Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


155 Mau a m'Baibulo Okhudza Nkhondo

155 Mau a m'Baibulo Okhudza Nkhondo

Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, n’zosavuta kugwidwa ndi mantha komanso kusadziwa choti chingachitike. Koma Baibulo limatipatsa chiyembekezo ndi mphamvu. Pakati pa chisokonezo ndi kutaya mtima, tingapeze chitonthozo mu lonjezo la Mulungu loti adzakhala nafe, ngakhale m’nthawi zovuta kwambiri. Monga mmene lemba la Masalmo 46:1-2 limanenera, “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka msanga m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, ngakhale dziko litasunthika, ndipo mapiri atagwera mkati mwa nyanja.”

Yesu, m’buku la Yohane 16:33, anatiuza, “Ndanena izi kwa inu kuti mukhale ndi mtendere mwa Ine. M’dziko lapansi mudzakhala ndi chisautso; koma limbikani mtima; Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”

Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, tikumbukire kuti zida zathu zenizeni si za thupi, koma zauzimu. Pemphero, chikhulupiriro, ndi chiyembekezo ndi zida zathu zamphamvu kwambiri. Tikamaika maganizo ndi mitima yathu pa Mulungu, tingathe kuthana ndi mavuto aliwonse molimba mtima komanso modzidalira.

Mulungu akutiitana kuti tikhale kuunika pakati pa mdima, kuti tikhale ofalitsa chiyembekezo ndi chikondi m’nthawi yovuta ino. Mwa zochita zathu ndi mawu athu, tingasonyeze chikondi ndi mtendere wa Khristu, kupereka chitonthozo ndi chithandizo kwa omwe akutizungulira.

M’nthawi yovuta ino, tidalira Mulungu, tigwire mwamphamvu lonjezo lake la chipulumutso, ndipo tilole chikondi chake chitsogolere miyoyo yathu.




Yakobo 4:1-2

Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu? Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani. Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza. Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako? Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,” m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira. Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.” Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa. Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa. Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:3

popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:6-7

Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai. Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 120:7

Ine ndimafuna mtendere, koma ndikalankhula za mtendere, iwo amafuna nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:1

Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:22

Munthu wamangaŵa amautsa mikangano, munthu wokalipakalipa amabweretsa zolakwa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 4:3

Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 15:3

Chauta ndi wankhondo, Chauta ndilo dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 20:1

Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 25:12

Anthu a ku Yuda adagwira anthu ena amoyo okwaniranso 10,000. Adakwera nawo pamwamba pa thanthwe, naŵaponya pansi kuchoka pamenepo. Ndiye onsewo adangotekedzeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 14:2

Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:4

Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 20:4

Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 22:8

Koma Chauta adandiwuza kuti, ‘Iwe udapha anthu ambiri ndipo udamenya nkhondo zikuluzikulu. Chifukwa cha zimenezi, sindiwe amene udzandimangire nyumba ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:34

Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 17:47

Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 22:35

Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:15

Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1-3

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto. “Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.” Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu. Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama, ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 76:3

Kumeneko adathyola mivi youluzika, zishango, malupanga ndi zida zonse zankhondo za adani ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:2

Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:5

Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 31:4

Chauta adandiwuza kuti, “Monga momwe mkango kapena msona wa mkango umabangulira utagwira nyama, ndipo abusa sangaupirikitse, ngakhale auwopseze ndi kufuula chotani, motero palibe chimene chingaletse Chauta Wamphamvuzonse kutchinjiriza Phiri la Ziyoni ndi gomo lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:13

Chauta akupita ku nkhondo ngati ngwazi, akuutsa ukali wake ngati munthu wankhondo. Akukuŵa, akufuula mfuu zankhondo. Akuwonetsa mphamvu zake pakuposa adani ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:19

Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:20-23

Iwe Babiloni ndiwe nyundo yanga, chida changa chankhondo: ndi iwe ndimaphwanyaphwanya mitundu ya anthu, ndimaononga maufumu. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya akavalo ndi okwerapo ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya magaleta ndi oyendetsa ake. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abusa ndi ziŵeto zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya alimi ndi ng'ombe zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri ankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 30:3

Ndithudi layandikira, tsiku la Chauta lili pafupi. Tsiku lamitambo, tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 39:9

Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 1:1

Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:9

“Mulengeze pakati pa anthu a mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo, itanani ankhondo amphamvu. Asilikali onse afike pafupi, ayambe nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:12

Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:3-4

Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe. Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:1

Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:32-34

Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri. Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa, ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 14:14-16

Abramu atamva kuti mbale wake wagwidwa, adasonkhanitsa anthu ake odziŵa kumenya nkhondo. Onse pamodzi analipo 318, ndipo adalondola mafumu aja njira yonse mpaka ku Dani. Atafika kumeneko, adagaŵa anthu ake m'magulu, ndipo iye ndi anthu ake adakamenyana nawo ndi usiku mpaka kuŵagonjetseratu. Adaŵapirikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko, ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 14:14

Chauta ndiye amene akumenyereni nkhondo. Inuyo simuchitapo kanthu konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 1:30

Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani, ndipo adzaponyanso nkhondo m'malo mwanu, monga momwe mudaonera ku Ejipito kuja

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 3:22

Musaŵaope, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaponye nkhondo pamodzi nanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 20:8

Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 1:9

Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 10:25

Tsono Yoswa adauza akuluakuluwo kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Mukhale amphamvu ndiponso mulimbe mtima, poti Chauta adzaŵachita zimenezi adani anu onseŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 5:2

“Pakuti atsogoleri adatsogoleradi m'dziko la Israele, ndipo anthu adadzipereka okha mwaufulu, tamandani Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Oweruza 7:20

Apo magulu ena aŵiri aja nawonso adaimba malipenga, naswa mbiya zija, onse atatenga nsakali zija m'dzanja lakumanzere, ndi malipenga oti aziimba m'dzanja lamanja. Ndipo adafuula kuti, “Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 10:5

Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 13:3

Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 14:6

Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 14:52

Pa moyo wake wonse Saulo ankakhalira kuchita nkhondo ndi Afilisti. Tsono ankati akaona munthu wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamulemba m'gulu lake lankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 17:1-2

Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu. Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono. Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri. Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. Davide anali mzime. Ana akuluakulu atatuwo ndiwo anali ku nkhondo ndi Saulo. Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu. Pa masiku makumi anai Goliyati uja adakhala akutuluka, namadziwonetsa m'maŵa ndi madzulo. Tsiku lina Yese adauza mwana wake Davide kuti, “Abale ako uŵatengere makilogramu khumi a tirigu wokazinga, ndi mitanda khumi yabulediyi, ndipo upite nazo mofulumira ku zithando zao. Utengenso mphumphu khumizi za tchizi, upite nazo kwa mkulu wolamulira ankhondo. Ukaone m'mene abale ako akukhalira, ndipo ubwereko ndi chizindikiro china chosonyeza kuti ali bwino. Saulo, abale akowo ndi Aisraele ena, akumenyana nkhondo ndi Afilisti ku chigwa cha Ela.” Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 10:12

Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 11:1

Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 20:23

Kwao kuja akuluakulu a mfumu ya ku Siriya adauza mfumu yao kuti, “Milungu ya anthu a ku Israele ndi milungu yam'mapiri, nchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambanira ife. Koma tiyeni tikamenyane nawo ku chigwa, ndithudi tidzaŵapambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 6:16

Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 19:35

Ndiye usiku umenewo mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 5:22

Adani ena ambiri adaphedwa, pakuti Mulungu ankaŵathandiza pa nkhondoyo. Choncho anthuwo adakhala bwino kumeneko mpaka nthaŵi yotengedwa ukapolo ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 14:11

Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:11

Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 15:7

Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:20

Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:14

Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:18

Adzapulumutsa moyo wanga pa nkhondo imene ndikumenya, pakuti anthu ambiri akukangana nane.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:9

Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:30

Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 83:1-4

Inu Mulungu, musakhalenso chete. Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu. amene adaŵaononga ku Endori, ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka. Akalonga ao muŵachite zomwe mudachita Orebu ndi Zeebu, ndipo ana a mafumu ao onse, muŵachite zomwe mudachita Zeba ndi Zalimuna, amene adati, “Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.” Inu Mulungu wanga, muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu, akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo. Monga momwe moto umatenthera nkhalango, monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri, momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho, ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu. Inu Chauta, muŵachititse manyazi, kuti azifunafuna dzina lanu. Achitedi manyazi ndi mantha mpaka muyaya, ndipo afe imfa yonyozeka. Adziŵe kuti Inu nokha, amene dzina lanu ndinu Chauta, ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi. Onani, adani anu akuchita chiwawa. Amene adana nanu akukuukirani. Akuchitira anthu anu upo wonyenga. Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza. Iwo amati, “Tiyeni tifafanize mtundu wao wonse. Dzina la Israele lisakumbukikenso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:43

Inde, mwabunthitsa lupanga lake, ndipo simudamlimbitse pa nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:1

Inu Chauta, ndinu Mulungu wolipsira, Inu Mulungu wolanga, dziwonetseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:5-6

Ng'ambani thambo, Inu Chauta, ndi kutsikira pansi. Khudzani mapiri kuti afuke nthunzi. Ng'animitsani zing'aning'ani ndi kuŵamwaza adani anga. Ponyani mivi yanu, ndi kuŵapirikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:31

Kavalo amamkonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Chauta amene amapambanitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:2

“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:15

Ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu, chatsopano, cha mano akuthwa. Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya. Magomo udzaŵasandutsa mankhusu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:46

Musataye mtima. Musaope maphephe amene awanda m'dziko monse. Chaka ndi chaka pamabuka ndithu maphephe onena za nkhondo pa dziko lapansi, ndiponso zakuti mfumu yakutiyakuti ikumenyana ndi inzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:19

Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:14

Makamu ndi makamu a anthu ali m'Chigwa cha Chiweruzo. Ndithu tsiku la Chauta layandikira m'Chigwa cha Chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 2:1

Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Amowabu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adanyoza mafupa a mfumu ya ku Edomu poŵatentha mpaka kuŵasandutsa phulusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Obadiya 1:15

“Posachedwapa lifika tsiku la Chauta pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena. Zimene mudachitazo zidzakubwererani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 7:16

Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:6

Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:52

Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:9

Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipoloŵe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chifika nthaŵi yomweyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:43

Munkanyamula hema la Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene mudaŵapanga kuti muziŵapembedza. Ndidzakuchotsani kukutayani kutali, kupitirira dziko la Babele.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 12:4

Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:4

pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:30

Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:10

Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:8-9

Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:17

Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:6

Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:8

Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:4

Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:18

Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:3

Umve nao zoŵaŵa monga msilikali wabwino wa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 11:34

ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:1

Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:7

Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:11

Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 60:12

Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 98:1

Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:95

Anthu oipa amandiŵenda kuti andiwononge, koma ine ndimalingalira za malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1

Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:10

Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:9

Ngodala anthu odzetsa mtendere, pakuti Mulungu adzaŵatcha ana ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:25

Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:7

Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:8

Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:31

“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 22:36

Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 2:14

Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:14

Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:28

osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:20

Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:21

Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:11

Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:8

Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:39

Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:28

Pakuti ulamuliro ndi wake wa Chauta, Iye amalamula anthu a mitundu yonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 24:8

Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:3

Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:9

Amaletsa nkhondo mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amathyola uta, ndi kupokonyola mkondo. Amatentha magaleta ankhondo ndi moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:7

Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:30

Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:2-4

Pa masiku akudzaŵa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza. Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'ming'alu yam'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi. Musakhulupirirenso munthu, poti moyo wake sukhalira kutha. Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati! Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:10

Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:16-17

Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge. Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 4:1-3

Pa masiku akudzaŵa, phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo. Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu. Tsopano mitundu yambiri yasonkhana kuti imenyane ndi iwe Ziyoni. Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse, tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.” Koma anthuwo maganizo a Chauta saŵadziŵa, zimene Iye akukonzekera, iwo sazimvetsa. Sadziŵa kuti Iye waŵaunjika ngati mitolo ya tirigu pa malo opunthira. Yamba kupuntha iwe Ziyoni, ndidzakusandutsa wamphamvu ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo, ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa. Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu, zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta, chuma chao udzachipereka kwa Ambuye a dziko lonse lapansi. Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta. Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:34

“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:14

Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:31-32

“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri. Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:13

Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:7-9

Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai. Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima. Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:9

Tisatope nkuchita zabwino, chifukwa pa nthaŵi yake tidzakolola, ngati sitilefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:3-4

Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:6

Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:12

Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:14

Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:10

Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:5

Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:17

Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:4

Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:3

Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga wachikondi, mzimu wanga ukutamanda dzina lanu ndi kukongola kwa chiyero chanu. Ndinu wamkulu, wabwino, wangwiro. Ndikuona chikondi chanu mmawa uliwonse, ndikuzunguliridwa ndi chifundo chanu chachikulu. Zikomo chifukwa chokhala nane nthawi zonse, chifukwa ndinu mphamvu yanga, amene amandilimbikitsa. Zikomo chifukwa cha banja lomwe mwandipatsa, chifukwa cha zonse zomwe ndili nazo, ndipo chifukwa chokhala mtendere wanga pakati pa mkuntho. Zikomo chifukwa cha zinthu zonse, chifukwa ndikudziwa kuti chisamaliro chanu chimakhalapo kosatha kwa onse okukhulupirirani. Tsopano Ambuye, ndikupempha kuti chifuniro chanu chilamulire dziko lino, kuti muchite mogwirizana ndi maganizo anu, ndi kuti muteteze miyoyo. Ndikudziwa kuti tili m'masiku otsiriza, ndipo Mawu anu amati tidzamva za nkhondo ndi mphekesera za nkhondo, koma mitima yathu isachite mantha. Ndikukupemphani kuti mutithandize kukhala chete m'chiyembekezo chomwe tili nacho mwa Inu. Atate wokondedwa, tibiseni pamalo anu otetezeka, ndipo mutenge ulamuliro pa zinthu zonse. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa