Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


101 Mauthenga a M'Baibulo Okhudza Ubatizo

101 Mauthenga a M'Baibulo Okhudza Ubatizo

Ubatizo ndi mwambo woyamba wa Uthenga Wabwino. Yesu Khristu analamulira atumwi ake kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani mitundu yonse ya anthu, muwabatize m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la Mzimu Woyera, ndipo muziwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani; ndipo onani, Ine ndili pamodzi nanu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ino.” (Mateyu 28:19-20). Masiku ano, monga m’nthawi ya Yesu, pali mfundo ndi miyambo ya Uthenga Wabwino yomwe tiyenera kuphunzira ndi kutsatira.

Mfundo ya Uthenga Wabwino ndi chikhulupiriro kapena chiphunzitso choona; mwambo ndi mwambo kapena lamulo. Mfundo ziwiri zoyambirira za Uthenga Wabwino ndi chikhulupiriro mwa Ambuye Yesu Khristu ndi kulapa. Ndikukhulupirira kuti ngati tiphunzira ndikutsatira mfundo izi, tidzadalitsidwa kwambiri.




Machitidwe a Atumwi 2:38

Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:16

Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:27

Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:5

Pali Mbuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:3

Kodi inu simukudziŵa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:4

Zimenezi zidachitikadi pamene Yohane Mbatizi adaafika ku chipululu, nayamba kulalika. Ankauza anthu kuti, “Tembenukani mtima, mubatizidwe, ndipo Mulungu adzakukhululukirani machimo anu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 3:26-27

Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:19-20

Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:11

“Ine ndimakubatizani ndi madzi, kusonyeza kuti mwatembenuka mtima. Koma amene akubwera pambuyo panga ndi wamphamvu kuposa ine. Ameneyo ine ndine wosayenera ngakhale kunyamula nsapato zake. Iyeyo adzakubatizani mwa Mzimu Woyera ndiponso m'moto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:21

Madziwo akufanizira ubatizo umene masiku ano umakupulumutsani chifukwa cha kuuka kwa Yesu Khristu. Kubatizidwa kumeneku si kuchotsedwa litsiro la m'thupi, koma kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima woona, kudzera mwa Yesu Khristu

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:15

kuti aliyense wokhulupirira akhale ndi moyo wosatha mwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 22:16

Nanga tsono ukuchedweranji? Dzuka ndi kutama dzina lake mopemba, ubatizidwe ndi kusambitsidwa kuti machimo ako achoke.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:5

Anthu ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi a ku Yerusalemu ankadza kwa iye. Tsono ankati iwo akaulula machimo ao, iye nkumaŵabatiza mu Mtsinje wa Yordani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:12

Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47

“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:13

Pajatu ngakhale ndife Ayuda kapena a mitundu ina, akapolo kapena mfulu, tidabatizidwa mwa Mzimu Woyera mmodzimodzi kuti tikhale thupi limodzi. Ndipo tonse tidalandira nao Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:3-4

Kodi inu simukudziŵa kuti tonse amene tidasanduka amodzi ndi Khristu Yesu pakubatizidwa, ndi ubatizo womwewo tidasandukanso amodzi ndi Iye mu imfa yake? Nchifukwa chake pa ubatizo tidachita ngati kufa ndi kuikidwa m'manda pamodzi naye, kuti monga Khristu adauka kwa akufa ndi mphamvu ya Atate, momwemonso ife tikhale ndi moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:47-48

“Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?” Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:16-17

Yesu atangobatizidwa, adatuluka m'madzimo. Pomwepo kuthambo kudatsekuka, ndipo adaona Mzimu wa Mulungu akutsika ngati nkhunda nkutera pa Iye. Tsono kuthamboko kudamveka mau akuti, “Uyu ndiye Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera naye kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:21-22

Tsiku lina anthu onse aja atabatizidwa, Yesu nayenso adabatizidwa. Pamene Iye ankapemphera, kuthambo kudatsekuka, ndipo Mzimu Woyera adatsikira pa Iye, akuwoneka ndi thupi ngati la nkhunda. Tsono kudamveka mau ochokera Kumwamba akuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga wapamtima. Ndimakondwera nawe kwambiri.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:2

Mundisambitse kwathunthu pochotsa kulakwa kwanga, mundiyeretse mtima pochotsa machimo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:36-38

Ndipo pamene ankapita mumseumo, adafika pena pamene panali madzi. Nduna ija idati, “Madzi si aŵa. Monga pali choletsa kuti ndisabatizidwe?” [ Filipo adayankha kuti, “Mungathe kubatizidwa ngati mukhulupirira ndi mtima wanu wonse.” Iye adati, “Ndikukhulupirira kuti Yesu Khristu ndi Mwana wa Mulungu.”] Pamenepo ndunayo idalamula kuti galetalo liime. Aŵiri onsewo, Filipo ndi nduna ija, adatsikira ku madzi, Filipo nkumubatiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:5

Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati munthu sabadwa m'madzi ndi mwa Mzimu Woyera, sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:5

Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:4

Paulo adati, “Yohane ankabatiza anthu otembenuka mtima, koma iye yemwe ankauza anthuwo kuti akhulupirire wina amene analikudza pambuyo pa iyeyo. Winayo ndiye Yesu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:17

Paja Khristu adandituma, osati kuti ndizibatiza ai, koma kuti ndizilalika Uthenga Wabwino. Ndipo ndiyenera kumaulalika mosagwiritsa ntchito luso lake la ulaliki, kuwopa kuti mtanda wa Khristu ungatheretu mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:5

Ngati takhala amodzi ndi Khristu mu imfa yake, momwemonso tidzakhala amodzi naye pa kuuka kwa akufa, monga momwe adaukira Iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:30-33

Tsono adaŵatulutsira kunja, naŵafunsa kuti, “Mabwana, Kodi ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.” Kenaka adamlalikira mau a Ambuye iyeyo ndi onse a m'nyumba mwake. Nthaŵi yomweyo, ngakhale unali usiku, iye adaŵatenga nakaŵatsuka mabala ao. Ndipo pompo iye pamodzi ndi onse a m'nyumba mwake adabatizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 18:8

Krispo, mkulu wa nyumba yamapempheroyo pamodzi ndi onse a pa banja lake adakhulupirira Ambuye. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto atamva mau a Paulo, adakhulupirira nabatizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:1

Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:50

Koma ndiyenera kuyamba ndaloŵa m'masautso akulu, ndipo mtima wanga sukhazikika mpaka zitachitika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:14

“Inu ndinu kuŵala kounikira anthu onse. Mudzi wokhala pamwamba pa phiri sungabisike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44-48

Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo. Ndipo okhulupirira achiyuda amene adaaperekeza Petro, adadabwa kuti Mulungu adapereka mphatso ya Mzimu Woyera ndi kwa anthu akunja omwe. Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, “Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?” Motero adalamula kuti abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Ndipo anthuwo adampempha kuti akhale nawo masiku angapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41

Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:10

Kufa kumene adafako kunali kufa kolekana ndi uchimo, ndipo adafa kamodzi kokhako. Tsono moyo umene ali nawo tsopano ndi moyo woperekedwa kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 3:13-15

Pa masiku amenewo Yesu adachoka ku Galileya kubwera kwa Yohane ku mtsinje wa Yordani, kuti Yohaneyo amubatize. Yohane poyesa kukana, adati, “Ndine amene ndiyenera kubatizidwa ndi Inuyo. Nanga mukubweranso kwa ine kodi?” Koma Yesu adamuyankha kuti, “Tsopano lino vomera, chifukwa ndi m'mene tiyenera kuchitira zonse zimene Mulungu akufuna.” Apo Yohane adavomera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:6-8

Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona. Motero pali atatu aŵa ochitira umboni: Mzimu Woyera, madzi ndi magazi, ndipo atatuŵa amavomerezana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:105

mau anu ndiye nyale ya mapazi anga, ndipo amaunikira njira yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 11:16

Pamenepo ndidakumbukira mau aja amene adaalankhula Ambuye akuti, ‘Yohane adabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 116:13

Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31-32

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani? Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:47

Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:2

Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 6:1-2

Tsono tisangoima pa maphunziro oyamba enieni a Khristu. Tisachite kubwerezanso kuphunzitsa zomwe zili ngati maziko, monga za kutembenuka mtima kusiya ntchito zosapindulitsa moyo wosatha, za kukhulupirira Mulungu, Paja Mulungu ngwolungama, sangaleke kusamalako za ntchito zanu, ndi chikondi chimene mudaamuwonetsa pakutumikira oyera ake, monga m'mene mukuchitirabe tsopano. Tikufunitsitsa kuti aliyense mwa inu apitirire kuwonetsa changu chomwechi mpaka potsiriza, kuti chiyembekezo chanu chifike pake penipeni. Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza. Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo. Ndiye Mulungu adati, “Ndithudi ndidzakudalitsa kwakukulu, ndipo ndidzachulukitsa kwambiri zidzukulu zako.” Nchifukwa chake Abrahamu adaayembekeza molimbikira, nalandira zimene Mulungu adaamlonjeza. Anthu amalumbira m'dzina la wina amene akuŵaposa, ndipo lumbiro lotere lotsimikizira mau, limathetsa kutsutsana konse pakati pao. Mulungu pofuna kuŵatsimikizira anthu odzalandira zimene adaalonjeza, kuti Iye sangasinthe maganizo, adatsimikiza lonjezo lakelo pakulumbira. Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu. Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati. za maubatizo, za kusanjika manja, za kuuka kwa akufa, ndi za chiweruzo chotsiriza. Koma tiyeni tipitirire mpaka tikafike pa kukhwima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:9

Iye ndi ine tikhale amodzi. Sindiyesanso pandekha kukhala wolungama pakutsata Malamulo, koma ndizikhala ndi chilungamo chopezeka pakukhulupirira Khristu, chilungamo chochokera kwa Mulungu, chochilandira pakukhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:40-41

Petro adalankhulanso mau ena ambiri, naŵachenjeza kuti, “Muthaŵe maganizo opotoka a mbadwo woipa uno.” Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:29

Ngati Yesu sadauke kwa akufa, nanga amafunanji anthu amene amabatizidwa m'malo mwa amene adafa? Ngati akufa sauka konse, nanga chifukwa chiyani anthu amabatizidwa m'malo mwao?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:37-38

Mukudziŵa zimene zidachitika ku Yudeya konse, kuyambira ku Galileya pambuyo pa nthaŵi imene Yohane ankalalika za ubatizo wake. Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:17

Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:12-14

Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala. Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:12

Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:16

Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:15-16

Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino. Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:38-39

Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:47

kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:20

Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:19

Tsono tembenukani mtima ndi kubwerera kwa Mulungu, kuti akufafanizireni machimo anu. Motero Ambuye adzakupatsani nthaŵi ya mpumulo,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:9

Kwa Inu kuli kasupe wamoyodi, m'kuŵala kwanu ifenso timaona kuŵala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:10-12

Ndipo mwa Iye inu mudapatsidwa moyo wonse wathunthu. Iye ndiye mutu wolamulira maulamuliro onse ndi mphamvu zonse zosaoneka. Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku. Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:27

Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:13

Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:46-47

Pakuti adaŵamva akulankhula zilankhulo zosadziŵika ndi kutamanda ukulu wa Mulungu. Tsono Petro adati, “Anthu aŵa alandira Mzimu Woyera monga ife. Nanga alipo amene angaŵaletse kubatizidwa ndi madzi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:24

Amene ali ake a Khristu Yesu, adalipachika pa mtanda khalidwe lao lokonda zoipa, pamodzi ndi zokhumba zake ndi zilakolako zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:7

Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:7

Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:5-6

Okhulupirira aja atamva zimenezi, adabatizidwa m'dzina la Ambuye Yesu. Pamene Paulo adaŵasanjika manja, Mzimu Woyera adadza pa iwo, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zosadziŵika, ndi kumalalika mau ochokera kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:11

Enanu munali otere kale, koma mudayeretsedwa, mudasanduka anthu a Mulungu, ndipo mudapezeka olungama pamaso pake. Zimenezi zidachitika m'dzina la Ambuye Yesu Khristu, ndiponso mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:17

Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:9

Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lopendekera ku zoipa. Mumalamulidwa ndi Mzimu Woyera, ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu sali wake wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:15

Iye ndi a m'banja mwake atabatizidwa, iyeyo adatipempha kuti, “Ngati mwandiwonadi kuti ndine munthu wokhulupirira Ambuye, dzaloŵeni m'nyumba mwanga, mudzakhale nafe.” Mwakuti adatikakamiza ndithu, ife nkukaloŵadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:50

Chimene chimandisangalatsa m'masautso anga nchakuti malonjezo anu amandipatsa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:25

Ngati Mzimu Woyera adatipatsa moyo, tilolenso kuti Mzimu yemweyo azititsogolera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:23

Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:36-38

“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-14

Nchifukwa chake musalole uchimo kuti ulamulire matupi anu otha kufaŵa, ndipo musagonjere zilakolako zake. Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo. Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 5:17

Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:14

Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:106

Ndalumbirira, ndipo ndatsimikiza kuti ndidzamvera malangizo anu olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:19

Yesu adaŵauza kuti, “Inu, munditsate, ndikakusandutseni asodzi a anthu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:13-14

Inu kale munali akufa chifukwa cha machimo anu, ndiponso chifukwa munali osaumbalidwa mu mtima. Koma tsopano Mulungu wakupatsani moyo pamodzi ndi Khristu. Adatikhululukira machimo athu zonse. Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:12

Koma pamene Filipo ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu, ndiponso za dzina la Yesu Khristu, anthu adakhulupirira, ndipo adabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:15

Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:15

Kuumbalidwa si kanthu, kusaumbalidwa si kanthunso, chachikulu nchakuti Mulungu apatse munthu moyo watsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:27

Chauta ndi Mulungu, ndipo watipatsa kuŵala. Yambani mdipiti wachikondwerero mutatenga nthambi, mpaka kukafika ku guwa lansembe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:8-9

Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:41-42

Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao. Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:22

Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:3

Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:44

Petro akulankhulabe, Mzimu Woyera adaŵatsikira anthu onse amene ankamva mauwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:7

“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndinu Alfa ndi Omega! Atate, Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, ndinu woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi chimaliziro. Mulungu wokondedwa, munatiuza m'mawu anu kuti aliyense wokhulera mwa Mwana wanu Yesu ndi uthenga wanu abatizidwe. Chifukwa chake lero ndikupemphani kuti muvumbulutsire anthu anu osankhidwa kufunika ndi madalitso auzimu omwe amabwera chifukwa cha kubatizidwa. Yesu, ndinu chitsanzo chachikulu cha kumvera pobatizidwa mu mtsinje wa Yorodani. Ndi kumvera kwanu, titithandizeni kusintha ndi kukonzanso kudzera mwa Mzimu Woyera wanu m'batizo la madzi ndi malilime. Tsiku limenelo, munatipanga ana a Mulungu ndi olowa ufumu wanu. Tsiku limenelo, munatilandira monga mamembala a Mpingo kuti tikatenge uthenga wa chipulumutso ndi chiwombolo padziko lonse lapansi, kwa cholengedwa chilichonse. Mawu anu amati: “Nanga tsopano uchedwanji? Nyamuka, ubatizidwe, nutsitsidwe machimo ako, ndipo udzatchula dzina lake.” Ndipereka mitima ndi zilakolako za ana anu kwa Mzimu wanu wabwino, awapatse chikhulupiriro ndi chilakolako chochita malamulo anu m'miyoyo yawo, kuti tiyende m'chikondi wina ndi mnzake monga momwe mawu anu amanenera. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa