Mawu a Mulungu ndi odabwitsa komanso achinsinsi kwambiri m'mbiri ya anthu. Ine ndikuganiza, kodi si chodabwitsa?
M'malemba oyera muli nkhani zambiri zomwe Mulungu amalankhula mwachindunji ndi anthu ake, akuwavumbulira chifuniro chake, akuwapatsa nzeru ndikuwatsogolera m'njira zawo. Kudzera m'mawu Ake, Mlengi amafotokoza chikondi chake chosatha, chilungamo chake, komanso chikhumbo chake chokhala pa ubwenzi ndi ine ndi iwe.
Nthaŵi zina Mulungu amalankhula kudzera mwa aneneri ndi atumiki, akufalitsa mawu ndi ziphunzitso zake. Nthaŵi zina mawu Ake amaonekera m'maloto ndi masomphenya, monga momwe zinalili ndi aneneri a m'Chipangano Chakale. Komanso, Mulungu amalankhulanso kudzera m'chikumbumtima chathu, akutilangiza ndi kunong'oneza m'mitima mwathu pamene tikufunika kuzindikira chifuniro Chake.
Koma Mulungu angalankhulenso kudzera muzomwe zimachitika tsiku ndi tsiku m'miyoyo yathu. Kudzera m'mikhalidwe ndi zochitika zomwe zimawoneka ngati zopanda pake, Mulungu angatilankhule ndikutivumbulira dongosolo lake ndi cholinga chake. Ndikofunikira kukhala tcheru ndi omvera mawu ake, chifukwa angaonekere m'njira zosayembekezereka.
Mawu a Mulungu ndi apadera komanso amphamvu. Mosiyana ndi mawu ena omwe timamva m'dziko lino, mawu a Mulungu satikana, koma amationetsa chikondi chake ndi chifundo chake chosatha. Ndi mawu omwe amatitsogolera m'njira zolungama ndi mtendere, amatilimbikitsa m'nthaŵi zovuta, ndi kutipatsa malangizo pakati pa chisokonezo.
M'Baibulo muli zitsanzo zokhudza mtima za momwe anthu anayankhira mawu a Mulungu. Kuchokera kwa Abrahamu, amene anasiya dziko lake n'kutsatira malangizo a Mulungu kuti akhale tate wa mitundu yambiri, mpaka Mose, amene anatulitsa Aisiraeli mu ukapolo ku Igupto motsogozedwa ndi Mulungu.
Mawu a Mulungu amapitirira malire a nthaŵi ndi malo, akutiitana kuti tidalira Iye ndikumvera malamulo ake. Ine ndikukhulupirira kuti tingathe kumva mawu ake ndikutsata njira zake.
Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”
Liwu la Chauta likumveka pamwamba pa nyanja. Mulungu waulemerero wachita bingu, liwu lake lamveka pa nyanja yaikulu.
Liwu la Chauta ndi lamphamvu, liwu la Chauta ndi laulamuliro.
Mitundu ya anthu ikunjenjemera kwambiri, maufumu akugwedezeka, Mulungu akalankhula mau ake, dziko lapansi likusungunuka.
Chauta amene amayenda mu mlengalenga, mlengalenga wakalekale. Imvani liwu lake, liwu lake lamphamvu zedi.
Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Ulemerero wa Chauta udatsikira pa phiri la Sinai, ndipo lidaphimbidwa ndi mtambo masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri Chauta adaitana Mose m'kati mwa mtambomo.
Chitapita chivomezi chija, padafika moto, koma Chauta sanali m'motomo. Utapita motowo, padamveka kamphepo kongoti wii.
Tsono Mose ataloŵa m'chihema chamsonkhano kukalankhula ndi Chauta, adamva mau kuchokera pa chivundikiro chokhala pamwamba pa Bokosi laumboni, pakati pa akerubi. Mulungu adalankhula naye.
Paja Malembo akuti, “Lero lino mukamva mau a Mulungu, musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira poukira Mulungu.”
mapazi ake ali chezichezi ngati mkuŵa woyeretsedwa m'ng'anjo ya moto; liwu lake ngati mkokomo wa madzi ochuluka.
Kumeneko ndidaona ulemerero wa Mulungu wa Israele ukuchokera kuvuma. Liwu lake linali ngati mkokomo wa madzi, ndipo dziko lapansi lidaŵala ndi ulemerero wakewo.
Kumwamba Chauta adagunda ngati bingu, Wopambanazonse liwu lake lidamveka m'kati mwa matalala ndi makala amoto.
Liwu la mbetete linkakulirakulira. Apo Mose adalankhula, ndipo Mulungu adamuyankha ndi mabingu.
Ndipo mau ameneŵa ifeifeyo tidaŵamva kuchokera kumwamba chifukwa tidaali naye pamodzi pa phiri loyera lija.
ndipo adati, “Chauta, Mulungu wathu, adatiwonetsa ukulu ndi ulemerero wake, ndipo tidamumva akulankhula m'moto muja. Lero taona kuti munthu angathe kukhalabe ndi moyo ndithu, ngakhale kuti Mulungu walankhula naye.
Nthaŵi imeneyo mau a Mulungu adaagwedeza dziko, koma tsopano lino walonjeza ndi mau akuti, “Kamodzi kenanso ndidzagwedeza, osati dziko lokha ai, koma ndi thambo lomwe.”
Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine. Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha, ndipo ndidzakuwonetsani chikondi chosasinthika ndi chosapeneka, chimene ndidaalonjeza Davide.
Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo.
Ndipo Atate omwewo amene adandituma, adandichitira umboni. Koma inu simudamve konse liwu lao, maonekedwe aonso simudaŵaone.
Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.”
Madzulo dzuŵa litapepa, aŵiriwo adamva mtswatswa, Chauta akuyenda m'mundamo, ndipo iwo adabisala m'katikati mwa mitengo, kuti Iye angaŵaone.
Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.
Chauta adalola kuti mumve mau ake kuchokera kumwamba, kuti pakutero akuphunzitseni. Pa dziko lapansi pano Chauta adakuwonetsani moto waukulu, ndipo mudamva akulankhula nanu kuchokera m'motomo.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Ndaima pakhomo pano, ndipo ndikugogoda. Wina akamva mau anga, nkutsekula chitseko, ndiloŵa, ndipo Ine ndi iye tidyera limodzi.
Mumvetsetse kulira kwa liwu la Mulungu, ndiye kuti kugunda kotuluka m'kamwa mwake.
Kodi nkofunikira kumdziŵitsa Mulungu kuti ndili naye ndi mau? Kodi kutero si kuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke?
“Tsopano anthu sangathe kuyang'anitsitsa kuŵala, pamene kukunyezimira kwambiri mu mlengalenga, pamene mphepo yaomba nkuchotsa mitambo yonse.
Kuŵala kwake kumaonekera chakumpoto. Mulungu amaonetsa ulemerero woopsa.
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
Nchifukwa chake anthu amamuwopa kwambiri. Iye sasamalako wina aliyense amene amadzinyenga kuti ndi wanzeru.” Chauta alankhula.
Amaponya ching'aning'ani pansi pa thambo, kuŵala kwake kumafika ku ngodya zonse za dziko lapansi.
Pambuyo pake kugunda kwa Mulungu kumamveka, amagunda ndi liwu lake lalikulu pamene mphezi zikung'anipa.
Mulungu amachita zodabwitsa ndi liwu lake. Amachita zazikulu zimene sitingathe kumvetsa.
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake!
Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja, monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja,
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Pa tsiku la Ambuye ndidaagwidwa ndi Mzimu Woyera, nkumva kumbuyo kwanga liwu lamphamvu ngati kulira kwa lipenga.
Mukapanda kundimvera, mukapanda kulemekeza dzina langa, ndidzakutembererani. Zabwino zimene mumazilandira nazonso ndidzazitemberera. Ndithu, ndazitemberera kale chifukwa simudamvere ndi mtima wonse.
Mutsate Chauta, Mulungu wanu, ndi kuwopa Iye yekha. Mutsate malamulo ake ndi kumvera mau ake. Mutumikire Iye ndi kuphathana naye.
Chauta adabwera nadzaimirira pomwepo, ndipo adaitananso monga nthaŵi zina zija kuti, “Samuele, Samuele!” Samuele adayankha kuti, “Lankhulani, poti mtumiki wanune ndilikumva.”
Adati, “Mukamandimvera Ine Chauta, Mulungu wanu, kumachita zolungama, kumasamala malamulo anga ndi kumamvera zimene ndikukulamulani, sindidzakulangani ndi nthenda zilizonse zimene ndidalanga nazo Aejipito. Ine ndine Chauta amene ndimakuchiritsani.”
Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolera, izo nkumamtsatira, chifukwa zimadziŵa mau ake.
Yesu adabwereranso kutsidya kwa mtsinje wa Yordani, kumene Yohane ankabatizira anthu poyamba paja, ndipo adakhala komweko.
Anthu ambiri adadza kwa Iye, nkumanena kuti, “Yohane sadachite chizindikiro chozizwitsa ai, koma zonse zimene ankanena za Munthuyu zinali zoonadi.”
Motero anthu ambiri adakhulupirira Yesu kumeneko.
Mlendo sizidzamtsatira ai, zidzamthaŵa, chifukwa sizidziŵa mau a alendo.”
Kenaka ndidamva mau a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani, ndani adzatipitire?” Apo ndidati “Ndilipo ineyo, tumeni.”
Pajatu Mulungu amalankhula mwa njira zosiyanasiyana, koma anthu sazindikira zimenezo.
M'maloto, m'masomphenya usiku, pamene anthu ali m'tulo tofa nato, pamene akungosinza chabe pa bedi,
Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo.
Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao.
Chenjerani tsono kuti musakane kumvera amene akulankhula nanu. Anthu amene adakana kumvera iye uja amene adaaŵachenjeza pansi pano, sadapulumuke ku chilango ai. Nanji tsono ifeyo, tidzapulumuka bwanji ngati timufulatira wotilankhula kuchokera Kumwambaku?
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
Liwu la Chauta likutulutsa malaŵi amoto.
Liwu la Chauta likugwedeza chipululu, Chauta akugwedeza chipululu cha Kadesi.
Liwu la Chauta likuzunguza miŵanga likupulula masamba a mitengo yonse m'dondo. Onse a m'nyumba mwake akufuula kuti, “Ulemererowo!”
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Ambuye Chauta anditsekula makutu, ndipo sindidaŵanyoze kapena kuŵapandukira.
Chauta ataona kuti Mose akuyandikira, adamuitana m'chitsambamo kuti, “Mose, Mose!” Mose adayankha kuti “Ŵaŵa.”
Zakumwamba zimalalika ulemerero wa Mulungu, thambo limasonyeza ntchito za manja ake.
Zonsezi nzoyenera kuzikhumbira kupambana golide, ngakhale golide wambiri wamtengowapatali, nzotsekemera kupambana uchi, ngakhale uchi wozuna kwambiri.
Malamulo anu amandiwunikira ine mtumiki wanu, poŵasunga ndimalandira mphotho yaikulu.
Nanga ndani angathe kudziŵa zolakwa zake? Inu Chauta, mundichotsere zolakwa zanga zobisika.
Musalole kuti ine mtumiki wanu ndizichimwa dala, kulakwa koteroku ndisakutsate. Tsono ndidzakhala wangwiro wopanda mlandu wa uchimo waukulu.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Usana umasimbira zimenezo usana unzake, usiku umadziŵitsa zimenezo usiku unzake.
Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse.
Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.
Atate, onetsani ulemerero wa dzina lanu.” Pamenepo kudamveka mau ochokera kumwamba akuti, “Ndauwonetsa ulemererowo ndipo ndidzauwonetsanso.”
Panali khamu la anthu pamenepo. Tsono pamene adamva mauwo, adati, “Kwagunda bingu.” Koma ena adati, “Mngelo walankhula naye.”
Tsono Maria adatenga mafuta onunkhira zedi a narido weniweni, amtengowapatali, okwanira theka la lita, nayamba kudzoza mapazi a Yesu, nkumaŵapukuta ndi tsitsi lake. M'nyumba monsemo mumvekere guu ndi fungo la mafutawo.
Yesu adaŵauza kuti, “Mauŵa amveka osati chifukwa cha Ine ai, koma chifukwa cha inu.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati, “Aleluya! Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira.
Tamandani Chauta, inu angelo ake, inu amphamvu amene mumamva mau ake, amene mumachita zimene amalamula.
Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu.
Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini.
Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere.
Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera.
Nzeru ikufuula mu mseu, ikulankhula mokweza mau m'misika.
Ikufuula pa mphambano za miseu, ikulankhula pa zipata za mzinda, kuti,
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Ndipo Chauta adalamula Mose kuti, “Kauze Aisraele kuti, ‘Mwapenyatu kuti Ine Mulungu ndalankhula nanu ndili kumwamba.
Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula, akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi, kuyambira kotulukira dzuŵa mpaka koloŵera kwake.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.
Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
Chauta akunena kuti, “Fuula kwambiri, usaleke, mau ako amveke ngati lipenga. Uŵauze anthu anga za kulakwa kwao, uŵauze a m'fuko la Yakobe za machimo ao.
Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.
Liwu la Chauta limathyola mikungudza, Chauta amathyolathyoladi mikungudza ya ku Lebanoni.
Amagwedeza phiri la Lebanoni kuti lizivinavina ngati likonyani, amavinitsa phiri la Sirioni ngati mwanawanjati.
Pilato adati, “Tsono ndiye kuti ndiwedi mfumu, ati?” Yesu adati, “Mwanena nokha kuti ndine mfumu. Ine ndidabwera pansi pano ndipo ndidabadwa kuti ndidzachitire umboni choona. Aliyense wokonda choona amamva mau anga.”
Koma chimene ndidaalamula nchimodzi, ndidati, ‘Mukamandimvera, ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata malamulo anga onse kuti zinthu zikukomereni!’
Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo.
Kale lija pa nthaŵi zosiyanasiyana, mwa njira zosiyanasiyana, Mulungu adaalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri.
Adatinso, “Inu Ambuye, ndinu amene mudalenga dziko lapansi pachiyambi pomwe, zakumwambaku ndi ntchito ya manja anu.
Zimenezi zidzatha, koma Inu ndinu achikhalire. Zonsezi zidzafwifwa ngati chovala.
Mudzazipindapinda ngati mwinjiro, ndipo zidzasinthika ngati chovala, koma Inu ndinu osasinthika, zaka zanu sizidzatha konse.”
Nkale lonse Mulungu sadauzepo mngelo aliyense kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.”
Nanga angelo, kodi suja iwo ndi mizimu yotumikira chabe, imene Mulungu amaituma chifukwa cha anthu odzalandira chipulumutso?
Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake.
Mose adapita kukauza anthu mau ndi malangizo onse amene Chauta adamuuza. Ndipo anthu onse adayankha kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.”
Mose adaitana Aisraele onse naŵauza kuti: Inu Aisraele, mverani malamulo ndi malangizo onse amene ndikukupatsani lero. Muŵaphunzire, ndipo musamaledi kuti muzimvera.
Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu.
Akulankhula choncho, kudadza mtambo woŵala nuŵaphimba. Mumtambomo mudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimamkonda, ndipo ndimakondwera naye kwambiri. Muzimumvera.”
Bwerani, timpembedze ndi kumlambira. Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu.
Pakuti ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pa busa lake, ndife nkhosa zodyera m'manja mwake. Lero mukadamverako mau ake!
Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.
“Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe?
Ndili nazo nkhosa zina zimene sizili za m'khola lino. Zimenezonso ndiyenera kuzikusa. Zidzamva mau anga, ndipo padzakhala gulu limodzi mbusa wakenso mmodzi.
Iye adzakutumizirani mneneri wonga ine wochokera mwa inu amene, ndipo mudzayenera kumumvera iyeyo.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
Kodi suja nzeru imaitana? Suja nzeru zomvetsera zinthu zimakweza mau ake?
Landirani malangizo anga m'malo mwa siliva, funitsitsani kudziŵa zinthu, osati kuthamangira golide wabwino kwambiri.
Nzerutu ndi yabwino kuposa miyala yamtengowapatali. Zonse zimene ungazilakelake sizingafanefane ndi nzeru.
Ine nzeru ndimakhalira limodzi ndi kuchenjera. Ndimadziŵa zinthu ndipo ndimaganiza moyenera.
Kuwopa Chauta nkudana ndi zoipa. Kunyada, kudzitama, kuchita zoipa ndi kulankhula zonyenga, zonsezo ndimadana nazo.
Ndili ndi uphungu ndi maganizo abwino. Ndimamvetsa bwino zinthu, ndilinso ndi mphamvu.
Ndimathandiza mafumu polamulira ndine, olamulira ndimaŵathandiza ndine kulamula zolungama.
Ndine ndimathandiza akalonga polamula, ndine ndimathandiza akuluakulu poweruza m'dziko.
Anthu ondikonda, ine nzeru ndimaŵakonda, anthu ondifunafuna mosamala, amandipeza.
Ndili nacho chuma, ndili nawo ulemu, chuma chosatha ndiponso kukhuphuka konkirankira.
Zimene mumalandira kwa ine nzokoma kuposa golide, ngakhale golide wosalala. Phindu lochokera mwa ine nloposa siliva wabwino zedi.
Nzeru imakhala pa zitunda m'mbali mwa njira, imakaima pa mphambano za miseu.
Ndimachita zomwe zili zoyenera, sindipatuka kuchoka m'njira za chilungamo.
Ndimaŵapatsa chuma anthu ondikonda, ndi kudzaza nyumba zao zosungiramo chuma.
“Chauta adandilenga ine nzeru pa chiyambi cha ntchito zake. Mwa ntchito zake zakalekale woyambirira ndinali ine.
Ndidapangidwa masiku akalekale, pachiyambiyambi, dziko lapansi lisanalengedwe.
Nyanja zozama zisanalengedwe, padakalibe akasupe odzaza ndi madzi, nkuti ine nditabadwa kale.
Mapiri asanaumbidwe, magomo asanakhalepo, Mulungu anali atandilenga ineyo;
lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake, lisanakhaleponso dothi loyamba la dziko lapansi.
Ine ndinalipo kale, pamene ankakhazikitsa zakumwamba, pamene ankalemba mzere wa malire a nyanja yozama,
pamene ankaika thambo m'malo mwake, pamene ankatsekula akasupe a m'nyanja yozama,
pamene ankaika malire a nyanja kuti madzi ake asabzole malirewo, pamene ankaika maziko a dziko lapansi.
Imafuula pafupi ndi zipata kumaso kwa mzinda, ndiponso pamakomo poloŵera, imati,
Nthaŵiyo nkuti ndili pambalipa ngati mmisiri wake, ndikumkondweretsa tsiku ndi tsiku, ndikusangalala pamaso pake nthaŵi zonse.
Ndinkasangalala m'dziko lake lokhalamo anthu, ndi kumakondwa nawo ana a anthu.
“Ndipo tsopano, ana anga, tamverani, ngodala anthu amene amasunga malangizo anga.
Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga.
Ngwodala munthu amene amatchera khutu kwa ine, amene amakhala pakhomo panga tsiku ndi tsiku, amene amadikira pa chitseko changa.
Paja wondipeza ine, wapeza moyo, ndipo amapeza kuyanja pamaso pa Chauta.
Koma wosandipeza ine, akudzipweteka ameneyo. Onse odana ndi ine, ngokonda imfa amenewo.”
“Inu anthu, ndikukuitanani, kuitanaku ndikuitana anthu nonsenu.
Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Iwo adzaperekedwa kuti akaphedwe ku nkhondo, motero adzasanduka chakudya cha nkhandwe.
Koma mfumu idzakondwera mwa Mulungu. Onse olumbirira Iye, adzamtamanda, koma pakamwa pa anthu abodza padzatsekedwa.
Ndikukhumbira kukuwonani m'malo anu oyera ndi kuwona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.
Ndalumbira dzina langa lomwe, pakamwa panga palankhula moona mau amene sadzasinthika konse, akuti, ‘Bondo lililonse lidzandigwadira, anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
Ine ndidaŵaonekera ndili chakutali. Inu Aisraele ndakukondani kwambiri ndi chikondi chopanda malire, ndakhala wokhulupirika kwa inu mpaka tsopano.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.
Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena.
Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako.
Nchifukwa chake tsono, monga Mzimu Woyera akunenera, “Lero lino mukamva mau a Mulungu,
musaumitse mitima yanu monga muja zidaachitikira pomuukira Mulungu, tsiku la kumuyesa m'chipululu muja.
Sadzafuula kapena kukweza mau, mau ake sadzamveka mu mseu.
Iwe waona zambiri, koma zonsezo sudazisamale. Makutu ako ndi otsekuka, koma suumva.”
Chifukwa cha chilungamo chake, Chauta adafunitsitsa kuti malamulo ake akhale opambana ndi aulemu.
Koma tsono anthu ameneŵa aŵalanda ndi kuŵafunkhira zinthu zao. Onseŵa adaŵakola m'mbuna, ndi kuŵabisa m'ndende. Adaŵafunkhira, popanda wina woŵapulumutsa, adaŵabera, popanda wina wonena kuti, “Bwezani!”
Kodi alipo wina mwa inu amene adzamvetsere zimenezi? Ndani adzatchere khutu ndi kuzisamala kutsogolo kuno?
Ndani adapereka Yakobe kwa ofunkha? Ndani adapereka Israele kwa anthu akuba? Kodi akuchita zimenezi si Chauta? Paja tidamchimwira, sitidatsate njira zake, ndipo sitidamvere malamulo ake.
Motero adatikwiyira kwambiri, nativutitsa ndi nkhondo. Adayatsa moto ponseponse potizungulira, ife osamvetsa. Moto udatipsereza, koma ife osapezapo phunziro ai.
Bango lopindika sadzalithyola, moto wozilala sadzauzima. Adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.
“Bwanji mumangoti, ‘Ambuye, Ambuye,’ koma chonsecho simuchita zimene ndimanena?
Munthu aliyense wodza kwa ine, namva mau anga nkumaŵagwiritsa ntchito, ndikuuzani amene amafanafana naye.
Paja aneneri adalemba kuti, ‘Onse adzakhala ophunzitsidwa ndi Mulungu.’ Munthu aliyense womva Atate, nkuphunzira kwa Iwo, amadza kwa Ine.
Uzisamala mayendedwe ako ukamapita ku Nyumba ya Mulungu. Kuli bwino kupita kumeneko kukaphunzirako, kupambana kukangopereka nsembe chabe ngati anthu opusa, amene sadziŵa kuti akuchita zoipa.
Anthu okonda ndalama sakhutitsidwa nazo ndalamazo. Chimodzimodzinso anthu okonda chuma, sakhutitsidwa nalo phindu. Zimenezinso nzachabechabe.
Chuma chikachuluka, odya nawo chumacho amachulukanso. Nanga mwini wake amapindulapo chiyani? Si kumangoziyang'ana basi?
Wantchito amagona tulo tabwino, ngakhale adye pang'ono kapena kudya kwambiri. Koma wolemera, chuma sichimgonetsa tulo.
Pansi pano pali choipa china chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndachiwona: Chuma chopweteka mwiniwake yemwe.
Ndiye chuma chimenecho chikamwazika moipa, munthuyo nkukhala ndi ana, amachita kusoŵa choŵapatsa ana akewo.
Monga momwe munthu adabadwira m'mimba mwa mai wake opanda kanthu, chonchonso adzapita maliseche. Pa zonse zimene adakhetsera thukuta, palibe nchimodzi chomwe chimene adzatenge m'manja mwake.
Chimenechinso nchoipa chomvetsa chisoni kwambiri: kuti munthu adzapita monga momwe adabwerera. Nanga phindu lake nchiyani, popeza kuti iyeyo adagwira pachabe ntchito yolemetsa?
Masiku ake onse moyo wake unali wodzaza ndi mdima ndi chisoni, unali moyo wa mavuto, matenda ndi nkhaŵa.
Tsono chimene ndimachiwona kuti nchabwino ndi choyenera ndi ichi: kumadya, kumamwa, ndi kumakondwerera ntchito zonse zolemetsa zimene munthu umagwira pansi pano, pa masiku oŵerengeka a moyo wako amene Mulungu wakupatsa. Nchokhachi chimene ungati nchako, choyenera kulandira.
Mwina Mulungu amamlemeretsa munthu pakumpatsa chuma ndi zabwino zina, namlola kuti akondwerere zonsezo. Munthuyo azilandire zimenezo ndi kumakondwerera ntchito zake zonse zolemetsa. Imeneyi ndi mphatso yochokeradi kwa Mulungu.
Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.
Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Utchere khutu lako, umve mau a anthu anzeru, uike mtima wako pa zophunzitsa zanga, kuti uzidziŵe.