Mavesi a Baibulo

Zotsatsa


Gulu Laling'ono

64 Mau a m'Baibulo okhudza Yerusalemu

Kwa ine, monga mwana wa Mulungu, Yerusalemu ndi malo ofunika kwambiri pa utumiki wa Yesu. Malinga ndi Chipangano Chatsopano, Yerusalemu ndi komwe Yesu ankabwera ali mwana kuti akawonetsedwe ku Kachisi.

Ndi chifukwa chake tiyenera kupemphera kwa Mulungu chifukwa cha dziko lodalitsali, monga momwe Mawu ake amanenera: "Pempherani mtendere wa Yerusalemu; iwo akuchikondani akhale ndi moyo wabwino" (Masalmo 122:6).

Ndikofunika kwambiri kuti, monga anthu a Mulungu, tipempherere Yerusalemu, tipemphe Yesu kuti chifundo chake chifikire mzindawu ndipo akwaniritse chifuniro chake pakati pawo.

Tiyeni tipemphere kuti atsegule maso awo auzimu kuti abwerere kwa Mulungu ndi mtima wonse ndipo aliyense wa iwo avomereze kuti Khristu ndiye Ambuye, akumvetsa kuti Yesu anatenga chilango cha mtendere wawo ndipo akhoza kupulumutsidwa kudzera mu nsembe yake pa mtanda.

Ndikupemphera kuti chikondi chimene Mulungu ali nacho pa Yerusalemu chidzaze mitima yathu nthawi iliyonse imene tipemphera kwa Iye chifukwa cha mzindawu.


Yesaya 62:1

Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete, chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete, mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuŵala, ndipo chipulumutso chake chitaoneka ngati muuni woyaka.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 23:37

“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana!

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 48:1-2

Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,

Inu Mulungu, anthu amakutamandani ponseponse, monga dzina lanu latchuka pa dziko lonse lapansi. Dzanja lanu lamphamvu limapambana nthaŵi zonse.

Anthu okhala mu Ziyoni akondwe. A ku Yuda asangalale chifukwa cha kaweruzidwe kanu kolungama.

Zungulirani Ziyoni yense, inde zungulirani mzinda wonsewo, ndipo muŵerenge nsanja zake.

Yang'anani bwino machemba ake, penyetsetsani malinga ake, kuti mudzathe kusimbira mbadwo wakutsogolo.

Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”

mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 62:6-7

Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndaikapo alonda, usana wonse ndi usiku wonse sadzakhala chete. Inu amene mumakumbutsa Chauta za malonjezo ake, musapumule.

Musaleke kumkumbutsa mpaka atakhazikitsanso Yerusalemu, ndi kuusandutsa mzinda umene dziko lapansi lidzautamanda.

Mutu    |  Mabaibulo
Maliro 1:1

Ha! Mzinda wa Yerusalemu wakhala wokhawokha, m'menemo kale udaali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu, koma tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mzinda wolemekezeka koposa mizinda ina, koma tsopano wasanduka kapolo.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 12:2-3

“Ndidzasandutsa Yerusalemu kuti akhale ngati chikho cha vinyo amene adzasokoneza mitundu yonse ya anthu yomzungulira. Adani omwewo adzathira nkhondo dziko la Yuda ndiponso mzinda wa Yerusalemu.

Tsiku limenelo Yerusalemu ndidzamsandutsa mwala wolemera kwambiri kwa mitundu yonse ya anthu. Onse oyesa kuunyamula, udzaŵapweteka koopsa. Mitundu yonse ya anthu a pansi pano idzasonkhana pamodzi kuti imuukire Yerusalemu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 2:17

Tsono ndidaŵauza kuti, “Mukuwona mavuto amene tili nawo. Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake azitentha. Tiyeni timange makoma a Yerusalemu, kuti tisamachitenso manyazi.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 5:5

“Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa dziko lapansi, ndipo maiko onse akumzungulira.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 14:16

Zitatha zimenezi anthu onse otsala mwa adani amene ankamenyana ndi Yerusalemu, azidzabwera chaka ndi chaka kudzapembedza Mfumu, Chauta Wamphamvuzonse, ndiponso kudzachita chikondwerero chamisasa.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mbiri 6:6

Koma ndidasankha Yerusalemu kuti dzina langa lizimveka kumeneko, ndipo ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 52:1

Dzuka, dzuka, vala dzilimbe iwe Ziyoni. Vala zovala zako zabwino, iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo sadzaloŵanso pa zipata zako.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 11:32

Solomoni ndidzamsiyira fuko limodzi, chifukwa cha Davide mtumiki wanga, ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndausankha pa mafuko onse a Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 68:28-29

Kungani mphamvu zanu, Inu Mulungu, onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatichitira zamphamvu.

Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu, mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 137:5-6

Ndikakuiŵala iwe Yerusalemu, dzanja langa lamanja liwume.

Lilime langa likangamire ku mnakanaka m'kamwa mwanga, ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu ndi kukuwona kuti ndiwe wondisangalatsa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 19:41-44

Yesu atayandikira, nkuwona Yerusalemu, adalira chifukwa cha mzindawo.

Adati, “Ha, iwenso ukadangodziŵa lero lino zinthu zopatsa mtendere! Koma ai, tsopano maso ako sangathe kuziwona.

Nthaŵi idzakufikira pamene adani ako adzakuzinga ndi machemba, nadzakuzungulira, nkukutsekereza ponseponse.

Adzakusakaziratu iweyo pamodzi ndi anthu ako onse. Sadzasiya mwa iwe mwala pamwamba pa unzake, chifukwa chakuti sudazindikire nthaŵi imene Mulungu adaati adzakupulumutse.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 52:1-2

Dzuka, dzuka, vala dzilimbe iwe Ziyoni. Vala zovala zako zabwino, iwe Yerusalemu, mzinda woyera. Anthu osaumbalidwa ndi onyansa pa chipembedzo sadzaloŵanso pa zipata zako.

Chauta wagwiritsa ntchito mphamvu zake zoyera pamaso pa anthu a mitundu yonse, dziko lonse lapansi mpaka ku mathero lidzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

Nyamukani, nyamukani, chokaniko msanga ku Babiloniko, musakhudze kanthu konyansa pa chipembedzo. Tulukanimo ndipo mudziyeretse, inu amene mukunyamula ziŵiya zopatulikira Chauta.

Koma ulendo uno simudzachoka mofulumira, simudzachita chothaŵa. Chauta azidzayenda patsogolo panu, Mulungu wa Aisraele azidzakutetezani kumbuyo kwanu.

Chauta akuti, “Mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake. Adzakwezedwa ndi kulemekezedwa, ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.

Anthu ambiri atamuwona adadzidzimuka, chifukwa nkhope yake inali itasakazika, kotero kuti siinkachitanso ngati ya munthu. Maonekedwe ake sanalinso ngati a munthu.

Chimodzimodzinso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye, Mafumu omwe adzasoŵa naye chonena, popeza kuti zinthu zosaŵauzapo chiyambire adzaziwona, ndipo zinthu zosamvapo nkale lonse, adzazimvetsa.”

Udzisanse fumbi ndipo udzuke, iwe Yerusalemu wogwidwa. Inu omangidwa a ku Ziyoni, aduleni maunyolo ali m'khosi mwanuwo.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 1:17

Ulengezenso kuti Chauta Wamphamvuzonse akuti, “M'mizinda yangayi mudzakhalanso chuma chambiri. Ndidzasangalatsanso Ziyoni, ndipo Yerusalemu ndidzamsandutsanso mzinda wanga wapamtima.” ’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 24:23

Mwezi udzanyala, ndipo dzuŵa lidzachita manyazi, pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu. Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 29:7

Muzikometsa ku mizinda kumene ndidakupirikitsirani ku ukapoloko, kuti zonse zizikuyenderani bwino. Muzipempherera mizindayo kwa Chauta, chifukwa choti mizindayo ikakhala pa mtendere, inunso mudzakhala pabwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:12

Chauta akunena kuti, “Ndidzakupatsa zabwino zochuluka ngati mtsinje wa madzi. Chuma cha mitundu ya anthu chidzafika kwa inu ngati mtsinje wosefukira. Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene mai wake wamnyamulira pambalipa, kapena akumluluza pa maondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 40:2

“Muŵalankhule mofatsa anthu a ku Yerusalemu. Muŵauze kuti nthaŵi ya mavuto ao yatha, machimo ao akhululukidwa. Ndaŵalanga moŵirikiza chifukwa cha machimo ao.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 3:17

“Motero mudzadziŵa kuti ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndimakhala ku Ziyoni, ku phiri langa loyera. Yerusalemu adzakhala woyera ndipo alendo sadzamthiranso nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 65:18-19

Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya, chifukwa cha zimene ndidzalenga. Ndidzalengadi Yerusalemu watsopano wodzaza ndi chimwemwe, ndipo anthu ake adzakhala okondwa.

Mwiniwakene ndidzakhala wokondwa kwambiri chifukwa cha Yerusalemu, ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu ake. Kumeneko sikudzamvekanso kulira kapena kudandaula.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 21:2

Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 33:16

Nthaŵi imeneyo anthu a ku Yuda adzapulumuka, ndipo a ku Yerusalemu adzakhala pa mtendere. Motero mzindawu udzakhala ndi dzina loti ‘Chauta ndiye chipulumutso chathu.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezara 1:3

Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Mateyu 5:35

Usalumbire kuti, ‘Pali dziko lapansi!’ Paja dziko lapansi ndi chopondapo mapazi ake. Usalumbire kuti, ‘Pali Yerusalemu!’ Paja Yerusalemu ndi mzinda wa Mfumu yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 11:36

Komabe mwana wake ndidzamsiyira fuko limodzi kuti pakhalebe Davide mtumiki wanga azidzakhala ndi nyale nthaŵi zonse pamaso panga ku Yerusalemu, mzinda umene ndausankha kuti azindipembedza kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 2:10

“Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 31:5

Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake, Chauta Wamphamvuzonse adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu. Adzauteteza ndi kuupulumutsa, adzausiya pambali ndi kuuwombola.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 17:27

Koma inu mukapanda kundimvera, mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika, ndipo mukamanyamula katundu aliyense nkumakaloŵa pa zipata za Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ndiye kuti ndidzazitentha zipata zimenezo. Moto udzapsereza nyumba zaufumu za ku Yerusalemu, moto wake wosazimika.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 4:3-4

Tsono otsalira ku Ziyoni, amene Mulungu waŵasankha kuti akhale ndi moyo ku Yerusalemu, adzatchedwa oyera.

Pamenepo Ambuye adzakhala atasambitsa akazi a ku Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zao, ndipo adzakhala atatsuka magazi amene adakhetsedwa mu Yerusalemu. Adzachita zimenezi ndi mpweya woweruza ndi woyeretsa ndi moto.

Mutu    |  Mabaibulo
Nehemiya 11:1-2

Nthaŵi imeneyo atsogoleri a mabanja a Aisraele ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse adachita maele kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse oti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulikawo, ndipo anthu asanu ndi anai otsala azikhalabe m'midzi.

Ansembe anali aŵa: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini,

Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi amene anali mkulu wa ansembe ku Nyumba ya Mulungu,

ndiponso achibale ao amene ankagwira ntchito m'Nyumbamo, onse pamodzi analipo 822. Panalinso Adaya, mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya

ndiponso achibale ao amene anali akuluakulu a banja lao. Onse pamodzi analipo 242. Amasisai, mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri,

ndiponso achibale ao amene anali ankhondo olimba mtima. Onse pamodzi analipo 128, ndipo kapitao wao anali Zabidiele, mwana wa Hagedolimu.

Alevi anali aŵa: Semaya, mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni.

Sabetai ndiponso Yozabadi anali atsogoleri a Alevi amene ankayang'anira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu.

Mataniyo, mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, amene anali mtsogoleri pa mapemphero achiyamiko m'Nyumba ya Mulungu, ndiponso Bakibukiya, amene anali wachiŵiri pakati pa abale ake. Panalinso Abida, mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.

Alevi onse amene ankakhala mu mzinda wopatulika analipo 284 pamodzi.

Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: Akubu, Talimoni ndiponso achibale ao onse pamodzi analipo 172.

Ndipo anthu adayamika anzao onse amene adadzipereka kuti azikhala ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 66:10

“Kondwera nayeni Yerusalemu, musangalale chifukwa cha iye, inu nonse amene mumakonda mzinda umenewu. Kondwera nayeni mwachimwemwe, nonsenu amene mukumlira.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 32:31

“Mzinda umenewu wakhala ukuutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira nthaŵi imene adaumanga mpaka lero lino. Nchifukwa chake ndiyenera kuuchotsa pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 122:2-3

Mapazi athu akhala akuima m'kati mwa zipata zako, iwe Yerusalemu.

Yerusalemu adamangidwa bwino, zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Mika 4:2

Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe, ndipo adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tiziyenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 2:3

Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
2 Mafumu 19:31

Ku Yerusalemu kudzafumira anthu otsala, ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka. Changu cha Chauta chidzachitadi zimenezi.

Mutu    |  Mabaibulo
Yoweli 2:32

Ndipo aliyense amene adzatama dzina la Chauta mopemba, adzapulumuka. Monga Iye adanenera, kudzakhala ena opulumuka ku phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo mwa otsalawo padzapezeka ena amene Chauta adzaŵaitana.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 30:18

Chauta akunena kuti, “Ndidzabwezeranso a banja la Yakobe ku dziko lao. Ndidzaonetsanso chikondi changa ku malo ake onse. Mzinda wa Yerusalemu uja udzamangidwanso pabwinja pake pompaja. Nyumba yaufumu idzamangidwanso pamalo pake.

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 16:3

Umuuze kuti, Ambuye Chauta akukuuza kuti, ‘Kanani ndi dziko la makolo ako, ndipo udabadwira kumeneko. Atate ako anali Mwamori, amai ako anali Muhiti.

Mutu    |  Mabaibulo
Chivumbulutso 3:12

Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 9:9

Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 9:11

Apo Chauta adati, “Yerusalemu ndidzamsandutsa bwinja, ndidzamusandutsa mokhala nkhandwe. Mizinda ya ku Yuda idzasiyidwa, simudzakhala anthu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 31:38-40

Chauta akuti, “Ikubwera nthaŵi pamene mzinda uja wa Chauta udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananele mpaka ku Chipata cha Ngodya.

Kuyambira pamenepo malire ake adzapitirira mpaka ku phiri la Garebe, nkudzakhota kuloza ku Gowa.

Ndidzakusamaliraninso inu anthu a ku Israele, motero mudzapezanso bwino. Mudzakondwanso poimba ting'oma tolira, ndipo mudzapita nawo limodzi anthu ovina mwachimwemwe.

Chigwa chonse m'mene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku mtsinje wa Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Kavalo chakuvuma, zonsezo zidzakhala zopatulikira Chauta. Mpakampaka mzinda wa Yerusalemu sudzaonongedwanso kapena kugwetsedwa.”

Mutu    |  Mabaibulo
2 Samueli 5:7

Komabe Davide adalanda linga la Ziyoni, ndiye kuti Mzinda wa Davide.

Mutu    |  Mabaibulo
Yesaya 44:26

Ndine amene ndimatsimikiza mau a mtumiki wanga, ndi kupherezetsa zimene amithenga anga adaneneratu. Ndine amene ndimanena za Yerusalemu kuti anthu adzakhalanso kumeneko, ndi kunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti idzamangidwanso. Ine ndidzautsanso malo ao amene adagwetsedwa.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 8:48

Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 122:6

Pemphererani mtendere wa Yerusalemu ponena kuti, “Anthu amene amakukonda iwe Yerusalemu, zinthu ziziŵayendera bwino.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 122:3

Yerusalemu adamangidwa bwino, zigawo zake zonse nzogwirizana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 125:2

Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo
Masalimo 48:2

mzinda wokongola wa Ziyoni pa phiri la Mulungu, wopatsa chimwemwe ku dziko lonse lapansi. Mzinda wa Ziyoni umene uli kumpotowu, ndi mzinda wa Mfumu yathu yaikulu.

Mutu    |  Mabaibulo
1 Mafumu 15:4

Komabe chifukwa cha Davideyo, Chauta adapatsa Abiya mwana, kuti azilamulira ku Yerusalemu, iyeyo atafa.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 8:3

Ine Chauta Wamphamvuzonse mau anga ndi aŵa: Tsopano ndidzabweranso ku phiri la Ziyoni, ndidzakhalanso ku Yerusalemu. Yerusalemuyo adzatchedwa Mzinda Wokhulupirika. Phiri la Ine Chauta Wamphamvuzonse lidzatchedwa Phiri Loyera.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 30:17

Koma inuyo, ndidzachiza matenda anu, ndidzapoletsa mabala anu, chifukwa anthu ena amati ndinu otayika, amati, ‘Ndi anthu a ku Ziyoni aŵa, opanda oŵasamala,’ ” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo
Yeremiya 3:17

Nthaŵi imeneyo Yerusalemu adzatchulidwa Mpando waufumu wa Chauta. Ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana kumeneko pamaso pa Chauta. Sadzaumiriranso kutsata mtima wao woipa.

Mutu    |  Mabaibulo
Luka 24:47

kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo
Zekariya 12:9

Tsiku limenelo ndidzaononga mitundu yonse ya anthu yofuna kuthira nkhondo Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo
Amosi 2:5

Nchifukwa chake Ineyo ndidzaponya moto ku Yuda, ndipo motowo udzapsereza malinga a Yerusalemu.”

Mutu    |  Mabaibulo
Ezekieli 36:38

Adzachuluka ngati nkhosa za ku Yerusalemu zimene ankazipereka kale ku nsembe pa nthaŵi ya chikondwerero. Motero mizinda yao yamabwinja ija idzadzazadi ndi magulu a anthu, ndipo iwowo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wodalitsika, ulemerero wonse ndi ulemu zikhale zanu m'dzina la Yesu. Atate, ndikupemphani kuti mtendere wanu, wopambana chidziwitso chonse, ukhale pa Yerusalemu ndipo Mzimu Woyera wanu waulemerero utsanulidwe pa miyoyo yawo. Mudzitamandire mwa atsogoleri awo ndi anthu okhalamo, kuti adziwe kuti ndinu Ambuye, Mpulumutsi ndi Kalonga wa mtendere. Ndikukupemphani kuti muwadzaze ndi nzeru kuti apange zisankho zomwe zimabweretsa mtendere, osati nkhondo, mawu anu amati: Monga momwe Yerusalemu ili ndi mapiri ozungulira, momwemonso Yehova ali kuzungulira anthu ake, kuyambira tsopano mpaka kalekale. Ambuye, mwalonjeza kuteteza ndi kukhala nawo nthawi zonse ndikuwalimbitsa ku zoyipa za adani awo. Ndikupemphaninso, kuti mupereke nzeru ndi njira kwa wokhulomera aliyense wachikhristu, amene akulalikira mawu anu ku Yerusalemu pakali pano, mupereke luntha kuti athe kugawana uthenga wanu wa mtendere pa miyoyo ya anthu okhalamo. M'dzina la Yesu. Ameni!