Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


100 Mau a Mulungu Okhudza Utatu Woyera

100 Mau a Mulungu Okhudza Utatu Woyera

Mulungu ndi mmodzi, koma ali ndi maonekedwe atatu ofanana ndi amphamvu, ngakhale ali ndi ntchito zosiyana: Atate, Mwana (Yesu), ndi Mzimu Woyera. Ndikuganiza kuti zimenezi n’zovuta kuzimvetsa mokwanira, koma ndizofunika kuzikhulupirira.

Tangoganizani mmene zinaliri pachiyambi, monga momwe Baibulo limatiuza mu Genesis 1:1, "Dziko lapansi linali lopanda kanthu ndipo linali bwinja. Mdima unali pamadzi akuya, ndipo Mzimu wa Mulungu unali kuyendayenda pamwamba pa madzi." Apa tikuona Mzimu wa Mulungu akuchitapo kanthu.

Ndipo mu Genesis 1:26, Mulungu anati, "Tipange munthu m'chifaniziro chathu, kuti afanane nafe. Alamulire pa nsomba za m'nyanja, mbalame za m'mlengalenga, ziweto, dziko lonse lapansi, ndi zokwawa zonse za pansi." Mawu akuti "tipange" ndi "chifaniziro chathu" amasonyeza kuti Mulungu analipo kale ngati Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera kuyambira pachiyambi.

Yesu, mu Yohane 14:20, anatiuza kuti, "Tsiku limenelo mudzadziwa kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu." Izi zimatithandiza kumvetsa ubale wapakati pa Atate, Mwana, ndi ife omwe timakhulupirira.

Ndikudziwa kuti zimenezi sizingakhale zomveka bwino nthawi zonse, koma Baibulo limatiphunzitsa zimenezi, ndipo chikhulupiriro chathu chimatithandiza kuvomereza choonadi cha Utatu Woyera. Ndi chifukwa cha chikondi cha Mulungu m’maonekedwe ake atatuwa, ife tingakhale ndi moyo wosatha.




2 Akorinto 13:14

Madalitso a Ambuye Yesu Khristu ndi chikondi cha Mulungu ndiponso chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:30

Ine ndi Atate ndife amodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:2

Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:26

“Koma pali Nkhoswe imene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate. Nkhosweyo ndi Mzimu wa choona wofumira mwa Atate. Iyeyo akadzabwera, adzandichitira umboni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:35

Mngeloyo adayankha kuti, “Mzimu Woyera adzakutsikirani, ndipo mphamvu za Mulungu Wopambanazonse zidzakuphimbani. Nchifukwa chake Mwana wodzabadwayo adzakhala Woyera, ndipo adzatchedwa Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:16-17

Pamenepo ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthaŵi zonse. Nkhosweyo ndi Mzimu wodziŵitsa zoona. Anthu ongokonda zapansipano sangathe kumlandira ai, chifukwa samuwona kapena kumdziŵa. Koma inu mumamdziŵa, chifukwa amakhala ndi inu, ndipo adzakhala mwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 2:5

Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:4-6

Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi. Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:16-17

Yesu atangobatizidwa, adatuluka m'madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 8:6

Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:15

Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:26

Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13-15

Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziŵitsani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:7

Motero pali atatu aŵa ochitira umboni:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:26

Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 11:7

Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 6:8

Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:16

Bwerani pafupi tsono, kuti mumve zimene nditi ndinene. Kuyambira pa chiyambi sindidalankhule mobisa, nthaŵi imene zimenezo zinkachitika, nkuti Ine ndilipo.” Tsono Ambuye Chauta andipatsa Mzimu wao, ndipo andituma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:1

Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:10

Komabe iwo adampandukira, namkwiyitsa Mulungu. Motero Chauta adasanduka mdani wao, ndipo adamenyana nawo nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 1:23

“Namwali wina wosadziŵa mwamuna adzatenga pathupi nkubala mwana wamwamuna. Mwanayo adzatchedwa dzina loti Imanuele,” ndiye kuti “Mulungu ali nafe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:28

Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:5

Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:10-11

Potuluka m'madzimo, adangoona kuthambo kukutsekuka, ndipo Mzimu Woyera akutsika pa Iye ngati nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:21-22

Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:1

Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:14

Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:34-35

Amene Mulungu adamtumayo, amalankhula mau a Mulungu, pakuti Mulungu amapereka Mzimu Woyera mosaumira. Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:18

Pamenepo ndiye Ayuda adankirankira kufuna kumupha. Ankati Yesu akuphwanya lamulo lokhudza Sabata, ndiponso ponena kuti Mulungu ndi Atate ake, ankadzilinganiza ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:38

Koma ngati ndimazichitadi, khulupirirani ntchitozo, ngakhale simukhulupirira Ine. Apo mudzadziŵa mosapeneka konse kuti Atate amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa Atate.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:21-22

Ndikuŵapempherera kuti iwo onse akhale amodzi. Monga Inu Atate mumakhala mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife. Motero anthu onse adzakhulupirira kuti mudandituma. Ulemerero womwewo umene mudandipatsa, ndaŵapatsanso iwoŵa. Akhale amodzi monga Ife tili amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:4-5

Pamene anali nawo pamodzi, Yesu adaŵalamula kuti, “Musachoke mu Yerusalemu, koma mudikire mphatso imene Atate adalonjeza, monga ndidaakuuzani. Pajatu Yohane ankabatiza ndi madzi, koma pasanapite masiku ambiri, inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:32-33

Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:3-4

Koma Petro adamufunsa kuti, “Iwe Ananiya, chifukwa chiyani walola mtima wako kugwidwa ndi Satana mpaka kumanamiza Mzimu Woyera pakupatula ndalama zina za munda wako? Mulungu wa makolo athu adaukitsa Yesu kwa akufa, Iye amene inu mudaamupha pakumpachika pa mtanda. Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe. Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.” Pamene abwalo aja adamva zimenezi, adakwiya kwambiri nafuna kuŵapha. Koma wina mwa iwo, Mfarisi dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa Malamulo, amene anthu onse ankamlemekeza, adaimirira. Adalamula kuti anthu aja abaapita panja. Tsono adauza abwalowo kuti, “Inu Aisraele, chenjerani ndi zimene mukufuna kuŵachita anthuŵa. Pajatu si kale pamene munthu wina dzina lake Teudasi adaabwera nkuyesa kudzimveketsa, ndipo anthu ngati mazana anai adamtsata. Iye uja adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana natheratu. Pambuyo pake, pa nthaŵi ya kalembera, padabweranso wina dzina lake Yudasi, wa ku Galileya, nakopa anthu ambiri kuti amtsate. Iyenso adaphedwa, ndipo anthu onse amene ankamtsata aja adabalalikana. Nchifukwa chake pa nkhani imeneyi ndikukuuzani kuti, muŵaleke anthuŵa, ndipo muŵalole azipita. Ngati zimene iwo akuganiza ndiponso zimene akuchitazi nzochokera kwa anthu, zidzakanika zokha. Koma ngati nzochokera kwa Mulungu, inu simungathe kuŵaletsa ai. Mwina mungapezeke kuti mukulimbana ndi Mulungu.” Usanaugulitse, sunali wako kodi? Ndipo utaugulitsa, suja ndalama zake zinali m'manja mwako? Nanga udalola bwanji zoterezi mumtima mwako? Pamenepatu sudanamize anthu, koma wanamiza Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:55-56

Koma Stefano, atadzazidwa ndi Mzimu Woyera, adayang'ana kumwamba naona ulemerero wa Mulungu, ndiponso Yesu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu. Tsono adati, “Onani! Ndikuwona Kumwamba kotsekuka, ndipo Mwana wa Munthu ataimirira ku dzanja lamanja la Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:4

koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:14-17

Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:16

pakundipatula kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Adandipatsa ntchito yolalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu ngati wansembe, kuti anthuwo akhale ngati nsembe yokomera Iye ndi yoperekedwa mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:30

Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 2:10-11

Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:11

Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:4-6

Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timaŵatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:21-22

Mulungu ndi amene amatikhazikitsa pamodzi nanu mwa Khristu. Ndiye amene adatidzoza, natisindikiza chizindikiro chake, ndi kuika Mzimu Woyera m'mitima mwathu ngati chikole.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:4-6

Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu. Pofuna kutsimikiza kuti ndinu ana ake, Mulungu adatitumizira Mzimu wa Mwana wake m'mitima mwathu, ndipo Mzimuyo amatinenetsa kuti, “Abba! Atate!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:18

Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:22

Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:14-17

Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate, amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao. Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:30

Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera amene Mulungu adakusindikizani chizindikiro chake chotsimikizira kuti ndinu ake pa tsiku limene Mulunguyo adzatipulumutse kwathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:5-6

Motero nonse mukhale ndi mtima womwe uja umene adaali nawonso Khristu Yesu: Iyeyu anali ndi umulungu chikhalire, komabe sadayese kuti kulingana ndi Mulungu ndi chinthu choti achigwiritsitse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:3

Paja ifeyo ndiye oumbala enieni, ife amene timapembedza Mulungu motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Timanyadira Khristu Yesu, osadalira miyambo ya thupi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:15-17

Khristuyo ndiye chithunzi chenicheni cha Mulungu wosaoneka. Iye ndiye Mwana wake woyamba, wolamulira zolengedwa zonse. Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:9

Pakuti m'thupi la Khristu umulungu wonse umakhalamo wathunthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:8

Motero munthu wokana mau ameneŵa, sakukana munthu chabe ai, koma akukana Mulungu amene amakupatsani Mzimu wake Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:13-14

Koma ife tikuyenera kumathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu, abale, amene Ambuye amakukondani. Paja Mulungu adakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke. Mudapulumuka chifukwa Mzimu Woyera adakusandutsani anthu akeake a Mulungu, ndipo mudakhulupirira choona. Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:16

Ndithudi, chinsinsi cha chipembedzo chathu nchachikulu: “Iye uja adaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu Woyera adamchitira umboni kuti ndi wolungama, angelo adamuwona, adalalikidwa pakati pa anthu a mitundu yonse, anthu a pa dziko lonse lapansi adamkhulupirira, Iyeyo adatengedwa kunka kumwamba mu ulemerero.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:4-6

Koma pamenepo Mulungu Mpulumutsi wathu adaonetsa kukoma kwake ndiponso chifundo chokonda anthu. Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano. Mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu, Mulungu adatipatsa Mzimu Woyerayo moolowa manja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:1-3

Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu. Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala. Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.” Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.” Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso? Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake. Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:14

Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:13-14

Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera. Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:4-5

Ndine, Yohane, ndikulembera mipingo isanu ndi iŵiri ya ku Asiya. Akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere Mulungu amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza. Ikukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere mizimu isanu ndi iŵiri yokhala patsogolo pa mpando wachifumu wa Mulungu. Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 4:8

Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko asanu ndi limodzi, ndipo zinali ndi maso ponseponse ndi m'kati momwe. Usana ndi usiku zimaimba mosalekeza kuti, “Ngoyera, ngoyera, ngoyera Ambuye, Mulungu Mphambe, amene analipo, amene alipo, amene alikudza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:1

Pambuyo pake mngelo uja adandiwonetsa mtsinje wa madzi opatsa moyo. Mtsinjewo madzi ake anali onyezimira ngati galasi, ndipo unkachokera ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:22-23

Atate saweruza munthu aliyense, koma adaika Mwana wake kuti akhale woweruza pa zonse. Atate amafuna kuti anthu onse azilemekeza Mwana, monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana, salemekezanso Atate amene adamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:3

Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:28

Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:5

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:6

akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:19

Ndiye kuti mwa Khristu Mulungu ankayanjanitsa anthu a pa dziko lonse lapansi ndi Iye mwini, osaŵaŵerengera machimo ao. Ndipo adatipatsa ifeyo mau onena za chiyanjanitsocho kuti tiŵalalike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:31

Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu, amene tiyenera kumtamanda nthaŵi zonse, akudziŵa kuti sindikunama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:17

ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:19

Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:19

Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:3-5

Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu. Abale athu, inu amene Mulungu amakukondani, tikudziŵa kuti Iye adakusankhani kuti mukhale ake. Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:1-2

Ndine, Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulemba kalatayi kwa anthu amene adalandira chikhulupiriro chomwe ifenso tidalandirako. Iwonso adachilandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse. Choncho adzakutsekulirani kwathunthu khomo loloŵera mu Ufumu wosatha wa Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu, Yesu Khristu. Nchifukwa chake cholinga changa nchakuti ndizikukumbutsani zimenezi nthaŵi zonse, ngakhale mukuzidziŵa ndipo mumakhulupirira ndi mtima wonse choona chimene mudalandira. Ndiyesa nkoyenera kuti, ndikadali mu msasa uno, nditsitsimutse mitima yanu pakukukumbutsani zimenezi. Pakuti ndikudziŵa kuti nthaŵi yakutuluka mu msasa wanga uno yayandikira, monga andidziŵitsira Ambuye athu Yesu Khristu. Ndipo ndidzayesetsa kukonza zoti nditachoka ine, muzidzatha kuzikumbukira zimenezi nthaŵi iliyonse. Ife sitidatsate nthano zongopeka chabe, pamene tidakudziŵitsani za mphamvu zao ndi za kubweranso kwao kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Koma tidachita kuuwona ndi maso athu ukulu wake. Iye adalandira ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu Atate, ndipo adamufikira mau ochokera kwa Atate aulemererowo akuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwera naye.” Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija. Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumdziŵa Iyeyo ndiponso Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:24

Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:11

Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:8

“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:14

“Mtsogoleri wa mpingo wa ku Laodikea umlembere kuti, Naŵa mau ochokera kwa Iye amene amatchedwa Amen uja, amene ali mboni yokhulupirika ndi yoona, ndiponso gwero la zolengedwa zonse za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 5:13

Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 3:22

Chauta adati, “Tsopano munthuyu wakhala monga tiliri ife, popeza kuti akudziŵa zabwino ndi zoipa. Asaloledwe kudya zipatso za mtengo wopatsa moyowo ndi kukhala moyo mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:6

Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 44:6

Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:12

Chauta akunena kuti, “Mverani Ine, inu zidzukulu za Yakobe, inu Aisraele, amene ndidakuitanani. Mulungu uja ndine, ndine woyamba ndipo ndine wotsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:58

Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti Abrahamu asanabadwe, Ine ndilipo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 20:28

Tomasi adati, “Ambuye anga! Mulungu wanga!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 17:28

Paja “ ‘Mwa Iye ife timakhala ndi moyo, timayenda ndipo timakhala tilipo.’ Monga adanenera opeka ndakatulo anu ena kuti, “ ‘Ifenso ndife ofumira mwa Iye ngati ana ake.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 9:5

Iwoŵa ndi zidzukulu za makolo athu akale aja, ndipo Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndi wa mtundu wao, kunena za umunthu wake. Mulungu amene amalamulira zonse, alemekezeke mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:4-5

Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani. Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:13

Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:17-18

Nditamuwona, ndidagwa kumapazi kwake ngati munthu wakufa. Koma Iye adandisanjika dzanja lake lamanja nati, “Usaope. Woyamba ndiponso Wotsiriza ndine. Wamoyo uja ndine. Ndidaafa, koma tsopano ndili moyo mpaka muyaya. Imfa ndi Malo a anthu akufa makiyi ake ali ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu Wamphamvuzonse, ulemelero ndi ulemu zikhale zako! Mulungu wanga wakumwamba, ndikukuthokozani chifukwa cha Utatu wa mphamvu yanu, Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera. Ulemelero ndi matamando ndikupatsani chifukwa chotumiza Yesu kudzatifera ine ndi kundimasula ku zibwalo za imfa yosatha. Mawu anu amati: “Koma Mpumziti akafika, amene Ine ndidzakutumizirani kuchokera kwa Atate, Mzimu wa choonadi, amene achokera kwa Atate, Iye adzachitira umboni za Ine.” Zikomo chifukwa cha kukoma mtima kwanu potitsimikizira Mzimu Woyera kuti akhale Mpumziti wathu ndi mtsogoleri wanga pakati pa mayesero ndi zovuta. Ndikukuthokozani, chifukwa, mwa chifuniro chanu choyera ndi Mwana wanu yekhayo pamodzi ndi Mzimu Woyera, munalenga zonse zauzimu ndi zakuthupi, ndi ife, tolengedwa m'chifaniziro chanu ndi m'chifanizo chanu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa