Mulungu ndiye mlengi wako, mtetezi wako, wosamalira wako. Ndi wamphamvuzonse, wachifundo, wokhululuka, wabwino. Tingadziwe Mulungu kudzera m'mawu ake. Amakuikira mtima ndipo wakupangira dongosolo labwino pa moyo wako.
Amadziwa zonse zisanachitike. Ndi chikondi chosatha. Pakuti Ine Yehova ndine Mulungu wako, wakugwira dzanja lako lamanja, nanena ndi iwe, Usawopa; Ine ndikuthandiza. (Yesaya 41:13)
Choncho Mulungu nthawi zonse adzakhala nafe, timangofunika kumuyandikila. Iye ndiye mlengi ndi wosamalira zinthu zonse, amene anapulumutsa dziko kudzera mwa Mwana wake, Yesu Khristu.
“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya.
Mzinda umenewu udzamveketsa mbiri yanga yabwino, ndipo udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemu. Anthu a mitundu yonse pansi pano adzanditamanda ndi kundilemekeza pakumva za zabwino zonse zimene ndauchitira mzinda umenewu. Adzachita mantha ndi kunjenjemera, poona kuti mzindawo ndaupatsa madalitso ndi zokoma zosaŵerengeka.”
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri. Nwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Koma ine sindidzaleka kukondwera, ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobe mpaka muyaya.
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira. Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu.
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake!
Koma ine ndidzapereka nsembe kwa Inu ndi mau okuthokozani. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita ndithu. Chipulumutso nchochokera kwa Inu Chauta.”
Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Tsono nanenso ndidzalalika za kulungama kwanu. Ndidzakutamandani masiku onse, Inu Chauta.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.”
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
“Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Sitidzabisira ana ao, koma tidzafotokozera mbadwo wakutsogolo ntchito zotamandika za Chauta, tidzaŵasimbira mphamvu zake ndi zodabwitsa zimene wakhala akuchita.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.
Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pa busa lanu, tidzakuthokozani mpaka muyaya, tidzakutamandani m'mibadwo yonse.
Ndidzakutamandani pa msonkhano waukulu chifukwa cha zimene mwandichitira. Zimene ndidalonjeza ndidzazichita pamaso pa onse okumverani.
Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.
Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti, “Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake, inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.”
Pambuyo pake abusa aja adabwerera akuyamika ndi kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anali atamva ndi kuziwona. Zonse zinali monga momwe mngelo uja adaaŵauzira.
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Apo Yesu adati, “Choka, Satana! Paja Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye, Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera, idzakuŵeramirani, Inu Ambuye, ndipo idzalemekeza ukulu wanu.
Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Bwerani ndi zopereka, ndipo muloŵe m'mabwalo a Nyumba yake. Pembedzani Chauta waulemerero ndi woyera.
Musadzapembedze mulungu wina aliyense, chifukwa Chauta amene dzina lake ndi Kansanje, ndi Mulungu wansanjedi.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Paja ifeyo ndiye oumbala enieni, ife amene timapembedza Mulungu motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Timanyadira Khristu Yesu, osadalira miyambo ya thupi chabe.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.”
Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Koma ine ndidzatha kuloŵa m'Nyumba mwanu chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu. Ndidzaŵeramitsa mutu pansi, kupembedza Inu m'Nyumba yanu yoyera.
Amandipembedza inde, koma kupembedza kwaoko nkopanda phindu, chifukwa zimene amaphunzitsa ngati zophunzitsa zenizeni ndi malamulo a anthu chabe.’ ”
Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.
Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu.
Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu.
Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu.
Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa
mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga.
Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga.
mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.
Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama.
Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja.
Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu.
Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu.
Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu.
Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera.
Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zotamanda mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.
Mulungu ndiye Mfumu ya dziko lonse lapansi. Imbani mwaluso nyimbo zotamanda.
Muziwopa Chauta, Mulungu wanu. Muzipembedza Iye yekha, ndipo mukamalumbira, muzitchula dzina lake lokha.
Angelo onse adaimirira kuzungulira mpando wachifumu uja, kuzunguliranso Akuluakulu aja ndi Zamoyo zinai zija. Angelowo adadzigwetsa chafufumimba patsogolo pa mpando wachifumuwo, napembedza Mulungu.
Adati, “Amen! Mulungu wathu alandire matamando, ulemerero, nzeru, chiyamiko, ulemu, mphamvu ndi nyonga mpaka muyaya. Amen.”
Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.
Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.”
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa.
Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Ndidzatamanda dzina la Mulungu pomuimbira nyimbo, ndidzalalika ukulu wake pomuthokoza.
Zimenezi zidzakondwetsa Chauta kupambana nsembe, ngakhale nsembe ya ng'ombe yamphongo.
Apo Yesu adati, “Malembo akuti, ‘Uzipembedza Ambuye Mulungu wako, ndipo uziŵatumikira Iwo okha.’ ”
Adasiya zoona za Mulungu namatsata zabodza. Adayamba kupembedza ndi kutumikira zolengedwa m'malo mwa kupembedza ndi kutumikira Mlengi mwini, amene ali woyenera kumlemekeza mpaka muyaya. Amen.
Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”