Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 23:19 - Buku Lopatulika

19 Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mulungu sali ngati munthu kuti angathe kunama, si munthu kuti angathe kusintha maganizo ake. Kodi sadzachitadi zomwe adanena? Kapena sadzachitadi zimene adalankhula?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Mulungu si munthu kuti aname, kapena mwana wa munthu kuti asinthe maganizo ake. Kodi amayankhula koma osachita? Kodi amalonjeza koma osakwaniritsa?

Onani mutuwo Koperani




Numeri 23:19
36 Mawu Ofanana  

khala mlendo m'dziko muno, ndipo Ine ndidzakhala ndi iwe, ndipo ndidzadalitsa iwe chifukwa kuti ndidzakupatsa iwe ndi mbeu zako maiko onse awa, ndipo ndidzalimbikitsa chilumbiriro ndinachilumbirira kwa Abrahamu atate wako;


Taonani, Ine ndili pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakusunga iwe konse kumene upitako, ndipo ndidzakubwezanso iwe ku dziko lino; chifukwa kuti sindidzakusiya iwe, kufikira kuti nditachita chimene ndanena nawe.


Agalu adzadya aliyense wa Yerobowamu wakufa m'mzinda; ndi mbalame za m'mlengalenga zidzadya yense wakufera kuthengo; popeza wanena ndi Yehova.


Awa ndi mau a Yehova anawanena ndi Yehu, ndi kuti, Ana ako kufikira mbadwo wachinai adzakhala pa mpando wachifumu wa Israele. Ndipo kunatero momwemo.


Pamenepo kazembe amene mfumu ankatsamira padzanja lake anamyankha munthu wa Mulungu, nati, Taonani, Yehova angachite mazenera m'mwamba chidzachitika ichi kodi? Nati iye, Taona, udzachiona ndi maso ako, koma iwe sudzadyako ai.


Ndipo ichi nchaching'ono pamaso panu, Mulungu, koma mwanena za nyumba ya mtumiki wanu nthawi yam'tsogolo ndithu, ndipo mwandiyesera ngati munthu womveka, Yehova Mulungu.


Yehova walumbira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melkizedeki.


Yehova analumbira Davide zoona; sadzalibweza; ndi kuti, Wa iwo okhala zipatso za thupi lako ndidzaika pa mpando wachifumu wako.


Kodi Mulungu waiwala kuchita chifundo? Watsekereza kodi nsoni zokoma zake mumkwiyo?


Sindidzaipsa chipangano changa, kapena kusintha mau otuluka m'milomo yanga.


Ndinalumbira kamodzi m'chiyero changa; sindidzanamizira Davide.


ndi otsala amauta, ngwazi za ana a Kedara zidzachepa, pakuti Yehova Mulungu wa Israele wanena.


Koma Iyenso ndi wanzeru, nadzatengera choipa, ndipo sadzabwezanso mau ake, koma adzaukira banja la ochita zoipa, ndi amene athandiza iwo akugwira ntchito yoipa.


Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.


ndiitana mbalame yolusa kuchokera kum'mawa, ndiye munthu wa uphungu wanga, kuchokera kudziko lakutali; inde, ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.


momwemo adzakhala mau anga amene atuluka m'kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula m'mene ndinawatumizira.


Chifukwa chimenecho dziko lidzalira maliro, ndipo kumwamba kudzada; chifukwa ndanena, ndatsimikiza mtima, sindinatembenuka, sindidzabwerera pamenepo.


Chonsechi chinagwera mfumu Nebukadinezara.


Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mzinda.


Mudzapatsa kwa Yakobo choonadi, ndi kwa Abrahamu chifundo chimene munalumbirira makolo athu kuyambira masiku a kale lomwe.


Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumirira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.


Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.


Ine Yehova ndanena, ndidzachitira ndithu ichi khamu ili lonse loipa lakusonkhana kutsutsana nane; adzatha m'chipululu muno, nadzafamo.


Ndipo ananena fanizo lake, nati, Ukani, Balaki, imvani; ndimvereni, mwana wa Zipori.


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Pakuti mphatso zake ndi kuitana kwake kwa Mulungu sizilapika.


Koma sikuli ngati mau a Mulungu anakhala chabe ai. Pakuti onse akuchokera kwa Israele siali Israele;


ngati tikhala osakhulupirika, Iyeyu akhala wokhulupirika; pakuti sangathe kudzikana yekha.


m'chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthawi zosayamba;


kuti mwa zinthu ziwiri zosasinthika, m'mene Mulungu sangathe kunama, tikakhale nacho chotichenjeza cholimba, ife amene tidathawira kuchigwira chiyembekezo choikika pamaso pathu;


koma Iye ndi lumbiro mwa Iye amene anenana kwa Iye, Walumbira Ambuye ndipo sadzalapa, iwe ndiwe wansembe nthawi yosatha).


Mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro zichokera Kumwamba, zotsika kwa Atate wa mauniko, amene alibe chisanduliko, kapena mthunzi wa chitembenukiro.


Kodi muyesa kapena kuti malembo angonena chabe? Kodi Mzimuyo adamkhalitsa mwa ife akhumbitsa kuchita nsanje?


Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinenera nyumba ya Israele; zidachitika zonse.


Ndiponso Wamphamvu wa Israele sanama kapena kulapa; popeza Iye sali munthu kuti akalapa.


Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa