Mulungu ndiye mlengi ndi wosunga zonse ndi chilichonse. Iye ndi wamuyaya, wopanda malire, ndi wosasinthika mu mphamvu ndi ungwiro wake, ubwino ndi ulemerero wake, nzeru zake, chilungamo chake, ndi choonadi chake. Palibe chomwe chimachitika popanda Iye ndi chifuniro chake.
Monga momwe lemba la Masalmo 86:8-10, 15 limanenera, "Palibe wina wonga Inu pakati pa milungu, Ambuye, ndipo palibe ntchito zonga zanu. Mitundu yonse yomwe munalenga idzabwera ndi kulambira pamaso panu, Ambuye, ndi kulemekeza dzina lanu. Pakuti Inu ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa; Inu nokha ndinu Mulungu. Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndi wodzala ndi chifundo. Wodekha kukwiya ndipo wochuluka chifundo ndi choonadi."
Kwa ena, Mulungu ndi kumverera kosaneneka, kapena chiyambi cha chilengedwe chonse, kapena munthu wodzala ndi ukulu. Koma tikulankhula za Mulungu wa m'Baibulo, ndipo Mulungu wa m'Baibulo amadzidziwitsa yekha. Amanena kuti ndi wamuyaya ndi wolungama. Ndi Mulungu wachikondi. Ndi Mulungu wopambana zonse; kutanthauza kuti, ali pamwamba pa malo, nthawi, ndi mbiri. Komabe, Iye ndi Mulungu wapafupi; kutanthauza kuti, ali pafupi kwambiri ndi ife moti sitingathe kumuthawa. Ali paliponse, ndi wosasinthika, ndi wodalirika, ndi munthu weniweni.
Baibulo siliyesa kutsimikizira kukhalapo kwa Mulungu, koma limayamba ndi mfundo yakuti alipo kuyambira pachiyambi. Mulungu ndiye Mlengi ndi Wolamulira wa zonse zomwe zilipo, wangwiro mu mphamvu, ubwino, ndi nzeru. Mulungu ndi mzimu, wopanda malire, ndi wosaoneka. Alipo mwa Anthu atatu osiyana: Mulungu Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera. Ndi wosayerekezeka, wosasinthika, ndipo ali paliponse.
Tsono Chauta adzakhala mfumu ya dziko lonse lapansi. Tsiku limenelo Chauta yekha anthu onse adzampembedza, adzamdziŵa ndi dzina lake limodzi lokhalo.
Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu.
Pajatu Mulungu ndi mmodzi yekha, Mkhalapakati mmodzi yekhanso pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja timati Khristu Yesu.
Nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wakutiwakuti, koma amene adapanga zonse, ndi Mulungu.
Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.
Mapiri asanabadwe, ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya.
“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.
Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Musadzinyenge, nkosatheka kupusitsa Mulungu. Zimene munthu amabzala, adzakolola zomwezo.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.
Chithandizo chathu chimachokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Ndimamuuza Chauta kuti, “Inu ndinu Ambuye anga. Ndilibe chinthu china chabwino koma Inu nokha.”
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.
Kumeneko inu mudzafunafuna Chauta, Mulungu wathu, ndipo ngati mudzamfunafuna ndi mtima wonse ndi moyo wanu wonse, mudzampeza.
Koma Inu Chauta, ndinu mfumu mpaka muyaya, mpando wanu waufumu udzakhalapo pa mibadwo yonse.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Mpaka mudzakalambe ndidzakhalabe Yemwe uja, mpaka mudzamere imvi ndidzakusamalani ndithu. Ndidakulengani, ndipo ndidzakunyamulani. Ndidzakusenzani ndipo ndidzakuwombolani.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Abramu ali wa zaka 99, Chauta adamuwonekera namuuza kuti, “Ine ndine Mulungu Mphambe. Tsono uzindimvera nthaŵi zonse, ndipo uzichita zolungama.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha. Nyama zakuthengo zidzandilemekeza, nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda, chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma, kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa. Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera, ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.” Chauta akuti, “Koma simudapemphere kwa Ine, inu am'banja la Yakobe, mudatopa nane, inu Aisraele. Simudadzatule kwa Ine nkhosa kuti zikhale zopereka zopsereza, simudandilemekeze ndi nsembe zanu. Sindidakulemetseni pomakupemphani zopereka zanu, sindidakutopetseni pomakupemphani lubani. Simudandigulire bango lonunkhira, simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu. Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu, mwandilemetsa ndi zolakwa zanu. “Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu. Mundikumbutse zakale, titsutsane. Mufotokoze mlandu wanu kuwonetsa kuti simudalakwe. Atate anu oyamba adachimwa, atsogoleri anu aja adandilakwira. Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika. Nchifukwa chake ndidalola kuti banja la Yakobe liwonongedwe, ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.” Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako. Ndine Woyera uja wa Israele, Mpulumutsi wako. Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe. Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Nchifukwa chake monga Atate anu akumwamba ali abwino kotheratu, inunso mukhale abwino kotheratu.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi. Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake. Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri. Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu. Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika. Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu. Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga. Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake. Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
Tamandani Chauta, Mulungu wathu, mpembedzeni ku phiri lake loyera. Chauta, Mulungu wathu, ndi woyera.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Chiyambire unyamata wanga mpaka ukalamba wanga uno, sindidaonepo munthu wabwino atasiyidwa ndi Mulungu, kapena ana ake akupempha chakudya.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja. Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.
Paja mau a Mulungu akuti, “Muzikhala oyera mtima popeza kuti Ineyo ndine woyera mtima.”
Makolo athu ankadalira Inu. Zoonadi, ankakhulupirira Inu, ndipo Inu munkaŵapulumutsa. Ankalirira Inu, ndipo Inu munkaŵalanditsa. Ankakhulupirira Inu, ndipo Inu simunkaŵagwiritsa mwala.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina. Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu.
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Tikudziŵa kuti Mwana wa Mulungu adafika, ndipo adatipatsa nzeru kuti timdziŵe Mulungu woona. Ndipo tili mwa Mulungu woonayo, chifukwa tili mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iyeyo ndiye Mulungu woona ndiponso moyo wosatha.
Sadaŵakayikire konse mau a Mulunguyo, koma adalimbikira m'chikhulupiriro, nayamika Mulungu. Adakhulupirira ndithu kuti Mulungu angathe kuchita zimene adalonjeza.
Ndimakukondani Chauta, Inu mphamvu zanga. Adakwera pa mkerubi nauluka. Adayenda mwaliŵiro ndi mphepo. Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. M'kuŵala kumene kunali pamaso pake, munkafumira matalala ndi makala amoto, amene adabzola mitambo yophimba ija. Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto. Adaponya mivi yake nabalalitsa adani ake, adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Ngalande zozama zam'nyanja zidaonekera, maziko a dziko lapansi adakhala poyera, pamene Inu Chauta mudakhuluma mokalipa, pamene mudatulutsa mpweya wamphamvu m'mphuno mwanu. Ali kumwamba Chauta adatambalitsa dzanja nandigwira, ndi kundivuula m'madzi ozama. Adandipulumutsa kwa adani anga amphamvu, kwa onse amene ankadana nane, pakuti iwo anali amphamvu kwambiri kupambana ine. Adaniwo adandithira nkhondo pamene ndinali m'mavuto, koma Chauta adandichirikiza. Adakandifikitsa ku malo amtendere, adandipulumutsa chifukwa adakondwera nane. Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Anthu okonda malamulo anu ali ndi mtendere waukulu, palibe china chotha kuŵagwetsa.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Zitatha izo Mulungu adati, “Tiyeni tipange munthu m'chifanizo chathu, adzakhale wonga Ifeyo. Adzalamulire nsomba zam'nyanja, mbalame zamumlengalenga, nyama zoŵeta, ndi zokwaŵa zonse za pa dziko lapansi.” Motero Mulungu adalenga munthu, m'chifanizo chake, adaŵalengadi m'chifanizo cha Mulungu. Adaŵalenga wina wamwamuna wina wamkazi.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Ndikupereka mtima wanga kwa Inu Chauta. Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake. Malinga ndi ulemerero wa dzina lanu, Inu Chauta, mundikhululukire machimo anga pakuti mlandu wanga ndi waukulu. Kodi pali munthu woopa Chauta? Munthuyo Chauta adzamphunzitsa njira yoti aitsate. Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao. Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake. Maso anga akuyang'ana kwa Chauta nthaŵi zonse, pakuti adzaonjola mapazi anga mu ukonde. Inu Chauta yang'aneni ine, ndipo mundikomere mtima, pakuti ndili ndekhandekha, ndipo ndazunzika kwambiri. Mundichotsere nkhaŵa za mumtima mwanga, ndipo munditulutse m'masautso anga. Penyani mazunzo anga ndi mavuto anga, ndipo mundikhululukire machimo anga onse. Onani m'mene adani anga ankhalwe achulukira ndi m'mene chidani chao ndi ine chakulira. Ndikuika mtima wanga pa Inu Mulungu wanga. Musalole kuti adani anga andichititse manyazi, musalole kuti akondwere pamene ine ndikuvutika. Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu. Kukhulupirika kwanga ndi kulungama kwanga kunditeteze, popeza kuti ndakukhulupirirani. Inu Mulungu apulumutseni m'mavuto ao onse anthu anu Aisraele. Zoonadi, onse okhulupirira Inu asaŵachititse manyazi, koma muchititse manyazi onse ochita dala zosakhulupirika.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake. Mtima wanga umayembekeza Chauta kupambana m'mene alonda amayembekezera mbandakucha, kupambanadi m'mene alonda amayembekezera mbandakucha.
Pa nthaŵi yake Mulungu adzamuwonetsa kwa ife. Mulunguyo ngwodala ndipo Iye yekha ndiye Wolamula, ndiye Mfumu ya mafumu onse, ndiponso Mbuye wa ambuye onse.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ngwodala munthu amene amadalira Chauta, munthu amene sapatukira ku mafano kapena kutsata milungu yonama.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Tsono ngati Mulungu amaveka motere udzu wakuthengo, umene ungokhalapo lero lokha, maŵa lino nkuponyedwa pa moto, nanji inuyo, angapande kukuvekani, inu a chikhulupiriro chochepanu? “Nchifukwa chake musamada nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Tidzadyanji? Tidzamwanji? Tidzavalanji?’
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Tsono tikamati, “Ambuye,” tikunena Mzimu Woyera. Ndipo kumene kuli Mzimu wa Ambuye, kuli ufulu.
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.