Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, n’zosavuta kugwidwa ndi mantha komanso kusadziwa choti chingachitike. Koma Baibulo limatipatsa chiyembekezo ndi mphamvu. Pakati pa chisokonezo ndi kutaya mtima, tingapeze chitonthozo mu lonjezo la Mulungu loti adzakhala nafe, ngakhale m’nthawi zovuta kwambiri. Monga mmene lemba la Masalmo 46:1-2 limanenera, “Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezeka msanga m’masautso. Chifukwa chake sitidzachita mantha, ngakhale dziko litasunthika, ndipo mapiri atagwera mkati mwa nyanja.”
Yesu, m’buku la Yohane 16:33, anatiuza, “Ndanena izi kwa inu kuti mukhale ndi mtendere mwa Ine. M’dziko lapansi mudzakhala ndi chisautso; koma limbikani mtima; Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
Ndi nthawi ya nkhondo ndi mavuto, tikumbukire kuti zida zathu zenizeni si za thupi, koma zauzimu. Pemphero, chikhulupiriro, ndi chiyembekezo ndi zida zathu zamphamvu kwambiri. Tikamaika maganizo ndi mitima yathu pa Mulungu, tingathe kuthana ndi mavuto aliwonse molimba mtima komanso modzidalira.
Mulungu akutiitana kuti tikhale kuunika pakati pa mdima, kuti tikhale ofalitsa chiyembekezo ndi chikondi m’nthawi yovuta ino. Mwa zochita zathu ndi mawu athu, tingasonyeze chikondi ndi mtendere wa Khristu, kupereka chitonthozo ndi chithandizo kwa omwe akutizungulira.
M’nthawi yovuta ino, tidalira Mulungu, tigwire mwamphamvu lonjezo lake la chipulumutso, ndipo tilole chikondi chake chitsogolere miyoyo yathu.
Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?
Mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndipo adzakukwezani.
Abale, musamasinjirirana. Wosinjirira mbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo a Mulungu. Koma ukaweruza Malamulo a Mulungu, ndiye kuti sukuchita zimene Malamulowo akunena, ukudziyesa woweruza.
Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
Onani tsono, inu amene mukuti, “Lero kapena maŵa tipita ku mzinda wakutiwakuti, ndipo tikachitako malonda chaka chimodzi kuti tikaphe ndalama,”
m'menemo inuyo zamaŵa simukuzidziŵa. Kodi moyo wanu ngwotani? Pajatu inu muli ngati utsi chabe, umene umangooneka pa kanthaŵi, posachedwa nkuzimirira.
Kwenikweni muyenera kumanena kuti, “Ambuye akalola, tikakhala ndi moyo, tidzachita chakutichakuti.”
Koma monga zilirimu, mumanyada ndi kudzitama. Kunyada konse kotere nkoipa.
Munthu akadziŵa zabwino zimene ayenera kuchita, napanda kuzichita, ndiye kuti wachimwa.
Mumalakalaka zinthu, koma zimakusoŵani, nchifukwa chake mumapha munthu. Mumasirira zinthu, koma simungathe kuzipeza, nchifukwa chake mumamenyana, nkumachita nkhondo. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu.
popeza kuti mukudalirabe zapansipano. Pakati panu pali kaduka ndi kukangana. Nanga zimenezi sizikutsimikiza kuti mukudalirabe zapansipano, ndipo kuti mumachita monga momwe amachitira anthu odalira zapansipanozo?
Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.
Atamandike Chauta, thanthwe langa londitchinjiriza, amene amaphunzitsa manja anga ndi zala zanga kumenya nkhondo.
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
Mukadzapita kukamenyana ndi adani anu, ngati muwona kuti magaleta ao ngochuluka kuposa anu, ngamira zao ndi zochulukanso, ndipo ngakhale ankhondo ao omwe ngokuposani, musakaŵaope. Chauta, Mulungu wanu, amene adakupulumutsani ku Ejipito, adzakhala nanu.
Anthu a ku Yuda adagwira anthu ena amoyo okwaniranso 10,000. Adakwera nawo pamwamba pa thanthwe, naŵaponya pansi kuchoka pamenepo. Ndiye onsewo adangotekedzeka.
Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa.
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
Chauta, Mulungu wanu, apita nanu Iye yemwe kuti akuthandizeni pa nkhondoyo ndipo kuti akupambanitseni.”
Koma Chauta adandiwuza kuti, ‘Iwe udapha anthu ambiri ndipo udamenya nkhondo zikuluzikulu. Chifukwa cha zimenezi, sindiwe amene udzandimangire nyumba ai.
Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.
Anthu onse amene asonkhanaŵa adzadziŵa kuti Chauta sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo wokha. Wopambanitsa pa nkhondo ndi Chauta, ndipo akuperekani m'manja mwathu.”
Amaphunzitsa manja anga kamenyedwe ka nkhondo, kotero kuti ndingathe kupinda uta wachitsulo.
Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Chauta Wamphamvuzonse ali nafe, Mulungu wa Yakobe ndiye kothaŵira kwathu.
Nchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisinthike, ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja zozama,
ngakhale nyanja zikokome ndi kututuma. Ngakhale mapiri anjenjemere ndi kulindima kwa nyanja.
Kumeneko adathyola mivi youluzika, zishango, malupanga ndi zida zonse zankhondo za adani ake.
Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Ndithu, nsapato iliyonse ya munthu wankhondo ndi chovala chilichonse chothonyezekera magazi, zidzatenthedwa pa moto ngati nkhuni.
Chauta adandiwuza kuti, “Monga momwe mkango kapena msona wa mkango umabangulira utagwira nyama, ndipo abusa sangaupirikitse, ngakhale auwopseze ndi kufuula chotani, motero palibe chimene chingaletse Chauta Wamphamvuzonse kutchinjiriza Phiri la Ziyoni ndi gomo lake.
Chauta akupita ku nkhondo ngati ngwazi, akuutsa ukali wake ngati munthu wankhondo. Akukuŵa, akufuula mfuu zankhondo. Akuwonetsa mphamvu zake pakuposa adani ake.
Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.
Iwe Babiloni ndiwe nyundo yanga, chida changa chankhondo: ndi iwe ndimaphwanyaphwanya mitundu ya anthu, ndimaononga maufumu.
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya akavalo ndi okwerapo ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya magaleta ndi oyendetsa ake.
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya amuna ndi akazi ao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya nkhalamba ndi achinyamata. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya anyamata ndi anamwali.
Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abusa ndi ziŵeto zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya alimi ndi ng'ombe zao. Ndi iwe ndimaphwanyaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri ankhondo.
Ndithudi layandikira, tsiku la Chauta lili pafupi. Tsiku lamitambo, tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu.
Okhala m'mizinda ya Aisraele adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo zosiyidwa kuti azitenthe ngati nkhuni: ndiye kuti zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga ndi mikondo. Adzazisonkhere moto pa zaka zisanu ndi ziŵiri.
Naŵa mau a Amosi amene ankaŵeta nkhosa ku Tekowa. Zimenezi, zodzachitikira Aisraele, Chauta adamuululira pa nthaŵi ya Uziya, mfumu ya ku Yuda, ndi pa nthaŵi ya Yerobowamu, mwana wa Yowasi, mfumu ya ku Israele, kutatsala zaka ziŵiri kuti chivomezi chija chichitike.
“Mulengeze pakati pa anthu a mitundu ina kuti, ‘Konzekerani nkhondo, itanani ankhondo amphamvu. Asilikali onse afike pafupi, ayambe nkhondo.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe.
Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,
Kodi ndinenenso chiyani tsopano? Nthaŵi yachepa yoti ndinene za anthu enanso ambiri monga Gideoni, Balaki, Samisoni, Yefita, Davide, Samuele ndiponso aneneri.
Pokhala ndi chikhulupiriro anthu ameneŵa adagonjetsa maufumu, adakhazikitsa chilungamo, ndipo adalandira zimene Mulungu adaaŵalonjeza. Ena adapuya mikango pakamwa,
ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.
Abramu atamva kuti mbale wake wagwidwa, adasonkhanitsa anthu ake odziŵa kumenya nkhondo. Onse pamodzi analipo 318, ndipo adalondola mafumu aja njira yonse mpaka ku Dani.
Atafika kumeneko, adagaŵa anthu ake m'magulu, ndipo iye ndi anthu ake adakamenyana nawo ndi usiku mpaka kuŵagonjetseratu. Adaŵapirikitsa mpaka ku Hoba, kumpoto kwa Damasiko,
ndipo adaŵalanda zao zonse. Adabwera naye Loti, mwana wa mbale wake, pamodzi ndi zake zonse, kuphatikizapo akazi ndi anthu ena onse.
Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzakutsogolerani, ndipo adzaponyanso nkhondo m'malo mwanu, monga momwe mudaonera ku Ejipito kuja
Musaŵaope, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, ndiye amene adzaponye nkhondo pamodzi nanu.”
Pamenepo akuluakuluwo adzafunsanso anthu kuti, “Kodi alipo pano wina aliyense amene akuwopa ndipo mtima wake wafumuka ndi mantha? Ngati alipo, abwerere kwao, kuti angamakadederetse anzake.”
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Tsono Yoswa adauza akuluakuluwo kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Mukhale amphamvu ndiponso mulimbe mtima, poti Chauta adzaŵachita zimenezi adani anu onseŵa.”
“Pakuti atsogoleri adatsogoleradi m'dziko la Israele, ndipo anthu adadzipereka okha mwaufulu, tamandani Chauta.
Apo magulu ena aŵiri aja nawonso adaimba malipenga, naswa mbiya zija, onse atatenga nsakali zija m'dzanja lakumanzere, ndi malipenga oti aziimba m'dzanja lamanja. Ndipo adafuula kuti, “Lupanga la Chauta ndi la Gideoni.”
Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa.
Yonatani adapha mkulu wa ankhondo wachifilisti amene anali ku Geba, ndipo Afilisti adamva zimenezi. Apo Saulo adatuma amithenga kuti alize lipenga lankhondo m'dziko lonselo, nanena kuti, “Ahebri amve.”
Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.”
Pa moyo wake wonse Saulo ankakhalira kuchita nkhondo ndi Afilisti. Tsono ankati akaona munthu wamphamvu kapena wolimba mtima, ankamulemba m'gulu lake lankhondo.
Afilisti adasonkhanitsa magulu ao ankhondo ku Soko, m'dziko la Yuda. Adamanga zithando zao pakati pa Soko ndi Azeka ku Efesi-Damimu.
Tiwonane lero lino basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.”
Atamva mau a Mfilistiyo, Saulo ndi Aisraele onse adachita mantha nathyoka m'nkhongono.
Davide anali mwana wa Mwefurati wa ku Betelehemu dzina lake Yese, amene anali ndi ana aamuna asanu ndi atatu. Pa nthaŵi ya ufumu wa Saulo, Yese anali atakalamba kale kwambiri.
Ana ake aamuna anali aŵa: Eliyabu mwana wake wachisamba, wachiŵiri Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama.
Davide anali mzime. Ana akuluakulu atatuwo ndiwo anali ku nkhondo ndi Saulo.
Koma Davide ankapita ku zithando za Saulo, namabwerako nthaŵi zina kukaŵeta nkhosa za bambo wake ku Betelehemu.
Pa masiku makumi anai Goliyati uja adakhala akutuluka, namadziwonetsa m'maŵa ndi madzulo.
Tsiku lina Yese adauza mwana wake Davide kuti, “Abale ako uŵatengere makilogramu khumi a tirigu wokazinga, ndi mitanda khumi yabulediyi, ndipo upite nazo mofulumira ku zithando zao.
Utengenso mphumphu khumizi za tchizi, upite nazo kwa mkulu wolamulira ankhondo. Ukaone m'mene abale ako akukhalira, ndipo ubwereko ndi chizindikiro china chosonyeza kuti ali bwino.
Saulo, abale akowo ndi Aisraele ena, akumenyana nkhondo ndi Afilisti ku chigwa cha Ela.”
Saulo adasonkhanitsa Aisraele, namanga zithando zao zankhondo m'chigwa cha Ela, nandanditsa gulu lankhondo kuti amenyane ndi Afilistiwo.
Limba mtima, ndipo tichite chamuna chifukwa cha anthu athu, ndiponso chifukwa cha mizinda ya Mulungu wathu. Chauta achite zimene zimkomere.”
Pa nyengo yophukira mitengo, nthaŵi imene mafumu ankakonda kukamenya nkhondo, Davide adatuma Yowabu ndi atsogoleri ake ndi ankhondo a Aisraele onse. Adaononga Aamoni, nazinga mzinda wa Raba ndi zithando zankhondo. Koma Davide adatsalira ku Yerusalemu.
Kwao kuja akuluakulu a mfumu ya ku Siriya adauza mfumu yao kuti, “Milungu ya anthu a ku Israele ndi milungu yam'mapiri, nchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambanira ife. Koma tiyeni tikamenyane nawo ku chigwa, ndithudi tidzaŵapambana.
Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.”
Ndiye usiku umenewo mngelo wa Chauta adapita ku zithando zankhondo za Aasiriya naphako asilikali 185,000. M'maŵa mwake adangoona asilikaliwo ali ngundangunda, atafa onsewo.
Adani ena ambiri adaphedwa, pakuti Mulungu ankaŵathandiza pa nkhondoyo. Choncho anthuwo adakhala bwino kumeneko mpaka nthaŵi yotengedwa ukapolo ija.
Pamenepo Davide adapita ku Baala-Perazimu, ndipo adagonjetsa Afilistiwo kumeneko. Tsono adati, “Ndi dzanja langa Mulungu waŵang'amba pakati adani anga ngati madzi a chigumula.” Nchifukwa chake malo amenewo amatchedwa kuti Baala-Perazimu.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Koma inu limbani mtima, manja anu asafooke chifukwa mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”
Tsono anthuwo adadzuka m'mamaŵa nakaloŵa m'chipululu cha ku Tekowa. Pamene ankatuluka, Yehosafati adaima nati, “Tamverani inu anthu a ku Yuda ndi inu okhala mu Yerusalemu. Khulupirirani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalimbika, khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzapambana.”
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Anthu oipa amasolola lupanga, ndipo amakoka mauta, kuti aphe anthu ovutika ndi osoŵa, amene amayenda molungama.
Adzapulumutsa moyo wanga pa nkhondo imene ndikumenya, pakuti anthu ambiri akukangana nane.
Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo.
Inu Mulungu, musakhalenso chete. Musangoti phee, musangoti duu, Inu Mulungu.
amene adaŵaononga ku Endori, ndi kuŵasandutsa ndoŵe m'nthaka.
Akalonga ao muŵachite zomwe mudachita Orebu ndi Zeebu, ndipo ana a mafumu ao onse, muŵachite zomwe mudachita Zeba ndi Zalimuna,
amene adati, “Tiyeni tilande dziko la Mulungu likhale lathu.”
Inu Mulungu wanga, muŵasandutse ngati fumbi louluka ndi kamvulumvulu, akhale ngati mankhusu ouluka ndi mphepo.
Monga momwe moto umatenthera nkhalango, monga momwe malaŵi amayakira pa mapiri,
momwemonso Inu muŵapirikitse ndi mkuntho, ndipo muŵaopseze ndi kamvulumvulu wanu.
Inu Chauta, muŵachititse manyazi, kuti azifunafuna dzina lanu.
Achitedi manyazi ndi mantha mpaka muyaya, ndipo afe imfa yonyozeka.
Adziŵe kuti Inu nokha, amene dzina lanu ndinu Chauta, ndinu Wopambanazonse wolamulira dziko lonse lapansi.
Onani, adani anu akuchita chiwawa. Amene adana nanu akukuukirani.
Akuchitira anthu anu upo wonyenga. Akuŵapangira zoipa anthu anu amene mumaŵateteza.
Iwo amati, “Tiyeni tifafanize mtundu wao wonse. Dzina la Israele lisakumbukikenso.”
Ng'ambani thambo, Inu Chauta, ndi kutsikira pansi. Khudzani mapiri kuti afuke nthunzi.
Ng'animitsani zing'aning'ani ndi kuŵamwaza adani anga. Ponyani mivi yanu, ndi kuŵapirikitsa.
“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu, chatsopano, cha mano akuthwa. Udzanyenya mapiri ndi kuŵaphwanyaphwanya. Magomo udzaŵasandutsa mankhusu.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Musataye mtima. Musaope maphephe amene awanda m'dziko monse. Chaka ndi chaka pamabuka ndithu maphephe onena za nkhondo pa dziko lapansi, ndiponso zakuti mfumu yakutiyakuti ikumenyana ndi inzake.
Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele.
Makamu ndi makamu a anthu ali m'Chigwa cha Chiweruzo. Ndithu tsiku la Chauta layandikira m'Chigwa cha Chiweruzo.
Zimene akunena Chauta ndi izi: “Chifukwa Amowabu akunka nachimwirachimwira, sindileka kuŵalanga. Iwo adanyoza mafupa a mfumu ya ku Edomu poŵatentha mpaka kuŵasandutsa phulusa.
“Posachedwapa lifika tsiku la Chauta pamene Iye adzaweruza mitundu yonse ya anthu. Aedomu inu, adzakuchitani zomwe mudaŵachita ena. Zimene mudachitazo zidzakubwererani.
Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo adzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzangogwira pakamwa, ndi kutseka makutu motaya mtima.
Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.
Apo Yesu adamuuza kuti, “Bwezera lupangalo m'chimake, pakuti onse ogwira lupanga adzaphedwa ndi lupanga.
Ndipo pamene mudzamva za nkhondo ndi za zipoloŵe, musadzachite mantha. Zimenezi zidzayenera kuyamba zaoneka, koma sindiye kuti chimalizo chifika nthaŵi yomweyo.”
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Munkanyamula hema la Moleki, ndi nyenyezi ya mulungu wanu Refani, mafano amene mudaŵapanga kuti muziŵapembedza. Ndidzakuchotsani kukutayani kutali, kupitirira dziko la Babele.’
Atamgwira, adamtsekera m'ndende, nampereka kwa magulu anai a asilikali kuti azimlonda, gulu lililonse asilikali anai. Tsono Herode ankafuna kuzenga mlandu wake pamaso pa anthu onse, chikondwerero cha Paska chitapita.
pakuti iyeyo ndi mtumiki wa Mulungu wokutsogolera kuchita zabwino. Koma ngati ukuchita zoipa uwope, pakuti ali ndi mphamvu ndithu zokulanga. Iye ndi mtumiki wa Mulungu wogwetsa mkwiyo wa Mulungu pa wochita zoipa, pomulanga.
Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Pakuti khalidwelo limalakalaka zotsutsana ndi zimene Mzimu Woyera afuna, ndipo zimene Mzimu Woyera afuna zimatsutsana ndi zimene khalidwe lokonda zoipalo limafuna. Ziŵirizi zimadana, kotero kuti simungachite zimene mufuna kuchita.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Koma ife, popeza kuti zathu nzausana, tisamaledzera. Tikhale titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala chachitsulo chapachifuwa. Ndipo ngati chisoti choteteza kumutu tivale chiyembekezo chakuti tidzapulumuka.
Nchifukwa chake ife timakunyadirani, m'mipingo yonse ya Mulungu, chifukwa cha kulimbika kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso ndi mazunzo onse amene adakugwerani.
Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,
ena adazimitsa moto waukali, ndipo ena adapulumuka, osaphedwa ndi lupanga. Anali ofooka, koma adalandira mphamvu. Adasanduka ngwazi pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani ao.
Kodi nkhondo zimachokera kuti? Kukangana pakati panu kumachokera kuti? Kodi suja zimachokera ku zilakolako zanu zathupi, zimene zimachita nkhondo mwa inu?
Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo,
Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama.
Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo.
Yesu adaadziŵa zimenezi, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo anthu a m'mudzi uliwonse kapena a m'banja lililonse akayamba kuukirana, mudzi wotere kapena banja lotere silingalimbe ai.
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.
Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana, ndipo kudzakhala njala. Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.
“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri.
Yesu adaŵauza kuti, “Koma tsopano amene ali ndi thumba la ndalama, asalisiye. Chimodzimodzinso thumba lake lapaulendo. Ndipo amene alibe lupanga, agulitse mwinjiro wake nkugula lupanga.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Tithokoze Mulungu amene mwa Khristu amatitsogolera nthaŵi zonse m'kupambana kwake. Kudzera mwa ife Mulungu akupatsa anthu onse nzeru zodziŵira Khristu, ndipo nzeruzo zikuwanda ponseponse ngati fungo labwino.
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.
osalola kuti adani anu azikuwopsezani pa kanthu kalikonse. Zimenezi zidzaŵatsimikizira kuti iwowo adzaonongeka, koma inu mudzapulumuka. Mulungu ndiye amene adzakuchitirani zimenezi.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye.
Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.
Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu.
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.
Inu Chauta, ndinu olungama, munditsogolere pakati pa adani ondizonda. Mundikonzere njira yoongoka kuti ndidzeremo.
Paja ndinu mudandipatsa mphamvu zomenyera nkhondo, ndinu mudandigonjetsera anthu ondiwukira.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
Ngakhale gulu lankhondo lindizinge, mtima wanga sudzachita mantha konse. Ngakhale nkhondo ibuke kulimbana nane, ine sindidzaleka kukhulupirira.
Amaletsa nkhondo mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amathyola uta, ndi kupokonyola mkondo. Amatentha magaleta ankhondo ndi moto.
Amasungira anthu olungama nzeru zenizeni, ali ngati chishango choteteza oyenda mwaungwiro.
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
Pa masiku akudzaŵa phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.
Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza.
Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'ming'alu yam'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.
Musakhulupirirenso munthu, poti moyo wake sukhalira kutha. Nanga iye nkumuyesanso kanthu ngati!
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.
Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Pa masiku akudzaŵa, phiri la Nyumba ya Chauta adzalisandutsa lalitali koposa mapiri ena onse, lidzangoti joo pamwamba pa magomo onse. Mitundu yonse ya anthu idzathamangira ku phiri limenelo.
Muphiriphithe ndi kubuula, inu anthu a ku Ziyoni, ngati mkazi pa nthaŵi yake yochira. Pakuti tsopano mudzachoka mumzindamo, mukakhala mumidzi. Mudzachotsedwa kupita ku Babiloni. Komabe kumeneko mudzapulumutsidwa, kumeneko Chauta adzakuwombolani kwa adani anu.
Tsopano mitundu yambiri yasonkhana kuti imenyane ndi iwe Ziyoni. Ikunena kuti, “Tiyeni timuipitse, tiwone kutha kwake kwa mzinda wa Ziyoniwu.”
Koma anthuwo maganizo a Chauta saŵadziŵa, zimene Iye akukonzekera, iwo sazimvetsa. Sadziŵa kuti Iye waŵaunjika ngati mitolo ya tirigu pa malo opunthira.
Yamba kupuntha iwe Ziyoni, ndidzakusandutsa wamphamvu ngati nkhunzi ya nyanga zachitsulo, ngati nkhunzi ya ziboda zamkuŵa. Udzatswanya mitundu yambiri ya anthu, zimene adapindula udzazipereka kwa Chauta, chuma chao udzachipereka kwa Ambuye a dziko lonse lapansi.
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko amphamvu, ngakhale akutali omwe. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
“Kodi mukuyesa kuti ndidadzapereka mtendere pansi pano? Sindidadzapereke mtendere ai, koma nkhondo.
Asilikali omwe adamufunsa kuti, “Nanga ifeyo tizichita zabwino zanji?” Iye adati, “Musamalanda za munthu aliyense pakuwopseza kapena pakumnamizira. Muzikhutira ndi malipiro anu.”
“Chimodzimodzinso kodi ndi mfumu iti, popita ku nkhondo kukamenyana ndi mfumu ina, siiyamba yakhala pansi nkuganiza bwino? Imaganiziratu ngati ndi asilikali zikwi khumi ingathe kukamenyana ndi mfumu ina ija, imene ikubwera ndi asilikali zikwi makumi aŵiri.
Tsono ngati siingathe, idzatuma nthumwi kukapempha mtendere, mfumu ina ija ikali kutali.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai.
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.
Khristu ndiye moyo wanu weniweni tsopano, choncho pamene Iye adzaonekerenso, inunso mudzaonekera mu ulemerero pamodzi naye.
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Ngwodala munthu amene amalimbika pamene ayesedwa, pakuti atapambana, adzalandira moyo. Moyowo ndi mphotho imene Ambuye adalonjeza anthu oŵakonda.
Koma ngakhale mumve zoŵaŵa chifukwa cha chilungamo, mudzakhala odala ndithu. Musachite mantha ndi anthu, kapena kuvutika mu mtima,
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Motero aliyense amene adzapambane, adzamuvekanso zovala zoyera. Dzina lake sindidzalifafaniza m'buku la amoyo, ndipo ndidzamchitira umboni pamaso pa Atate anga, ndi pamaso pa angelo ao.
Pakuti Mwanawankhosa uja amene ali pakatikati pa mpando wachifumu, adzakhala Mbusa wao, adzaŵatsogolera ku akasupe a madzi amoyo. Ndipo Mulungu adzaŵapukuta misozi yonse m'maso.”
Iye adzaŵapukuta misozi yonse m'maso mwao. Sipadzakhalanso imfa, chisoni, kulira, kapena kumva zoŵaŵa. Zakale zonse zapitiratu.”
Mumzindamo simudzapezekanso kanthu kalikonse kotembereredwa ndi Mulungu. Mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja udzakhala m'menemo, ndipo atumiki ake adzampembedza.