Koma iwe, munthu chabe, ndiwe yani kuti nkumatsutsana ndi Mulungu? Kodi mbiya nkufunsa woiwumba kuti, “Bwanji mwandiwumba motere?” Kodi kapena woumba sangathe kuumba mbiya ziŵiri ndi dothi lomwelo, ina ya masiku apadera ina ya masiku onse?
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Munthu mumtima mwake amakonzekera zambiri, koma cholinga cha Chauta ndiye chimene chidzachitike.
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
“Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse, chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse.
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
“Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu.
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ndidakuyeretsa, komatu osati ngati siliva, ndidakuyesa m'ng'anjo yamasautso. Chifukwa cha ulemu wanga, ulemu wanga wokha, ndiye ndimachita zonse. Ndingalole bwanji kuti dzina langa linyozeke? Ulemerero wanga sindidzapatsa wina ai.”
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Zolengedwa zikupezeka lero lino chifukwa cha kulamula kwanu, pakuti zinthu zonse zimakutumikirani.
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Amaphimba zakumwamba ndi mitambo, amapatsa nthaka mvula, amameretsa udzu pa magomo. Amapereka chakudya kwa nyama ndi kwa ana a khungubwi pamene akulira chakudya.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo.
Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo?
Chauta ndiye mfumu. Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba. Iye adakhazikitsa dziko lapansi, silidzagwedezeka konse.
Mtima wa mfumu uli ngati mtsinje wa madzi m'manja mwa Chauta. Amauwongolera ku zimene Iyeyo akufuna.
Chauta amene amalamulira kumwambako akungoŵaseka ndi kuŵanyoza. Tsono adzaŵadzudzula ali wokwiya adzaŵaopseza ali wokalipa. Adzati, “Ine ndakhazika kale mfumu yanga, ili pa phiri langa loyera la Ziyoni.”
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Iye sachita zokondera kwa akuluakulu, kapena kulemekeza olemera kupambana osauka, pakuti onsewo Mulungu adaŵalenga ndi manja ake.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Tamandani Chauta! Tamandani Chauta inu okhala kumwamba, mtamandeni inu okhala mu mlengalenga! Inu nyama zakutchire ndi zoŵeta zonse, inu zinthu zokwaŵa ndi mbalame zouluka! Inu mafumu a pa dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse, inu akuluakulu ndi olamulira dziko lapansi! Inu anyamata pamodzi ndi anamwali, inu nkhalamba ndi ana omwe! Onsewo atamande dzina la Chauta, pakuti dzina lake lokha nlolemekezeka, ulemerero wake ndi woposa, pansi pano nkumwamba komwe. Chauta wakweza anthu ake poŵapatsa mphamvu. Walemekeza anthu ake onse oyera mtima, Aisraele amene Iye amaŵakonda. Tamandani Chauta! Mtamandeni inu angelo ake onse, mtamandeni inu magulu a ankhondo ake onse! Mtamandeni inu dzuŵa ndi mwezi, mtamandeni inu nonse nyenyezi zoŵala! Mtamandeni inu thambo lakumwambamwamba, ndi inu madzi a pamwamba pa thambo! Zonsezo zitamande dzina la Chauta! Paja Iye adaalamula, izo nkulengedwa.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko, ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
“Ndimalenga kuŵala ndi mdima, ndimadzetsa madalitso ndi tsoka. Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi.
“Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pamwamba pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lonse lapansi. Mudalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi.
Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Chifukwa chiyani mukulimbana ndi Mulungu nkumanena kuti, ‘Pa mau angaŵa sadzayankhapo ndi amodzi omwe?’ Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo.
Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu.
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse.
Kukhulupirika kwanu kumakhala mpaka pa mibadwo yonse. Inu mwakhazikitsa dziko, ndipo siligwedezeka.
Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine, Ine ndekha, palibenso mulungu wina. Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo, ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga.
Koma Chauta akuti: “Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Kodi sowo ingathe kudzikuza kupambana munthu woigwiritsa ntchito? Ndiye kukhala ngati kuti mkwapulo ukuzunguza munthu, kapena ndodo yanyamula munthu!”
Motero chachikulu si zimene munthu azifuna, kapena zimene munthu amayesetsa kuchita, koma chachikulu ndi chifundo cha Mulungu.
Zolinga za anthu akunja Chauta amazisandutsa zopandapake. Maganizo ao onse amaŵasandutsa achabechabe. Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga.
“Iyeyo ndi wosasinthika, nanga ndani angathe kumsintha maganizo? Zimene wafuna, amazichitadi. Zimene adatsimikiza kuti adzandichita, adzachitadi, ndipo amalingalira zambiri zoterezi.
Zoonadi, Ambuye Chauta akubwera kudzaweruza mwamphamvu, ndipo akulamulira ndi dzanja lake. Akubwera ndi malipiro ake, watsogoza mphotho yake. Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse. Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse.
Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse.
Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa. Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Chiweruzo cha Chauta nchoona, ncholungama nthaŵi zonse.
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe. Kudagwa mvula, mitsinje idadzaza, ndipo chimphepo chidadza nkuwomba pa nyumbayo. Koma siidagwe, chifukwa chakuti adaaimanga polimba.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo? Ndani adaayamba waperekapo kanthu kwa Mulungu, kuti Mulunguyo amubwezereko kanthu?” Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Mulungu pofuna kuŵatsimikizira anthu odzalandira zimene adaalonjeza, kuti Iye sangasinthe maganizo, adatsimikiza lonjezo lakelo pakulumbira. Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu.
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Dzina lake laulemerero litamandike mpaka muyaya. Ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi. Inde momwemo. Inde momwemo.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
“Mulungu amapenya njira zonse za anthu, amaona mayendedwe ao onse. Palibe usiku kapena mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoipa angathe kubisalira Mulungu.
“Mundimvere, inu zidzukulu za Yakobe, inu nonse otsala a m'nyumba ya Israele. Ndakhala ndikukusamalani chibadwire chanu, ndidakunyamulani kuyambira m'mimba mwa amai anu. Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Ndidzauza akumpoto kuti ‘Muŵaleke.’ Ndidzalamula akumwera kuti ‘Musaŵagwire.’ Ana anga aamuna abwerere kuchokera ku maiko akutali, ana anga aakazi abwerere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera, Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse. Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama. Zungulirani Ziyoni yense, inde zungulirani mzinda wonsewo, ndipo muŵerenge nsanja zake. Yang'anani bwino machemba ake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo. Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.” mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.
Paja tikumdziŵa kale amene adati, “Kulipsira nkwanga, ndidzakhaulitsa ndine.” Adatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”
Chauta amayang'anira bwino anthu odziŵa zinthu, koma mau a anthu osakhulupirika, Iye amaŵalepheretsa.
Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.
Pakuti Inu Chauta, mwandipulumutsa ku imfa, mwaletsa misozi yanga, mwanditeteza kuti ndisaphunthwe. Ndimayenda pamaso pa Chauta m'dziko la amoyo.
Zolengedwa zonse zikudikira molakalaka kuti Mulungu aonetse ana ake poyera. Pakuti lamulo la Mzimu Woyera, lotipatsa moyo mwa Khristu Yesu, landimasula ku lamulo la uchimo ndi la imfa. Pakuti zolengedwazo zidaasanduka zogonjera zopanda pake, osati chifukwa zidaafuna kutero ai, koma chifukwa Mulungu adaagamula choncho. Komabe zili ndi chiyembekezo ichi, chakuti izonso zidzamasulidwa ku ukapolo wa kuwola, ndi kulandirako ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
Zakumwamba ndi zanu, dziko lapansi nalonso ndi lanu. Mudapanga dziko lonse ndi zonse zam'menemo.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa. Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Chauta salola kuti munthu womukondweretsa iye, azikhala ndi njala, koma zimene woipa amazilakalaka, Mulungu amam'mana.
Tamandani Chauta, inu okhala kumwamba. Tamandani ulemerero wake ndi mphamvu zake. Chauta amalamulira nyanja zonse, amakhala kwamuyaya pa mpando wake wachifumu. Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu Tamandani ulemerero wa dzina la Chauta. Mumpembedze mu ulemu wa ungwiro wake.
Iye adzabwezera aliyense molingana ndi ntchito zake. Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha. Koma ochita zaupandu, namatsutsa zoona nkumachita zosalungama, Mulungu adzaŵakwiyira ndi kuŵazazira.
Mafano a mitundu ina ya anthu ndi asiliva ndi agolide chabe, ndi opangidwa ndi manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma salankhula, maso ali nawo, koma sapenya. Makutu ali nawo, koma saamva, ndipo alibe mpweya m'kamwa mwao. Anthu amene amapanga mafanowo afanefane nawo, chimodzimodzi onse amene amaŵakhulupirira.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.
Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu.
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
“Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena mudzamwanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji. Kodi suja moyo umaposa chakudya? Kodi suja thupi limaposa zovala? Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
“Inu Ambuye, anthu amakhala moyo ndi zimenezi, moyo wa mzimu wanga uli mu zomwezo. Mundichiritse ndi kundibwezera moyo. Chimene ndidamvera zoŵaŵa nkuti ndipeze bwino. Mwapulumutsa moyo wanga ku manda, mwataya machimo anga onse kumbuyo kwanu.
Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”
Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.
Ndikudziŵa kuti zimene Mulungu amazichita zimakhazikika mpaka muyaya. Palibe zimene zingathe kuwonjezedwa kapena kuchotsedwapo pa zimenezo. Mulungu adazipanga motero, kuti choncho anthu azimumvera.
Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Paja mau a Mulungu amanena kuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo. Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka, koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.” Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu.
Chauta akunena kuti, “Mverani Ine, inu zidzukulu za Yakobe, inu Aisraele, amene ndidakuitanani. Mulungu uja ndine, ndine woyamba ndipo ndine wotsiriza.
Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira. Adzaonetsa poyera kusalakwa kwako, ndipo kulungama kwako kudzaŵala ngati usana.
Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko,
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu. Kuli nyanja yaikulu ndi yotambalala, yodzaza ndi zinthu zosaŵerengeka, zinthu zamoyo, zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.