Moyo wanga, tamva mawu a Mulungu akugogoda pa mtima wako. Ndi chifuniro chake pa moyo wako, chifukwa chomwe unalengedwera.
Buku Lopatulika, mu Chivumbulutso 3:20, limati: “Taonani, ndaima pakhomo ndi kugogoda; ngati wina amva mawu anga ndi kutsegula chitseko, ndidzalowa kwa iye, ndi kudya naye, ndi iye ndi Ine.” Mulungu akukuyitana iwe, lero.
Uyitanidwe umenewu ndi wosasinthika. Eya, Mulungu wakuyitana! Wakuyitana ku chipulumutso, ku kulapa, ku chikondi chake, ku moyo wake, ku njira imene wakukonzera, ku Moyo Wosatha.
Osadandaula, sudzakhala wekha. Aliyense amene Mulungu amamuyitana, amam’patsanso mphamvu. Iye adzakhala mphunzitsi wako, mtsogoleri wako, Mtetezi wako. Sudzasiyidwa yekha. Adzasunga moyo wako nthawi zonse mpaka utakwaniritsa ntchito imene wakupatsa padziko lapansi.
Usadzione ngati wopanda pake kapena wodzichepetsa. Kwa Mulungu, uli wamtengo wapatali kwambiri ndipo ndi wokondedwa kwambiri m’maso mwake.
Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.
Mulungu adakuitanirani zimenezi kudzera mwa Uthenga Wabwino umene tidakulalikirani. Adakuitanani kuti mulandire nao ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Koma monga Iye amene adakuitanani ali woyera mtima, inunso khalani oyera mtima m'makhalidwe anu onse. Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Atatero Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Munthu wofuna kutsata Ine, adzikane mwiniwakeyo, ndipo asenze mtanda wake nkumanditsata.
Abale, ndinu oyera ake a Mulungu, inuyo adakuitanani kuti nanunso mukhale ndi moyo wakumwamba. Nchifukwa chake muzisinkhasinkha za Yesu, mtumwi wa Mulungu, ndiponso Mkulu wa ansembe onse wa chikhulupiriro chimene timavomereza.
Ndipo zimene anthu amaziyesa zachabe, zonyozeka ndi zosakhala zenizeni, Mulungu adazisankha kuti athetse mphamvu zinthu zimene iwowo amayesa kuti ndiye zenizeni. Mulungu adachita zimenezi kuti pasakhale wina aliyense woti nkumadzitukumula pamaso pake.
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera. Pakuti anthu amene Mulungu adaŵasankhiratu, Iye adaŵapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake, kuti choncho Mwanayo akhale woyamba mwa abale ambiri. Mulungu adachita zimene Malamulo a Mose sadathe kuzichita, chifukwa khalidwe la anthu lopendekera ku zoipa lidaŵafooketsa. Iye adatsutsa uchimo m'khalidwe lopendekera ku zoipalo, pakutuma Mwana wakewake, ali ndi thupi longa la ife anthu ochimwa, kuti m'thupilo adzagonjetse uchimowo. Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake.
Uzimenya nkhondo yabwino ya kusunga chikhulupiriro, mpaka ukalandire moyo wosatha. Paja Mulungu adakuitanira zimenezi, ndipo udavomera bwino chikhulupiriro chako pamaso pa mboni zambiri.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu Woyera mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene Mulungu adakuitanirani.
Nchifukwa chake abale, chitani changu koposa kale kutsimikiza kuti Mulungu adakuitanani ndipo adakusankhani. Mukatero simudzagwa konse.
Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera, ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako. Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu. Sitidzakhalanso ngati ana akhanda ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, ndiponso otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya zophunzitsa za anthu onyenga amene amasokeretsa anthu ndi kuchenjera kwao Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi. Tsono m'dzina la Ambuye ndikukuuzani, ndipo ndikunenetsa, kuti musayendenso monga amachitira akunja potsata maganizo ao achabe. Nzeru zao zidachita chidima, sangalandire nao konse moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene udadza mwa iwo kaamba ka kuuma mtima kwao. Mitima yao idaludzulala ndipo adangodzipereka ku zonyansa, kuti azichita zoipa zilizonse mosadziletsa. Muzikhala odzichepetsa, ofatsa ndi opirira nthaŵi zonse. Muzilezerana mtima mwachikondi,
Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.”
Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.
Mkhalidwe wotere ndi umene Mulungu adakuitanirani. Paja Khristu nayenso adamva zoŵaŵa chifukwa cha inu, nakusiyirani chitsanzo kuti muzilondola mapazi ake.
“Inu anthu onse a pa dziko lapansi, tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke. Paja Ine ndine Mulungu, palibenso wina ai.
Chauta adati, “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a anthu amene sadandipemphere. Ndinali wokonzeka kuti andipeze anthu amene sadandifunefune. Mtunduwo sudapemphere kwa Ine ngakhale nthaŵi zonse ndinali wokonzeka kuŵayankha kuti, ‘Ine ndili pano, ndikuthandizani.’
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
Anthu okuchitani choipa, osaŵabwezera choipa, okuchitani chipongwe osaŵabwezera chipongwe. Koma inu muziŵadalitsa, pakuti inuyo Mulungu adakuitanirani mkhalidwe wotere, kuti mulandire madalitso ake.
Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.”
Paja Malembo akuti, “Ndidzaononga nzeru za anthu anzeru, ndidzathetsa kuchenjera kwa anthu ochenjera.”
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake.
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Koma Mulungu adandipatula ndisanabadwe, ndipo mwa kukoma mtima kwake adandiitana. Tsono pamene adatsimikiza zondiwululira Mwana wake, kuti choncho ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Iye kwa anthu amene sali Ayuda, sindidapite kwa munthu aliyense kuti ndikapemphe nzeru.
Ndidakutenga kuchokera ku mapeto a dziko lapansi, ndidakuitana kuchokera ku mbali zakutali za dziko. Ndipo ndidzakuuza kuti, “Iwe ndiwe mtumiki wanga, ndidakusankhula, sindidakutaye.”
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Abale, taganizani m'mene munaliri pamene Mulungu adakuitanani. Pakati panu panalibe ambiri amene anthu ankaŵayesa anzeru. Panalibenso ambiri amphamvu, kapena obadwa m'mabanja omveka. Koma Mulungu adasankha zimene anthu amaziyesa zopusa, kuti Iye anyazitse nazo anthu anzeru. Adasankhanso zimene anthu amaziyesa zofooka, kuti Iye anyazitse nazo anthu amphamvu.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.”
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
Chauta adandiwuza kuti, “Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Adaŵauza kuti, “Dzinthu ndzambiri, koma antchito ngochepa. Nchifukwa chake pemphani Mwini dzinthu kuti atume antchito kukatuta dzinthudzo.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.