Ndili ndi chisoni nthawi zina, ndipo izi sizoipa ayi. Ngakhale Yesu analira pamene anamva kuti Lazaro, bwenzi lake, wamwalira (Yohane 11:35). Ndikofunika kutiuza Mulungu zomwe tikumva tikamva chisoni.
M’malemba oyera mumapezeka mtendere ndi mpumulo. Nthawi za chisoni ndi zovuta zimatha kutithandiza ndiponso kuthandiza ena amene akufunika kuona kuti pali chiyembekezo ngakhale pakati pa mavuto.
Lolani Mulungu akhale pothawirapo panthawi zovuta, ndipo mudzaona chikondi chake chikukulimbitsani. Musamafufuze kwina kuti mupeze chitonthozo; m’manja mwa Yesu mokha ndi momwe mungapezere mtendere umene moyo wanu ukufuna.
Chitonthozo chake chimalimbikitsa mzimu wanu ndikukupatsani mphamvu zopitirira, pakuti misozi ingakhalepo usiku wonse, koma chimwemwe chidzabwera m’mawa mwa Yesu.
Zimenezi zikadandisangalatsa, ndikadakondwa nazo kwambiri ngakhale zipweteke chotani, podziŵa kuti sindidakane mau a Woyera uja.
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
“Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
“Pakuti sadanyoze munthu wozunzika, sadaipidwe ndi masautso ake, sadamubisire nkhope yake, koma adamumvera pamene adamdandaulira.”
M'maso mwanga mwada ndi chisoni. Tsiku ndi tsiku ndimakuitanani, Inu Chauta, Ndimakweza manja anga kwa Inu.
Inu ana anga, monga mkazi amamva zoŵaŵa pochira, inenso ndikumva zoŵaŵa chifukwa cha inu mpaka moyo wa Khristu ukhazikike mwa inu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Paja chisoni chokomera Mulungu chimamtembenuza munthu ndi kumpulumutsa, kotero kuti chisoni chake chimathera pomwepo. Koma kumva chisoni monga m'mene amachitira anthu odalira zapansipano, kumadzetsa imfa.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
“Ndithudi, iye adapirira masautso amene tikadayenera kuŵamva ifeyo, ndipo adalandira zoŵaŵa zimene tikadayenera kuzilandira ifeyo. Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumlanga, ndi kumkantha ndi kumsautsa.
Tsono Nehemiya adapitiriza nati, “Kazipitani, mukachite phwando ku nyumba, kenaka muŵapatseko anzanu amene sadakonze kanthu. Pakuti lero ndi tsiku loyera kwa Chauta, Mulungu wathu. Tsono musakhale ndi chisoni, popeza kuti chimwemwe chimene Chauta amakupatsani, chimakulimbikitsani.”
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathe kukugonjetsa iwe Yoswa, nthaŵi yonse ya moyo wako. Ine ndidzakhala nawe monga momwe ndidakhalira ndi Mose, sindidzakusiya konse.
Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola, komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.
Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Angathe kulanga mwankhalwe, komabe adzaonetsa chifundo, chifukwa chikondi chao nchochuluka. Savutitsa mwadala, sakonda kusautsa munthu aliyense.
“Mtengo chiyembekezo chake nchakuti akaudula udzaphukanso, nthambi zake sizidzaleka kuphuka.
“Munthu wobadwa mwa mkazi amakhala masiku oŵerengeka, komanso masiku ake ndi amavuto okhaokha. Koma munthu akafa, kutha kwake nkomweko. Kodi munthuyo akafa, amapita kuti? Monga madzi amaphwa m'nyanja, monganso mtsinje umaphwa nuuma, momwemonso munthu amagona pansi osadzukanso. Mpaka zamumlengalenga zidzatha, iyeyo sadzadzuka. Palibe aliyense angamdzutse kutulo kwake. Ha! Achikhala mudaangondibisa ku manda, kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita. Achikhala mudaangondiikira nthaŵi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. Kodi munthu atafa, nkudzakhalanso ndi moyo? Koma masiku onse a moyo wanga wovutikawu, ndidzadikira mpaka kumasulidwa kwanga kutafika. Inu mudzandiitana, ine nkukuyankhani. Mudzafunitsitsanso kuwona ine, ntchito ya manja anune. Nthaŵiyo mudzayang'ana mayendedwe anga onse, koma simudzalondoloza machimo anga. Zolakwa zanga zidzakhululukidwa, Inu mudzafafaniza machimo anga onse. “Komabe monga phiri limagwa nkuswekasweka, ndipo thanthwe limasendezeka kuchoka pamalo pake, monganso madzi oyenda amaperesa miyala, ndipo madzi othamanga amakokolola nthaka, momwemonso Inu mumaononga chiyembekezo cha munthu. Amaphuka ngati duŵa, kenaka nkufota. Sakhalitsa, amathaŵa ngati mthunzi.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango. Ambuye adzandipulumutsanso ku chilichonse chofuna kundichita choipa, ndipo adzandisunga bwino mpaka kundiloŵetsa mu Ufumu wake wa Kumwamba. Kwa Iye kukhale ulemerero kwamuyaya. Amen.