Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


119 Mau a Mulungu Okhudza Malamulo

119 Mau a Mulungu Okhudza Malamulo

Kodi Mulungu amafotokoza bwanji lamulo lake? Funso lofunika ili, chifukwa limagwirizana ndi kumvetsa kwathu zauzimu, za mmene Iye alili pa moyo wathu. Mwachidule, malamulo a Mulungu ndi amene amatsogolera njira yake ya moyo ndipo ndiwo maziko a ufumu wake wakutsogolo; ndi malamulo ochokera kwa Mulungu, angwiro, okwanira pa cholinga chake, olungama, komanso ogwira mtima.

Monga mtumwi Paulo ananenera, lamulo la Mulungu “ndi loyera, ndipo lamulolo ndi loyera, lolungama, komanso labwino,” komanso “lauziimu” (Aroma 7:12,14). Ndipo monga mfumu Davide inalemba: “Chilamulo cha Yehova n’changwiro, chimabwezeretsa moyo.” Kenako anapitiriza kufotokoza kukongola ndi ubwino wa umboni, mawu, malamulo, ndi maweruzo a Mulungu, zomwe ndi mitundu yosiyanasiyana ya lamulo lake (Masalimo 19:7-11).

Malamulo a m’Baibulo ndi dongosolo la Mulungu la malamulo, mawu, ndi maweruzo omwe mtundu uliwonse komanso munthu aliyense ayenera kulemekeza, chifukwa Mulungu ndiye Mlengi wa zonse. Ndiponso, malamulo a Mulungu amafotokoza tanthauzo la chilungamo ndi tchimo. Ndipo, ngati tiwamvera, nthawi zonse tidzapindula.

Ngakhale anthu ena angakuuze zotani, kusunga lamulo la Mulungu kuyenera kukhala chisangalalo ndi chizindikiro cha chikondi chanu kwa Mulungu, podziwa kuti sizingatheke kuchita zimenezi ndi mphamvu zathu, koma mwa Khristu tingathe kuchita zonse. Wamasalimo Davide amatiphunzitsa kuti lamulo la Mulungu si katundu konse, iye analemba m’Masalimo kuti: “Koma chilamulo cha Yehova chimkondweretsa, ndipo amalingirira chilamulo chake usana ndi usiku.” Ndi chisangalalo cha moyo wathu lamulo la Mulungu, ndipo tiyenera kulingiriramo nthawi zonse popanda kusiya zimene Atate wathu wakumwamba anatikhazikitsira.




Masalimo 19:7

Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:92

Malamulo anu akadapanda kundisangalatsa, bwenzi nditafa ndi mazunzo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:34

Patseni nzeru kuti ndizisunga malamulo anu, ndiziŵatsata ndi mtima wanga wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-2

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:2

Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi ngongole ina iliyonse kwa munthu wina aliyense, koma kukondana kokha. Wokonda mnzake, watsata zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoswa 1:8

Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:2

Ndikufunseni chinthu chimodzi chokha: Kodi mudalandira Mzimu Woyera pakutsata Malamulo, kapena pakumva ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:21

Sindiisandutsa yopandapake mphatso yaulere ya Mulungu. Pakuti ngati munthu atha kusanduka wolungama pamaso pa Mulungu pakutsata Malamulo, ndiye kuti Khristu adafa pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:13

Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:1-17

Tsono Mulungu adalankhula mau onseŵa, adati, Koma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ndi la Sabata loperekedwa kwa Chauta, Mulungu wako. Usamagwira ntchito pa tsiku limenelo iweyo, kapena ana ako, kapena antchito ako, kapena zoŵeta zako, kapena mlendo amene amakhala m'mudzi mwako. Paja pa masiku asanu ndi limodzi Chauta adalenga zonse zakumwamba, za pa dziko lapansi, nyanja ndi zinthu zonse zam'menemo, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri adapumula. Nchifukwa chake Chauta adadalitsa tsiku la Sabata, nalisandutsa loyera. “Uzilemekeza atate ndi amai ako, kuti masiku a moyo wako achuluke m'dziko limene Chauta, Mulungu wako, akukupatsa. “Usaphe.” “Usachite chigololo.” “Usabe.” “Usachite umboni womnamizira mnzako.” “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 24:12

Chauta adauza Mose kuti, “Bwera kwa Ine kuphiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malamulo, kuti ndiphunzitse anthu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:12

Anthu onse amene adachimwa osadziŵa Malamulo, iwonso adzaonongeka ngakhale sadaŵadziŵe Malamulowo. Ndipo onse amene adachimwa atadziŵa Malamulo, adzaweruzidwa potsata Malamulowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:14

Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:15

Bwanji tsono? Kodi tizichimwabe popeza kuti chimene chimalamulira moyo wathu si Malamulo, koma kukoma mtima kwa Mulungu? Iyai, mpang'ono pomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:1

Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani, inu anthu anga. Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 30:16

Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:5-7

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse. Muziŵasunga bwino mumtima mwanu malamulo amene ndikukupatsani leroŵa. Muziŵaphunzitsa mwachangu kwa ana anu kulikonse kumene muli, mutakhala pansi m'nyumba mwanu, kapena muli paulendo, kapena mukupumula, kapena mukugwira ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 8:8

Aleviwo adaŵerenga buku la Malamulo a Mulungu momveka bwino, ndipo adatanthauzira mauwo kuti anthu amvetse bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:20

Pajatu palibe munthu amene Mulungu amamuwona kuti ngwolungama chifukwa cha kutsata Malamulo chabe. Malamulo amangotizindikiritsa kuchimwa kwathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:20-21

Mulungu adapereka Malamulo kuti anthu azindikire kuchuluka kwa machimo ao. Koma pamene uchimo udachuluka, kukoma mtima kwa Mulungu kudachuluka koposa. Choncho monga uchimo unkalamulira anthu ndi kudzetsa imfa pa iwo, momwemonso kunali koyenera kuti kukoma mtima kwa Mulungu kulamulire pakudzetsa chilungamo kwa anthu, ndi kuŵafikitsa ku moyo wosatha mwa Yesu Khristu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:1-2

Ngodala amene moyo wao ulibe choŵadzudzulira, amene amayenda motsata malamulo a Chauta. Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse, musalole kuti ndisiye kumvera malamulo anu. Ndili ndi nzeru kupambana okalamba, pakuti ndimatsata malamulo anu. Ndimaletsa miyendo yanga kuti isayende m'njira yoipa iliyonse, kuti choncho ndizisunga mau anu. Sindisiyana nawo malangizo anu, pakuti Inu mudandiphunzitsa mau anu ndi otsekemera kwambiri ndikaŵalaŵa. Amatsekemera kuposa uchi m'kamwa mwanga. Ndimakhala ndi nzeru za kumvetsa chifukwa cha malamulo anu. Nchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga. Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama. Ndazunzika koopsa, Chauta, patseni moyo, molingana ndi mau anu aja. Chauta, landirani mapemphero anga oyamika, ndipo mundiphunzitse malangizo anu. Moyo wanga uli m'zoopsa nthaŵi zonse, komabe sindiiŵala malamulo anu. Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni. Anthu oipa anditchera msampha, komabe sindisokera kuchoka m'njira ya malamulo anu. Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga. Mtima wanga muuphunzitse kuti uzikonda malamulo anu nthaŵi zonse. Ndimadana nawo anthu apaŵiripaŵiri, koma ndimakonda mau anu. Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu. Chokereni inu, anthu ochita zoipanu, kuti ine ndizitsata malamulo a Mulungu wanga. Chirikizeni molingana ndi malonjezo anu aja, kuti ndizikhala ndi moyo, ndipo anthu asandichititse manyazi, chifukwa ndine wokhulupirika. Chirikizeni kuti ndipulumuke, kuti nthaŵi zonse ndizitsata malamulo anu. Inu mumaŵakana anthu onse osamvera malamulo anu, zoonadi, kuchenjera kwao nkopandapake. Anthu onse oipa a pa dziko lapansi, mumaŵayesa ngati zakudzala, nchifukwa chake ndimakonda malamulo anu. Mutamandike, Inu Chauta, phunzitseni malamulo lanu. Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu. Ndachita zimene zili zolungama ndi zabwino. Musandisiye m'manja mwa ondizunza. Lonjezani kuti mudzandichitira zabwino mtumiki wanune, musalole anthu osasamala za Mulungu kuti andizunze. Maso anga atopa chifukwa cha kuyembekeza chipulumutso chanu, chifukwa cha kudikira kuti malonjezo anu olungama aja achitikedi. Komereni mtima mtumiki wanune, chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Ndine mtumiki wanu, mundipatse nzeru zomvetsa, kuti ndizidziŵa malamulo anu. Yakwana nthaŵi yakuti Inu Chauta muchitepo kanthu, popeza kuti anthu aphwanya malamulo anu. Koma ine ndimasamala malamulo anu kupambana golide, golide wosungunula bwino. Malamulo anu onse amalungamitsa mayendedwe anga. Ndimadana ndi njira iliyonse yonyenga. Malamulo anu ndi abwino, nchifukwa chake ndimaŵatsata ndi mtima wanga wonse. Ndimalalika ndi mau anga malangizo onse a pakamwa panu. Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru. Ndimapuma mwaŵefuŵefu nditatsekula pakamwa, chifukwa ndimalakalaka malamulo anu. Yang'aneni, ndipo mundikomere mtima monga m'mene mumachitira ndi anthu okukondani. Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira. Pulumutseni kwa anthu ondizunza, kuti ndizitsata malamulo anu. Yang'anireni ine mtumiki wanu ndi chikondi chanu, ndipo mundiphunzitse malamulo anu. Maso anga akudza misozi yambiri ngati mitsinje, chifukwa anthu satsata malamulo anu. Ndinu olungama Chauta, ndipo kuweruza kwanu nkolungama. Malamulo amene mwatipatsa, ndi olungama ndi okhulupirika ndithu. Changu changa chikuyaka ngati moto mumtima mwanga, chifukwa adani anga amaiŵala mau anu. Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse. Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda. Ine ndine wamng'ono ndi wonyozeka, komabe sindiiŵala malamulo anu. Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona. Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo. Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu. Ndimadzuka tambala asanalire, kuti ndipemphe chithandizo. Ndimakhulupirira mau anu. Ndimakhala maso usiku wonse, ndikusinkhasinkha za malonjezo anu. Imvani liwu langa chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika. Inu Chauta, sungani moyo wanga chifukwa cha chilungamo chanu. Ndidzasinkhasinkha za malamulo anu, ndipo ndidzatsata njira zanu. Anthu ankhanza ondizunza akuyandikira. Iwo ali kutali ndi malamulo anu. Koma Inu Chauta muli pafupi, ndipo malamulo anu onse ndi oona. Poŵerenga malamulo anu ndidadziŵa kale lomwe kuti Inu mudaŵakhazikitsa mpaka muyaya. Yang'anani masautso anga, ndipo mundipulumutse, popeza kuti sindiiŵala malamulo anu. Munditchinjirize pa mlandu wanga, ndipo mundiwombole. Mundipatse moyo molingana ndi malonjezo anu aja. Chipulumutso chili kutali ndi anthu oipa, pakuti safunafuna malamulo anu. Chifundo chanu nchachikulu, Inu Chauta, mundipatse moyo molingana ndi chilungamo chanu. Anthu ondizunza ndiponso adani anga ngochuluka, koma sindisiyana nawo malamulo anu. Ndimanyansidwa ndikamayang'ana anthu osakhulupirika, chifukwa satsata malamulo anu. Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya. Mafumu amandizunza popanda chifukwa, koma mtima wanga umaopa mau anu. Ndimakondwa ndi mau anu monga munthu amene wapeza chuma chambiri. Ndimadana ndi anthu abodza, zoonadi, ndimanyansidwa nawo, koma ndimakonda malamulo anu. Ndimakutamandani kasanunkaŵiri pa tsiku, chifukwa cha malangizo anu olungama. Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa. Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu. Mzimu wanga umatsata malamulo anu, pakuti ndimaŵakonda ndi mtima wanga wonse. Ndimatsata malamulo anu ndi malangizo anu, pakuti makhalidwe anga onse mukuŵaona. Kulira kwanga kumveke kwa Inu, Chauta. Mundipatse nzeru zomvetsa potsata mau anu aja. Komereni mtima ine mtumiki wanu, kuti ndikhale ndi moyo ndi kusunga mau anu. Kupempha kwanga kumveke kwa Inu. Mundipulumutse potsata malonjezo anu. Pakamwa panga padzakutamandani, chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu. Ndidzaimba nyimbo zoyamikira mau anu, chifukwa malamulo anu onse ndi olungama. Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza, chifukwa ndatsata malamulo anu. Ndikulakalaka nthaŵi yoti mudzandipulumutse. Inu Chauta, malamulo anu amandikondwetsa. Lolani kuti ndikhale moyo, kuti ndizikutamandani, ndipo malangizo anu azindithandiza. Ndasokera ngati nkhosa yoloŵerera, koma mundifunefune ine mtumiki wanu, pakuti sindiiŵala malamulo anu. Nyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu. Tsekulani maso anga kuti ndiwone zodabwitsa zochokera m'malamulo anu. Ndine munthu wongokhala nawo pa dziko lapansi, musandibisire malamulo anu. Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:9

Wina akamakana kumvera malamulo, ngakhale mapemphero ake amanyansira Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:142

Kulungama kwanu nkwamuyaya, ndipo malamulo anu ndi oona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 24:3

Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:17

Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:1

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 51:4

“Mverani, inu anthu anga, tcherani khutu, inu mtundu wanga. Malamulo adzachokera kwa Ine, ndipo chilungamo changa chidzaunikira anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:7

Tsono tinene chiyani? Kodi tinene kuti Malamulo ndi auchimo? Mpang'ono pomwe. Koma Malamulowo ndiwo adandizindikiritsa za uchimo. Pakuti sindikadadziŵa kuipa kwa kusirira, Malamulo akadapanda kunena kuti, “Usasirire”.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:24-25

Motero Malamulowo anali ngati namkungwi wathu, mpaka atabwera Khristu, kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira. Popeza kuti tsopano chikhulupiriro chafika, namkungwiyo satilamuliranso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:17-18

“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 10:12-13

Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:3-4

Pakutsata malamulo a Mulungu, ndi pamene tingatsimikize kuti timamdziŵa. Munthu akamati, “Ine ndimadziŵa Mulungu”, koma chikhalirecho satsata malamulo ake, angonama ameneyo, ndipo mwa iye mulibe choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:14

Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 8:10

“Nachi tsono chipangano chimene ndidzachita ndi fuko la Israele atapita masiku ameneŵa,” akutero Ambuye: “Ndidzaika Malamulo anga m'maganizo ao ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Choncho Ine ndidzakhala Mulungu wao, iwowo adzakhala anthu anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:12

Mosakayika konse, Malamulo a Mose ndi ochokera kwa Mulungu, ndipo lamulo lililonse mwa Malamulowo ndi loyera, lolungama ndi labwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:18

Koma ngati Mzimu Woyera akutsogolerani, ndiye kuti sindinunso akapolo a Malamulo a Mose.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:72

Malamulo a pakamwa panu amandikomera kuposa ndalama zikwizikwi zagolide ndi zasiliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37-40

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe. Idatumanso antchito ena nkunena kuti, ‘Kaŵauzeni oitanidwa aja kuti chakudya chakonzeka. Ndapha ng'ombe ndi nyama zina zonenepa. Zonse zakonzeka, bwerani ku phwando laukwati.’ Malamulo onse a Mose ndiponso zonse zimene aneneri adaphunzitsa zagona pa malamulo aŵiriŵa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:16

Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:25

Malamulo a Mulungu ndi angwiro ndiponso opatsa anthu ufulu. Munthu amene amalandira Malamulowo nkumaŵatsata mosamala, amene samangomva mau nkuŵaiŵala, koma amaŵagwiritsa ntchito, ameneyo Mulungu adzamdalitsa pa zochita zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:10

Onse amene amadalira ntchito za Malamulo ndi otembereredwa. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense amene satsata zonse zolembedwa m'buku la Malamulo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:165

Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:1-3

Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa, wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa, wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu, koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:2

Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:18

Musabwezere choipa, ndipo musakwiyire anthu a mtundu wanu, koma mukonde mnzanu monga momwe mumadzikondera inu nomwe. Ine ndine Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:4

Amene samvera malamulo amatamanda anthu oipa mtima, koma otsata malamulo amatsutsana nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:18

Kumene kulibe mithenga yochokera kwa Mulungu, anthu saweruzika, ndi wodala munthu amene amatsata malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:1

Malamulo a Mose ndi chithunzi chabe cha madalitso amene alikudza, osati madalitso enieniwo. Ngakhale nsembe zimodzimodzi zimaperekedwa kosalekeza chaka ndi chaka, Malamulowo sangathe konse mwa nsembezo kuŵasandutsa angwiro anthu oyandikira pamenepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:16

“Malamulo a Mose ndi zolemba za aneneri zinkagwirabe ntchito mpaka nthaŵi ya Yohane Mbatizi. Kuyambira pamenepo Uthenga Wabwino ukulalikidwa wakuti Mulungu akukhazikitsa ufumu wake, ndipo anthu onse akuyesetsa mwamphamvu kuloŵamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:3-4

Mulungu adachita zimene Malamulo a Mose sadathe kuzichita, chifukwa khalidwe la anthu lopendekera ku zoipa lidaŵafooketsa. Iye adatsutsa uchimo m'khalidwe lopendekera ku zoipalo, pakutuma Mwana wakewake, ali ndi thupi longa la ife anthu ochimwa, kuti m'thupilo adzagonjetse uchimowo. Mulungu sadangoŵapatula, komanso adaŵaitana. Sadangoŵaitana, komanso adaŵaona kuti ngolunga pamaso pake. Ndipo sadangoona kuti ngolunga pamaso pake, komanso adaŵagaŵirako ulemerero wake. Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere? Ndani angaŵaimbe mlandu anthu amene Mulungu adaŵasankha? Mulungu mwiniwake amaŵaona kuti ngolungama pamaso pake. Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo. Tsono ndani angatilekanitse ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zoŵaŵa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zoopsa, kapenanso kuphedwa? Paja Malembo akuti, “Chifukwa cha Inu tsiku lonse akufuna kutipha, pamaso pao tili ngati nkhosa zimene akukazipha.” Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda. Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Mulungu adachita zimenezi, kuti chilungamo chimene Malamulo a Mose amatipempha, chiwoneke kwathunthu mwa ife amene sitimveranso khalidwe lathu lopendekera ku zoipa, koma timamvera Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 4:40

Muzimvera malangizo ndi malamulo ake onse amene ndakupatsani leroŵa. Mukatero, zinthu zidzakuyenderani bwino inuyo ndi zidzukulu zanu, ndipo mudzakhalitsa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani kuti likhale lanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:43

Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:19

Choncho aliyense wonyozera limodzi mwa malamulo ameneŵa, ngakhale laling'ono chotani, nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamng'ono ndithu mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense amene amaŵatsata nkumaphunzitsa anthu ena kuti azitero, adzakhala wamkulu mu Ufumu wakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 9:21

Kwa amene alibe Malamulo a Mose, ndidakhala ngati iwo omwe, kuti ndiŵakope. Sindiye kuti ndilibe Malamulo a Mulungu ai, popeza kuti ndili nawo malamulo a Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:16

Komabe tikudziŵa kuti munthu sangapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu pakuchita ntchito zolamulidwa ndi Malamulo, koma pakukhulupirira Yesu Khristu. Ifenso tidakhulupirira Khristu Yesu kuti tisanduke olungama pamaso pa Mulungu pakukhulupirira Khristu, osati chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo. Pakuti palibe munthu amene angapezeke kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito zolamulidwa ndi Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:144

Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:13

Pakuti amene ali olungama pamaso pa Mulungu si amene amangomva Malamulo chabe ai. Koma okhawo amene amachitadi zonenedwa m'Malamulo ndiwo amene Mulungu adzaŵaona kuti ngolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:10

Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:4

Aliyense amene amachimwa, alinso ndi mlandu wa kuphwanya malamulo. Paja kuchimwa nkuphwanya malamulo kumene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 17:18-20

Munthuyo ataloŵa mu ufumu wakewo, adzalembe m'buku lakelake malamulo a Mulunguŵa ochokera mu buku la malamulo limene lili m'manja mwa ansembe Achilevi. Buku limeneli adzalisunge ndipo azidzaŵerengamo pa moyo wake wonse, kuti adzaphunzire kuwopa Chauta, Mulungu wake, pakutsata mokhulupirika zonse zolembedwa m'bukumo. Mwina padzapezeka kuti mu mzinda wina umene Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani, muli munthu wina wamwamuna kapena wamkazi amene wachimwira Chauta, Mulungu wanu, Zimenezi zidzamthandiza kudziŵa kuti iyeyo saposa Aisraele anzake, ndiponso kuti sayenera kukhala wonyozera malamulo a Chauta mpang'ono pomwe. Motero iyeyo, pamodzi ndi zidzukulu zake zomwe, adzalamulira nthaŵi yaitali mu Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:31

Ndimakangamira malamulo anu, Inu Chauta, musalole kuti anthu andichititse manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 7:22

Mtima wanga umakondwa ndi Malamulo a Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:26

Pamene ndidasimba za njira zanga, Inu mudandiyankha. Phunzitseni malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:3

Yesu adaŵayankha kuti, “Nanga bwanji inuyo, chifukwa choumirira miyambo yanu, mumaphwanya lamulo la Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:4

Inu amene mukuyesa kusanduka olungama pakutsata Malamulowo, mudadzipatula nokha kusiya Khristu. Pamenepo mudalekana ndi madalitso aulere a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:12

Pakuti pakakhala kusintha pa unsembe, ndiye kuti pa Malamulonso sipangalephere kukhala kusintha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:24

Pamenepo Mulungu wathu adatilamula kuti tizimvera malamulo onseŵa, ndiponso kuti tizimuwopa. Tikamatero, Iyeyo adzasunga mtundu wathu, ndipo adzautukula monga momwe akuchitiramu tsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:31

Kodi ndiye kuti tikutaya Malamulo pamene tikunenetsa kuti pafunika chikhulupiriro? Mpang'ono pomwe. Makamaka tikuŵafikitsa pake penipeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:14

Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:8

Tikudziŵa kuti Malamulo ngabwino, malinga nkuŵagwiritsa ntchito moyenera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:13

Wonyoza malangizo amadziwononga, koma wosamala lamulo amalandira mphotho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:120

Thupi langa limanjenjemera chifukwa chokuwopani, ndimachita mantha ndi kuweruza kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 42:21

Chifukwa cha chilungamo chake, Chauta adafunitsitsa kuti malamulo ake akhale opambana ndi aulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:31

Malamulo a Mulungu amakhala mumtima mwake, motero sagwedezeka poyenda m'moyo uno.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:12

Zomwe mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muŵachitire zomwezo. Izi ndiye zimene Malamulo a Mose ndiponso aneneri amaphunzitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:32

Amalidziŵa lamulo la Mulungu lakuti anthu ochita zotere ndi oyenera kufa, komabe iwo omwe amachita zomwezo, ndiponso amavomerezana ndi anthu ena ozichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:1-2

Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi. Tsono anthu onse a pa dziko lonse lapansi adzaona kuti Chauta, Mulungu wanu, wakusankhani inu kuti mukhale anthu akeake, ndipo azidzakuwopani. Chauta adzakudalitsani pokupatsani ana ambiri, zoŵeta zambiri ndiponso zokolola zambiri. Zonsezi adzakupatsani m'dziko limene Iye adalonjeza kwa makolo anu kuti adzakupatsani. Pa nyengo yake, adzakutumizirani mvula kuchokera kumene amaisunga mu mlengalenga, ndipo adzadalitsa ntchito zanu zonse, kotero kuti inuyo muzidzakongoza mitundu ina zinthu, koma inuyo osakongola kwa aliyense. Mulungu wanu adzakusandutsani atsogoleri pakati pa mitundu ya anthu, osati otsata pambuyo. Mukamamvera malamulo ake amene ndikukupatsani lero ndi kuŵatsatadi mosamala, mudzakhala okwera nthaŵi zonse, osati otsika. Choncho pa mau ndikukuuzani leroŵa, musapatuke kumanja kapena kumanzere, pakutsata milungu ina ndi kumaitumikira. Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa: Chauta adzatemberera mizinda yanu ndi minda yanu. Chauta adzatemberera zokolola zanu ndiponso zokandiramo ufa wanu. Chauta adzakutembererani pokupatsani ana oŵerengeka, zokolola zochepa, ndiponso ng'ombe ndi zoŵeta zina pang'ono chabe. Chauta adzatemberera ntchito zanu zonse. Mverani Chauta, Mulungu wanu, ndipo mudzalandira madalitso onse aŵa:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:160

mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:19

Nanga tsono cholinga cha Malamulo chinali chiyani? Mulungu adaonjezapo Malamulo kuti azindikiritse anthu machimo, mpaka mbeu ija ya Abrahamu, imene Mulungu adaaipatsa lonjezo lija, itabwera. Mulungu adapereka Malamulowo kudzera mwa angelo, ndiponso kudzera mwa munthu wochita ntchito ya mkhalapakati.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:28

Koma ngati Ine ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Mulungu wayamba kukhazikitsa ufumu wake pakati panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:14-15

Anthu amene sali Ayuda alibe Malamulo, koma pamene mwa iwo okha amachita zimene Malamulowo anena, amaonetsa kuti ali nawo malamulo mumtima mwao, ngakhale alibe Malamulo a Mose. Ntchito zaozo zimatsimikiza kuti Malamulowo ndi olembedwa m'mitima mwao. Mitima yao yomwe imatsimikiza kuti ndi momwemodi, popeza kuti maganizo ao m'chikatikati mwina amaŵatsutsa, mwina amaŵavomereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:8

Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 103:17-18

Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 8:20

kuti akalandireko mau enieni ndi malangizo? Iyai, amene amalankhula motero, mwa iwo mulibe konse kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:14

Yesetsani kukhala ndi mtendere ndi anthu onse, ndi kukhala oyera mtima, pakuti palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaona Ambuye popanda kuyera mtimako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 12:49

Lamulo limeneli ndi la mbadwa yeniyeni ya Israele, ndiponso la mlendo woumbalidwa amene ali pakati panu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:48

Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:4

Khristu adafikitsa Malamulo a Mose ku mapherezero, kotero kuti aliyense wokhulupirira, amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:46

Ndidzalankhula malamulo anu pamaso pa mafumu, ndipo anthu sadzandichititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:1

Chauta akuuza anthu ake kuti, “Muzichita zabwino ndi zolungama, chifukwa ndikuwombolani posachedwa, chipulumutso changa chiwoneka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:2-3

Chodziŵira kuti timakonda ana a Mulungu nchakuti timakonda Mulungu ndi kutsata malamulo ake. Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha. Ana inu, dzisungeni bwino, osapembedza mafano. Paja kukonda Mulungu ndiye kuti kutsata malamulo ake, ndipo malamulo ake si olemetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:59

Ndikamalingalira njira zanga, ndimatembenuka kuti nditsate malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Mu ufumu wa Mulungu chachikulu si chakudya kapena zakumwa ai, koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe, zimene Mzimu Woyera amapereka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:8

Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:13

Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36

Muphunzitse mtima wanga kuti uzikonda malamulo anu, osati chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:10

Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:16-17

Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:77

Mundichitire chifundo kuti ndikhale ndi moyo, pakuti malamulo anu amandikondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:1-2

Munthu aliyense azimvera akulu olamulira, chifukwa palibe ulamuliro umene sudachokere kwa Mulungu. Ndipo olamulira amene alipo, adaŵaika ndi Mulungu. Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena. Muchite zimenezi chifukwa mukudziŵa kuti yafika kale nthaŵi yakuti mudzuke kutulo. Pakuti chipulumutso chili pafupi tsopano kuposa pamene tidayamba kukhulupirira. Usiku uli pafupi kutha, ndipo mbandakucha wayandikira. Tiyeni tsono tileke ntchito za mdima, tivale zida zomenyera nkhondo kutayera. Mayendedwe athu akhale oyenera, ngati a anthu oyenda usana. Pasakhale dyera kapena kuledzera, dama kapena zonyansa, ndeu kapena nsanje. Ambuye Yesu Khristu mwini akhale chida chanu chankhondo. Lekani mtima wofunafuna zosangalatsa thupi, musagonjere zilakolako zake zoipa. Motero munthu wokana kumvera olamulira, akukana dongosolo limene adaliika Mulungu. Ndipo ochita zimenezi, adzadzitengera okha chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:12

Zinthu zonse nzololedwa kwa ine, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwadi kwa ine, koma sindingalole kuti chilichonse chindigonjetse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:89

Inu Chauta, mau anu ngokhazikika kumwambako mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:14

Kuyenda m'njira ya malamulo anu kumandikondwetsa, kupambana kukhala ndi chuma chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 12:13-14

Basi, zonse zamveka. Mfundo yeniyeni ya zonsezi ndi iyi: Uzimvera Mulungu, ndipo uzitsata malamulo ake, pakuti umenewu ndiwo udindo wake wonse wa munthu. Pajatu Mulungu adzaweruza zonse zimene timachita, zabwino kapena zoipa, ngakhale ndi zam'chinsinsi zomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 4:21-24

Inu ofuna kukhala akapolo a Malamulo, tandiwuzani. Kodi simukumvetsa zimene Malamulowo akunena? Paja Malembo akuti, Abrahamu anali ndi ana aamuna aŵiri: wina mai wake anali kapolo, winayo mai wake anali mfulu. Mwana amene mai wake anali kapolo uja, adabadwa monga momwe amabadwira ana onse. Koma mwana wina uja, amene mai wake anali mfulu, adabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu. Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:1-2

Chipangano choyamba chija chinali nawo malamulo okhudza chipembedzo, chinalinso ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu. Zimangonena za zakudya, za zakumwa, ndi za miyambo yosiyanasiyana ya kasambidwe. Zonsezo ndi malamulo olinga pa zooneka ndi maso chabe, oikidwa kuti azingokhalapo mpaka nthaŵi imene Mulungu adzakonzenso zonse. Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha. Magazi a atonde ndi a ng'ombe zamphongo, ndiponso phulusa la mwanawang'ombe wamkazi zimawazidwa pa anthu amene ali odetsedwa chifukwa chosasamala mwambo wachiyuda. Zimenezi zimaŵayeretsa pakuŵachotsa litsiro lam'thupi. Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo. Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija. Ngati munthu alemba Chipangano chosiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba chipanganocho wamwaliradi. Paja chipangano chotere chilibe mphamvu, asanamwalire wochilemba. Chimakhala ndi mphamvu pokhapokha wochilembayo atamwalira. Nchifukwa chake ngakhale Chipangano choyamba chija sichidachitike popanda kukhetsa magazi. Poyamba Mose adaalengeza kwa Aisraele malamulo onse, motsata Malamulo amene Mulungu adaampatsa. Pambuyo pake adatenga magazi a anaang'ombe amphongo ndi madzi, nawaza pa buku la Malamulo ndi pa anthu onse. Adaachita zimenezi ndi kanthambi ka chitsamba cha hisope, ndiponso ndi ubweya wankhosa wofiira. Anthu adaamanga chihema, ndipo m'chipinda chake choyamba munkakhala choikaponyale, tebulo, ndi mikate yoperekedwa kwa Mulungu. Chipinda chimenechi chinkatchedwa “Malo Opatulika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:6

Pakutero, chifukwa cha mwambo wanuwo, mau a Mulungu inu mumaŵasandutsa achabechabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23-24

popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chachikulu ndi zodabwitsa ntchito zanu Mulungu, mphamvu yanu ndi yopanda malire, ndinu wamuyaya komanso wangwiro m'njira zanu zonse, woyenera ulembo ndi kutambasula, palibe wina ofanana nanu, ndinu Mulungu woposa zonse, mavuto, mayesero ndi zochitika, nonse ndinu olungama, mulibe choipa chilichonse, mawu otuluka mkamwa mwanu ndi oona, palibe angawakayikire, wamasalimo anati ngati lamulo lanu silinali chisangalalo chake, m'masautso ake akanatha, choncho panopa ndikupemphani mundithandize kuyenda m'malamulo anu ndi kuwasunga chifukwa mmenemo ndimapeza phindu limene moyo wanga ukufuna, musalole kuti ndipatukane ndi mawu ndi malamulo anu, chifukwa ndikufuna kukusangalatsani Mulungu wanga, chifukwa chake ndikupemphani, wodzichepetsa pamaso panu kuti mundilole kukhala molungama pamaso panu, nthawi zonse ndikuchita chokondweretsa inu. Landirani ulemerero wonse, ulemu ndi mphamvu, ndikukuthokozani chifukwa cha kukoma mtima kwanu m'moyo wanga ndi zonse zomwe mwandithandiza, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa