Ndipo chodabwitsa kwambiri n’chakuti chiyambi cha zilankhulo chili m’Mawu a Mulungu, ndipo uthenga wake wafikira anthu amitundu yosiyanasiyana. Mawu a Mulungu alipo m’Chichewa chomwe ndimalankhula, ndipo izi zimandipatsa mphamvu panthawi yovuta ngati palibe amene akundimvetsa.
Nthawi zina, zimandivuta kwambiri ndipo ndimamva ngati palibe amene akundimvetsa. Koma ndikamatsegula Baibulo, ndimamva Mulungu akulankhula nane m’chinenero changa. Ndimamva mtendere ndi chiyembekezo, ndipo ndimapeza mayankho a mavuto anga.
Baibulo ndi buku lofunika kwambiri pa moyo wanga. Limandiphunzitsa zoyenera kuchita ndi zosayenera kuchita. Ndili ndi mwayi waukulu chifukwa Mulungu, m’chifundo chake, anatipatsa mphatso yolankhulana wina ndi mnzake, kulikonse kumene tili.
Paja Malembo akunena kuti, “Ambuye akuti, ‘Pali Ine ndemwe, anthu onse adzandigwadira ndi kuvomereza kuti ndine Mulungu.’ ”
Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi. Nayi mibadwo yofumira mwa Semu: Patangopita zaka ziŵiri chitatha chigumula, Semu ali wa zaka 100, adabereka mwana dzina lake Aripakisadi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 500, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pamene Aripakisadi anali wa zaka 35, adabereka mwana dzina lake Sela. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pamene Sela anali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Eberi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 403, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Eberi ali wa zaka 34, adabereka mwana dzina lake Pelegi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 430, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Pelegi ali wa zaka 30 adabereka mwana dzina lake Reu. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 209, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Atasamukira chakuvuma, adakafika ku chigwa ku dziko la Sinara kumene adakhazikika. Reu ali wa zaka 32, adabereka mwana dzina lake Serugi. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 207, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Serugi ali wa zaka 30, adabereka mwana dzina lake Nahori. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka zina 200, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Nahori ali wa zaka 29, adabereka mwana dzina lake Tera. Pambuyo pake adakhala ndi moyo zaka 119, ndipo adaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. Tera ali wa zaka 70, adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Nazi zidzukulu za Tera: Tera adabereka Abramu, Nahori ndi Harani. Harani adabereka Loti. Haraniyo adafera m'mudzi wa kwao dzina lake Uri, wa ku Kaldeya. Adafa atate ake akali moyo. Abramu ndi Nahori adakwatira. Abramu adakwatira Sarai, ndipo Nahori adakwatira Milika mwana wa Harani, amene analinso bambo wake wa Isika. Tsono adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tiwumbe njerwa ndi kuzitentha.” Motero m'malo mwa miyala adatenga njerwa, namangira phula m'malo mwa matope. Sarai analibe ana chifukwa anali wosabala. Tsono Tera adatenga mwana wake Abramu ndi Loti mdzukulu wake, mwana wa Harani, ndiponso mpongozi wake Sarai, mkazi wa Abramu. Adanyamuka ulendo kuchoka ku mzinda uja wa Uri wa ku Kaldeya napita nawo ku dziko la Kanani. Adakafika ku Harani, nakhazikika kumeneko. Ndipo Tera adafera kumeneko ali wa zaka 205. Ndipo adati, “Tsopano tiyeni timange mzinda wathu, ndipo nsanja yake italike mpaka kukafika kumwamba. Tikatero tidzatchuka ndithu, ndipo sitidzamwazikanso pa dziko lapansi.” Tsono Chauta adatsika kudzaona mzindawo, pamodzi ndi nsanja imene anthu ankamanga. Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna. Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.” Motero Chauta adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi, ndipo iwowo adaleka kumanga mzindawo. Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi.
Kulankhula kwabwino sikuyenerana ndi chitsiru. Nanji kulankhula kwabodza, kodi kungayenerane ndi mfumu?
Ndipo adati, “Tsopano anthu onseŵa ndi amodzi, ndipo akulankhula chilankhulo chimodzi. Zinthu akuchitazi ndi chiyambi chabe cha zimene adzachite. Kenaka iwoŵa adzachita chilichonse chimene afuna. Tiyeni titsikire komweko, tikasokoneze chilankhulo chao kuti asamvane.”
Adalipereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene zinkatuluka m'dziko la Ejipito. Ndikumva liwu limene sindidalimve ndi kale lonse, lakuti,
Palibe kulankhula, palibe kunena mau aliwonse. Liwu lao silimveka konse. Komabe uthenga wao umafalikira pa dziko lonse lapansi. Mau aowo amafika mpaka ku mathero a dziko. Mulungu adamangira dzuŵa nyumba m'thambomo.
Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu.
Ndithudi, Mulungu adzakuphunzitsani kudzera mwa anthu a chilankhulo chachilendo, anthu a chilankhulo chamtundu.
Simudzaonanso anthu amwano aja amene chilankhulo chao nchosadziŵika, chachilendo ndi chosamveka.
Nchifukwa chake tsono, abale anga, ikani mtima pa kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndipo musaletse anthu kulankhula zilankhulo zosadziŵika. Munthu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, amangothandizidwa yekha, koma wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, amathandiza mpingo. Koma tsono, zonse zizichitika moyenera ndi molongosoka.
Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu.
Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse. Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika. Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi? Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo,
Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira. Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao. Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi. Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita. Okhulupirira onse anali amodzi, ndipo ankagaŵana zinthu zao. Ankagulitsa minda yao ndi katundu wao, ndalama zake nkumagaŵira onse, malinga ndi kusoŵa kwa aliyense. Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso. Tsono, m'Yerusalemu muja munali Ayuda ena, anthu okonda Mulungu, ochokera ku maiko onse a pa dziko lapansi. Pamene mkokomo uja udamveka, anthu ambirimbiri adasonkhana. Onse adadodoma, chifukwa aliyense mwa iwo ankaŵamva akulankhula chilankhulo chake.
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.
Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati,
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.
Amapatsa wina mphamvu zochitira zozizwitsa, wina mphatso ya kulalika mau a Mulungu, wina nzeru za kusiyanitsa pakati pa zinthu zochokera kwa Mzimu Woyera ndi zochokera kwina. Amapatsa wina mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndipo amapatsa wina mphatso ya kutanthauzira zilankhulozo.
Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira.
Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.
Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Munthutu wolankhula chilankhulo chosadziŵika, salankhula ndi anthu ai, koma ndi Mulungu. Palibe munthu womvetsa zimene iyeyo akunena, Mzimu Woyera ndiye amamlankhulitsa zachinsinsi.
Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate.
akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndikadakonda kuti nonsenu mukhale nayo mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika, koma makamaka ndikadakonda kuti nonsenu mukhale ndi mphatso ya kulankhula mau ochokera kwa Mulungu. Pakuti munthu wolankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndiye wofunika kwambiri kuposa wolankhula zilankhulo zosadziŵika, ngati palibe munthu wotanthauzira zilankhulo, kuti mpingo upindulepo.
Mosapeneka konse pali zilankhulo zamitundumitundu pa dziko lapansi, ndipo palibe ndi chimodzi chomwe chimene mau ake alibe tanthauzo. Koma ngati ine sindidziŵa tanthauzo la mau a m'chilankhulo, ndidzakhala mlendo kwa amene akulankhula, ndipo iyenso adzakhala mlendo kwa ine.
Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Ndikuthokoza Mulungu kuti ine ndimalankhula m'zilankhulo zosadziŵika kuposa nonsenu. Komabe mu msonkhano wa mpingo, m'malo molankhula mau ochuluka m'chilankhulo chosadziŵika, ndingakonde kwambiri kunena mau asanu okha omveka bwino, kuti ndiphunzitsire anthu.
Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima. Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula. Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
M'Malembo mudalembedwa kuti, “Ndidzalankhula ndi mtundu uwu kudzera mwa anthu a zilankhulo zachilendo, ndiponso ndi pakamwa pa anthu achilendo. Koma ngakhale nditero, sadzandimvera, akutero Chauta.” Motero kulankhula m'zilankhulo zosadziŵika, ndi chizindikiro kwa anthu osakhulupirira, osati kwa anthu okhulupirira. Koma kulankhula mau ochokera kwa Mulungu, ndi chizindikiro kwa anthu okhulupirira, osati kwa osakhulupirira.
Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo. Ngati alipo ena ofuna kulankhula m'chilankhulo chosadziŵika, alankhule aŵiri okha, kapena atatu, koma osapitirira pamenepo. Alankhule modikirana, ndipo pakhale wina wotanthauzira mauwo. Koma ngati palibe munthu wotha kutanthauzira mauwo, iyeyo akhale chete mu msonkhano, ndipo azingolankhula ndi Mulungu payekha.
Pambuyo pake nditayang'ana, ndidaona chinamtindi cha anthu osaŵerengeka. Anthuwo anali ochokera m'mitundu yonse ya anthu, ndi m'mafuko onse, ndipo anali a zilankhulo zonse. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Mwanawankhosa uja; anali atavala mikanjo yoyera, nthambi zakanjedza zili m'manja.
Pamenepo adandiwuza kuti, “Uyenera kulengezanso za mitundu yambiri ya anthu, za zilankhulo zosiyanasiyana, ndi za mafumu ambiri.”
Pambuyo pake ndidaona mngelo wina akuuluka mu mlengalenga. Anali ndi Uthenga Wabwino wamuyaya woti akalalike kwa anthu okhala pa dziko lapansi, kwa anthu a mtundu uliwonse, a fuko lililonse, ndi a chilankhulo chilichonse.
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Mngelo wa Ambuye adauza Filipo kuti, “Nyamuka, pita chakumwera, kutsata mseu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu; mseu wodzera m'chipululu uja.” Filipo adanyamukadi napita. Ndipo munthu wina wa ku Etiopiya adaabwera ku Yerusalemu kudzapembedza. Iyeyu anali nduna yaikulu ya m'banja la mfumukazi Kandake wa ku Etiopiya, ndiponso woyang'anira chuma chake chonse. Nthaŵi imeneyo ankabwerera kwao. Anali pa galeta akuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono Mzimu Woyera adauza Filipo kuti, “Pita, kayandikane nalo galetalo.” Koma Saulo uja ankapasula Mpingo. Ankaloŵa m'nyumba za anthu, namagwira amuna ndi akazi omwe, nkumaŵaponya m'ndende. Filipo adathamangira nduna ija, ndipo adaimva ikuŵerenga buku la mneneri Yesaya. Tsono adaifunsa kuti, “Bwana, kodi mukumvetsa zimene mukuŵerengazi?” Iye adati, “Ha, ndingamvetse bwanji popanda wina wondimasulira?” Motero adaitana Filipo kuti adzakwere ndi kukhala naye pagaletapo. Mau a m'Malembo amene ankaŵerengawo ndi aŵa: “Iye anali ngati nkhosa yoitsogoza pokaipha, ngati mwana wankhosa wongokhala duu pomumeta. Sadalankhulepo kanthu. Adampeputsa, pa mlandu wake sadamchitire chilungamo. Palibe amene adzatha kusimba za zidzukulu zake, pakuti moyo wake wachotsedwa pa dziko lapansi.” Pamenepo nduna ija idati, “Pepani, tandiwuzani, kodi zimenezi mneneriyo akunena za yani, za iye mwini, kapena za wina?” Apo Filipo adayamba kumlalikira Uthenga Wabwino wa Yesu kuyambira pa Malembo ameneŵa.
Kenaka adaŵauza kuti, “Nzimenezitu zimene ndinkakuuzani pamene ndinali nanu. Paja ndinkanena kuti zonse ziyenera kuchitikadi zimene zidalembedwa za Ine m'Malamulo a Mose, m'mabuku a aneneri, ndi m'buku la Masalimo.” Tsono adaŵathandiza kuti amvetse bwino Malembo. Adaŵauza kuti, “Zimene zidalembedwa ndi izi: zakuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adayenera kumva zoŵaŵa, nkuuka kwa akufa patapita masiku atatu, kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao. Inuyo ndinu mboni zake za zimenezi.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Poyambayamba anthu onse a pa dziko lapansi ankalankhula chilankhulo chimodzi, ndipo mau amene ankalankhulawo anali amodzi.
Choncho mzinda umenewo adautcha Babele, chifukwa choti kumeneko Chauta adasokoneza chilankhulo cha anthu onse. Ndipo kuchokera kumeneko adaŵamwaza anthuwo pa dziko lonse lapansi.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Mwakuti theka limodzi la ana ao ankalankhula chilankhulo cha ku Asidodi, sankathanso kulankhula Chiyuda, koma ankalankhula chilankhulo cha anthu a mitundu inayo.
iwo ankamuuza kuti, “Chabwino, nena kuti, ‘Shiboleti.’ ” Munthuyo ankati, “Siboleti,” pakuti sankatha kutchula bwino mauwo. Ankamugwira ndi kumupha pompo pa madooko a mtsinje wa Yordani. Nthaŵi imeneyo adaphedwa Aefuremu 42,000.
Ameneŵa ndiwo zidzukulu za Semu. Mafuko ao anali osiyanasiyana, ndipo ankakhalanso m'maiko osiyanasiyana. Fuko lililonse linkalankhula chilankhulo chakechake.
Chimodzimodzinso pa nthaŵi ya Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Persiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabiyele ndi anzao ena, adalemba inanso kalata kwa Arita-kisereksesiyo. Kalatayo adailemba m'Chiaramu, ndipo poiŵerenga ankachita kutanthauzira.
Pamenepo Eliyakimu, mwana wa Hilikiya, ndiponso Sebina ndi Yowa adauza kazembeyo kuti, “Pepani, mutilankhule m'Chiaramu atumiki anufe, poti timachimvetsa. Musatilankhule m'Chiyuda pakuti anthu onse ali pakhomaŵa alikumva.”