ndipambane m'masautso awa ndikumvetsa kuti palibe chimphepo choposa inu, sinthani maganizo anga ndipo yeretsani mtima wanga. Ambuye, ulemerero ndi ulemelero zonse zikhale zanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa