Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Ine ndidaŵaonekera ndili chakutali. Inu Aisraele ndakukondani kwambiri ndi chikondi chopanda malire, ndakhala wokhulupirika kwa inu mpaka tsopano.
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana. Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu.
Palibe munthu amene ali ndi chikondi choposa ichi chakuti nkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Aliyense wokantha inu, wakantha chinthu cha mtengo wapatali zedi kwa Ine.” Tsono Chauta Wamphamvuzonse adandituma kwa mitundu imene idaagwira anthu ake kukaiwuza uthenga wake wakuti,
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni. Tulani pa Iye nkhaŵa zanu zonse, popeza kuti Iye ndiye amakusamalirani.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi. Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse. Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha. M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Chikondi cha Khristu ndicho chimatiwongolera mokakamiza, popeza kuti tikudziŵa mosakayika konse kuti Munthu mmodzi adafera anthu onse, ndiye kuti pamenepo onse adafa. Iye adafera anthu onse, kuti amene ali ndi moyo, asakhalenso ndi moyo wofuna kungodzikondweretsa okha, koma azikondweretsa Iye amene adaŵafera, nauka kwa akufa chifukwa cha iwowo.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Chikondi ncholeza mtima ndiponso nchofatsa. Chikondi chilibe kaduka, ndipo sichidzitamanda kapena kudzikuza. Chikondi chilibe matama kapena chipongwe, sichidzikonda, sichikwiya, sichisunga mangaŵa. Sichikondwerera zosalungama, koma chimakondwerera choona. Chikondi chimakhululukira zonse, chimakhulupirira nthaŵi zonse, sichitaya mtima, ndipo chimapirira onse. Chikondi nchosatha. Uneneri udzatha, kulankhula zilankhulo zosadziŵika kudzalekeka, ndipo nzeru za anthu zidzatha.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Onani mbalame zamumlengalenga. Sizifesa kapena kukolola kapena kututira m'nkhokwe ai. Komabe Atate anu akumwamba amazidyetsa. Nanga inu sindinu amtengowapatali kuposa mbalame?
Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Ambuye aongolere maganizo anu kuti muziyenda m'chikondi cha Mulungu, ndikutsata khama la Khristu.
“Munthu amene alandira malamulo anga naŵatsata, ndiye amandikonda. Ndipo amene andikonda Ine, Atate anga adzamkonda. Inenso ndidzamkonda munthuyo, ndipo ndidzadziwonetsa kwa iye.”
Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.
pakuti okukondani ndi Atate amene. Amakukondani chifukwa mumandikonda, ndipo mumakhulupirira kuti ndidachokera kwa Iwo.
Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Inu okondedwa, tizikondana, pakuti chikondi nchochokera kwa Mulungu. Aliyense amene ali ndi chikondi, ndi mwana wa Mulungu, ndipo amadziŵa Mulungu. Koma munthu wopanda chikondi sadziŵa Mulungu, pakuti Mulungu ndiye chikondi chimene.
Zoona, Ine ndiye amene ndimadziŵa zimene ndidakukonzerani, zakuti mudzakhala pabwino osati poipa, kuti mukhale ndi chiyembekezo chenicheni pa zakutsogolo.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano. Uchimo udaloŵa m'dziko lapansi chifukwa cha munthu mmodzi, ndipo uchimowo udadzetsa imfa. Motero imfa idafalikira kwa anthu onse, popeza kuti onse adachimwa. Uchimo udaalipo pa dziko lapansi Mulungu asanapereke Malamulo. Koma pamene palibe Malamulo, machimo a munthu saŵerengedwa ai. Komabe kuyambira nthaŵi ya Adamu kufikira nthaŵi ya Mose, imfa inali ndi ulamuliro pa anthu onse. Inali ndi ulamuliro ngakhalenso pa amene kuchimwa kwao kunkasiyana ndi kuchimwa kwa Adamu, amene adaphwanya lamulo la Mulungu. Adamuyo amafanizira Iye uja amene Mulungu adaati adzabwerayu. Koma sitingafananitse mphatso yaulere ya Mulungu ndi kuchimwa kwa Adamu ai. Pajatu anthu ambiri adafa chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodziyo, koma kukoma mtima kwa Mulungu, ndiponso mphatso yake yaulere, zidaposa ndithu, chifukwa zidabweretsera anthu ambiri madalitso ochuluka. Mphatso imene Mulungu adaperekayo ndiye Munthu mmodzi uja, Yesu Khristu. Palinso kusiyana pakati pa mphatso imeneyi ya Mulungu ndi zotsatira zake za kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja. Pakuti iye uja atachimwa kamodzi, Mulungu adagamula kuti alangidwe. Koma mphatso ya kukoma mtima kwa Mulungu ndi yakuti anthu amakhala olungama ngakhale zochimwa zao zinali zambiri. Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo. Motero, monga tchimo limodzi lidadzetsa chilango pa anthu onse, momwemonso ntchito imodzi yolungama imadzetsa chilungamo kwa anthu onse ndi kuŵapatsa moyo. Pakuti monga anthu ambiri adasanduka ochimwa, chifukwa cha kusamvera kwa munthu mmodzi uja, momwemonso anthu amapezeka kuti ngolungama, chifukwa cha kumvera kwa Munthu winanso mmodzi. Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu, kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya. Tamandani Chauta!
Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wachifundo. Sadzakulekererani kapena kukuwonongani. Chipangano chimene Iye adachita molumbira ndi makolo anu, sadzachiiŵala.
Motero ife timadziŵa ndipo timakhulupirira ndithu kuti Mulungu amatikonda. Mulungu ndiye chikondi, ndipo munthu wokhala ndi moyo wachikondi, amakhala mwa Mulungu, Mulungunso amakhala mwa iye.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Koma ndi monga Malembo anenera kuti, “Maso a munthu sanaziwone, makutu a munthu sanazimve, mtima wa munthu sunaganizepo konse zimene Mulungu adaŵakonzera amene amamkonda.”
Adayenda pamaso pa Mose nanena mokweza kuti, “Chauta, Chauta, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndiponso wokhulupirika kwa anthu ake. Amaonetsa chikondi chake kwa anthu zikwi zambirimbiri, ndipo amaŵakhululukira mphulupulu zao, zoipa zao, ndi machimo ao. Koma sadzalekerera ochimwa, ndipo adzalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha zoipa za atate ao, mpaka mbadwo wachitatu ndi wachinai.”
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Chikondwerero cha Paska chili pafupi, Yesu adaadziŵiratu kuti nthaŵi yake yafika yakuti achoke pansi pano kupita kwa Atate. Iye ankaŵakonda amene anali ake pansi pano, ndipo adaaŵakonda kotheratu.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Chikondi chanu chosasinthika chakhazikika kuti chikhale mpaka muyaya, kukhulupirika kwanu nkwachikhalire ngati mlengalenga.
Adzasamala nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa anaankhosa ndi kuŵakumbatira. Ndipo adzatsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni. Koma si pokhapo ai, timakondwera mwa Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, amene atiyanjanitsa ndi Mulungu tsopano.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika.
Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Ine ndikhale mwa iwo, Inu mwa Ine, kuti akhale amodzi kwenikweni. Motero anthu onse adzazindikira kuti mudandituma ndinu, ndipo kuti mumaŵakonda monga momwe mumandikondera Ine.
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chimafika mpaka kumwamba, kukhulupirika kwanu kumafika mpaka ku mitambo. Kulungama kwanu kumaonekera ngati mapiri aatali, kuweruza kwanu nkozama ngati nyanja yakuya, Inu Chauta, mumasamalira anthu ndi nyama zomwe.
Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera Kumwamba, kwa Atate a zounikira zonse zakuthambo. Iwo sasinthika konse, ndipo kuŵala kwao sikutsitirika mpang'ono pomwe.
Chauta ndiye mbusa wanga, sindidzasoŵa kanthu. Amandigoneka pa busa lamsipu. Amanditsogolera ku madzi odikha kokapumulirako. Amatsitsimutsa moyo wanga. Amanditsogolera m'njira za chilungamo malinga ndi ulemerero wa dzina lake.
Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake. Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake.
Tsono abale, kondwani. Mverani zimene ndikukulangizani, ndipo mukonze zimene zidalakwika. Muzimvana ndi kukhala mu mtendere. Pamenepo Mulungu wachikondi ndi wamtendere adzakhala nanu.
Iwe Israele, khulupirira Chauta. Paja Chauta ndi wa chikondi chosasinthika, ndi wokonzeka kupulumutsa.
Mukatero mudzakhaladi ana a Atate anu amene ali Kumwamba. Paja Iwo amaŵalitsa dzuŵa lao pa anthu abwino ndi pa anthu oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira. Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe. Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu. Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.
Ndidaakufulatira pa mphindi yaing'ono ndili wokwiya zedi, koma ndidzakuwonetsa chikondi changa mpaka muyaya,” akuterotu Chauta, Momboli wako.
Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.
Kuika mtima pa khalidwe lopendekera ku zoipa, ndi imfa yomwe, koma kuika mtima pa zimene Mzimu Woyera afuna, kumabweretsa moyo ndi mtendere.
Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?
Muzikomerana mtima ndi kuchitirana chifundo, ndipo muzikhululukirana monga momwe Mulungu mwa Khristu adakukhululukirani inunso.
Koma ine ndili ngati mtengo wauŵisi wa olivi m'Nyumba ya Mulungu. Ndimaika mtima nthaŵi zonse pa chikondi chosasinthika cha Mulungu.
Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza. Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika. Chauta ndi wabwino kwa onse, amachitira chifundo zamoyo zonse zimene adazilenga.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa. ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza. Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,” ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala. Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga. Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri. Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga. Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe. Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse. Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube. Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere. Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali. Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa. Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani? Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga. Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya. Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.
Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Ngati munthu akonda mnzake, sangamchite choipa ai. Nchifukwa chake amene amakonda mnzake, wasunga zonse zimene Malamulo a Mulungu akunena.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.” Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Mulungu ndi wokhulupirika, ndipo Iye ndiye amene adakuitanani kuti mukhale a mtima umodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu Ambuye athu.
Chauta akunena kuti, “Ukumbukire zimenezi, iwe Yakobe, popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israele. Ndidakulenga, ndiwe mtumiki wanga. Iwe Israele sindidzakuiwala.
Onse amene Mzimu wa Mulungu amaŵatsogolera, amenewo ndi ana a Mulungu. Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Ndidaŵadziŵitsa dzina lanu, ndipo ndidzaŵaphunzitsabe. Ndifuna kuti chikondi chimene mumandikonda nacho, chikhalenso mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Monga mnyamata amakwatira namwali, chonchonso mmisiri wodzakumanganso adzakukwatira. Monganso mkwati wamwamuna amakondwerera mkwati wamkazi, chonchonso Mulungu adzasangalala nawe.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
“Koma anthu amene mudaŵaombola, mudaŵatsogolera ndi chikondi chanu chosasinthika. Mudaŵatsogolera ku malo anu oyera ndi mphamvu zanu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera. Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Ambuye athu adandikomera mtima koposa, nkundipatsa chikhulupiriro ndi chikondi zimene tili nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza. Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka. Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Bwenzi lako ndiye amakukonda nthaŵi zonse, ndipo mbale wako adabadwira kuti azikuthandiza pa mavuto.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira.
Iye amachita zolungama ndi kuweruza mosakondera. Amaonetsa chikondi chosasinthika pa dziko lonse lapansi.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Mulungu Atate athu adatikonda, ndipo mwa kukoma mtima kwake adatipatsa kulimba mtima kosatha ndi chiyembekezo chokoma. Iye pamodzi ndi Yesu Khristu Ambuye athu athuzitse mitima yanu ndi kukupatsani mphamvu za kuchita ndi kulankhula zabwino zilizonse.
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo. Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake.