Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.
ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.
Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.
Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa.
Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?
Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga.
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.
Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.
Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga, Inu Chauta mumaŵadziŵa onse.
Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Ndi monga mau a Mulungu anenera kuti, “Ndani amadziŵa maganizo a Chauta, ndani angamupatse malangizo?
“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako, ndinali nditakudziŵa kale. Usanabadwe nkomwe, ndinali ntakupatula kale, ndidakuika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
“Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, uzimvera Mulungu wa atate ako, ndipo uzimtumikira ndi mtima wonse, modzipereka kwathunthu. Paja Chauta amasanthula mtima wa munthu aliyense, ndipo amadziŵa maganizo a munthu aliyense. Ukamfunafuna, udzampeza. Koma ukalekana naye, Iyeyo adzakutaya mpaka muyaya.
Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta.
Chauta ali kumwamba, amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse.
Kumene amakhala pa mpando wachifumuko, amapenya anthu onse okhala pa dziko lapansi
Amene amapanga mitima ya anthu onse, ndiye amene amapenya ntchito zao zonse.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.
Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
“Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo ndi kuuyesa mtimawo. Ndimamchitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenerera ntchito zake.”
Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Kodi alipo wina woti angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iyeyo amaweruza ngakhale anthu apamwamba?
Koma Yesu sadaikepo chikhulupiriro pa iwowo, popeza kuti Iye ankaŵadziŵa anthu onse.
Sankalira kuti wina achite chomuuza za munthu aliyense. Pakuti mwiniwakeyo ankadziŵa za m'mitima mwa anthu.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
Ndani adalamulirapo maganizo a Chauta? Ndani adamphunzitsapo kanthu ngati mlangizi wake?
Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
“Koma Ine ndimadziŵa zonse za iwe, pamene ukhala pansi, pamene uyenda kwina ndi kubwerako, ndiponso pamene undikwiyira.
Paja Iye amayang'ana mpaka ku mathero a dziko lapansi, amaona zonse zimene zili kunsi kwa thambo.
Pamenepo Mzimu wa Chauta udandigwira, ndipo udandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Chauta ndi izi, akuti, ‘Inu a m'banja la Israele, ndikudziŵa zimene zili mumtima mwanu.
Ukanena kuti, “Ife sitidazidziŵe zimenezi,” kodi iye amene amayesa mtima, zimenezi saziwona? Kodi amene amayang'anira moyo wako sazidziŵa? Kodi sadzambwezera munthu potsata ntchito zake?
Maso anga amaona makhalidwe ao onse oipa, ndi osabisika pamaso panga. Palibenso tchimo lililonse limene sindikulidziŵa.
Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino.
Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Pamene adatumphutsa madzi kuchoka kunsi kwa dziko, ndipo mitambo idagwetsa mvula, adaonetsa nzeru zodziŵa zinthu.
Anthu inu musalankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zodzikuza. Pakuti Chauta ndi Mulungu wanzeru, ndiye amene amaweruza ntchito za anthu.
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.
Muzikumbukira ntchito zodabwitsa za Chauta, zozizwitsa zimene adachita, ndi m'mene ankaweruzira anthu,
Palibe usiku kapena mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoipa angathe kubisalira Mulungu.
Tsoka kwa amene amabisira Chauta maganizo ao, amene amachita ntchito zao mu mdima, namaganiza kuti palibe amene akuŵaona ndi kudziŵa zimene akuchita.
pamenepo Inuyo mumve kumwambako kumene mumakhala. Mukhululuke, ndipo muchitepo kanthu. Mumchitire aliyense potsata makhalidwe ake onse, pakuti Inu mukudziŵa mtima wake. Inu nokha ndinu amene mumadziŵa mitima ya anthu.
Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.”
Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.
“Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga.
Yesu adamufunsa kachitatu kuti, “Iwe Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda?” Petro adayamba kumva chisoni kuti Yesu akumufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda?” Ndipo adati, “Ambuye, mumadziŵa zonse. Mukudziŵa kuti ineyo ndimakukondani.” Yesu adamuuza kuti, “Samala nkhosa zanga.
“Zonsezi udazimva, tsono uzilingalire bwino. Monga iweyo sungazivomereze? Kuyambira tsopano mpaka m'tsogolo muno ndidzakuuza zinthu zatsopano, zinthu zobisika zimene sudazidziŵe konse.
Komabe Mulungu amadziŵa m'mene ndimayendera, akandiyesa adzapeza kuti ndine wangwiro ngati golide.
Kodi amene adalenga makutu, sangathe kumva? Kodi amene adapanga maso, sangathe kupenya?
Tikudziŵa kuti timakhala mwa Mulungu, ndipo Iyenso amakhala mwa ife, chifukwa adatipatsa Mzimu wake Woyera.
“Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi!
Komabe maziko olimba, amene Mulungu adaŵaika, ngokhazikika, ndipo mau olembedwapo ndi aŵa: “Ambuye amadziŵa amene ali ao”, ndiponso, “Aliyense wotamanda dzina la Ambuye, asiye zosalungama.”
Kochokera mwa kholo limodzi Iye adalenga mitundu yonse ya anthu, kuti ikhale pa dziko lonse lapansi. Adakonzeratu nthaŵi ya moyo wao, ndiponso malire a pokhala pao.
Mulungu adafuna kuti anthu amufunefune, ndipo kuti pomfufuzafufuza, mwina nkumupeza. Komabe Iye sali kutali ndi aliyense mwa ife.
Chauta akumanga Yerusalemu, akusonkhanitsa Aisraele omwazika.
Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta!
Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Mzimu wa Chauta udzakhala pa Iye, mzimu wopatsa nzeru ndi kumvetsa, mzimu wopatsa uphungu ndi mphamvu, mzimu wopatsa kudziŵa zinthu ndi kuwopa Chauta.
Kwa Mulungu, amene ndiye yekha wanzeru, kukhale ulemerero mwa Yesu Khristu mpaka muyaya. Amen.
Tikadaiŵala Mulungu wathu, kapena kugwadira mulungu wachilendo,
kodi Mulungu sakadazipeza zimenezi? Paja Iye amadziŵa zinsinsi zonse zamumtima.
Kambani, fotokozani mlandu wanu. Mupatsane nzeru nonse pamodzi. Kodi ndani adaneneratu zimene zidzachitika? Ndani adaloseratu kalekale zimenezo? Kodi si Ineyo, Chautane? Ndithu, kupatula Ine palibe Mulungu wina, Mulungu wachilungamo ndi wopulumutsa. Palibenso wina aliyense kupatula Ine.”
zimene Mulungu adatipatsa mochuluka.
Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
“Kodi udaali kuti pamene ndinkaika maziko a dziko lapansi? Undiwuze ngati ndiwe womvetsa zinthu.
pamene ili khale m'mapanga mwake, kapena pamene ikubisala m'tchire?
Kodi khwangwala amampatsa chakudya chake ndani, pamene maunda ake akulirira kwa Mulungu, namadzandira chifukwa chosoŵa chakudya?”
Nanga kodi ukudziŵa amene adalemba malire ake, amene adayesapo ndi chingwe padzikopo?
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Koma Yesu adaadziŵa zimene iwo ankaganiza, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zoipa mumtima mwanu?
Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
Kodi Chauta adapemphapo nzeru kwa yani, kuti adziŵe zinthu? Ndani adamuphunzitsa kuweruza molungama? Ndani adamphunzitsa kudziŵa zinthu? Ndani adamlangiza njira ya kumvetsa zinthu?
Adandipatsanso ntchito yofotokozera anthu onse za m'mene Mulungu adzachitira zonse zimene Iye adakonzeratu mwa chinsinsi chake. Mulungu amene adalenga zonse, adasunga chinsinsichi chikhalire, nthaŵi isanayambe.
“Koma Mulungu ali ndi nzeru ndi mphamvu zopambana. Ali ndi uphungu wabwino, ndi kumvetsa zinthu zonse.
Inu Chauta ntchito zanu nzambiri, zonse mwazipanga mwanzeru, ndipo dziko lapansi ladzaza ndi zolengedwa zanu.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Apo Chauta adayankha Yobe m'kamvulumvulu kuti,
Ndidailembera malire, ndidaiikira mipiringidzo ndi zitseko zake.
Tsono ndidati, ‘Ufike mpaka apo osabzolapo, mafunde ako amphamvuwo aime pomwepo.’
“Kodi chibadwire chako udalamulapo dzuŵa kuti lituluke m'maŵa, ndi kuti mbandakucha ukhalepo pa nthaŵi yake?
Kodi iweyo udalamulapo kuti kuŵala kwa mbandakuchawo kuunikire dziko lonse lapansi, kuti kuthaŵitse anthu oipa obisala pamenepo?
Chifukwa cha kuŵala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala ngati zilembo za chidindo pa mtapo.
Kuŵala kwa dzuŵa sikuŵafika anthu oipa, choncho sangathe kugwira ntchito zao.
“Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja ndi kukafika pa magwero ake?
Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa? Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wokhawokha?
Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa? Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi.
“Kodi njira yopita kumene kumakhala kuŵala ili kuti? Nanga mdima, kwao nkuti?
“Kodi ndiwe amene ukusokoneza uphungu wanga polankhula mau opanda nzeru?
Pajatu chinthu chilichonse chobisika chidzaululuka, ndipo chilichonse chachinsinsi chidzadziŵika nkuwonekera poyera.
Ndidaneneratu zakumathero kuchokera pa chiyambi pomwe. Kuyambira kalekale ndidaloseratu zimene zidakali zosachitikabe. Ndidaanena kuti, ‘Maganizo anga sadzalephera, ndidzachitadi zonse zimene ndidafuna kuchita.’
Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Kulemekeza Chauta ndiye chiyambi cha nzeru, kudziŵa Woyera uja nkukhala womvetsa bwino zinthu.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Zinthu zimene ndidalosa zija zachitikadi. Tsono ndikuuzani zinthu zatsopano, zisanaoneke ndikukudziŵitsiranitu.”
Mauwo ndi chinsinsi chozama chimene chinali chobisika chikhalire kwa mibadwo yonse, koma tsopano Mulungu wachiwululira anthu ake.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Ndipo kuwopa Chauta ndiye chidzakhale chinthu chomkondweretsa. Sadzaweruza potsata zooneka pamaso, kapena kugamula mlandu potsata zakumva.
Pakuti anthu amene Mulungu adaŵasankhiratu, Iye adaŵapatulanso kale kuti akhale monga Mwana wake, kuti choncho Mwanayo akhale woyamba mwa abale ambiri.
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Pali zinthu zina zimene Chauta, Mulungu wathu, sanatiululire; koma watiululira ifeyo ndi zidzukulu zathu malamulo ake amene tiyenera kuwamvera nthaŵi zonse.
Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Wotsata malamulo ake amakhala ndi nzeru zenizeni. Chauta ndi wotamandika mpaka muyaya.
Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse.
Kodi ndani adayesa kuchuluka kwa madzi am'nyanja ndi chikhatho chake, kapena kuyesa kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake? Ndani adayesa dothi lonse la dziko lapansi ndi dengu? Ndani adayesa kulemera kwa mapiri ndi magomo pa sikelo?
“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungathe kudziŵa kukula kwa nzeru za Mphambe?
Malire a nzeru zake ali kutali kuposa mlengalenga. Nanga iwe ungachitepo chiyani? Malire a nzeru zake ndi ozama kupitirira dziko la anthu akufa. Nanga iwe ungathe kudziŵapo chiyani?
Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana kutalika kwa dziko lapansi, ndi kupingasa kwa nyanja zamchere.
Munthu amene amadziyesa wodziŵa kanthu, ndiye kuti sakudziŵabe kwenikweni monga momwe akadayenera kudziŵira.
Koma munthu akamakonda Mulungu, ndiye kuti amadziŵika ndi Mulungu.
Manja anu adandilenga ndi kundiwumba. Patseni nzeru zomvetsa, kuti ndiziphunzira malamulo anu.
Ine ndine Chauta, dzina langa nlimenelo. Ulemerero wanga sindidzapatsa wina aliyense. Mayamiko oyenera Ine, sindidzalola kuti mafano alandireko.
Zinthu zimene ndidalosa zija zachitikadi. Tsono ndikuuzani zinthu zatsopano, zisanaoneke ndikukudziŵitsiranitu.”
Komabe pakati pa anthu okhwima m'chikhulupiriro, timalankhula zanzeru. Koma nzeruzo si za masiku anozi, kapena za akulu olamulira dziko lino lapansi, amene mphamvu zao nzodzatha.
Nzeru zimene timalankhula, ndi nzeru za Mulungu, zachinsinsi, zobisika kwa anthu. Mulungu asanalenge dziko lapansi, adaakonzeratu zimenezi kuti atipatse ulemerero.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Ndipo Mulungu amene amayang'ana za m'kati mwa mitima ya anthu, amadziŵa zimene Mzimu Woyera afuna, pakuti Mzimuyo amapempherera anthu a Mulungu monga momwe Mulungu afunira.
Tsopano timaona zinthu ngati m'galasi, zosaoneka bwino kwenikweni. Koma pa nthaŵiyo tidzaona chamaso ndithu. Tsopano ndimangodziŵa mopereŵera, koma pa nthaŵiyo ndidzamvetsa kotheratu, monga momwe Mulungu akundidziŵira ine kotheratu.
Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo?
“Kondwera nayeni Yerusalemu, musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira.
Mudzalandira chitonthozo ndi kukondwera nacho kwambiri. Mudzagaŵana naye ulemerero wake ndi kusangalala nawo.”
Chauta akunena kuti, “Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo.
Ndidzakusangalatsani ku Yerusalemu monga momwe mai amasangalatsira mwana wake.
Mudzasangalala poona zimenezi. Zidzakulimbitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu. Tsono mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndimathandiza amene amandimvera, ndipo ndimakwiyira adani anga.”
“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto.
Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”
Chauta akunena kuti, “Amene akuti akudzipatula ndi kudziyeretsa pamene akufuna kuchita miyambo yam'minda ija, ali ndi mtsogoleri wao yemwe, nkumadya nyama yankhumba, mbeŵa ndi zonyansa zina, onsewo adzafera limodzi,” akuterotu Chauta.
“Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga.
“Ndidzaika chizindikiro pakati pao. Mwa iwowo padzakhala ena opulumukako amene ndidzaŵatuma kwa anthu a mitundu ina, monga a ku Tarisisi, a ku Puti ndi a ku Ludi, akatswiri a mauta, ndiponso ku Tubala, ku Yavani, ndi ku maiko akutali amene sadamvepo za mbiri yanga kapena kuwona ulemerero wanga. Iwowo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina.
Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Inu mwaona kupiripita kwanga, mudziŵa kuchuluka kwa misozi yanga. Kodi zonsezi sizidalembedwe m'buku lanu?
Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”
Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.”
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.
Nzeru zimenezi zimachokera kwa Chauta Wamphamvuzonse. Uphungu wake ndi wodabwitsa, nzeru zake nzopambana.
Monga unenera Uthenga Wabwino umene ndimalalika, zidzateronso pa tsiku lija limene Mulungu mwa Khristu Yesu adzaweruza zinsinsi za m'mitima mwa anthu.
“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.
Chauta amapalana chibwenzi ndi anthu omvera Iye, ndipo amaŵadziŵitsa chipangano chake.
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe.
Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Palibe nzeru, palibe kumvetsa zinthu, palibe ngakhale uphungu, zimene zingathe kupambana Chauta.
Ngakhale anawo asanabadwe, ndiye kuti tsono asanachite chilichonse chabwino kapena choipa, Mulungu adaafunabe kuti cholinga chake chosankhira munthu aliyense chipitirire. Izi adachita osati chifukwa cha ntchito za munthu koma chifukwa chakuti Mulungu adamuitana munthuyo.
ndimadzifunsa kuti, “Kodi munthu nchiyani kuti muzimkumbukira, mwana wa munthu nchiyani kuti muzimsamalira?”
Chauta Wamphamvuzonse walumbira kuti, “Monga momwe ndaganizira, zidzachitikadi choncho, ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
Koma inu okondedwa, chinthu chimodzi musaiŵale, kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka chikwi chimodzi, ndipo zaka chikwi chimodzi zili ngati tsiku limodzi.
Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.