“Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse, chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati, “Aleluya! Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
“Ndimalenga kuŵala ndi mdima, ndimadzetsa madalitso ndi tsoka. Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi.
Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake. Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire.
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
Pakuti Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wopambana milungu yonse, ndiponso ndi Ambuye oposa ambuye onse. Ndi wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, sakondera, ndipo salandira ziphuphu.
Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse. Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri. Palibe munthu amene angathe kulimbana naye, popanda kupwetekerapo.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa. Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse?
Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Iye amalamula ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amalonda mitundu ina ya anthu. Anthu oukira asadzikweze.
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
Komatu anthu ambirimbiri a mibadwo yosaŵerengeka amene amandikonda, namatsata malamulo anga, ndimaŵakonda ndi chikondi chosasinthika.
Mulungu, Chauta, adalenga zakuthambo ndi kuziyalika. Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka. Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo, ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo. Iyeyo akunena kuti,
Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’
Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Tsono iye adandiwuza kuti ndidziŵitse Zerubabele uthenga wa Chauta wakuti, “Inde udzapambana, koma osati ndi nkhondo kapena ndi mphamvu, koma ndi mzimu wanga.
Chauta ndiye mfumu. Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba. Iye adakhazikitsa dziko lapansi, silidzagwedezeka konse.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
“Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha? Mulungu wathu ndiye linga langa lolimba, wandichotsera zoopsa m'njira zanga.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake.
Ndidaonekera Abrahamu, Isaki ndi Yakobe ngati Mulungu Mphambe, koma sindidaŵadziŵitse dzina langa kuti ndine Chauta.
Musaŵaope anthu ameneŵa. Chauta Mulungu wanu ali nanu. Iyeyo ndiye Mulungu wamkulu woyeneradi kumuwopa.
Apo mngelo wa Chauta uja adamuwonekera namuuza kuti, “Chauta ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”
Komabe Iye adaŵapulumutsa malinga ndi ulemerero wa dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Koma Yesu adaŵauza kuti, “Atate anga akugwira ntchito mpaka tsopano, nanenso ndikugwira ntchito.”
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Koma ndakusungani ndi moyo kuti muwone mphamvu zanga, kuti mbiri yanga iwande pa dziko lonse lapansi.
Chauta adakuwonetsani zimenezi, kuti inu mudziŵe kuti Chauta yekha ndiye Mulungu, ndipo kuti palibenso wina.
Dzambatukani, Inu Chauta, dzambatukani! Valani dzilimbe. Dzambatukani monga momwe munkachitira masiku amakedzana, nthaŵi ya mibadwo yakale. Kodi sindinu uja mudaduladula Rahabu, chilombo cham'nyanja chija, ndi kubaya chinjoka cham'nyanja chija?
Chauta amene ali pamwamba, ndi wamphamvu kupambana kulindima kwa madzi ambiri, ndi wamphamvu kuposa mafunde am'nyanja.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake, ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”
Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Adandiwuzanso kuti, “Kwatha! Alefa ndi Omega ndine. Ndiye kuti, Woyamba ndi Wotsiriza ndine. Aliyense womva ludzu, ndidzampatsa mwaulere madzi a pa kasupe wa madzi opatsa moyo.
Kodi kapena woumba sangathe kuumba mbiya ziŵiri ndi dothi lomwelo, ina ya masiku apadera ina ya masiku onse?
Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu. Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala. Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.”
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu. Inu mumatumphutsa akasupe m'zigwa, mitsinje imayenda pakati pa mapiri. Imapatsa nyama zonse zakuthengo madzi akumwa, mbidzi zimapherapo ludzu. Mbalame zimamanga zisa pafupi ndi mitsinjeyo, zimaimba m'nthambi za mitengo. Inu mumathirira mapiri ndi madzi ochokera ku malo anu akumwamba. Dziko lapansi ladzaza ndi madalitso anu. Mumameretsa udzu kuti ng'ombe zidye, ndi zomera kuti munthu azilima ndi kupeza chakudya m'nthaka. Amapezamo vinyo wosangalatsa mtima wake, mafuta odzola kuti thupi lake lisisire, ndiponso buledi kuti ampatse mphamvu. Mitengo ya Chauta amaithirira ndi madzi ambiri, mikungudza ya ku Lebanoni imene adaibzala. Mbalame zimamanga zisa m'menemo, dokowe amamanga chisa m'mikungudzamo. M'mapiri aatali ndimo m'mene mumakhala mbalale, m'matanthwe ndimo m'mene mumathaŵira mbira. Inu mudapanga mwezi kuti uzisiyanitsa nyengo, ndipo dzuŵa limadziŵa nthaŵi yake yoloŵera. Mumadzifunditsa ndi kuŵala ngati chovala, mwatambasula mlengalenga ngati hema.
Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.
Ndidzasinkhasinkha za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu, ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa. Anthu adzasimba za mphamvu zanu zoopsa, inenso ndidzalalika za ukulu wanu.
Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula, akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi, kuyambira kotulukira dzuŵa mpaka koloŵera kwake.
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Koma Mulungu wa Yakobe sali ngati mafanowo, Iye ndiyedi Mlengi wa zonse. Aisraele ndi anthu ake amene Iye adaŵasankha, dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.
Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zake nzodabwitsa pakati pa anthu. Adasandutsa nyanja kuti ikhale nthaka youma. Anthu adaoloka mtsinje uja poyenda pansi. Nchifukwa chake timukondwerere Iye.
dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Ndine amene ndidalenga dziko lapansi ndi kulenga munthu kuti akhalemo. Ndidayalika zakuthambo ndi manja anga, ndipo tsopano ndimalamulira gulu lonse lamumlengalenga.
“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.
Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Mose adamuuza kuti, “Ndikangotuluka mumzinda muno, ndikweza manja anga kwa Chauta. Tsono mabingu ndi matalala aleka, kuti inuyo mudziŵe kuti dziko lonse lapansi ndi la Chauta.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika, Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu ndi kuŵalimbikitsa anthu ake. Mulungu atamandike.
Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake? Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
Ndi mphamvu zake adatontholetsa nyanja, ndi nzeru zake adakantha chilombo cham'madzi chija cha Rahabu.
Mumaonetsa chikondi chanu chosasinthika kwa anthu osaŵerengeka. Ndipo mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo ao. Inu Mulungu wamkulu ndi wamphamvu, dzina lanu ndinu Chauta Wamphamvuzonse. Zolinga zanu nzazikulu, ndipo ntchito zanu nzamphamvu. Maso anu amaona makhalidwe onse a anthu. Ndipo aliyense mumampatsa mphotho malinga ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake.
Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu, ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse. Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso. Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo. Mapemphero anga amkomere Chauta, popeza kuti ndimakondwa mwa Iye.
Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa.
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Tamanda Chauta, iwe Yerusalemu. Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni. Paja amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako. Amadalitsa anthu amene ali mwa iwe.
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga. Mverani nyimbo m'mahema mwa anthu a Mulungu, nyimbo zokondwerera kupambana, zakuti, “Dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu, dzanja lamanja la Chauta lapambana, dzanja lamanja la Chauta limagonjetsa mwamphamvu.”
Komabe Inu Chauta, ndinu Atate athu. Ife tili ngati mtapo, Inu muli ngati woumba. Mudatipanga tonse ndi manja anu.
Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo.
mwa mau oona, ndiponso mwa mphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili m'dzanja lathu lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
“Ndaninso kodi akuchokera ku Edomuyu, atavala zofiira za ku Bozira? Ndani ameneyu wovala zovala zokongola, akuyenda monyadira mphamvu zake? Ndi Ineyo, wolankhula zachilungamo, ndiponso wa mphamvu zoti nkupulumutsa.”
Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Palibe wolingana nanu, Inu Chauta. Inu ndinu aakulu, dzina lanu lili ndi mphamvu yaikulu.
Ndipo adati, “Chauta, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu Wakumwamba? Kodi suja mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu? M'manja mwanu muli mphamvu ndi nyonga, kotero kuti palibe ndi mmodzi yemwe woti nkulimbana nanu.
Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele. Iye yekha ndiye amene amachita zinthu zodabwitsa.
Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Chifukwa chiyani panalibe anthu, pamene ndidabwera kudzaŵapulumutsa? Chifukwa chiyani panalibe wondiyankha, pamene ndidaitana? Kodi dzanja langa nloti nkulephera kuwombola? Kodi kapena ndilibe mphamvu zopulumutsira? Nditangodzudzula chabe, nyanja yaikulu itha kuuma, ndipo mitsinje itha kusanduka chipululu. Chifukwa chosoŵa madzi nsomba zam'menemo nkuyamba kununkha, ndiponso kufa ndi ludzu.
Zoonadi, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye?
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”