Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Pakuti Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wopambana milungu yonse, ndiponso ndi Ambuye oposa ambuye onse. Ndi wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, sakondera, ndipo salandira ziphuphu.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri. Nwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndinu aakulu kwambiri. Mumavala ulemu ndi ufumu.
Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga. Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, amene akukhala kumwamba,
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire? Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo?
Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse. Ndiye yekha wosafa, ndipo amakhala m'kuŵala kosayandikizika. Chikhalire palibe munthu amene adamuwona, palibenso amene angathe kumuwona. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Amen.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu kwambiri, sitimdziŵa mpang'ono pomwe. Chiŵerengero cha zaka zake nchosadziŵika.
Chauta, Mfumu ndi Momboli wa Israele, Chauta Mphambe, akunena kuti, “Ine ndine woyamba ndi womaliza. Palibenso Mulungu wina, koma Ine ndekha.
Kodi Mfumu yaulemereroyo ndani? Ndi Chauta wanyonga ndi wamphamvu, Chauta ndiye ngwazi pa nkhondo.
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza.
Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Chauta, Ambuye athu, dzina lanu ndi lotchuka pa dziko lonse lapansi. Kumwamba amaimba nyimbo zotamanda ulemerero wanu. Nawonso ana ndi makanda omwe amauimbira. Mwamanga linga chifukwa cha adani anu, kuti mugonjetse onse okuukirani. Ndikamayang'ana ku thambo lanu limene mudapanga ndi manja anu, ndikamaona mwezi ndi nyenyezi zimene mudazikhazika kumeneko,
Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Palibe wolingana nanu, Inu Chauta. Inu ndinu aakulu, dzina lanu lili ndi mphamvu yaikulu. Ndani amene angaleke kukuwopani, Inu mfumu ya mitundu ya anthu? Paja kukuwopaniko nkokuyenerani. Pakati pa anthu anzeru onse ndiponso pakati pa maufumu onse a pansi pano palibe wina wolingana nanu.
Kodi ndani mu mlengalenga angathe kulingana ndi Chauta? Ndani pakati pa akumwamba amafanafana naye? Mulungu ndiye amene amamuwopa mu msonkhano wa anthu oyera mtima, ndiye wamkulu ndi wolemekezeka pakati pa onse omzungulira.
Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake.
Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.”
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse. Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse.
Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa. Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina. “Ndimalenga kuŵala ndi mdima, ndimadzetsa madalitso ndi tsoka. Ndine, Chauta, amene ndimachita zonsezi.
“Inu Ambuye athu ndi Mulungu wathu, ndinu oyenera kulandira ulemerero, ulemu ndi mphamvu, pakuti ndinu mudalenga zinthu zonse. Mudafuna kuti zonsezo zikhalepo, ndipo zidalengedwa.”
Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu? Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Mapiri asanabadwe, ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya.
Muuzeni Mulungu kuti, “Ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri. Mphamvu zanu nzazikulu, kotero kuti adani anu amakuŵeramirani moopa.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Inu Chauta, Mulungu wanga, mwatichitira zodabwitsa zambiri, mwatikonzera zabwino zambiri zakutsogolo. Palibe ndi mmodzi yemwe wotha kulingana nanu. Ndikati ndisimbe ndi kulongosola za zimenezo, sindingathe kuziŵerenga zonse chifukwa cha kuchuluka kwake.
Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi. Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
“Naŵa mau a Chauta amene adalenga dziko lapansi, naliwumba ndi kulikhazikitsa. Iyeyo dzina lakedi ndi Chauta. “Mau anga ndi aŵa: Ine ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku kotero kuti ziŵirizi zimafika pa nthaŵi yake. Ndipo chipanganocho sichingaphwanyike konse. Chimodzimodzinso ndidachita chipangano ndi Davide, mtumiki wanga, kuti nthaŵi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndidachitanso chipangano china ndi ansembe Achilevi kuti iwowo adzanditumikira nthaŵi zonse. Ndipo zipangano zimenezi sizingaphwanyike konse. Ndidzachulukitsa zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndi atumiki anga ansembe Achilevi, kuchuluka kwake ngati kwa nyenyezi zakuthambo kapena kwa mchenga wa m'mphepete mwa nyanja.” Chauta adafunsa Yeremiya kuti, “Kodi sudamve m'mene anthu ena akulankhulira, kumanena kuti, ‘Chauta wakana mabanja aŵiri aja amene adaŵasankha?’ Motero anthuwo amanyoza mpingo wanga osauyesanso ngati mtundu wa anthu. Koma Ine Chauta ndidachita chipangano ndi usana ndi usiku, ndipo ndidapanga malamulo oyendetsa zonse za pa dziko lapansi ndi zamumlengalenga. Tsono monga ndachita zimenezi motsimikiza, chonchonso ndidzachisunga chipangano chimene ndidachita ndi zidzukulu za Yakobe, ndiponso ndi Davide, mtumiki wanga. Ndidzasankhula mmodzi mwa zidzukulu za Davide kuti azilamulira zidzukulu za Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Komatu tsono ndidzaŵamvera chifundo ndi kuŵabwezeranso pabwino.” Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu. Wotchedwa Mauyo anali m'dziko lapansi, ndipo Mulungu adalenga dziko lapansilo kudzera mwa Iye, komabe anthu apansipano sadamzindikire. Adaabwera kwao ndithu, koma anthu ake omwe sadamlandire. Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu. Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja. Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.” Kuchokera m'kukoma mtima kwake kwathunthu ife tonse tidalandira madalitso, madalitso ake otsatanatsatana. Paja Mulungu adatipatsa Malamulo ake kudzera mwa Mose, koma kudzera mwa Yesu Khristu adatizindikiritsa kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake. Chikhalire palibe munthu amene adaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekha uja, amene ali wapamtima wa Atate, ndiye adaulula za Mulunguyo. Nthaŵi ina akuluakulu a Ayuda a ku Yerusalemu adaatuma ansembe ndi Alevi ena kukafunsa Yohane kuti, “Kodi iwe ndiwe yani?” Anali kwa Mulungu chikhalire. Iye adayankha mosabisa konse, adanenetsa ndithu kuti, “Inetu sindine Mpulumutsi wolonjezedwa uja ai.” Adamufunsanso kuti, “Nanga ndiwe yani? Ndiwe Eliya kodi?” Iye adati, “Iyai, sindine Eliya.” Iwo adati, “Kodi ndiwe Mneneri tikumuyembekeza uja?” Koma Yohane adayankha kuti, “Ainso.” Tsono adamuuza kuti, “Tanena zenizenitu, kuti tikaŵafotokozere bwino amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe yani?” Yohane adaŵayankha kuti, “Monga adaanenera mneneri Yesaya: “Ine ndine liwu la munthu wofuula m'chipululu; akunena kuti, ‘Ongolani mseu wodzadzeramo Ambuye.’ ” Anthu aja adaaŵatuma ndi Afarisi. Tsono adafunsa Yohane kuti, “Ngati sindiwe Mpulumutsi wolonjezedwa uja, kapena Eliya, kapenanso Mneneri tikumuyembekeza uja, nanga bwanji umabatiza?” Yohane adaŵayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panupa pali wina amene inu simukumdziŵa. Iyeyu ngwobwera pambuyo panga, komabe sindili woyenera ngakhale kumasula zingwe za nsapato zake.” Zimenezi zidachitikira ku Betaniya, kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatiza. M'maŵa mwake Yohane adaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo adati, “Suuyu Mwanawankhosa wa Mulungu uja, wochotsa machimo a anthu a pa dziko lonse lapansi. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
Chifukwa mwana watibadwira, mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife. Ulamuliro udzakhala m'manja mwake, ndipo adzamtchula dzina lake lakuti “Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Amuyaya, Mfumu ya Mtendere.”
Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu, amene amakhululukira machimo ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala? Simusunga mkwiyo mpaka muyaya, chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika. Mudzatichitiranso chifundo. Mudzapondereza pansi zolakwa zathu, mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.
Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Mulungu ndi wanzeru, ndipo ndi wamphamvu kwambiri. Palibe munthu amene angathe kulimbana naye, popanda kupwetekerapo.
Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta.
Chauta, Mpulumutsi wako, amene adakupanga m'mimba mwa mai wako, akunena kuti, “Ndine Chauta, amene ndidapanga zinthu zonse. Pamene ndinkayalika zakuthambo, ndinali ndekha. Pamene ndinkalenga dziko lapansi, kodi analipo amene adandithandiza?
Musaŵaope anthu ameneŵa. Chauta Mulungu wanu ali nanu. Iyeyo ndiye Mulungu wamkulu woyeneradi kumuwopa.
Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu. Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo.
Chauta ndiye mfumu. Wavala ulemerero, wavala mphamvu ngati lamba. Iye adakhazikitsa dziko lapansi, silidzagwedezeka konse.
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Dziŵani kuti Chauta ndiye Mulungu. Ndiye amene adapanga ife, ndipo ifeyo ndife ake. Ndife anthu ake, nkhosa za busa lake.
Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
“Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi!
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula, akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi, kuyambira kotulukira dzuŵa mpaka koloŵera kwake. “Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango ndi yanga, pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka. Mbalame zonse zamumlengalenga, zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga. “Ndikadakhala ndi njala sindikadakuuzani, pakuti dziko lonse ndi zonse zam'menemo, ndi zanga. Kodi ndimadya nyama yang'ombe kapena magazi ambuzi? “Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu, ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse. Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.” Koma kwa munthu woipa Mulungu amati, “Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga? Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa? Iwe sufuna kulangizidwa, umaponya mau anga ku nkhongo. “Ukaona mbala umasanduka bwenzi lake, ndipo umayenda ndi anthu achigololo. Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako, lilime lako limapeka mabodza. Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni, mzinda wake wokongola kotheratu.
Mitundu ya anthu ili ngati kadontho ka madzi mu mtsuko, ilinso ngati fumbi chabe pa sikelo. M'manja mwa Chauta zilumba nzopepuka ngati fumbi. Nkhalango ya ku Lebanoni siingakwanitse nkhuni zosonkhera moto, nyama zam'menemo sizingakwanire kuperekera nsembe yootcha. Mitundu yonse ya anthu si kanthu konse pamaso pa Chauta, Iye amaziyesa zachabe ndi zopandapake.
Chauta ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro, njira zake zonse ndi zolungama, ndi Mulungu wokhulupirika ndi wosaipa konse, wachilungamo ndi wosalakwa.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa. Kuwopa Chauta ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Chiweruzo cha Chauta nchoona, ncholungama nthaŵi zonse.
Chauta amene ali pamwamba, ndi wamphamvu kupambana kulindima kwa madzi ambiri, ndi wamphamvu kuposa mafunde am'nyanja.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.
Imbani mokondwa, inu zolengedwa zamumlengalenga! Fuula ndi chimwemwe, iwe dziko lapansi! Yambani nyimbo, inu mapiri! Chauta watonthoza mtima anthu ake, ndi kuŵamvera chifundo anthu ake ovutika.
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse? Mumalamulira nyanja yaukali. Mafunde ake akakwera, Inu mumaŵakhalitsa bata.
Kumwamba ndi zonse zili kumeneko ndi zake za Chauta, pamodzi ndi dziko lapansi pano ndi zonse zili m'menemo.
Komabe Iye adaŵapulumutsa malinga ndi ulemerero wa dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Apo Mose adapempha Chauta kuti, “Chonde mundiwonetse ulemerero wanu.” Pamenepo Chauta adayankha kuti, “Ndikudzakuwonetsa ulemerero wanga wonse, ndipo ndidzatchula dzina langa loti Chauta pamaso pako. Ndidzakomera mtima amene nditi ndimkomere mtima, ndipo ndidzachitira chifundo amene nditi ndimchitire chifundo.”
Ndani adachita zimenezi mpaka kuzitsiriza, osakhala amene adayambitsa mitundu yonse ya anthu? Ndi Ineyo, Chauta, amene ndine chiyambi, ndipo ndidzakhalabe yemweyo pakati pa otsiriza.”
“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.”
Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwao konse kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo.
Pakuti ndimadziŵa kuti Chauta ndi wamkulu, kuti Chauta, Mulungu wathu, ndi wamphamvu kupambana milungu yonse. Chilichonse chimene Chauta amafuna kuchita amachitadi kumwamba ndi pa dziko lapansi, m'nyanja ndi monse mozama.
Choncho anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe kuti Chauta ndiye Mulungu, palibenso wina.
Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.
Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
“Ndikudziŵa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse, chimene mufuna kuchita, wina sangaletse konse.
Inu mudaika maziko a dziko lapansi kalekale, ndipo zakumwamba mudazipanga ndi manja anu. Zonsezi zidzatha ngati malaya, koma Inu mulipobe. Inu mumazisintha ngati chovala, ndipo zimatha. Koma Inu simusintha, zaka zanu sizitha.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake, ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba.
Manja anga adamanga maziko a dziko lapansi, dzanja langa lamanja lidafunyulula mlengalenga. Ndikaitana dziko lapansi ndi dziko lakumwamba, zonsezo zimabwera pamodzi kwa Ine.
Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana. Maziko a ufumu wanu ndiwo kulungama ndi kuweruza mosakondera. Mumaonetsa chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika pa zonse zimene mumachita.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Mpando wanu waufumu, Inu Chauta, mudaukhazikitsa kuyambira makedzana, Inu ndinu amuyaya.
Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati, “Aleluya! Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira.
Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu, ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse. Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso. Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga.
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Moyo wosathawo ndi wakuti akudziŵeni Inu, amene nokhanu ndinu Mulungu weniweni, ndipo adziŵenso Yesu Khristu amene mudamtuma.
Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa. Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina.
Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye. “Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha?
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Munyadire dzina lake loyera. Ikondwe mitima ya anthu amene amapembedza Chauta. Dziko lao lidadzaza ndi achule, ngakhale m'zipinda za mafumu zomwe. Adalankhula, ndipo kudatuluka ntchentche zochuluka, mtundu wa udzudzu udaloŵa m'dziko mwao monse. Adaŵagwetsera matalala m'malo mwa mvula, adaŵagwetsera ching'aning'ani chimene chinkang'anima m'dziko mwao monse. Adagwetsa mipesa yao ndi mikuyu yao, adathyola mitengo yonse ya m'dziko mwao. Adalankhula, ndipo kudafika dzombe ndi mandowa osaŵerengeka, amene adaononga zomera zonse za m'dziko mwao, nadya zipatso zonse za m'minda mwao. Iye adapha ana onse achisamba m'dziko mwao, ana onse oyamba, oŵabala akadali abiriŵiri. Kenaka Chauta adaŵatulutsa Aisraele atatenga siliva ndi golide, pakati pa mafuko awo panalibe amene adafooka. Aejipito adasangalala pamene iwo adapita, chifukwa ankachita nawo mantha anthuwo. Chauta adaika mtambo kuti uziphimba anthu ake, adaika moto kuti uziŵaunikira usiku. Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
“Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu. Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake? Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, popeza kuti wachita zodabwitsa. Dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zampambanitsa.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula. Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali. Monga momwe nthaka imameretsera mbeu, ndiponso monga momwe munda umakulitsira zimene adabzalamo, momwemonso Chauta adzaonetsa chilungamo ndi ulemerero wake pamaso pa anthu onse. Wandituma kukalengeza za nthaŵi imene Chauta adzapulumutsa anthu ake ndi kulipsira adani ake. Wanditumanso kukatonthoza olira. Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu, ulamuliro wake uli pa Israele, mphamvu zake zili mu mlengalenga. Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika, Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu ndi kuŵalimbikitsa anthu ake. Mulungu atamandike.
Chauta ndiye amene adalenga dziko lapansi ndi mphamvu zake. Ndiye amene adapanga zonse ndi nzeru zake ndipo ndi umisiri wake adayala thambo lakumwamba. Iye akalankhula, kumamveka mkokomo wa madzi kumwamba, ndiye amene amadzetsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi. Amang'animitsa mphezi za mvula, amakunthitsa mphepo kuchokera kumene amaisunga.
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta, dziko lonse lapansi pamodzi ndi anthu onse okhalamo ndi ake.
“Ndaninso kodi akuchokera ku Edomuyu, atavala zofiira za ku Bozira? Ndani ameneyu wovala zovala zokongola, akuyenda monyadira mphamvu zake? Ndi Ineyo, wolankhula zachilungamo, ndiponso wa mphamvu zoti nkupulumutsa.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Mulungu, amene Iye yekha ndiye Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye athu, akhale ndi ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, isanayambe nthaŵi, tsopano, ndi mpaka muyaya. Amen.