Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 90:1 - Buku Lopatulika

1 Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ambuye, Inu munatikhalira mokhalamo m'mibadwomibadwo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Inu Ambuye, ndinu kothaŵira kwathu pa mibadwo yonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo pa mibado yonse.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 90:1
15 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, munthu wa Mulungu anachokera ku Yuda mwa mau a Yehova nadza ku Betele; ndipo Yerobowamu anali kuimirira m'mbali mwa guwa la nsembe kufukiza zonunkhira.


Mundikhalire thanthwe lokhalamo, lopitako kosaleka; mwalamulira kundipulumutsa; popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.


Ndidzaimbira zachifundo za Yehova nthawi yonse, pakamwa panga ndidzadziwitsira chikhulupiriko chanu ku mibadwomibadwo.


Iye amene akhala pansi m'ngaka yake ya Wam'mwambamwamba adzagonera mu mthunzi wa Wamphamvuyonse.


Popeza udati, Inu Yehova, ndinu pothawirapo panga! Udaika Wam'mwambamwamba chokhalamo chako;


Ndipo Iye adzakhala malo opatulika; koma mwala wophunthwitsa, ndi thanthwe lolakwitsa la nyumba zonse ziwiri za Israele, khwekhwe ndi msampha wa okhala mu Yerusalemu.


chifukwa chake uziti, Atero Yehova Mulungu, Ngakhale ndawachotsa kutali mwa amitundu, ngakhalenso ndawabalalikitsa m'maiko, koma ndidzawakhalira malo opatulika kanthawi kumaiko adafikako.


Si ndinu wachikhalire, Yehova Mulungu wanga, wopatulika wanga? Sitidzafa. Yehova munamuikiratu kuti aweruzidwe; ndipo Inu, Thanthwe, munamkhazika kuti alangidwe.


Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.


Ndipo mdalitso, Mose munthu wa Mulungu anadalitsa nao ana a Israele asanafe, ndi uwu.


Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.


Koma iwe, munthu wa Mulungu iwe, thawa izi; nutsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.


Ndipo ife tazindikira, ndipo takhulupirira chikondicho Mulungu ali nacho pa ife. Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m'chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa