Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


160 Mau a Mulungu Pa Makhalidwe Ake

160 Mau a Mulungu Pa Makhalidwe Ake

Mulungu, mwa ukulu wake wosatha, ali ndi makhalidwe amene sitingathe kuwamvetsa mokwanira. Mphamvu zake zonse zimatiphunzitsa kuti Iye ali ndi mphamvu zopanga ndi kulamulira zonse zimene zilipo m’chilengedwe chonse.

Nzeru zake ndi zopanda malire, chidziwitso chake chikufikira mbali zonse za nthawi ndi malo. Komanso, Mulungu amapitirira nthawi ndi imfa, umuyaya wake umatiwonetsa kuti kukhalapo kwake kulibe chiyambi kapena chimaliziro.

Ubwino wa Mulungu ukuwonekera m’chikondi chake chosatha kwa chilengedwe chonse. Iye ndiye gwero la moyo ndipo amatipatsa chisomo ndi chifundo chake chopanda malire, amatilimbikitsa m’nthawi zachisoni ndi kutitsogolera m’nthawi zosankha.

Chilungamo chake n’changwiro, nthawi zonse chokhazikika ndi cholungama. Mulungu ndi woweruza wosakondera amene amadziwa chilichonse chimene timachita ndipo amaweruza mwachilungamo.

Mtendere umene Mulungu amapereka umapitirira kumvetsa kwathu. Kukhalapo kwake sikuti kungotidzaza ndi mtendere, komanso kumatilimbikitsa kukhala mwamtendere ndi ife eni komanso ndi ena.

Kukhulupirika kwa Mulungu n’kosagwedezeka, ngakhale tili ndi zofooka ndi zolakwa zathu, Iye nthawi zonse ali wokonzeka kutikhululukira ndi kutipatsa mwayi wina. Chikondi chake n’chosatha ndipo sichitisiya, ngakhale m’nthawi zovuta kwambiri. Mulungu nthawi zonse amapezeka, wokonzeka kutipatsa chitsogozo ndi chitetezo chake.

Makhalidwe a Mulungu ndi chikumbutso cha ukulu ndi ubwino wake. Mphamvu zake zonse, nzeru, umuyaya, chiyero, chilungamo, mtendere ndi kukhulupirika ndi umboni wa chikondi chake chosatha kwa ife. Kuzindikira ndi kuganizira za makhalidwe amenewa kumatithandiza kumvetsa kuti Mulungu ndiye zonse zimene tikufunikira ndipo nthawi zonse tiyenera kumupatsa ulemerero wonse woyenera dzina lake ndi ukulu wake.




1 Yohane 4:16

Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:6-7

Ndipo Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula; wakulanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha mphulupulu ya atate ao, kufikira mbadwo wachitatu ndi wachinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 23:19

Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:34

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:5

Pakuti Yehova ndiye wabwino; chifundo chake chimanka muyaya; ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 1:1

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:3

Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Khristu amene munamtuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 37:23

Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamsanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 7:9

Chifukwa chake dziwani kuti Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu; ndiye Mulungu wokhulupirika, wakusunga chipangano ndi chifundo ndi iwo akumkonda ndi kusunga malamulo ake, kufikira mibadwo zikwi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 32:17

Ha! Yehova Mulungu, taonani, Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi mphamvu yanu yaikulu ndi mkono wanu wotambasuka; palibe chokanika Inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:8

Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:28

Kodi iwe sunadziwe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:15

limene adzalionetsa m'nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:1

Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:15

Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:48

Chifukwa chake inu mukhale angwiro, monga Atate wanu wa Kumwamba ali wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 1:37

Chifukwa palibe mau amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:68

Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino; mundiphunzitse malemba anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:5

Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri; nzeru yake njosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 90:2

Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:17

Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:142

Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha; ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:10

Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:13

Ndipo palibe cholembedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:17

Yehova ali wolungama m'njira zake zonse, ndi wachifundo m'ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 17:1

Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:4

Kapena upeputsa kodi kulemera kwa ubwino wake, ndi chilekerero ndi chipiriro chake, wosadziwa kuti ubwino wa Mulungu ukubwezera kuti ulape?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:5-6

Yehova ngwa chifundo ndi wolungama; ndi Mulungu wathu ngwa nsoni. Yehova asunga opusa; ndidafooka ine, koma anandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 32:4

Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:21

Muli zolingalira zambiri m'mtima mwa munthu; koma uphungu wa Yehova ndiwo udzaimika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 11:33

Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziwa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:16

popeza kwalembedwa, Muzikhala oyera mtima, pakuti Ine ndine woyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8-9

Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu. Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:23-26

pakuti onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu; ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Khristu Yesu; amene Mulungu anamuika poyera akhale chotetezera mwa chikhulupiriro cha m'mwazi wake, kuti aonetse chilungamo chake, popeza Mulungu m'kulekerera kwake analekerera machimo ochitidwa kale lomwe; kuti aonetse chilungamo chake m'nyengo yatsopano; kuti Iye akhale wolungama, ndi wakumuyesa wolungama iye amene akhulupirira Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:1-4

Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali. Popeza anena za Inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe. Kodi sindidana nao iwo akudana ndi Inu, Yehova? Ndipo kodi sindimva nao chisoni iwo akuukira Inu? Ndidana nao ndi udani weniweni, ndiwayesa adani. Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha. Muyesa popita ine ndi pogona ine, ndi njira zanga zonse muzolowerana nazo. Pakuti asanafike mau pa lilime langa, taonani, Yehova, muwadziwa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:18

kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:2

Ndidzagwadira kuloza ku Kachisi wanu woyera, ndi kuyamika dzina lanu, chifukwa cha chifundo chanu ndi choonadi chanu; popeza munakuzitsa mau anu koposa dzina lanu lonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:5-6

Yehova, m'mwamba muli chifundo chanu; choonadi chanu chifikira kuthambo. Chilungamo chanu chikunga mapiri a Mulungu; maweruzo anu akunga chozama chachikulu, Yehova, musunga munthu ndi nyama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:8

Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino; wodala munthuyo wakukhulupirira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:17

Ndipo Iye ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:11

Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:15

Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:1

Indedi Mulungu achitira Israele zabwino, iwo a mtima wa mbee.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umlemekeze m'njira zako zonse, ndipo Iye adzaongola mayendedwe ako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:1-2

Moyo wanga ukhalira chete Mulungu yekha; chipulumutso changa chifuma kwa Iye. Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu. Mulungu ananena kamodzi, ndinachimva kawiri, kuti mphamvu ndi yake ya Mulungu. Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa; msanje wanga, sindidzagwedezeka kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:5

Ndipo uwu ndi uthenga tidaumva kwa Iye, ndipo tiulalikira kwa inu, kuti Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwa Iye monse mulibe mdima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 30:5

Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha; koma kuyanja kwake moyo wonse. Kulira kuchezera, koma mamawa kuli kufuula kokondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

ndi kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulani inu; ndipo onani, Ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:2

Ndidzati kwa Yehova, Pothawirapo panga ndi linga langa; Mulungu wanga, amene ndimkhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:136

Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi, popeza sasamalira chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:28

Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye pothawirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m'masautso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:20

Pakuti monga mawerengedwe a malonjezano a Mulungu ali mwa Iye eya; chifukwa chakenso ali mwa Iye Amen, kwa ulemerero wa Mulungu mwa ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:130

Potsegulira mau anu paunikira; kuzindikiritsa opusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Dzina la Yehova ndilo nsanja yolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:76

Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani, monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:5

Koma Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango chotitengera ife mtendere chinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:26

Yang'anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m'nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa. Nanga inu mulibe kusiyana nazo kuziposa kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:13

Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:3-4

Tsiku lakuopa ine, ndidzakhulupirira Inu. Mwa Mulungu ndidzalemekeza mau ake, ndakhulupirira Mulungu, sindidzaopa; anthu adzandichitanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18-19

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi. Adzachita chokhumba iwo akumuopa; nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:2

Yesu, ameneyo, chifukwa cha chimwemwe choikidwacho pamaso pake, anapirira mtanda, nanyoza manyazi, nakhala padzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14

Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi. Mzinda wokhazikika pamwamba paphiri sungathe kubisika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:5

Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwitsa zanu mudazichita nzambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzitchula, zindichulukira kuziwerenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 58:11

ndipo Yehova adzakutsogolera posalekai, ndi kukhutitsa moyo wako m'chilala, ndi kulimbitsa mafupa ako; ndipo udzafanana ndi munda wothirira madzi, ndi kasupe wamadzi amene madzi ake saphwa konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:6

pokhulupirira pamenepo, kuti Iye amene anayamba mwa inu ntchito yabwino, adzaitsiriza kufikira tsiku la Yesu Khristu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Wakuopa Yehova akhulupirira kolimba; ndipo ana ake adzakhala ndi pothawirapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa; ndiyembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:31

koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Achiritsa osweka mtima, namanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:4-5

munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye? Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu, munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:4-5

koma Mulungu, wolemera chifundo, chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatikonda nacho, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumutsidwa ndi chisomo),

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:19

Ha! Kukoma kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu, kumene munachitira iwo akukhulupirira Inu, pamaso pa ana a anthu!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:9

Mulungu ali wokhulupirika amene munaitanidwa mwa Iye, ku chiyanjano cha Mwana wake Yesu Khristu, Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:8

Koma Mulungu atsimikiza kwa ife chikondi chake cha mwini yekha m'menemo, kuti pokhala ife chikhalire ochimwa, Khristu adatifera ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:12

Yehova, mudzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira ntchito zathu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:1-4

Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake. Ndizo zifunika koposa golide, inde, golide wambiri woyengetsa; zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake. Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo, m'kuzisunga izo muli mphotho yaikulu. Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika. Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu. Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga. Usana ndi usana uchulukitsa mau, ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru. Palibe chilankhulidwe, palibe mau; liu lao silimveka. Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi, ndipo mau ao ku malekezero a m'dziko muli anthu. Iye anaika hema la dzuwa m'menemo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:74

Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera; popeza ndayembekezera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:23

Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Udzikondweretsenso mwa Yehova; ndipo Iye adzakupatsa zokhumba mtima wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:3-4

Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake. Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko, ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo: Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:1

Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chitonthozo changa m'kuzunzika kwanga ndi ichi; pakuti mau anu anandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:1-2

Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino; pakuti chifundo chake nchosatha. Amitundu onse adandizinga, zedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga, inde, adandizinga: Indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Adandizinga ngati njuchi; anazima ngati moto waminga; indedi, m'dzina la Yehova ndidzawaduladula. Kundikankha anandikankha ndikadagwa; koma Yehova anandithandiza. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndipo anakhala chipulumutso changa. M'mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso: Dzanja lamanja la Yehova likwezeka, Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu. Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo, ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova. Kulanga anandilangadi Yehova: koma sanandipereke kuimfa ai. Nditsegulireni zipata za chilungamo; ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova. Anene tsono Israele, kuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:14

Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:30

komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1-2

Chifukwa chake ngati munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, funani zakumwamba, kumene kuli Khristu wokhala padzanja lamanja la Mulungu. ndipo munavala watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye; pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Msukuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse. Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu. Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika. Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu. Ndipo chilichonse mukachichita m'mau kapena muntchito, chitani zonse m'dzina la Ambuye Yesu, ndi kuyamika Mulungu Atate mwa Iye. Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye. Amuna inu, kondani akazi anu, ndipo musawawire mtima iwo. Lingalirani zakumwamba osati za padziko ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:92

Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa, ndikadatayika m'kuzunzika kwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:7

ndi kutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:1-2

Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kufuula kwanga. Chilungamo chanu sindinachibise m'kati mwamtima mwanga; chikhulupiriko chanu ndi chipulumutso chanu ndinachinena; chifundo chanu ndi choonadi chanu sindinachibisire msonkhano waukulu. Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire. Pakuti zoipa zosawerengeka zandizinga, zochimwa zanga zandipeza kotero kuti sindikhoza kupenya; ziposa tsitsi la mutu wanga, ndipo wandichokera mtima. Ndikupemphani, Yehova, ndilanditseni; fulumirani kudzandithandiza, Yehova. Achite manyazi nadodome iwo akulondola moyo wanga kuti auononge. Abwerere m'mbuyo, nachite manyazi iwo okondwera kundichitira choipa. Apululuke, mobwezera manyazi ao amene anena nane, Hede, hede. Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; iwo akukonda chipulumutso chanu asaleke kunena, Abuke Yehova. Ndipo ine ndine wozunzika ndi waumphawi; koma Ambuye andikumbukira ine. Inu ndinu mthandizi wanga, ndi Mpulumutsi wanga, musamachedwa, Mulungu wanga. Ndipo anandikweza kunditulutsa m'dzenje la chitayiko, ndi m'thope la pachithaphwi; nandipondetsa pathanthwe, nakhazika mayendedwe anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:9

Yehova achitira chokoma onse; ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20

Ndipo kwa Iye amene angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 53:6

Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Ndipo musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:28-30

Idzani kuno kwa Ine nonsenu akulema ndi kuthodwa, ndipo Ine ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. nati kwa Iye, Inu ndinu wakudza kodi, kapena tiyembekezere wina? Pakuti goli langa lili lofewa, ndi katundu wanga ali wopepuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 111:4

Anachita chokumbukitsa zodabwitsa zake; Yehova ndiye wachisomo ndi nsoni zokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:4

Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:8-9

Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:15-16

Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m'mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:17

Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:24

Pomwepo Yesu anati kwa ophunzira ake, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikane yekha, natenge mtanda wake, nanditsate Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:12-13

Pakuti kulibe kusiyana Myuda ndi Mgriki; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye; pakuti, aliyense amene adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:20

Ndipo tidziwa kuti Mwana wa Mulungu wafika, natipatsa ife chidziwitso, kuti tizindikire Woonayo, ndipo tili mwa Woonayo, mwa Mwana wake Yesu Khristu. Iye ndiye Mulungu woona ndi moyo wosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndili ndi moyo; wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndili nao tsopano m'thupi, ndili nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 106:1

Aleluya. Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino: Pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:10

Pakuti Inu ndinu wamkulu, ndi wakuchita zodabwitsa; Inu ndinu Mulungu, nokhanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:5-6

Yehova ndiye wakukusunga; Yehova ndiye mthunzi wako wa kudzanja lako lamanja. Dzuwa silidzawamba usana, mwezi sudzakupanda usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:3-4

Chifundo ndi choonadi zisakusiye; uzimange pakhosi pako; uzilembe pamtima pako; Usakangane ndi munthu chabe, ngati sanakuchitire choipa. Usachitire nsanje munthu wachiwawa; usasankhe njira yake iliyonse. Pakuti wamphulupulu anyansa Yehova; koma chinsinsi chake chili ndi oongoka. Yehova atemberera za m'nyumba ya woipa; koma adalitsa mokhalamo olungama. Anyozadi akunyoza, koma apatsa akufatsa chisomo. Anzeru adzalandira ulemu cholowa chao; koma opusa adzakweza manyazi. motero udzapeza chisomo ndi nzeru yabwino, pamaso pa Mulungu ndi anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:34

Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a kudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, lowani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:11

Iye adzadyetsa zoweta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa anaankhosa m'manja mwake, nadzawatengera pa chifuwa chake, ndipo adzatsogolera bwinobwino zimene ziyamwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:1-2

Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. kungakhale komweko dzanja lanu lidzanditsogolera, nilidzandigwira dzanja lanu lamanja. Ndipo ndikati, Koma mdima undiphimbe, ndi kuunika kondizinga kukhale usiku. Ungakhale mdima sudetsa pamaso panu, koma usiku uwala ngati usana; mdima ukunga kuunika. Pakuti Inu munalenga impso zanga; munandiumba ndisanabadwe ine. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu. Thupi langa silinabisikire Inu popangidwa ine mobisika, poombedwa ine monga m'munsi mwake mwa dziko lapansi. Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m'buku mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo. Potero, Mulungu, ndiziyesa zolingalira zanu za mtengo wake ndithu! Mawerengedwe ake ndi ambirimbiri! Ndikaziwerenga zichuluka koposa mchenga: Ndikauka ndikhalanso nanu. Indedi, mudzaomba woipa, Mulungu: Ndipo amuna inu okhumba mwazi, chokani kwa ine. Inu mudziwa kukhala kwanga ndi kuuka kwanga, muzindikira lingaliro langa muli kutali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:19

chimene tili nacho ngati nangula wa moyo, chokhazikika ndi cholimbanso, ndi chakulowa m'katikati mwa chophimba;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 136:26

Yamikani Mulungu wa Kumwamba, pakuti chifundo chake nchosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:32

Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 8:3-4

Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:6

Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:8

Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo; osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:18

Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:5

Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:29

Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa Ine; chifukwa ndili wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Ngati tivomereza machimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndi kutisambitsa kutichotsera chosalungama chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 113:7-8

Amene autsa wosauka kumchotsa kufumbi, nakweza waumphawi kumchotsa kudzala. Kuti amkhalitse pamodzi ndi akulu, pamodzi ndi akulu a anthu ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 14:17

Pakuti ufumu wa Mulungu sukhala chakudya ndi chakumwa, koma chilungamo, ndi mtendere, ndi chimwemwe mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:7

Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:7

Ha! Chifundo chanu, Mulungu, nchokondedwadi! Ndipo ana a anthu athawira kumthunzi wa mapiko anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:15-16

limene adzalionetsa m'nyengo za Iye yekha, amene ali Mwini Mphamvu wodala ndi wayekha, ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye; amene Iye yekha ali nao moyo wosatha, wakukhala m'kuunika kosakhozeka kufikako; amene munthu sanamuone, kapena sangathe kumuona; kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu yosatha. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:11

Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:27

kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 63:3-4

Pakuti chifundo chanu chiposa moyo makomedwe ake; milomo yanga idzakulemekezani. Potero ndidzakuyamikani m'moyo mwanga; ndidzakweza manja anga m'dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:11

Inu Yehova, simudzandikaniza nsoni zanu, chifundo chanu ndi choonadi chanu zindisunge chisungire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22

Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:7

Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 9:6

Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:8-9

Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse; popeza ali padzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. Chifukwa chake wasekera mtima wanga, nukondwera ulemu wanga; mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:88

Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu; ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:31

Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:18

Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye, onse akuitanira kwa Iye m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 61:3

ndikakonzere iwo amene alira maliro mu Ziyoni, ndi kuwapatsa chovala kokometsa m'malo mwa phulusa, mafuta akukondwa m'malo mwa maliro, chovala cha matamando m'malo mwa mzimu wopsinjika; kuti iwo atchedwe mitengo ya chilungamo yakuioka Yehova, kuti Iye alemekezedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:14

Yembekeza Yehova, limbika, ndipo Iye adzalimbitsa mtima wako; inde, yembekeza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:143

Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera; koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:11

akalankhula wina, alankhule ngati manenedwe a Mulungu; wina akatumikira, achite ngati mu mphamvu imene Mulungu ampatsa, kuti m'zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu, amene ali nao ulemerero ndi mphamvu kunthawi za nthawi. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, m'chifundo chanu chosatha, ndikukuthokozani chifukwa cha makhalidwe anu osaneneka. Zikomo chifukwa cha chikondi chanu chopanda malire, chomwe chimandilimbikitsa ndi kunditsogolera pa moyo wanga wonse. Zikomo chifukwa cha nzeru zanu zazikulu zomwe zimabweretsa kuwala m'moyo mwanga ndi kundionetsa njira yoyenera kutsata. Ndikukuthokozani chifukwa cha kuleza mtima kwanu kokongola, chifukwa chosandisiya, ngakhale ndikalakwitsa mobwerezabwereza. Zikomo chifukwa cha mphamvu zanu zodabwitsa, zomwe zimatipatsa ife mphamvu zopambana mavuto aliwonse omwe tikukumana nawo. Ndikukuthokozani chifukwa cha kukhalapo kwanu kosalekeza m'miyoyo yathu, nthawi zonse wokonzeka kutikumvera ndi kutithandiza nthawi zathu zovuta. Ndinu Mulungu wokhulupirika ndi wowolola mtima, ndipo chifukwa cha ichi ndikukuthokozani chifukwa chakuti mwakhala wabwino kwambiri kwa ine, popanda inu, ife si kanthu, koma ndi inu, tingathe kuchita zonse. Dzina lanu lilemekezeke ndi kutamandidwa kosatha. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa