Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo Okhudza Chilango ndi Kulangiza

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Chilango ndi Kulangiza

Mwana wa Mulungu, ndikufuna tikambirane za kulangizana mu mpingo. Ndikofunika kwambiri kuti tikule mwauzimu.

M’buku la Miyambi 3:11-12 (Baibulo Lopatulika), Mulungu amatiuza kuti, “Mwana wanga, usanyoze kulangizidwa ndi Yehova, Kapena kutopa ndi chidzudzulo chake; Pakuti Yehova amam’dzudzula iye amene amamukonda, Monga atate adzudzula mwana amene amamkondwera naye.” Apa tikumva kuti kulangizidwa ndi chizindikiro cha chikondi cha Mulungu kwa ife.

Nthaŵi zina zimakhala zovuta kulandiridwa, koma kumbukira kuti kudzikuza kungatilepheretse kuphunzira. Kulangizidwa kumatithandiza kukula mwauzimu, ngati mmene makolo athu amatithandizira.

Miyambi 15:32 imati, “Wonyoza malangizo adzanyoza moyo wakewake; koma wakumvera chidzudzulo adzapeza nzeru.” Ife amene sitilandira kulangizidwa, timatseka mwayi wophunzira ndi kukula mu nzeru za Mulungu.

Kulangizidwa si chilango, koma ndi njira yowongolera ndi kutitsogolera. Kumatikumbutsa kuti si ife angwiro ndipo pali zambiri zoti tiphunzire. Tikalangizidwa, timapeza mwayi wodziyesa tokha, kuvomereza zolakwa zathu, ndi kusintha.

Aheberi 12:11 imati, “Ndipo kulangizidwa konse panthaŵi yake sikumaoneka kukhala kwachisangalalo, koma kwachachabechabe; koma pambuyo pake kubalitsa chipatso cha mtendere wolungama kwa iwo amene aphunzitsidwa nako.” Choncho, tiyeni tione kulangizidwa ngati njira yophunzirira yomwe imatipatsa moyo wabwino ndi wolungama.




Ahebri 12:6

Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:11

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:13

Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:15

Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:11-12

Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:5-6

Mwaiŵala kodi mau olimbitsa mtima aja, amene Mulungu amakulankhulani ngati ana ake? Mauwo ndi aŵa: “Mwana wanga, usanyozere malango a Ambuye, kapena kutaya mtima pamene Iwo akudzudzula. Paja Ambuye amamlanga aliyense amene amamkonda, amakwapula mwana aliyense amene Iwo amamlandira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:16

Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:20

Uzimvera malangizo ndi kuvomera mwambo, kuti ukhale ndi nzeru m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 10:24

Langizeni, Inu Chauta, koma mwachilungamo. Musandikwiyire kuti mungandiwononge.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:12

Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:17

Uzimlanga mwana wako ndipo adzakupatsa mtendere mu mtima, adzakondweretsa mtima wako m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:12

Inu Chauta, ngwodala munthu amene mumamlangiza, amene mumamphunzitsa ndi malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:15

Kupusa kumakhala mumtima mwa mwana, koma ndodo yomlangira mwanayo idzachotsa kupusako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:10

Munthu woyambitsa mipatuko, utamdzudzula kaŵiri konse, usakhale nayenso nkanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 5:17

“Ndi wodala munthu amene Mulungu amamdzudzula. Nchifukwa chake usamanyoze chilango cha Mphambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:10-11

Azibambo athu apansipanowo ankatilanga pa kanthaŵi kochepa kokha, akazindikira kuti nkofunika. Koma Mulungu amatilanga kuti tipindulepo, ndipo tilandireko kuyera mtima kwake. Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 6:1

Abale, wina akagwa m'tchimo lililonse, inu amene Mzimu Woyera amakutsogolerani, mumthandize munthuyo ndi mtima wofatsa kuti akonzekenso. Koma mukhale maso kuti inu nomwe mungayesedwe ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 141:5

Munthu wolungama angathe kundimenya kapena kundidzudzula chifukwa andimvera chifundo, koma ndisalandire ulemu kwa anthu oipa, pakuti ndimapemphera motsutsana ndi ntchito zao zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:11

Pamene munthu akulandira chilango, kwa iye chilangocho chimaoneka ngati chinthu chomvetsa chisoni, ndi chosakondweretsa. Koma anthu amene adaleredwa mwa njira imeneyi, pambuyo pake amapata mtendere umene uli chipatso cha moyo wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:10

Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa. Amene amadana ndi kudzudzula adzafa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:5

Chitsiru chimanyoza malangizo a bambo wake, koma wochenjera amamvera chidzudzulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:14

Abale, tikukupemphani kuti anthu amene amangokhala osafuna kugwira ntchito muziŵadzudzula, anthu otaya mtima muziŵalimbikitsa. Anthu ofooka muziŵathandiza, anthu onsewo muziŵalezera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:17

Wosamala malangizo amayenda pa njira ya moyo, koma wokana chidzudzulo amasokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:14

Abale anga, ine mwini wake sindikayika konse kuti ndinu anthu a kufuna kwabwino ndithu, ndinu anthu odziŵa zinthu, ndipo mumatha kulangizana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:3

Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:8-9

Wonyoza usamdzudzule, angadane nawe. Koma ukadzudzula munthu wanzeru, adzakukonda. Wanzeru ukamlangiza, adzakhala wanzeru koposa. Munthu wochita chilungamo ukamuphunzitsa, adzadziŵa zambiri koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:23

Paja malamulowo ali ngati nyale, maphunzitsowo ali ngati kuŵala, madzudzulo a mwambo aja ndiwo mkhalidwe weniweni pa moyo wa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:1

Munthu wokonda mwambo amakonda kudziŵa zinthu, koma wodana ndi chidzudzulo ngwopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:32

Munthu wonyoza malangizo amangodzinyoza yekha, koma wovomera kudzudzula amapindula nzeru yomvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:71

Ndi bwino kuti ndidalangidwa, kuti ndiphunzire malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:1-2

Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:15

Mkwapulo ndi chidzudzulo zimapatsa nzeru, koma mwana womamlekerera amachititsa amake manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 8:33

Muzimva malangizo, kuti muzikhala anzeru, musamanyozere mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:19

Onse amene ndimaŵakonda, ndimaŵadzudzula ndi kuŵalanga motero. Tsono chitani khama, mutembenuke mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:24

Amene sakwapula mwana wake, ndiye kuti samkonda, koma amene amakonda mwana wake, sazengereza kumlanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 11:2

Popeza kuti si ana anu, koma ndinu amene mudazidziŵa ndi kuziwona zakale zonsezo, mukumbukire za Chauta, Mulungu wanu. Ukulu wake mudauwona, mudaonanso dzanja lake lamphamvu ndi mkono wake wotambalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:23

Musamale kudzudzula kwangaku, ine ndikuuzani maganizo anga, ndi kukudziŵitsani mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 11:32

Koma Ambuye amatilanga, kuti tiphunzirepo nzeru, kuwopa kuti tingaimbidwe mlandu pamodzi ndi anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:30

popeza kuti simudasamale malangizo anga, ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:25

Uphungu wanga simudaulabadire, kudzudzula kwanga simudakusamale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:6

Mwana muzimuphunzitsa njira yoti aziyendamo, ndipo atakalamba sadzachokamo m'njira imeneyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:12

Pamenepo iwe udzangoti, “Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo, mtima wanga unkanyoza chidzudzulo!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:67

Ndisanayambe kulangika ndinkasokera, koma tsopano ndimamvera mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:5-6

Kudzudzula munthu poyera nkwabwino kupambana kubisa chikondi chimene uli nacho. Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:4

Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:19

Munthu wotumikira samulanga ndi mau chabe, ngakhale aŵamvetse mauwo, sadzasamalako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 39:11

Inu mumalanga munthu pakumdzudzula chifukwa cha uchimo wake. Mumaonongeratu zimene iye amazikonda, monga m'mene chimachitira chifukufuku. Zoonadi, munthu aliyense ndi mpweya chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:3-4

Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke. “Tsiku limenelo, amene ali pa denga, asadzatsike kukatenga katundu wake m'nyumba. Chimodzimodzinso amene ali ku munda, asadzabwerere ku nyumba. Kumbukirani za mkazi wa Loti. Aliyense woyesa kudzisungira moyo wake, adzautaya, koma woutaya adzausunga. Kunena zoona, usiku umenewo, padzakhala anthu aŵiri pa bedi limodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja pamodzi, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya, Anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya.” Apo ophunzira ake adamufunsa kuti, “Kodi zimenezi zidzachitikira kuti, Ambuye?” Yesu adati, “Kumene kwafera chinthu, nkumeneko kumasonkhana miphamba.” Akakuchimwira kasanunkaŵiri pa tsiku, nabwera kasanunkaŵiri kudzanena kuti, ‘Pepani,’ umkhululukire ndithu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:1

Mwana wanzeru amamvera malangizo a atate ake, koma wonyoza samvetsera akamamdzudzula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:13-14

Usamaleka kumpatsa mwambo mwana, ukamkwapula ndi tsatsa sadzafa. Ngati umkwapula ndi tsatsa, udzapulumutsa moyo wake ku imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:7

Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru. Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:12-13

Nanga kuweruza anthu amene adakali kunja, ndi ntchito yanga ngati? Si koma amene ali mu mpingo ndiwo muyenera kuŵaweruza? Ndi Mulungu amene amaweruza anthu akunjawo. Paja mau a Mulungu akuti, “Munthu woipayo mumchotse pakati panu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:12

Kwa munthu womvetsera bwino, kudzudzula kuli ngati mphete yagolide, kapena chokongoletsera china chagolide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:75

Inu Chauta, ndikudziŵa kuti kuweruza kwanu nkolungama, ndipo mwandilanga potsata kukhulupirika kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:30

Mikwingwirima ndiye mankhwala ochotsa zoipa. Mikwapulo imachiza zam'katikati mwa munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:24-25

Amene amauza munthu woipa kuti, “Ndiwe wosalakwa,” anthu adzamtemberera, ndipo mitundu ya anthu idzaipidwa naye. Koma aweruzi amene amalanga anthu oipa adzapeza bwino, ndipo adzakhala ndi madalitso ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 9:7

Woyesa kukonza munthu wonyoza, amangonyozekerapo, wodzudzula munthu woipa, amangopwetekerapo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:10

Munthu wanzeru amamva kamodzi, munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:5

Kuli bwino kuti munthu azimva kudzudzula kwa anthu anzeru, kupambana kumvera nyimbo zotamanda za zitsiru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:7-8

Muzipirira masautso kuti muphunzirepo makhalidwe oyenera. Mulungu amakutengani ngati ana ake m'zochita zake zonse. Kodi nkale lonse analipo mwana amene bambo wake sadamlange? Ngati Mulungu sakulangani inuyo, monga amachitira ndi ana ake onse, ndiye kuti sindinu ana enieni, koma am'chigololo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:5

Inunso anyamata, muzimvera akulu. Ndipo nonsenu, khalani okonzeka kutumikirana modzichepetsa. Paja mau a Mulungu akuti. “Mulungu amatsutsa odzikuza, koma amaŵakomera mtima anthu odzichepetsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:18

Uzimlanga mwana wako chikhulupiriro chikadalipo, ukapanda kutero, wamuwononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:9

Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:15-17

“Mbale wako akakuchimwira, pita ukamdzudzule muli aŵiri nokha. Akakumvera, wamkonza mbale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, utengerepo wina mmodzi kapena ena aŵiri, kuti mau onse akatsimikizike ndi mboni ziŵiri kapena zitatu. Akapanda kuŵamvera iwowo, ukauze Mpingo. Ndipo akapanda kumveranso ndi Mpingo womwe, umuyese munthu wakunja kapena wokhometsa msonkho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:19-20

Abale anga, wina mwa inu akasokera pa kusiya choona, mnzake nkumubweza, Chuma chanu chaola, ndipo njenjete zadya zovala zanu. dziŵani kuti amene adzabweza munthu wochimwa ku njira yake yosokera, adzapulumutsa moyo wa munthuyo ku imfa, ndipo chifukwa cha iye machimo ochuluka adzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:15

Kwenikwenitu pakulankhula zoona ndi mtima wachikondi, tizikula pa zonse mwa Khristu. Iye ndiye mutu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:17

Muzimvera atsogoleri anu ndi kuŵagonjera. Iwo sapumulira konse poyang'anira moyo wanu, pakuti adzayenera kufotokoza za ntchito yao pamaso pa Mulungu. Mukaŵamvera, adzagwira ntchito yaoyo mokondwa osati monyinyirika, kupanda kutero ndiye kuti kwa inuyo phindu palibe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:15

Koma musamuwone ngati mdani. Makamaka mumchenjeze ngati mbale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:23

Amene amadzudzula mnzake, potsiriza pake mnzakeyo adzamkonda kwambiri kupambana amene ali ndi mau oshashalika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:20

Opitirirabe kuchimwa uziŵadzudzula pamaso pa onse, kuti ena onsewo achite mantha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:42

Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Mbale wanga, taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene iweyo sukuchiwona chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:14

Kumene kulibe uphungu, anthu amagwa, koma kumene kuli aphungu ambiri, kumakhala mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:8-9

Chauta ndi wabwino ndi wolungama. Nchifukwa chake amaphunzitsa ochimwa njira zake. Amatsogolera anthu odzichepetsa kuti achite zolungama, amaŵaphunzitsa njira zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:13

Uŵasamale zedi, pakuti moyo wako wagona pamenepo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:18

Umphaŵi ndi manyazi zimagwera wonyozera mwambo, koma munthu womvera chidzudzulo amalemekezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:18-19

Chauta akunena kuti, “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu: chifukwa cha machimo anu mwafiira kwambiri, koma Ine ndidzakutsukani, inu nkukhala oyera kuti mbee. Mwachita kuti psuu ngati magazi, koma mudzakhala oyera ngati thonje. Ngati muli okonzeka kundimvera, mudzalidyera dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:25

Ukamenya munthu wonyoza anzake, adzachenjererapo. Ukadzudzula munthu womvetsa bwino zinthu, adzapindulapo nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:11

Koma pamene Petro adafika ku Antiokeya, ndidamtsutsa poyera, chifukwa adaapezeka wolakwadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:26

Munthu wabwino amene amagonjera munthu woipa amafanafana ndi kasupe wodzaza ndi matope kapena chitsime cha madzi oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 30:21

Pamene mupatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva kumbuyo kwanu mau okulozerani njira oti, “Njira ndi iyi, muyende m'menemu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:11

Ngakhale mwana yemwe amadziŵika ndi ntchito zake, kuti zimene amachitazo ndi zabwino ndi zolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 3:12-14

Sindikunena kuti ndafikapo kale pa zimenezi, kapena kuti ndine wangwiro kale. Koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuzipata pakuti ndicho chinali cholinga cha Yesu Khristu pakundikopa kuti ndikhale wake. Abale, sindikuganiza konse kuti ndazipata kale. Koma pali chimodzi chokha chimene ndimachita: ndimaiŵala zakumbuyo, ndi kuyesetsa kufikira ku zakutsogolo. Ndikuthamangira ku mapeto a mpikisano wa liŵirowu, kuti ndikalandire mphotho Kumwamba, imene Mulungu akutiitanira kudzera mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:25-26

Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona. Pamenepo nzeru zao zidzabweramo, ndipo adzapulumuka mu msampha wa Satana, amene adaaŵagwira kuti azichita zofuna zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:8-9

Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira. “Musakhale opanda nzeru ngati kavalo kapena bulu amene ayenera kumuwongolera ndi chitsulo cham'kamwa ndi chapamutu, chifukwa ukapanda kutero, nyamazo sizidzakumvera.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 5:12-14

Pamenepo iwe udzangoti, “Kalanga ine, ndinkadana nkusunga mwambo, mtima wanga unkanyoza chidzudzulo! Sindidamvere mau a aphunzitsi anga, sindidatchere khutu kwa alangizi anga. Pang'onong'ono, bwenzi nditaonongekeratu pakati pa mpingo wonse utasonkhana.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:2

Iwo amadula nthambi iliyonse mwa Ine imene siibala zipatso. Ndipo nthambi iliyonse yobala zipatso, amaitengulira kuti ibale zipatso zambiri koposa kale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:17-18

Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata. Ukadamvera malamulo anga, bwenzi mtendere ukukufikira ngati madzi amumtsinje, ndipo bwenzi chilungamo chikukuphimba kosalekeza ngati mafunde apanyanja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:12

Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu, mulimbitse mwa ine mtima womvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:47-48

“Wantchito amene akudziŵa zimene mbuye wake amafuna, koma osakonzekera kuzichita, adzamkwapula kwambiri. Koma wantchito amene sadziŵa zimene mbuye wake amafuna, tsono nkumachita zoyenera kumlanga nazo, adzamkwapula pang'ono. Aliyense amene adalandira zambiri, adzayenera kubweza zambiri. Ndipo amene adamsungiza zambiri, adzamlamula kuti abweze zochuluka koposa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:27

Si kwabwino kudya uchi wambiri, tsono muchenjere nawo mau oyamikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:11

Pamene ine ndinali mwana, ndinkalankhula mwachibwana, ndinkaganiza mwachibwana ndipo zinthu ndinkazitengera chibwana. Koma nditakula, ndidazileka zachibwanazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 15:22

Koma Samuele adati, “Kodi Chauta amakondwa ndi chiti: nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kapena kumvera mau ake? Ndithu, ndi kumvera ndi kupereka nsembe kwabwino kwambiri nkumvera. Ndi kutchera khutu ndi kupereka mafuta ankhosa kwabwino kwambiri nkutchera khutu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:8-9

Chauta akunena kuti, “Maganizo anga ndi maganizo anu si amodzimodzi, ndipo zochita zanga ndi zochita zanu si zimodzimodzi. Monga momwe mlengalenga uliri kutali ndi dziko lapansi, momwemonso zochita zanga nzolekana kutali ndi zochita zanu, ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:5

Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake, ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:12

Mtima wako ukhale pa malangizo, ndipo makutu ako azimvetsera mau anzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:10

Kodi wolangiza mitundu ya anthu, sangathe kulanga? Kodi wophunzitsa anthu onse, alibe nzeru?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:3-5

Umaoneranji kachitsotso kamene kali m'maso mwa mnzako, koma osaganizako za chimtengo chimene chili m'maso mwako momwe? Ungamuuze bwanji mbale wako kuti, ‘Taima ntakuchotsa kachitsotso kali m'maso mwakoka,’ pamene m'maso mwako momwe muli chimtengo? Iwe wachiphamaso, yamba wachotsa chimtengo m'maso mwako, pamenepo ndiye udzatha kupenya bwino nkukachotsa kachitsotso kamene kali m'maso mwa mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:10

Chipongwe cha osasamala za anzao chimadzetsa mkangano, koma omvera malangizo a anzao ndiwo ali ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:24-25

Ndipo mtumiki wa Ambuye asamakhala wokanganakangana ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa onse, mphunzitsi wokhoza, munthu wodziŵa kupirira mavuto. Akhale wofatsa polangiza otsutsana naye. Mwina Mulungu angaŵapatse mwai woti atembenuke ndi kuzindikira choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:26

Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 13:5

Muzidziyesa nokha inuyo kuti mutsimikize ngati mukusungadi chikhulupiriro chanu. Muzidzifunsitsa nokha. Simudziŵa nanga kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Ngati si choncho, mwalephereratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:5-6

Tsono muyesetse kuchita khama kuwonjezera makhalidwe abwino pa chikhulupiriro chanu, ndi nzeru zoona pa makhalidwe anu abwinowo. Muwonjezerepo kudziletsa pa nzeru zoonazo, kulimbika pa kudziletsa kwanu, ndiponso kupembedza Mulungu pa kulimbika kwanuko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:133

Chirikizani mayendedwe anga molingana ndi mau anu aja, musalole kuti tchimo lililonse lizindilamulira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga wokondedwa, ndikutamanda dzina lanu lalikulu ndi ulemerero wanu. Ndinu woyenera kulemekezedwa ndi kupembedzedwa, ngakhale ndili ndi zolakwa zanga. Mwakhala wabwino kwambiri kwa ine, mundizinga ndi chifundo ndi chikondi chanu, mumandipatsa ubwino ndi chisomo chanu. Mtima wanga wadzaza ndi chiyamikiro pa zonse zimene mumandithandiza, chifukwa cha kuleza mtima kwanu ndi chifukwa cha kundigwira ndi dzanja lanu lamphamvu ngakhale kusamvera kwanga ndi kuipa kwanga konse. Inu Mulungu, ndikupemphani kuti ndi nzeru zanu zopanda malire ndi kuleza mtima, mundikonze zolakwa zanga. Mundilole kuzindikira zofooka zanga ndi kuphunzirapo, ndi kuyenda monga mwa chifuniro chanu. Ndikudziwa zolakwa zanga, tsiku lililonse ndikufunika kukonzedwa kwanu kuti ndikhale moyenera pamaso panu. Ndithandizeni kukhala munthu wolungama, wokhoza kukonza zochita zanga ndi kukhala bwino nthawi zonse. Munditsogolere panjira yolungama ndi mundipatse mphamvu zolandira ziphunzitso zanu ndi kudzikonza ndekha. Choonadi chanu chitsogolere njira yanga ndi kundithandiza kuzindikira zolakwa zanga. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa