Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


102 Mau a m'Baibulo Okhudza Ngongole

102 Mau a m'Baibulo Okhudza Ngongole

Choyamba, sungani mtima wanu. Muyenera kupewa chilichonse chomwe sichikukulimbikitsani. N'zoona kuti zinthu zonse ndi zovomerezeka kwa inu, koma sikuti zonse zimakukomerani. Choncho, samalani ndi zisankho zanu zonse, pemphani Mulungu nzeru ndipo musalole kuti maganizo anu akulamulireni, chifukwa angakutsogolereni panjira yoipa.

Nthawi zambiri mdani adzakupatsani mayankho omwe nthawi ya mavuto angawoneke ngati oyenera, koma samalani! Mapeto ake nthawi zonse amatsogolera ku imfa. Ngongole si njira yabwino yothetsera mavuto. M'malo mwake, pitani kwa Mulungu ndipo mudzapeza thandizo lanu panthawi yake. Yesu amadziwa zosowa zanu zonse ndipo akufuna kukuthandizani.

Ikani mavuto anu kwa iye ndipo mudzapeza mtendere. Mukatero, mudzawona momveka bwino zipangizo zomwe muli nazo, zomwe zingakuthandizeni kutuluka mu ngongole. Mukatero, musabwererenso kumeneko, chifukwa Yesu akufuna kuti muyende mu dalitso ndipo ngati munthu wopanda chochita manyazi.

Khalani okhutira ndi zomwe muli nazo tsopano; chifukwa iye anati: Sindidzakusiyani, kapena kukutayani; Aheberi 13:5.




Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:7

Tsono muzipereka kwa onse zimene zikukhalira iwowo: msonkho kwa okhometsa msonkho, zolipira kwa oyenera kuŵalipira. Muzilemekeza oyenera kuŵalemekeza, ndi kuchitira ulemu oyenera kuŵachitira ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera amalamulira wosauka, ndipo wokongola zinthu amakhala kapolo wa womkongozayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:6

Chauta adzakudalitsani inu monga momwe adalonjezera. Mudzakongoza mitundu yambiri, koma inuyo simudzakongola kwa wina aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri, koma palibe mtundu wina uliwonse umene udzakulamulireni inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:12

Mutikhululukire ife machimo athu, monga ifenso takhululukira otilakwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:20

Munthu wanzeru samwaza chuma chake, koma munthu wopusa amachiwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:27-28

Usaleke kumchitira zabwino woyenera kuzilandira, pamene uli nazo mphamvu zochitira choncho. Usamuuze mnzakoyo kuti, “Pita, ukachite kubweranso, ndidzakupatsa maŵa,” pamene uli nazo tsopano lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

“Munthu sangathe kutumikira mabwana aŵiri, pakuti kapena adzadana ndi mmodzi nkukonda winayo, kapena adzadzipereka kwa mmodzi nkumanyoza winayo. Simungathe kutumikira onse aŵiri, Mulungu ndi chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28-30

“Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza? Akapanda kutero, mwina adzaika maziko, nkulephera kuitsiriza. Apo anthu onse, poona zimenezi, adzayamba kumseka. Yesu adafunsa akatswiri a Malamulo ndi Afarisi kuti, “Kodi Malamulo amalola kuchiritsa munthu pa tsiku la Sabata, kapena ai?” Adzati, ‘Mkulu uyu adaayamba kumanga nyumba, koma adalephera kuitsiriza.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:21

Munthu woipa amakonda ngongole koma satha kubweza, koma munthu wabwino ali ndi mtima wokoma ndi wopatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:5

Kuli bwino kusalumbira kanthu kwa Mulungu, kupambana kuti ulumbire koma osachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:8

Amene amachulukitsa chuma chake polandira chiwongoladzanja ndi pochikundika, chumacho amachikundikira ena amene adzachitira chifundo anthu osauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zolinga za munthu wakhama zimachulukitsa dzinthu dzake, koma aliyense wochita zinthu mofulumira udyo, amangokhala wosoŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:25-26

“Uziyanjana msanga ndi mnzako wamlandu, mukali pa njira yopita ku bwalo lamilandu, kuwopa kuti angakakupereke kwa woweruza, woweruzayo angakakupereke kwa msilikali, ndipo msilikaliyo angakakuponye m'ndende. Ndithu ndikunenetsa kuti sudzatulukamo mpaka utalipira zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:26

Nthaŵi zonse munthu wolungama amapatsa mosaumira, ndipo amakongoza mwaufulu, ana ake amakhala madalitso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:26-27

Usakhale mmodzi mwa anthu opereka zikole, amene amasanduka chigwiriro cha ngongole. Ngati ulephera kulipira, adzakulanda ngakhale bedi lako lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:14

“Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:15

Woperekera wachilendo chigwiriro, adzapeza mavuto, koma wodana ndi za chigwiriro, amakhala pa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pajatu kukonda ndalama ndi gwero la zoipa zonse. Chifukwa cha kuika mtima pa ndalama anthu ena adasokera, adasiya njira ya chikhulupiriro, ndipo adadzitengera zoŵaŵitsa mitima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:1-5

Mwana wanga, kodi udalonjeza kumlipirira mnzako chikole, kodi udaperekera mlendo chigwiriro? Ukati ndingogonako pang'ono, ndingoodzerako pang'ono chabe, ndingopinda manja okhaŵa kuti ndipumuleko, umphaŵi udzakugwira ngati munthu wachifwamba, usiŵa udzakufikira mwadzidzidzi ngati mbala. Munthu wachabechabe, munthu woipa, amangoyendayenda nkumalankhula zabodza. Amatsinzinira masoŵa nkumakwekwesa pansi mapazi ake, amalozaloza ndi chala chake. Amalingalira zoipa ndi mtima wake wopotoka, amangokhalira kuvundula madzi pakati pa anthu. Nchifukwa chake tsoka lidzamgwera modzidzimutsa. Pa kamphindi kochepa adzaonongedwa, osapulumuka konse. Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Chauta amadana nazo, makamaka zisanu ndi ziŵiri ndithu zimene zimamunyansa: maso onyada, pakamwa pabodza, manja opha munthu wosalakwa, mtima wokonzekera kuchita zoipa, mapazi othamangira msangamsanga ku zoipa, mboni yonama yolankhula mabodza, ndi munthu woutsa chidani pakati pa abale. Kodi udakodwa ndi mau a pakamwa pako pomwe, kodi udagwidwa ndi mau olankhula iwe wemwe? Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza. Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu. Zimenezi zidzakupulumutsa kwa mkazi woipa, zidzakuthandiza kuti usamvere mau osalala a mkazi wachiwerewere. Mumtima mwako usamakhumbira kukongola kwake, usakopeke nawo maso ake. Paja mkazi wachiwerewere ungathe kumgula ndi buledi, koma wadama wokwatiwa amakulanda ndi moyo wako womwe. Kodi munthu angathe kufukata moto, zovala zake osapsa? Kodi munthu angathe kuponda makala amoto, mapazi ake osapserera? Ndizo zimamchitikira wokaloŵerera mkazi wamwini. Aliyense wokhudza mkazi wotero adzalangidwa. Ndiye iwe mwana wanga, popeza kuti wadziponya m'manja mwa mnzako, chita izi kuti udzipulumutse: nyamuka, pita msanga, ukampemphe kuti akumasule. Paja anthu sainyoza mbala, ikaba chifukwa cha njala. Komabe ikangogwidwa, imalipira kasanunkaŵiri, mpaka mwina kulandidwa katundu yense wa m'nyumba mwake. Amene amachita chigololo ndi wopanda nzeru, amangodziwononga yekha. Adzangolandira mabala ndi manyozo, ndipo manyazi ake sadzamchoka ai. Paja nsanje imakalipitsa mwini mkaziyo, sachita chifundo akati alipsire. Savomera dipo lililonse, sapepeseka ngakhale umpatse mphatso zochuluka chotani. Usagone tulo, usaodzere, Dzipulumutse monga imadzipulumutsira mphoyo kwa mlenje, monga imadzipulumutsira kwa wosaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:25

Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

“Mukakongoza ndalama munthu wina aliyense waumphaŵi pakati panupo, musamachita monga momwe amachitira anthu okongoza, musamuumirize kupereka chiwongoladzanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36-37

Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma. Letsani maso anga kuti asamayang'ane zachabe, mundipatse moyo monga momwe mudalonjezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:27

Ukonzeretu ntchito zako zonse makamaka zakumunda, pambuyo pake mpamene ungayambe kumanga nyumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 24:10-11

Mukakongoza munthu kanthu, musaloŵe m'nyumba mwake kukatenga chovala chimene afuna kukupatsani ngati pinyolo. Inu mukhale panja, mwini wakeyo achite kukupatsani yekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Chitetezo cha nzeru chili ngati chitetezo cha ndalama. Koma kudziŵa zinthu kukuposerapo, chifukwa nzeru zimasunga moyo wa amene ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:7

Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:18

Munthu wopanda nzeru amapereka chikole, ndipo amasanduka chigwiriro pamaso pa mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:12

Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala, koma wopusa amangopitirira ndipo amanong'oneza bondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Pa tsiku loyamba la sabata, aliyense mwa inu azipatulapo kanthu, potsata momwe wapezera. Zimene wapatulazo azisunge kunyumba, kuti pasakakhalenso kusonkhasonkha ine ndikabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:30-31

Munthu wabwino amalankhula zanzeru, pakamwa pake pamatuluka zachilungamo. Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 18:7

Sazunza munthu wina aliyense, koma amabwezera wangongole chigwiriro chake. Saaba, amadyetsa anjala, ndipo amaveka ausiwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10-12

Wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ngwokhulupirikanso pa zazikulu. Ndipo wonyenga pa zazing'ono, amanyenganso pa zazikulu. Tsono ngati mwakhala osakhulupirika pa chuma chonyengachi, ndani nanga adzakusungizeni chuma chenicheni? Ndipo ngati mwakhala osakhulupirika ndi za wina, ndani adzakupatseni zimene zili zanuzanu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:13-14

Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:72

Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:11-13

Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:21

Choloŵa chopata mofulumira poyamba, sichidzakhala dalitso pambuyo pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11

Yesetsani kukhala ndi moyo wabata. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kumagwira ntchito ndi manja ake. Chitani zimenezi, monga tidakulangizirani muja,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:23-35

“Tsono Ufumu wakumwamba tingaufanizire motere: Panali mfumu ina imene idaaitanitsa antchito ake kuti iwonenso bwino ngongole zao. Atangoyamba kumene, adabwera ndi wantchito wina amene anali ndi ngongole ya ndalama zochuluka kwabasi. Ndiye popeza kuti adaasoŵa chobwezera ngongoleyo, mbuye wake uja adalamula kuti amgulitse wantchitoyo pamodzi ndi mkazi wake ndi ana ake ndi zake zonse, kuti ngongole ija ibwezedwe. Apo wantchito uja adamgwadira nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani ndithu zonse.’ Mbuye wake uja adamumveradi chifundo, ndipo adamkhululukira ngongole ija, namlola kuti apite. “Koma pamene wantchitoyo ankatuluka, adakumana ndi mmodzi mwa antchito anzake, yemwe iye adaamkongoza ndalama zochepa. Adamgwira pa khosi mwaukali namuuza kuti, ‘Bweza ngongole yako ija.’ Apo wantchito mnzake uja adadzigwetsa pansi ku mapazi ake nati, ‘Pepani, ndakupembani, lezereni mtima, ndidzakubwezerani.’ ndipo adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti mukapanda kusintha ndi kusanduka ngati ana, simudzaloŵa konse mu Ufumu wakumwamba. Koma iye adakana, nakamponyetsa m'ndende kuti mpaka abweze ndithu ngongoleyo. “Antchito anzake ena ataona zimenezi, adamva chisoni kwambiri. Adapita kukafotokozera mbuye wao zonsezo. Tsono mbuye wakeyo adamuitana namuuza kuti, ‘Wantchito woipa iwe, ine ndinakukhululukira ngongole yonse ija pamene unandidandaulira. Kodi sunayenera kuti iwenso umchitire chifundo wantchito mnzako, monga ndinakuchitira iwe chifundo?’ Motero mbuye wakeyo adapsa mtima kwambiri, nampereka kuti akamzunze mpaka atabweza ngongole yonse ija. “Inunsotu Atate anga akumwamba adzakuchitani zomwezo, aliyense mwa inu akapanda kukhululukira mbale wake ndi mtima wonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono nkumaopa Chauta, kupambana kukhala ndi chuma chambiri nkupeza nacho mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:5

Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:7

Munthu wokoma mtima amasamalira zoyenerera osauka, koma munthu woipa salabadako za zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:1-2

Chikatha chaka chachisanu ndi chiŵiri chilichonse, muzikhululukira onse amene adakongola zinthu zanu. Dzampatseni mwaufulu mosaŵinya, ndipo Chauta adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse. Nthaŵi zonse padzakhala Aisraele ena osauka, osoŵa zinthu. Motero ndikukulamulani kuti otereŵa muzidzaŵachitira chifundo. Muhebri mnzanu, mwamuna kapena mkazi, akadzigulitsa kwa inu kuti akhale kapolo wanu, mummasule atangokutumikirani zaka zisanu ndi chimodzi zokha. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri, mumlole kuti apite mwaufulu. Mukammasula, musangomchotsa ali chimanjamanja. Mpatseniko momkomera mtima zonse zimene Chauta adakudalitsa nazoni monga: nkhosa, tirigu ndi vinyo. Kumbukirani kuti mudaali akapolo ku Ejipito, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adakuwombolani. Nchifukwa chake ndikukupatsani lamulo limeneli tsopano lino. Koma kapoloyo akakhala kuti akukukondani inu ndi banja lanu, chifukwa mukukhala naye bwino, mwina sangafune nkuchoka komwe. Ngati zili choncho, mutenge zingano ndipo muboole khutu la kapoloyo, mpaka zinganoyo iloŵe m'chitseko. Mukatero, adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Ngati ndi kapolo wamkazi, mudzamchite chimodzimodzi. Kumasula kapolo, kuti akhale mfulu, kusakuipireni. Adakutumikirani kale zaka zisanu ndi chimodzi pa theka la mtengo wa wantchito wolembedwa. Chitani zimenezi, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse. Ana onse amphongo oyamba kubadwa a ng'ombe ndi a zoŵeta zina, muŵapatule kuti akhale a Chauta, Mulungu wanu. Ng'ombe zimenezi musazigwiritse ntchito, ndipo nkhosazo musazimete bweya. Zimenezi zizichitika motere: aliyense amene adakongoza Mwisraele mnzake ndalama, afafanize ngongole imeneyo. Asamuumirize kapena mbale wake kuti abweze ndalamazo, popeza kuti Chauta walamula kuti ngongoleyo ifafanizidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:7

Amachitira anthu opsinjidwa zolungama, amaŵapatsa chakudya anthu anjala. Chauta amamasula am'ndende.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Kuli bwino kukhala ndi zinthu pang'ono uli ndi chilungamo kupambana kukhala ndi chuma chambirimbiri ulibe chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:3

Mafumu oipa sadzalamulira nthaŵi yonse dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake, kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 10:19

Phwando ndi lokondwetsa anthu, ndipo vinyo ndi wosangalatsa moyo. Komatu zonsezo nzolira ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 31:10-31

