Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 90:2 - Buku Lopatulika

2 Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Asanabadwe mapiri, kapena musanalenge dziko lapansi, ndi lokhalamo anthu, inde, kuyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha, Inu ndinu Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mapiri asanabadwe, ndipo musanalenge dziko lapansi ndi pokhala anthu, ndinu Mulungu kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mapiri asanabadwe, musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse, kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:2
23 Mawu Ofanana  

Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.


Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kapena unayamba kulengedwa ndiwe, osati mapiri?


Taonani, Mulungu ndiye wamkulu, ndipo sitimdziwa; chiwerengo cha zaka zake nchosasanthulika.


Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoni Ziyoni; popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.


Koma chifundo cha Yehova ndicho choyambira nthawi yosayamba kufikira nthawi yosatha kwa iwo akumuopa Iye, ndi chilungamo chake kufikira kwa ana a ana;


Amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zili m'mwemo. Ndiye wakusunga choonadi kosatha,


Pakuti ananena, ndipo chinachitidwa; analamulira, ndipo chinakhazikika.


Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija; Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.


Ndipo Aroni anatambasula dzanja lake pamadzi a mu Ejipito; ndipo anakwera achule, nakuta dziko la Ejipito.


Atero Yehova, mfumu ya Israele ndi Mombolo wake, Yehova wa makamu, Ine ndili woyamba ndi womaliza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.


Yang'anani kwa Ine, mupulumutsidwe, inu malekezero onse a dziko; pakuti Ine ndine Mulungu, palibe wina.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba ya kale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofewa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malawi amoto, ndi njinga zake moto woyaka.


Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Yesu Khristu ali yemweyo dzulo, ndi lero, ndi kunthawi zonse.


Ine ndine Alefa ndi Omega, ati Ambuye Mulungu, amene ali, amene adali, ndi amene alinkudza, Wamphamvuyonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa