Chauta akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi, koma ndikakhala patali ndiye kuti sindinenso Mulungu?
Kodi munthu nkubisala pobisika potani, pamene Ine sindingathe kumuwona? Kodi Ine sindili ponseponse, kumwamba ndi pa dziko lapansi pano?” Akuterotu Chauta.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Mulungu adafuna kuti anthu amufunefune, ndipo kuti pomfufuzafufuza, mwina nkumupeza. Komabe Iye sali kutali ndi aliyense mwa ife.
Paja “ ‘Mwa Iye ife timakhala ndi moyo, timayenda ndipo timakhala tilipo.’ Monga adanenera opeka ndakatulo anu ena kuti, “ ‘Ifenso ndife ofumira mwa Iye ngati ana ake.’
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.
ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.
Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.
Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Chauta ali kumwamba, amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse.
Kumene amakhala pa mpando wachifumuko, amapenya anthu onse okhala pa dziko lapansi
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Choncho dziŵani ndipo musamaiŵala kuti Chauta ndiye Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, palibe wina ai.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.”
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko, ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo.
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
Chauta akulamulira anthu a mitundu yonse, ulemerero wake ndi waukulu kuposa wa mlengalenga.
Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, amene akukhala kumwamba,
wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi.
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
“Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi!
Pali Mulungu mmodzi amene ali Atate a anthu onse. Iye ali pamwamba pa onse, amagwira ntchito kudzera mwa onse, ndipo ali mwa onse.
Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?
Khalani mwa Ine, ndipo Inenso ndidzakhala mwa inu. Nthambi siingathe kubala zipatso payokha ngati siikhala pa mtengo wake. Momwemonso inu ngati simukhala mwa Ine.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.”
Pamaso pa Mulungu palibe kanthu kobisika, zonse zili poyera ndipo nzovundukuka pamaso pa Iye amene tiyenera kumufotokozera zonse zimene tachita.
Ngakhale zinali choncho Mulungu Wopambanazonse sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja, monga akunenera mneneri kuti,
“Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?
Mtima wa munthu umalingalira zoti uchite, koma Chauta ndiye amene amaongolera mayendedwe a munthuyo.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Ndili nawe, ndidzakutchinjiriza kulikonse kumene udzapite, ndipo ndidzakubwezanso ku dziko lino. Sindidzakusiya mpaka nditachita zonse ndakuuzazi.”
“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.
Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu.
Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo?
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Kodi Mulungu angakhale nawodi anthu pa dziko lapansi? Onani kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi.
Mundimangire guwa ladothi, ndipo pamenepo muziperekapo nsembe zanu zopsereza, ndi zopereka zanu zamtendere, nkhosa ndi ng'ombe zanu. Pa malo onse amene ndikuuzani kuti muzindipembedzerapo, Ine ndidzabwera kudzakudalitsani.
Palibe munthu amene adaona Mulungu. Koma tikamakondana, Mulungu amakhala mwa ife, ndipo chikondi chake chafika pake penipeni mwa ife.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Chauta amatsogolera mayendedwe a munthu wolungama, amatchinjiriza amene njira zake zimakomera Iye.
Ngakhale agwe sadzapweteka, popeza kuti Chauta amamgwira dzanja.
Dziko lapansi lidalengedwa ndi Iye amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba, kuseri kwa mlengalenga. Amaona anthu pansi ngati ziwala. Adafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchingira, ngati hema lokhalamo anthu.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Koma Ambuye adakhala nane limodzi, adandilimbitsa mtima kuti ndilalike mau onse a Uthenga Wabwino, kuti anthu a mitundu yonse aŵamve. Motero ndidapulumuka m'kamwa mwa mkango.
Anthu sadzati, ‘Suuwu, uli pano,’ kapena, ‘Suuwo,’ pakuti ngakhale tsopano Mulungu akukhazikitsa ufumu wake pakati panu.”
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso.
Maso anga amaona makhalidwe ao onse oipa, ndi osabisika pamaso panga. Palibenso tchimo lililonse limene sindikulidziŵa.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Kodi amene adalenga makutu, sangathe kumva? Kodi amene adapanga maso, sangathe kupenya?
“Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungathe kudziŵa kukula kwa nzeru za Mphambe?
Malire a nzeru zake ali kutali kuposa mlengalenga. Nanga iwe ungachitepo chiyani? Malire a nzeru zake ndi ozama kupitirira dziko la anthu akufa. Nanga iwe ungathe kudziŵapo chiyani?
Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana kutalika kwa dziko lapansi, ndi kupingasa kwa nyanja zamchere.
Kodi sudziŵa? Kodi sudamve? Chauta ndiye Mulungu wachikhalire, Mlengi wa dziko lonse lapansi. Satopa kapena kufooka, palibe amene amadziŵa maganizo ake.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Chauta ndine, palibenso wina, kupatula ine palibe Mulungu wina. Ndidzakupatsa mphamvu ngakhale sukundidziŵa.
Ndidzachita zimenezi kuti kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe aliyense adziŵe kuti palibe wina koma Ine ndekha. Chauta ndine, palibenso wina.
Koma ndani angathe kummangira nyumba, poti ku mlengalenga ngakhale kumwambamwamba sikungathe kumkwanira Iye? Kodi ine ndinenso yani kuti ndingammangire nyumba, osati kamalo chabe koti nkumafukizapo lubani pamaso pa Mulungu?
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.
Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
“Mufunefune Chauta pamene angathe kupezeka, mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
Oipa asiye makhalidwe ao oipa, ndipo osalungama asinthe maganizo ao oipa. Abwerere kwa Chauta, kuti Iyeyo aŵachitire chifundo. Abwerere kwa Mulungu wathu, kuti Iye aŵakhululukire machimo ao mofeŵa mtima.”
Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Kodi Inu Chauta, suja mumafuna anthu onena zoona? Inu mudaŵakantha anthuwo, koma iwo sadamve kuŵaŵa. Mudaŵatswanya, koma sadafune kutembenuka mtima. Adaumitsa mitima yao ngati mwala, adakana kwamtuwagalu kulapa.”
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Paja zinthu zonse nzochokera kwa Iye, nzolengedwa ndi Iye ndipo zimalinga kwa Iye. Ulemerero ukhale wake mpaka muyaya. Amen.
Sadzalola phazi lako kuti literereke, Iye amene amakusunga sadzaodzera.
Zoonadi, amene amasunga Israele, ndithu sadzaodzera kapena kugona.
Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake. Mapiri aatali omwe ngakenso.
Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga. Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense.
Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.
Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
“Suja amagulitsa atimba asanu tindalama tiŵiri? Komabe Mulungu saiŵala ndi mmodzi yemwe.
Ndipo tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.”
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Usaope, ndili nawe. Ndidzabweza zidzukulu zako kuchokera kuvuma, ndidzakusonkhanitsani nonse kuchokera kuzambwe.
Mpweya wa munthu uli ngati nyale ya Chauta, nyaleyo imafufuza ziwalo zake zonse zam'kati.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.
Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha.
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.”
Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu.
Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.
Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.
Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Mulungu wathuyo zochita zake nzangwiro, mau a Chauta ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
“Palibe Mulungu wina koma Chauta yekha. Palibe thanthwe lina lothaŵirapo koma Mulungu wathu yekha?
Zinthu zonsezi ndidazilenga ndine, tsono zonsezi nzanga,” akutero Chauta. “Anthu amene ndimakondwera nawo ndi aŵa: odzichepetsa ndi olapa, ondiwopa ndi omvera mau anga.
Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
Mulungu adamuuza kuti, “Dzina langa ndine NDILIPO. Aisraelewo ukaŵauze kuti, NDILIPO wandituma kwa inu.”
Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake.
Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Aliyense wovomereza kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu, Mulungu amakhala mwa iye, ndipo iye amakhala mwa Mulungu.
Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa,
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
Koma Inu Chauta ine mumandidziŵa. Mumandiyang'ana, ndipo mumayesa mtima wanga, nkuwona kuti ndimakukondani. Muŵakoke anthu oipa ngati nkhosa zokaphedwa. Muŵaike padera mpaka tsiku loti akaphedwe.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Apo Chauta adati, “Tuluka, ukaime pa phiri, pamaso panga.” Tsono Chauta adadutsa pamenepo, ndipo mphepo yamphamvu idaomba ning'amba mapiri ndi kuswa matanthwe, koma Chauta sanali m'mphepomo. Itapita mphepoyo, padachita chivomezi, koma Chauta sanali m'chivomezimo.
Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m'motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii.
Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Yang'anani kumlengalenga. Kodi ndani adalenga nyenyezi mukuziwonazi? Ndiye amene amazitsogolera ngati gulu lankhondo, ndipo iliyonse amaiitana ndi dzina lake. Popeza kuti nyonga ndi mphamvu zake nzazikulu. Palibe ndi imodzi yomwe imene imasoŵapo.
Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja.
Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.
Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.”
Tsono Elisa adapemphera, adati, “Inu Chauta ndikukupemphani kuti mutsekule maso ake kuti apenye.” Motero Chauta adatsekula maso a wantchito uja, ndipo adangoona kuti phiri lili lodzaza ndi akavalo ndi magaleta amoto atamzungulira Elisa uja.
Chuma cha Mulungu nchachikulu zedi. Nzeru zake ndi kudziŵa kwake nzozama kwambiri. Ndani angamvetse maweruzidwe ake, ndipo njira zake ndani angazitulukire?
Akutero Chauta amene adalenga zakumwamba, ndi Iyeyo Mulungu amene adaumba ndi kulenga dziko lapansi, ndipo adalikhazikitsa mwamphamvu. Sadalipange kuti likhale lopanda kanthu, koma kuti likhale malo okhalamo anthu. Iyeyo akunena kuti: “Chauta ndine, palibenso wina ai.
Paja ndi Mulungu amene adaati, “Kuŵala kuunike kuchokera mu mdima.” Mulungu yemweyo ndiye adatiwunikiranso m'mitima mwathu, kuti anthu adziŵe ulemerero wa Mulungu umene ukuŵala pa nkhope ya Khristu.
Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai.
Hana adapemphera nati, “Mtima wanga ukukondwa chifukwa cha zimene Chauta wandichitira, Ndikuyenda ndi mdidi chifukwa cha Chauta. Pakamwa panga pakula nkuseka adani anga monyodola. Ndakondwa kwambiri chifukwa mwandipulumutsa.
Chauta adzatswanya adani ake, adzaŵaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba. Chauta adzaŵaweruza mpaka ku mathero a dziko lapansi. Koma adzalimbikitsa mfumu yake, adzakuza mphamvu za wodzozedwa wake.”
Tsono Elikana adabwerera kwao ku Rama. Koma mnyamata uja Samuele adatsala, ndipo ankatumikira Chauta pamaso pa wansembe Eli.
Tsono ana a Eli anali achabechabe, sankasamalako za Chauta.
Sankasamalanso za khalidwe loyenera ansembe pakati pa anthu. Ankachita motere: pamene munthu wina ankapereka nsembe, nyama ilikuŵira pa moto, mtumiki wake wa wansembe ankabwera, atatenga chiforoko cha mano atatu.
Ankachipisa mu mphika, ndipo zonse zimene chiforoko chija chinkajinya, wansembe ankatenga kuti zikhale zake. Aisraele onse amene ankafika ku Silo, ana a Eli ankaŵachita mokhamokhamo.
Kuwonjezera apo, mafuta asanatenthedwe, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi kuuza munthu wopereka nsembeyo kuti, “Patse nyama yoti ndikaotchere wansembe. Pakuti sadzalandira nyama yophika, koma yosaphika.”
Ndipo munthuyo akanena kuti, “Apserezeretu mafutaŵa poyamba, pambuyo pake ndiye mutenge monga momwe mufunira,” mtumiki uja ankati, “Iyai, patsiretu tsopano pompano. Ngati sutero, ndichita kukulanda.”
Motero tchimo la ana a Eli linali lalikulu pamaso pa Chauta, pakuti ankanyoza nsembe za Chauta.
Samuele pa unyamata wake ankatumikira pamaso pa Chauta, atavala efodi yabafuta.
Chaka chilichonse mai wake ankamsokera mkanjo, ndi kukampatsa pamene ankapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe ya chaka ndi chaka.
“Palibe woyera wina wofanafana ndi Chauta, palibe wina koma Iye yekha. Palibe thanthwe lina lotchinjiriza lofanafana ndi Mulungu wathu.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Apo mngelo wa Mulungu, yemwe ankatsogolera Aisraele aja, adakakhala cha kumbuyo kwao. Mtambo womwe unkakhala patsogolo pao uja, udakakhalanso chakumbuyo kwao.
“Uza Aisraele abwerere, amange zithando patsogolo pa Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, moyang'anana ndi Baala-Zefoni. Mumange zithando pamenepo m'mbali mwa nyanja.
Unali pakati pa gulu lankhondo la Aejipito ndi gulu lankhondo la Aisraele. Choncho panali mtambo ndi mdima, kotero kuti magulu ankhondo aŵiriwo sadayandikane usiku wonse.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Koma iwo adamuumiriza kuti, “Mukhale nafe konkuno, poti kwayamba kuda; onani dzuŵa likuloŵa.” Apo Iye adakaloŵa m'nyumba nakakhala nawo.
Adaloŵa m'mandamo koma sadaupeze mtembo wa Ambuye Yesu.
Pamene adakhala nawo podyera, Yesu adatenga buledi, ndipo atathokoza Mulungu, adamnyema naŵagaŵira.
Nthaŵi yomweyo maso ao adatsekuka, namuzindikira, Iye nkuzimirira.
Usunge bwino zokoma zimene adakusungitsa pakutsata Mzimu Woyera amene amakhala mwa ife.
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Kumeneko Chauta adzatiwonetsa ulemerero wake. Adzakhala malo a mitsinje yaikulu ndi yaing'ono. Ngalaŵa zankhafi sizidzapitapo, ndipo zombo zazikulu sizidzayendapo.
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza.
Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi.
Mulungu, Chauta, adalenga zakuthambo ndi kuziyalika. Adalenga dziko lapansi ndi zonse zimene limabereka. Adapatsa mpweya kwa anthu okhala m'dzikomo, ndi kuninkha moyo kwa onse oyendamo. Iyeyo akunena kuti,
Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti musamadera nkhaŵa moyo wanu, kuti mudzadyanji, kapena thupi lanu, kuti mudzavalanji.
Pakuti moyo umaposa chakudya, ndipo thupi limaposa zovala.
Onani makwangwala. Safesa, sakolola, alibe nyumba yosungiramo zinthu, kapena nkhokwe, komabe Mulungu amaŵadyetsa. Inu mumazipambana mbalamezo kutali.
Ndani mwa inu ndi maganizo ankhaŵa angathe kuwonjezera ngakhale tsiku limodzi pa moyo wake?
Tsono ngati simungathe kuchita ngakhale kanthu kakang'ono kotere, bwanji mukudera nkhaŵa zinazo?
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
“Zoonadi, ndinu aakulu, Inu Chauta Wamphamvuzonse. Malinga ndi zimene tidamva ndi makutu athu, palibenso wina aliyense wonga Inu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha.
Mulungu adzandiyankha ali kumwamba, ndipo adzandipulumutsa. Iye adzasokoneza amene andipondereza. Adzaonetsa chikondi chake chosasinthika, adzaonetsa kukhulupirika kwake.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta.
Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera, Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba. Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
“Ndikudziŵa ntchito zao ndi maganizo ao. Ndikubwera kudzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse ndi a zilankhulo zonse. Adzabweradi ndipo adzaona ulemerero wanga.
“Kodi udakayendapo pansi penipeni pa nyanja ndi kukafika pa magwero ake?
Kodi adakuwonetsa iwe zipata za imfa? Kodi udaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wokhawokha?
Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziŵa? Undiwuze tsono ngati umazidziŵa zonsezi.
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Mundilole ndizikhala m'Nyumba mwanu nthaŵi zonse. Mundilole ndibisale pansi pa mapiko anu kuti munditeteze.
Akadakhala nane pa bungwe langa, bwenzi atalalikadi mau anga kwa anthu anga. Bwenzi ataŵachotsa m'njira zao zoipa, kuti aleke machimo ao.”
Mulungu amene adalenga dziko lapansi ndiponso zonse zili m'menemo, ndiye Mwini Kumwamba ndi dziko lapansi. Iye sakhala m'nyumba zachipembedzo zomangidwa ndi anthu ai.
Anthu sangamtumikire ndi manja ao, ngati kuti Iye amasoŵa kanthu. Pajatu Iye ndiye amapatsa anthu onse moyo, mpweya ndi zina zonse.
Koma kwa ife, Mulungu ndi mmodzi yekha, ndiye Atate, amene adalenga zonse, ndipo moyo wathu umalinga kwa Iye. Tilinso ndi Ambuye amodzi okha, Yesu Khristu. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo ife tili ndi moyo chifukwa cha Iye.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.