Ndikufuna ndikuuzeni nkhani yokhudza mpingo wathu. Yesu Khristu, poyambitsa mpingo wake, adatipatsa masomphenya ndi ntchito: kukulitsa mgwirizano ndi chikondi pakati pathu, ndipo adatipatsanso mphamvu yochita zimenezi. Malo ano adakhazikitsidwa kuti uthenga wabwino wa chipulumutso ufalikire, kuti mawu olimbikitsa afalikire, kuti ziphunzitso zilimbikitse okhulupirira, ndi kuti tonse tilimbikitsidwe kukhala oyera. Ndiponso, malo ano ndi ngati nyumba ya banja la Mulungu, komwe mtendere umapezeka kwa iwo amene akuusowa, ndipo chifaniziro cha Khristu chikuwonekera pa chilichonse.
Tsiku lokumbukira kubadwa kwa mpingo wathu, womwe Mulungu watipatsa mwayi wopezekapo, ndi lofunika kwambiri kwa ine. Tiyeni tisangalale ndi chilichonse chomwe Mulungu watichitira, ndi kupambana kulikonse komwe takhala nako. Tiyeni tikumbukire ubwino wake, ndi kuzindikira kuti wakhala wokhulupirika mpaka pano. Ndipo tiyeni tigawane chimwemwechi pamodzi, podziwa kuti Iye adzapitiriza kutithandiza mtsogolomu.
Tikukuthokozani Inu Mulungu, ndithu tikukuthokozani. Tikutchula dzina lanu mopemphera ndipo tikulalika ntchito zanu zodabwitsa.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Komabe ife ndife okhaokha ogwira ntchito ya Mulungu, inuyo ndinu munda wa Mulungu, ndinunso nyumba ya Mulungu.
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Amasunga chipangano chake nthaŵi zonse, sangaiŵale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse.
Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu.
Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.
Muzithandizana kusenza zokulemetsani, ndipo pakutero mumvere ndithu lamulo la Khristu.
Chitsulo amachinola nchitsulo chinzake, chonchonso munthu amasulidwa ndi munthu mnzake.
Khristu ali ngati thupi limodzi limene lili ndi ziwalo zambiri. Ngakhale ziwalozo nzambiri, komabe thupilo ndi limodzi lokha. Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo. Thupitu si chiwalo chimodzi chokha ai, koma lili ndi ziwalo zambiri.
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake! Paja Iye ndi wabwino. Chikondi chake nchamuyaya, kukhulupirika kwake nkosatha.
Anthu anu adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthaŵi yaitali. Adzamanganso pa maziko akalekale. Apo mudzatchedwa anthu okonza makoma, omanganso nyumba zamabwinja, kuti anthu azikhalamo.”
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Nchifukwa chake muzilimbitsana mtima ndi kumathandizana, monga momwe mukuchitiramu.
Mosapeneka, moyo wanu mwa Khristu umakulimbitsani mtima. Chikondi chake chimakuchotsani nkhaŵa. Mumakhala a mtima umodzi mwa Mzimu Woyera, ndipo mumamvera anzanu chifundo ndi chisoni. Adachita zimenezi kuti pakumva dzina la Yesu, zolengedwa zonse kumwamba, pansi pano ndi pansi pa dziko, zidzagwade pansi mopembedza, Zonse zidzavomereze poyera kuti, “Yesu Khristu ndi Ambuye,” ndipo pakutero zilemekeze Mulungu Atate. Nchifukwa chake, inu okondedwa anga, mwakhala omvera nthaŵi zonse pamene ndinali nanu. Nanji tsopano pamene sindili nanu, ndiye muzikhala omvera koposa. Mupitirize ndi kufikitsa chipulumutso chanu pa chimake mwamantha ndi monjenjemerera. Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye. Muzichita zonse mosanyinyirika ndi mosatsutsapo, kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi, pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe. Ndipotu mwina mwake ndidzaphedwa, magazi anga nkukhala ngati otsiridwa pa nsembe imene chikhulupiriro chanu chikupereka kwa Mulungu. Ngati ndi choncho ndili wokondwa, ndipo ndikusangalala nanu pamodzi nonsenu. Chimodzimodzi inunso muzikondwa, ndi kusangalala nane pamodzi. Ngati Ambuye Yesu alola, ndikhulupirira kuti ndidzatha kutuma Timoteo kwanuko msanga, kuti mtima wanga ukhale pansi nditamva za kumeneko. Nchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundikondweretse kwenikweni pakuvomerezana maganizo ndi kukondana chimodzimodzi, kukhala a mtima umodzi ndi a cholinga chimodzi.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Motero palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakati pa akapolo ndi mfulu, kapenanso pakati pa amuna ndi akazi, pakuti nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.
Ndi ngati mame a ku Heremoni, omatsikira ku mapiri a Ziyoni. Ku Ziyoni Chauta amaperekako madalitso, ndiye kuti moyo wamuyaya.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.
Tsono adauza ophunzira ake kuti, “Dzinthu ndzochulukadi, achepa ndi antchito. Nchifukwa chake mupemphe Mwini dzinthu kuti atume antchito okatuta dzinthu dzakedzo.”
Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu.
Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.
M'thupi lathu limodzi lomweli tili ndi ziwalo zambiri, ndipo ziwalozo zili ndi ntchito zosiyanasiyana. Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona.
Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo.
Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.
Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Pamenepo mudzatha kuyenda m'njira zimene Ambuye amafuna, ndi kuŵakondweretsa pa zonse. Pakugwira ntchito zabwino zamitundumitundu, moyo wanu udzaonetsa zipatso, ndipo mudzanka muwonjezerawonjezera nzeru zanu za kudziŵa Mulungu.
Tamandani Chauta. Ndidzathokoza Chauta ndi mtima wanga wonse pa msonkhano wa anthu olungama mtima.
Mau otsiriza ndi aŵa: nonse mukhale a mtima umodzi, ndi omverana chisoni. Muzikondana nawo abale. Mukhale a mtima wachifundo ndi odzichepetsa.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Timathokoza Mulungu nthaŵi zonse chifukwa cha inu nonse ndi kumakutchulani m'mapemphero athu. Timakumbukira kosalekeza pamaso pa Mulungu Atate athu za m'mene mumatsimikizira chikhulupiriro chanu mwa ntchito zanu, za m'mene chikondi chanu chimakuthandizirani kugwira ntchito kolimba, ndiponso za m'mene mumachitira khama poyembekeza Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano.
Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu. Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake? Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.
Koma si pokhapo ai, timakondweranso m'masautso athu. Pakuti tikudziŵa kuti masautso amaphunzitsa munthu kupirira, kupirira kumabweretsa makhalidwe ovomerezedwa ndi Mulungu, ndipo makhalidwe ovomerezedwawo amabweretsa chiyembekezo. Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Ndimayembekeza chithandizo cha Chauta, ndimayembekeza ndi mtima wonse, ndipo ndimakhulupirira mau ake.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika. Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Limeneli ndiye lamulo lalikulu ndi loyamba ndithu. Lachiŵiri lake lofanana nalo ndi ili: Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Pajatu palibe maziko enanso amene wina aliyense angathe kukhazika osiyana ndi maziko amene alipo kale. Mazikowo ndi Yesu Khristu.
Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Tsono popeza kuti mudavomereza kuti Khristu Yesu ndi Mbuye wanu, moyo wanu wonse ukhale wolunzana naye. Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.
Ndipo aliyense wopatsa ngakhale chikho cha madzi ozizira kwa mmodzi mwa ophunzira angaŵa, chifukwa chakuti ndi wophunzira wanga, ndithu ndikunenetsa kuti ameneyo sadzalephera kulandira mphotho yake.”
Makamaka ndinene kuti tikalimbikitsane pamene ndidzakhale pakati panu. Inu mudzandilimbikitsa ndi chikhulupiriro chanu, ine nkukulimbikitsani ndi chikhulupiriro changa.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu, umene umalamula thupi lonse, ndi kulilumikiza pamodzi ndi mfundo zake zonse. Motero chiwalo chilichonse chimagwira ntchito yake moyenera, ndipo thupi lonse limakula ndi kudzilimbitsa ndi chikondi.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.