Kodi mkazi wolemerera angathe kumpeza ndani? Ndi wokwera mtengo kuposa miyala ya yamtengowapatali. Mtima wa mwamuna wake umamkhulupirira, ndipo mwamunayo sadzasoŵa phindu. Masiku onse a moyo wake, mkaziyo amachitira mwamuna wake zabwino osati zoipa. Amanka nafunafuna ubweya ndi thonje, ndipo amagwira ntchito ndi manja ake mwaufulu. Ali ngati zombo za anthu amalonda, zakudya zake amakazitenga kutali. Amadzuka usikusiku nkuyamba kukonzera chakudya anthu a pabanja pake, ndi kuŵagaŵira ntchito adzakazi ake. Amalingalira za munda, naugula. Amalima munda wamphesa ndi ndalama zozipeza ndi manja ake. Amavala dzilimbe ndipo sachita manja khoba pogwira ntchito. Amazindikira kuti malonda ake ndi aphindu, choncho nyale yake sizima usiku wonse. Thonje amadzilukira yekha, ndipo nsalu amadziwombera yekha. Nchiyani, mwana wanga? Nchiyani, mwana wa m'mimba mwanga? Nchiyani, mwana wanga amene ndidachita kukupempha polonjeza ndi malumbiro? Anthu osauka amaŵachitira chifundo, amphaŵi amaŵapatsa chithandizo. A pabanja pake saŵaopera kuti nkufa nacho chisanu, poti amadziŵa kuti onsewo amavala zovala zofunda. Amadzipangira yekha zofunda, ndipo iye amavala zovala zabafuta ndi za mtengo wapatali. Mwamuna wake ndi wodziŵika ndithu ku mabwalo, akakhala pakati pa akuluakulu a dziko. Mkazi ameneyu amasoka zovala za nsalu yabafuta, nazigulitsa, amaperekanso mipango kwa anthu amalonda. Mphamvu ndi ulemu zimakhala ngati chovala chake. Amaganiza zakutsogolo mosangalala. Amalankhula mwanzeru, ndipo amaphunzitsa anthu ndi mau okoma. Amayang'anira makhalidwe a anthu a pabanja pake, ndipo sachita ulesi mpang'ono pomwe. Ana ake amamnyadira nkumutchula kuti ndi wodala. Mwamuna wake nayenso amamtamanda, amati, “Inde alipo akazi ambiri olemerera kwabasi, koma kuyerekeza ndi iwe, onsewo nchabe.” Mphamvu zako usathere pa akazi, usamayenda nawo ameneŵa, amaononga ndi mafumu omwe. Nkhope yachikoka ndi yonyenga, kukongola nkosakhalitsa, koma mkazi woopa Chauta ndiye woyenera kumtamanda. Muzimlemekeza chifukwa cha zochita zake, ntchito zake zizimpatsa ulemu ku mabwalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:23

Koma munthu akamadya ali wokayika, waweruzidwa kale kuti ngwolakwa, popeza kuti zimene akuchita nzosagwirizana ndi zimene iye amakhulupirira kuti nzoyenera. Paja chilichonse chimene munthu achita, chotsutsana ndi zimene iye amakhulupirira, chimenecho ndi tchimo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:18

Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo, koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:14-15

“Munthu akabwereka choŵeta kwa mnzake, tsono choŵeta chija nkupweteka mpaka kufa pamene sichili kwa mwiniwakeyo, wobwerekayo alipire ndithu choŵetacho. Koma ngati chili kwa mwiniwakeyo, wobwereka uja asalipire. Choŵetacho akachibwereka, tsono nkuwonongeka, mtengo wolipira pobwereka ndiwo udzakonze mlanduwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:22

Anthu amene Chauta adaŵadalitsa, adzalandira dziko kuti likhale lao, koma amene Chauta adaŵatemberera adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:21

Paja chidakwa ndi munthu wadyera adzasanduka amphaŵi, ndipo munthu waulesi adzasanduka mvalansanza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:1

Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:1-2

Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:15

Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:7-9

Inu Mulungu, ndikukupemphani zinthu ziŵiri, musandimane zimenezo ndisanafe: Musalole kuti ndikhale wabodza kapena wonama. Ndisakhale mmphaŵi kapena khumutcha. Muzindidyetsa chakudya chondiyenera, kuwopa kuti ndikakhuta kwambiri, ndingayambe kukukanani nkumanena kuti, “Chauta ndiye yaninso?” Kuwopanso kuti ndikakhala mmphaŵi, ndingayambe kuba, potero nkuipitsa dzina la Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:4

Ukalumbira chinthu kwa Mulungu, usachedwe kuchichita, chifukwa Mulungu sakondwera nazo zitsiru. Zimene wazilumbira, uzichitedi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:23

Atsogoleri ako apanduka, ndipo amagwirizana ndi mbala. Aliyense amakonda chiphuphu, ndipo amathamangira mphatso. Satchinjiriza ana amasiye, ndipo samvera madandaulo a akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wokomera mtima anthu osauka amachita ngati wokongoza Chauta, ndipo ndi Chautayo amene adzambwezera chifukwa cha ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:45

ndipo ndidzayenda ndi ufulu, chifukwa ndasamala malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:33

Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:12

Koma koposa zonse abale anga, musamalumbira. Musalumbire potchula Kumwamba, kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. Pofuna kutsimikiza kanthu, muzingoti, “Inde”. Pofuna kukana kanthu, muzingoti, “Ai”. Muzitero, kuwopa kuti Mulungu angakuweruzeni kuti ndinu opalamula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:27

Amene amapatsa osauka sadzasoŵa kanthu koma amene amatsinzina dala kuti asaŵapenye, adzatembereredwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:5

Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:23

“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:9

Munthu wanzeru atatsutsana ndi chitsiru, chitsirucho chimangochita phokoso nkumaseka, ndipo sipakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12

Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:25

Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:24-25

Pali zinthu zinai zing'onozing'ono pa dziko lapansi, koma ndi zochenjera kwambiri: Nyerere zili ngati anthu opanda nyonga, komabe zimakonzeratu chakudya chake m'chilimwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:22

Kodi amene amakonzekera zoipa sachimwa? Koma amene amakonzekera zabwino anthu amaŵaonetsa chifundo ndi kukhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kwa nyerere, mlesi iwe. Kapenyetsetse makhalidwe ake, ukaphunzireko nzeru. Ilibe ndi mfumu yomwe, ilibe kapitao kapena wolamulira. Komabe imakonzeratu chakudya chake m'malimwe, ndipo imatuta chakudyacho m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:30-34

Ndinkayenda m'mbali mwa munda wa munthu waulesi, m'mbali mwa munda wamphesa wa munthu wopanda nzeru. M'minda monsemo munali mutamera minga yokhayokha, m'nthaka imeneyo munali mutamera khwisa, ndipo mpanda wake wamiyala unali utagwa. Tsono nditaona, ndidayamba kuganizirapo pa zimenezo, nditayang'ana, ndidatolapo phunziro ili: Ukati, “Taimani ndigoneko pang'ono,” kapena “Ndiwodzereko chabe,” kapena “Ndingopumulako pang'ono,” umphaŵi udzakufikira monga mbala, kusauka kudzakupeza ngati mbala yachifwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-20

“Musadziwunjikire chuma pansi pano, pamene njenjete ndi dzimbiri zimaononga, ndiponso mbala zimathyola ndi kuba. “Nchifukwa chake pamene mukupereka zachifundo, musachite modziwonetsera, monga amachitira anthu achiphamaso aja m'nyumba zamapemphero ndiponso m'miseu yam'mizinda. Iwoŵa amachita zimenezi kuti anthu aŵatame. Ndithu ndikunenetsa kuti amenewo alandiriratu mphotho yao. Koma mudziwunjikire chuma Kumwamba, kumene njenjete kapena dzimbiri siziwononga, ndiponso mbala sizithyola ndi kuba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Atatero adauza anthu aja kuti, “Chenjerani, ndipo mupewe khumbo lililonse lofuna zambiri. Pajatu ngakhale munthu akhale ndi chuma chochuluka chotani, chumacho sichingatchinjirize moyo wake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 128:2

Udzadya zimene manja ako adagwirira ntchito. Udzasangalala, ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:8

Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Uike ntchito zako m'manja mwa Chauta, ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:5

Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:19

Pa nthaŵi ya mavuto sadzazunzika, pa nthaŵi yanjala, adzakhala nazo zakudya zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:14

Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36

Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4

Usadzitopetse nkufuna chuma, udziŵe kuchita zinthu mwanzeru ndi kudziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:17

Anthu amene aja akuchita changu kwambiri pothandiza inu kuti akukopeni, koma changu chaocho sichili chabwino ai. Amangofuna kukupatutsani kuti muzichita changu pakuŵathandiza iwowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:40

Munthu akakuzenga mlandu nafuna kukulanda mkanjo wako, umlole atengenso ndi mwinjiro wako womwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:3-4

Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:28

Kukoma mtima ndi kukhulupirika ndizo zimasunga mfumu, chilungamo ndiye chimalimbitsa ufumu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:3

Khulupirira Chauta ndipo uzichita zabwino. Khala m'dziko ndi kutsata zokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:1-2

Ulemu woulandira chitsiru uli ngati chisanu chambee chomagwa nthaŵi yachilimwe, kapena mvula yomagwa nthaŵi yokolola. Amene amalemba ntchito chitsiru chongodziyendera kapena chidakwa, ali ngati munthu woponya mivi amene amangolasa anthu chilaselase. Chitsiru chimene chimabwerezabwereza za uchitsiru wake chili ngati galu wodya masanzi ake omwe. Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi, pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa. Waulesi amati, “Pali mkango pa njira! Mumseumo muli mkango!” Monga chitseko chimatembenukira uku ndi uku pa zomangira zake, ndimonso waulesi amangokunkhulira pabedi pake. Waulesi amati akapisa dzanja lake m'mbale, kumamtopetsa kuti alifikitse kukamwa kwake. Waulesi amadziyesa wanzeru kupambana anthu asanu ndi aŵiri amene angathe kuyankha mochenjera. Amene angoloŵerera ndeu ya eniake, ali ngati munthu wombwandira galu wongodziyendera. Monga munthu wopenga amene amangoponya nsakali zamoto, kapena mivi yoopsa, ndimonso amakhalira munthu wonyenga mnzake, amene amati, “Ai, ndi zoseka chabe!” Monga imachitira mpheta yokhalira kuuluka, monga amachitira namzeze kumangoti zwezwezwe, ndimonso limachitira temberero lopanda chifukwa, silitha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Atate wanga wakumwamba, moyo wanga ukulambira dzina lanu ndi kukuthokozani chifukwa cha chifundo chanu chosatha. Mwandikomera ine, nthito zonse mwandionetsa kukhulupirika kwanu, chikondi ndi chikhuluriro. Lero ndabwera pamaso panu chifukwa ndikufuna thandizo lanu pa moyo wanga. Mavuto a ngongole andilemetsa, sindingathe kupita patsogolo, ndataya mtendere ndipo ndikusowa pothawira. Ndikukupemphani kuti mundithandize, mundipatse zomwe ndikufunikira kuti ndimalipire ndikhale mfulu ku zinthu izi. Mundikhululukire chifukwa cha zosankha zanga zopanda nzeru ndi kusasamala pazinthu zomwe ndimalonjeza. Mundikhululukire chifukwa cha kupanda kwanga nzeru, sindifuna kukhala chonchi. Sinthani maganizo anga, zochita zanga ndi moyo wanga. Mundipange monga momwe mulili inu mpaka ndikakhale wolungama pamaso panu. Ambuye, ndikukuthokozani chifukwa mwamva pemphero langa, thandizo langa ndi zoperekedwa zidzachokera kumwamba. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa