Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 25:7 - Buku Lopatulika

7 Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Musakumbukire zolakwa za ubwana wanga kapena zopikisana nanu. Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu, chifukwa cha ubwino wanu, Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Musakumbukire machimo a unyamata wanga ndi mphulupulu zanga. Koma mundikomere mtima, Inu Chauta, chifukwa cha chikondi chanu, pakuti Inu ndinu abwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Musakumbukire machimo a ubwana wanga ndi makhalidwe anga owukira; molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine, pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 25:7
25 Mawu Ofanana  

Pakuti mundilembera zinthu zowawa, ndi kundipatsa ngati cholowa mphulupulu za ubwana wanga.


Mafupa ake adzala nao unyamata wake, koma udzagona naye pansi m'fumbi.


Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthawi zonse.


Mundikumbukire, Yehova, monga momwe muvomerezana ndi anthu anu; mundionetsa chipulumutso chanu:


Mphulupulu za makolo ake zikumbukike ndi Yehova; ndi tchimo la mai wake lisafafanizidwe.


Chifukwa kuti sanakumbukire kuchita chifundo, koma analondola wozunzika ndi waumphawi, ndi wosweka mtima, kuti awaphe.


Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu;


Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu, ndipo ndiphunzitseni malemba anu.


Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu, mundipulumutse ndi chifundo chanu.


Mundichitire ine chifundo, Mulungu, monga mwa kukoma mtima kwanu; monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma mufafanize machimo anga.


Bwererani Yehova, landitsani moyo wanga; ndipulumutseni chifukwa cha kukoma mtima kwanu.


Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu; nsoni zokoma zanu zitipeze msanga, pakuti tafooka kwambiri.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.


Chifukwa cha Ine ndekha, chifukwa cha Ine ndekha ndidzachita ichi, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? Ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.


Musakwiye kopambana, Yehova, musakumbukire zoipa nthawi zonse; taonani, yang'anani ife, tikupembedzani Inu, ife tonse tili anthu anu.


Tigone m'manyazi athu, kunyala kwathu kutifunde ife; pakuti tamchimwira Yehova Mulungu wathu, ife ndi makolo athu, kuyambira ubwana wathu kufikira lero lomwe; ndipo sitidamvere mau a Yehova Mulungu wathu.


ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.


Zitapita izi Yesu anampeza mu Kachisi, nati kwa iye, Taona, wachiritsidwa; usachimwenso, kuti chingakugwere choipa choposa.


Koma panali munthu wina apo, ali m'kudwala kwake zaka makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu.


Kuti ndidzachitira chifundo zosalungama zao, ndipo zoipa zao sindidzazikumbukanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa