Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 7:11 - Buku Lopatulika

11 Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Chomwecho, ngati inu, muli oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kopambana kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa zinthu zabwino kwa iwo akumpempha Iye?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono ngati inu, nkuipa kwanuku, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanji Atate anu amene ali Kumwamba, angalephere bwanji kupereka zinthu zabwino kwa amene aŵapempha?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Tsono ngati inu woyipitsitsa mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, nanga Atate anu akumwamba sadzapereka mphatso zabwino kwa iwo amene amupempha?

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 7:11
35 Mawu Ofanana  

Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Ndipo ichinso chinali pamaso panu chinthu chaching'ono, Yehova Mulungu; koma munanenanso za banja la mnyamata wanu kufikira nthawi yaikulu ilinkudza; ndipo mwatero monga mwa machitidwe a anthu, Yehova Mulungu!


Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Inde Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.


Koma Inu, Ambuye, ndinu Mulungu wansoni ndi wachisomo, wopatsa mtima msanga, ndi wochulukira chifundo ndi choonadi.


Pakuti Inu, Ambuye, ndinu wabwino, ndi wokhululukira, ndi wa chifundo chochulukira onse akuitana Inu.


Kodi mkazi angaiwale mwana wake wa pabere, kuti iye sangachitire chifundo mwana wombala iye? Inde awa angaiwale, koma Ine sindingaiwale iwe.


Ndidzatchula zachifundo chake cha Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wake waukulu kwa banja la Israele, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa chifundo chake, ndi monga mwa ntchito zochuluka za chikondi chake.


Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?


Taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, ndidzakhazikitsa mau abwino aja ndinanena za nyumba ya Israele ndi za nyumba ya Yuda.


Mukani nao mau, nimubwerere kwa Yehova; nenani kwa Iye, Chotsani mphulupulu zonse, nimulandire chokoma; ndipo tidzapereka mau milomo yathu ngati ng'ombe.


Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, wakukhululukira mphulupulu, wakupitirira zolakwa za otsala a cholowa chake? Sasunga mkwiyo wake kunthawi yonse popeza akondwera nacho chifundo.


Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?


Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wanu wa Kumwamba.


Kapena pompempha nsomba, adzampatsa iye njoka kodi?


Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo chiyani tsono? Kodi tiposa ife? Iai ndithu; pakuti tidawaneneza kale Ayuda ndi Agriki omwe, kuti onsewa agwidwa ndi uchimo;


Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?


Komatu lembo linatsekereza zonse pansi pa uchimo, kuti lonjezano la kwa chikhulupiriro cha Yesu Khristu likapatsidwe kwa okhulupirirawo.


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Taonani, chikondicho Atate watipatsa, kuti titchedwe ana a Mulungu; ndipo tili ife otere. Mwa ichi dziko lapansi silizindikira ife, popeza silimzindikira Iye.


Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa