Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


117 Mau a Mulungu Pa Zizindikiro za Masiku Otsiriza

117 Mau a Mulungu Pa Zizindikiro za Masiku Otsiriza

Baibulo limatiuza za zinthu zambiri zimene zidzachitika nthawi ya Chisautso Chachikulu isanafike. Tikumva za nkhondo, mphekesera za nkhondo, zivomezi, njala, matenda, ndi kuzunzidwa kwa okhulupirira. Ndikofunika kwambiri kuti titenge zimenezi ngati chenjezo loti tilimbitse ubwenzi wathu ndi Mulungu ndikukhala moyo wotsatira malangizo ake.

Tiyeni tiganizire za chikhulupiriro chathu. Kodi ndife okonzeka kukumana ndi mavuto aliwonse amene angabwere? Pakati pa mavuto onsewa, ntchito yathu yaikulu monga okhulupirira ndi kukonda Mulungu ndi kukonda anzathu, kuwauza uthenga wabwino wa chipulumutso amene sadaudzidwa.

Zizindikiro za Chisautso Chachikulu zimatipatsa mpata woganizira za kufunika kokhala moyo wabwino tsiku lililonse ngati kuti ndi lomaliza, kukonda Mulungu ndi anzathu. Sitingathe kukhala ndi nkhawa kwambiri ndi zam'tsogolo, koma tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse ndipo tiyenera kutsatira malangizo ake pa chilichonse chimene timachita.

Mwachidule, zizindikiro za Chisautso Chachikulu zimatilimbikitsa kuti tiganizire za moyo wathu wauzimu ndi kukonzekera nthawi zonse, kutsatira malamulo ndi mawu a Mulungu. Zimatipatsa mpata woti tikumbukire kufunika kokhala moyo wotsatira mfundo ndi ziphunzitso za m'Baibulo. Monga okhulupirira, tiyenera kukhulupirira kuti Mulungu ali nafe nthawi zonse za mavuto ndipo chikondi chake ndi chitetezo chake zidzatithandiza pa ulendo wathu wonse.




Mateyu 24:27

Mwana wa Munthutu kubwera kwake kudzakhala monga muja mphezi imang'animira ndi kuŵala kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:5

Anthu ena ankalankhula za Nyumba ya Mulungu kuti adaikongoletsa ndi miyala yokoma, ndiponso ndi mitulo yopereka kwa Mulungu. Yesu adati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:6-7

Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai. Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:11

Kudzachita zivomezi zazikulu. Kudzakhala njala ndi mliri ku malo osiyanasiyana. Kudzakhalanso zoopsa ndi zizindikiro zodabwitsa mu mlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:33

Momwemonso, mukadzaona zonse ndanena zija, mudzadziŵe kuti Mwana wa Munthu ali pafupi, ali pakhomo penipeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:1

Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:29-31

“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka. Tsono Yesu atakhala pansi, pa Phiri la Olivi, ophunzira ake adadza kwa Iye paokha. Adamufunsa kuti, “Tatiwuzani, zimenezi zidzachitika liti? Tidzaonera chiyani kuti nthaŵi yakwana ya kubweranso kwanu, ndiponso ya kutha kwa dziko lapansi?” Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Kudzamveka lipenga lamphamvu, ndipo Iye adzatuma angelo ake, kuti akasonkhanitse osankhidwa ake kuchokera ku mbali zonse, kuyambira ku malekezero ena a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:19

chifukwa masautso amene adzaoneke masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:21

Chifukwa masautso amene adzaoneka masiku amenewo, sanaonekepo chilengedwere dziko lapansi mpaka pano, ndipo sadzaonekanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:8

Tsono zonsezitu nkuyamba chabe kwa mavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:14

Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:12-17

Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho. Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake. Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri. Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo. Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:16-17

Chinkakakamiza anthu onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu, olemera ndi osauka, mfulu ndi akapolo, kuti alembedwe chizindikiro pa dzanja lamanja kapena pa mphumi. Chinkachita zimenezi kuti wina aliyense asaloledwe kugula kapena kugulitsa kanthu ngati alibe chizindikiro chimenechi, ndiye kuti dzina la chilombo choyamba chija, kapena nambala yotanthauza dzina lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:23

“Pa nthaŵi imeneyo wina akadzakuuzani kuti, ‘Ali panotu Khristu uja! Uyo ali apoyo!’ musadzakhulupirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:3-4

Musalole kuti wina akupusitseni mwa njira iliyonse. Pajatu lisanafike tsikulo, kudzayamba kwachitika zoti anthu ochuluka akupandukira Mulungu, ndipo kudzaoneka Munthu Woipitsitsa uja, woyenera kutayikayu. Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:3

Ndipo m'maŵa mumati, ‘Lero ndiye kugwa mvula yamkuntho, popeza kuti kumwambaku kwachita mitambo yabii.’ Mumatha kutanthauzira m'mene kukuwonekera kumwambaku, koma osatha kutanthauzira zizindikiro za nthaŵi zino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:37

Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 9:6

Masiku amenewo anthuwo adzafunafuna imfa, koma osaipeza. Adzafunitsitsa kufa, koma imfa izidzaŵathaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:7

Mitundu yosiyanasiyana idzaukirana, maiko osiyanasiyana adzamenyana nkhondo. Kudzakhala njala, ndipo kudzachita zivomezi ku malo osiyanasiyana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:10

Pa nthaŵi imeneyo ambiri adzataya chikhulupiriro chao, azidzaperekana nkumadana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:10

Popeza kuti mwasunga mau anga oti mupirire mosatepatepa, Inenso ndidzakusungani pa nthaŵi yamayeso imene ilikudza m'dziko lonse lapansi, kuti anthu onse okhalamo adzayesedwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:6

Mudzamva phokoso la nkhondo za kufupi kuno ndi mphekesera za nkhondo zakutali. Ndiye inu musadzade nkhaŵa. Zimenezi zidzayenera kuchitika, koma sindiye kuti chimalizo chija chafika kale ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:29

“Akadzangotha mavuto a masiku amenewo, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala, nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:1-2

Pambuyo pake ndidamva mau amphamvu ochokera m'Malo Opatulika aja. Adauza angelo asanu ndi aŵiri aja kuti, “Pitani, kathireni pa dziko lapansi ukali wa Mulungu, umene uli m'mikhate isanu ndi iŵiri ija.” Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva. Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao. Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chimodzi adakhuthulira za mumkhate mwake pa mtsinje waukulu uja wa Yufurate. Pomwepo madzi ake adaphwa, kuti pakhale njira yodzera mafumu ochokera kuvuma. Kenaka ndidaona mizimu yonyansa itatu, yonga achule, ikutuluka wina m'kamwa mwa chinjoka chija, wina m'kamwa mwa chilombo chija, wina m'kamwa mwa mneneri wonama uja. Imeneyi ndi ija timati mizimu yoipa imene imachita zozizwitsa. Imapita ponseponse kwa mafumu a pa dziko lapansi kukaŵaitana kuti adzabwere ku nkhondo ya pa tsiku lalikulu lija la Mulungu Mphambe. “Mvetsetsani! Ndikubwera ngati mbala. Ngwodala munthu amene ali maso, nasunga zovala zake, kuwopa kuti angamayende osavala, ndipo anthu angaone maliseche ake.” Pamenepo mizimu ija idasonkhanitsa mafumu aja ku malo amene pa Chihebri amatchedwa “Armagedoni.” Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!” Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi. Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali. Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:19

Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:1-5

Udziŵe kuti pa masiku otsiriza kudzafika nthaŵi ya zovuta. Tsono iwe wakhala ukunditsatira m'zophunzitsa zanga, mayendedwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, kupirira kwanga, mazunzo anga, ndi masautso anga, monga amene adaandigwera ku Antiokeya, ku Ikonio ndi ku Listara. Ndidaazunzikadi koopsa! Koma Ambuye adandipulumutsa pa zonsezi. Onse ofuna kukhala ndi moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, m'menemo anthu ochimwa ndi onyenga, adzanka naipiraipira, ndipo azidzanyenga ena nkumanyengedwanso iwo omwe. Koma iwe, limbika pa zimene waphunzira ndipo wadziŵa kuti nzoona, paja ukuŵadziŵa amene adakuphunzitsa. Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse. Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, onyada, odzikuza, onyoza Mulungu, osamvera anakubala ao, osayamika, ndi oipitsa zinthu za Mulungu. Adzakhala opanda chifundo, osapepeseka, ndi osinjirira anzao. Adzakhala osadzigwira, aukali, odana ndi zabwino, opereka anzao kwa adani ao. Adzakhala osaopa chilichonse, odzitukumula, okonda zosangalatsa m'malo mokonda Mulungu. Adzasamala maonekedwe ake okha a chipembedzo, nkumakana mphamvu zake. Anthu otere uziŵalewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:34

Ndithu ndikunenetsa kuti zonsezi zidzaoneka anthu a mbadwo unoŵa asanamwalire onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:3

Ndidzatuma mboni zanga ziŵiri zovala chiguduli, kuwonetsa chisoni, kuti zidzalalike mau ochokera kwa Mulungu pa masiku 1,260.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:5

Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:3

Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:25-26

“Padzakhala zizindikiro zodabwitsa pa dzuŵa, pa mwezi ndi pa nyenyezi. Pansi pano anthu a mitundu yonse adzada nkhaŵa nkutha nzeru, pomva kukokoma kwa nyanja ndi mafunde ake. Ena adzakomoka ndi mantha poyembekezera zimene zikudza pa dziko lonse lapansi, pakuti mphamvu zonse zakuthambo zidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:18

Ananu, ino ndi nthaŵi yotsiriza. Mudamva kuti kukubwera Woukira Khristu, ndipo tsopano aoneka kale ambiri oukira Khristu. Zimenezi zikutizindikiritsa kuti ino ndi nthaŵi yotsirizadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:24

Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:18-23

Pa nthaŵi imeneyo, pamene Gogi adzabwera kudzalimbana ndi dziko la Israele, mkwiyo wanga udzayaka zedi. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo, ndikulumbira kuti kudzachita chivomezi chachikulu m'dziko lonse la Israele. “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Gogi, wa ku dziko la Magogi, kalonga wamkulu wa mzinda wa Meseki ndi wa Tubala, ndipo umuimbe mlandu. Nsomba za m'nyanja ndi mbalame zamumlengalenga, nyama zakuthengo ndi zokwaŵa zonse, pamodzi ndi anthu onse okhala pa dziko lapansi, zonsezo zidzanjenjemera ndi mantha. Mapiri adzaphwanyika, magomo adzanyenyeka, ndipo makoma onse adzagwa pansi. Gogi ndidzamuutsira nkhondo kuchokera ku mapiri anga onse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. Ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ndi matalala ndiponso sulufure ndi miyala yamoto pa iye, pa magulu ake ankhondo ndiponso pa mitundu yonse ya anthu omperekeza. Umu ndimo m'mene ndidzaonetsere kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Choncho ndidzadziŵika kwa anthu a mitundu yonse. Tsono adzadziŵadi kuti Ine ndine Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:21

Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:30-31

“Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka magazi, tsiku lalikulu ndi loopsa la Chauta lisanafike.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zefaniya 1:15-18

Tsikulo lidzakhala tsiku la mkwiyo wa Chauta, tsiku la mavuto ndi mazunzo, tsiku la kuwonongeka ndi kupasuka kwa zinthu, tsiku la mdima ndi chisoni, tsiku la mitambo ndi labii kuda. Tsiku limenelo kudzamveka lipenga ndi kufuula kwankhondo, kwa asilikali othira nkhondo mizinda ya malinga ndiponso nsanja zankhondo za Yerusalemu. Chauta akuti, “Chifukwa anthuwo adandichimwira, ndidzaŵasautsa koopsa, kotero kuti azidzayenda ngati akhungu. Magazi ao adzachita kuti mwaa ngati fumbi, matupi adzangoti vuu, nkumaola ngati ndoŵe. Ngakhale siliva wao kapena golide wao sadzatha kuŵaombola, tsiku la mkwiyo wa Chautalo. Ukali wake wotentha ngati moto, udzapsereza dziko lonse, ndipo mwadzidzidzi adzathetsa onse okhala m'menemo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 2:30

“Mu mlengalenga ndi pa dziko lapansi ndidzaonetsa zodabwitsa izi: magazi, moto ndi utsi watoloo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:22

Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 3:10

Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikulo zakumwamba zidzatha ndi phokoso loopsa. Zinthu zonse zidzayaka moto nkusungunuka, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili m'menemo zidzapseratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:13

Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:12

Choncho kondwerani inu, Dziko la Kumwamba, ndi onse okhalamo. Koma muli ndi tsoka, inu dziko lapansi ndi nyanja, pakuti Satana adatsikira kwa inu, ali wokalipa kwambiri, chifukwa wadziŵa kuti yangomutsalira nthaŵi pang'ono.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:1-2

Pambuyo pake ndidaona Mwanawankhosa uja akumatula chimodzi mwa zimatiro zisanu ndi ziŵiri zija. Ndipo ndidamva chimodzi mwa Zamoyo zinai zija chikunena ndi liwu lomveka ngati bingu kuti, “Bwera!” Mizimuyo idafuula mokweza mau kuti, “Ambuye, Inu ndinu Mfumu yathu yoyera ndi yoona. Mudzaŵalekerera mpaka liti osaŵaimba mlandu ndi kuŵalanga anthu aja okhala pansi pano amene adatipha?” Apo aliyense adapatsidwa mkanjo woyera, ndipo adamva mau akuti, “Bapumulani pang'ono mpaka chitakwanira chiŵerengero chathunthu cha atumiki anzanu ndi abale anu, amene nawonso ayenera kuphedwa monga inu nomwe.” Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachisanu ndi chimodzi. Ndipo padachitika chivomezi champhamvu. Dzuŵa lidadzangoti bii ngati chiguduli chakuda, mwezi wathunthu nkungoti psuu ngati magazi. Nyenyezi zakuthambo zidagwa pansi, ngati muja zimayoyokera nkhuyu zaziŵisi, mkuyu ukamagwedezeka ndi mphepo yamkuntho. Thambo lidachoka monga momwe imakulungidwira mphasa akamaiyalula. Ndipo phiri lililonse ndi chilumba chilichonse zidachotsedwa m'malo mwake. Apo mafumu a dziko lapansi, atsogoleri a dziko, akulu a ankhondo, anthu olemera, anthu amphamvu, akapolo onse ndi mfulu zonse, onsewo adakabisala m'mapanga ndi m'matanthwe am'mapiri. Iwowo ankafuulira mapiri ndi matanthwewo kuti, “Tigwereni ndi kutivundikira, kuti wokhala pa mpando wachifumu uja angatiwone, ndipo kuti tipulumuke ku chilango cha Mwanawankhosayo. Lafikadi tsiku loopsa la mkwiyo wao, ndipo angathe kulimbapo ndani?” Nditayang'ana, ndidaona kavalo woyera. Wokwerapo wake anali ndi uta, ndipo adaapatsidwa chisoti chaufumu. Adatulukira ngati wogonjetsa kuchokera kumwamba, kuti akagonjetsenso ena pa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:3-4

Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachiŵiri. Ndipo ndidamva Chamoyo chachiŵiri chija chikunena kuti, “Bwera!” Pamenepo kavalo wina, wofiira, adatulukira. Wokwerapo wake adaalandira mphamvu zothira nkhondo pa dziko lapansi, kuti anthu aziphana. Choncho adampatsa lupanga lalikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:5-6

Pambuyo pake Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachitatu. Ndipo ndidamva Chamoyo chachitatu chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m'manja. Tsono ndidamva ngati liwu kuchokera pakati pa Zamoyo zinai zija. Lidati, “Nsengwa imodzi ya tirigu, mtengo wake ndi malipiro a tsiku limodzi. Ndipo nsengwa zitatu za barele, mtengo wake ndi womwewonso. Koma usaononge mitengo ya mafuta ndi ya mphesa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 6:7-8

Kenaka Mwanawankhosa uja adamatula chimatiro chachinai. Ndipo ndidamva Chamoyo chachinai chija chikunena kuti, “Bwera!” Nditayang'ana, ndidaona kavalo wotuŵa. Wokwerapo wake dzina lake anali Imfa, ndipo Malo a anthu akufa ankamutsata pambuyo. Aŵiriwo adaalandira ulamuliro pa chimodzi mwa zigawo zinai za dziko lapansi, kuti aphe anthu ndi nkhondo, njala, nthenda, ndi zilombo zolusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:10-11

Kenaka mngelo wachisanu adakhuthulira za mumkhate mwake pa mpando wachifumu wa chilombo chija. Nthaŵi yomweyo mdima udagwa ponse pamene panali ufumu wake. Anthu ankadziluma lilime chifukwa cha ululu umene ankaumva. Adayamba kunyoza dzina la Mulungu wa Kumwamba chifukwa cha zoŵaŵa zao ndi zilonda zao. Komabe sadatembenuke mtima ndi kuleka zochita zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:12

Tsono popeza kuti zoipa zizidzachulukirachulukira, chikondi chizidzacheperachepera pakati pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:34-36

“Chenjerani kuti mitima yanu ingapusitsidwe ndi maphwando, kuledzera, ndi kudera nkhaŵa za moyo uno, kuti tsikulo lingakufikireni modzidzimutsa. Pajatu lidzaŵagwera ngati msampha anthu onse okhala pa dziko lonse lapansi. Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 14:14-20

Pambuyo pake nditayang'ana ndidaona mtambo woyera. Pamtambopo padaakhala wina ngati Mwana wa Munthu, kumutu atavala chisoti chaufumu chagolide, m'manjamu ali ndi chikwakwa chakuthwa. Mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu nafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala pamtamboyu. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chako, yambapo kudula dzinthu. Tsopano nyengo yamasika yafika, ndipo dzinthu dza pa dziko lapansi dzidacha kale.” Pamenepo wokhala pamtambo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula dzinthu dzonse dza pa dziko lapansi. Pambuyo pake mngelo wina adatuluka m'Nyumba ya Mulungu Kumwamba. Nayenso anali ndi chikwakwa chakuthwa. Kenaka mngelo winanso, amene amalamulira moto, adatulukira kuchokera ku guwa lansembe. Adafuula ndi mau amphamvu kwa Uja wokhala ndi chikwakwa chakuthwa. Adati, “Gwiritsa ntchito chikwakwa chakocho, yambapo kudula mphesa za m'munda wamphesa wa pa dziko lapansi, pakuti mphesazo zidapsa kale.” Pamenepo mngelo uja adakayambadi ntchitoyo ndi chikwakwa chake, nadula mphesa zonse za pa dziko lapansi, nkuziponya m'chopondera mphesa cha ukali woopsa wa Mulungu. Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao. Mphesazo zidapondedwa m'chopondera mphesa kunja kwa mzinda. Ndipo m'chopondera mphesacho mudatuluka magazi nkumayenderera ngati mtsinje, kutalika kwake makilomita 300, kuzama kwake ngati mita ndi hafu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:3

Pamene anthu azikati, “Pali mtendere, tili pabwino”, pamenepo chiwonongeko chidzaŵagwera modzidzimutsa. Chidzaŵadzidzimutsa monga momwe zoŵaŵa zimamchitira mkazi pa nthaŵi yoti achire; ndipo sadzatha konse kuchizemba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:3-4

Paja nthaŵi idzafika pamene anthu azidzakana chiphunzitso choona. M'malo mwake, chifukwa cholakalaka kumva zoŵakomera zokha, adzadzisankhira aphunzitsi ochuluka omaŵauza zimene iwo akufuna. Adzafulatira choona, osafunanso kuchimva, ndipo adzangotsata nthano chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 8:11-12

Ambuye Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene ndidzagwetsa njala m'dzikomo. Siidzakhala njala ya buledi, kapena ludzu la madzi ai, koma njala yosoŵa mau a Chauta. Anthu azidzangoyenda uku ndi uku kuchoka ku nyanja ina kunka ku nyanja inanso, azidzangoti piringupiringu kuchoka chakumpoto kunka chakuvuma. Azidzafunafuna mau a Chauta, koma osaŵapeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:1-6

Zoona, Chauta adzaononga dziko lapansi ndi kulisandutsa chipululu. Adzalisakaza, nadzamwaza anthu ake onse. Mu mzinda wachisokonezo uja zonse zaonongedwa, nyumba iliyonse yatsekedwa, kotero kuti palibe wotha kuloŵamo. Anthu akufuula m'miseu chifukwa cha kusoŵa kwa vinyo. Chimwemwe chonse chatheratu, palibenso chisangalalo pa dziko lonse lapansi. Mzinda wasanduka bwinja, zipata zake zagumuka. Zimenezi ndizo zimene zidzachitikire mtundu uli wonse wa pa dziko lapansi. Kudzakhala ngati khunkha la olivi ndi khunkha la mphesa, pamene kholola latha. Koma otsala aja adzafuula ndi kuimba mokondwa. Akuzambwe adzatamanda ukulu wa Chauta. Nchifukwa chake inu akuvuma, tamandani Chauta. Anthu okhala m'mphepete mwa nyanja, yamikani Ambuye, Mulungu wa Israele. Kuchokera ku maiko akutali tilikumva nyimbo zotamanda, zoyamika Wolungama uja. Koma ine ndikuti: Ndatheratu, ndatheratu! Tsoka kwa ine! Onyenga akupitirizabe ndipo kunyenga kwao kukupitabe m'tsogolo. Inu anthu a dziko lapansi, zoopsa, mbuna ndi misampha zikukudikirani. Aliyense wothaŵa phokoso la zoopsazo adzagwa m'mbuna, ndipo wotuluka m'mbunamo adzakodwa mumsampha. Kudzagwa mvula yachigumula ndipo maziko onse a dziko adzagwedezeka. Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu. Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza. Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso. Tsiku limenelo Chauta adzalanga kumwamba zamphamvu zakumwamba, ndipo pansi pano mafumu a pansi pano. Mulungu adzasonkhanitsa mafumu onse pamodzi, ngati am'ndende amene ali m'dzenje. Adzaŵatsekera m'ndende, ndipo patapita nthaŵi yaitali, adzalangidwa. Mwezi udzanyala, ndipo dzuŵa lidzachita manyazi, pakuti Chauta Wamphamvuzonse adzakhala mfumu. Adzalamulira pa phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu, ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu. Dziko lapansi lidzaonongedwa kwathunthu, lidzasakazikiratu, pakuti Chauta wanena zimenezi. Dziko likulira ndipo likufota. Dziko lonse lapansi likuvutika ndipo likuuma. Mlengalenga ukuvutika pamodzi ndi dziko lapansi. Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo. Nchifukwa chake Mulungu watemberera dziko lapansi, anthu am'dzikomo akuzunzika chifukwa cha machimo ao. Iwo amalizika, ndipo atsala ndi oŵerengeka okha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 24:19-20

Dziko lapansi lidzathyokathyoka, lidzang'ambika kwathunthu ndi kugwedezeka kwamphamvu. Aliyense adzaona zimodzimodzi: ansembe ndi anthu, akapolo aamuna ndi ambuyao aamuna, adzakazi ndi ambuyao aakazi, ogula ndi ogulitsa, obwereka ndi oŵabwereka, ndiponso okongola ndi okongoza. Dziko lapansi lidzadzandira ngati munthu woledzera, lidzagwedezeka ngati chisimba nthaŵi ya mkuntho. Dziko lapansi lalemedwa ndi zoipa zake, lidzagwa ndipo silidzaukanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 30:3

Ndithudi layandikira, tsiku la Chauta lili pafupi. Tsiku lamitambo, tsiku la kutha kwa mitundu ya anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:17-21

Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adakhuthulira za mumkhate mwake mu mlengalenga. Pomwepo kudamveka mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu wa m'Nyumba ya Mulungu. Adati, “Kwatha!” Nthaŵi yomweyo kudachita mphezi, phokoso ndi mabingu. Kudachitanso chivomezi champhamvu. Chilengedwere cha anthu pa dziko lapansi sikudachitikeponso chivomezi chotero: chimenecho chinali choopsa zedi. Mzinda waukulu uja udagaŵika patatu, ndipo mizinda ya m'maiko ena onse idagwa. Mulungu adakumbukira Babiloni wamkulu uja, ndipo adamumwetsa chikho cha vinyo wa mkwiyo wake waukali. Motero mngelo woyamba adakakhuthulira za mumkhate mwake pa dziko lapansi. Pamenepo zilonda zonyansa ndi zopweteka zidabuka pa anthu onse aja, amene adaalembedwa chizindikiro cha chilombo chija, napembedza fano lake. Zilumba zonse zidafafanizika, mapiri osaonekanso. Matalala akuluakulu adagwa pa anthu kuchokera kumwamba. Lililonse kulemera kwake pafupi makilogaramu 45. Ndipo anthu adanyoza Mulungu chifukwa cha mliri wa matalalawo, pakuti mliriwo unali woopsadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 14:2-4

Chauta adzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti adzathire nkhondo Yerusalemu. Adzaulanda mzindawo ndi kuphwasula nyumba zonse, ndipo akazi am'menemo adzaŵachita chigololo. Theka la anthu a mu mzindawo lidzatengedwa ukapolo, koma ena onse otsala mumzindamo sadzachotsedwa. Pa tsiku limenelo pa mabelu ovala akavalo ankhondo padzalembedwa mau akuti, “Woperekedwa kwa Chauta.” Ndipo mbiya za ku Nyumba ya Chauta nazonso zidzakhala zoyera ngati mbale zakuguwa. Mbiya iliyonse ya ku Yerusalemu ndi ku Yuda idzakhala yoperekedwa kwa Chauta Wamphamvuzonse. Onse opereka nsembe ku Yerusalemu adzagwiritsa ntchito mbiyazo pophika nyama za nsembe. Nthaŵi imeneyo ikadzafika, sipadzaonekanso wamalonda aliyense m'Nyumba ya Chauta Wamphamvuzonse. Pambuyo pake Chauta adzabwera kudzamenyana ndi adani amenewo, monga m'mene amachitira pa tsiku la nkhondo. Tsiku limenelo adzaimirira pa phiri la Olivi loyang'anana ndi Yerusalemu chakuvuma, ndipo phirilo lidzagaŵika paŵiri ndi chigwa chachikulu choyenda kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe. Theka la phiri lidzasunthira chakumpoto, theka lina chakumwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:12-14

“Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija. Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija. Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:8

Nchifukwa chake miliri yomugwera idzamufikira pa tsiku limodzi. Miliriyo ndi iyi: nthenda, chisoni, ndi njala. Ndipo adzamtentha ndi moto. Pakuti ndi amphamvu Ambuye Mulungu amene amuweruza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:22

Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha Ine. Koma yemwe adzalimbikire mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:14

Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:22

Masiku amenewo, akadapanda kuŵachepetsa, sakadapulumukapo munthu ndi mmodzi yemwe. Koma Mulungu adzaŵachepetsa masikuwo chifukwa cha anthu amene Iye adaŵasankha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 17:26-30

“Monga momwe zidaachitikira pa nthaŵi ya Nowa, zidzateronso pa nthaŵi ya Mwana wa Munthu. Masiku amenewo anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kumakwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Pamenepo chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Monga momwe zidaachitikiranso pa nthaŵi ya Loti. Anthu ankangodya ndi kumwa, ankagulitsana malonda, ankabzala mbeu, ankamanga nyumba. Koma tsiku limene Loti adatuluka m'Sodomu, Mulungu adagwetsa moto ndi miyala yoyaka ya sulufule nkuŵaononga onsewo. Chenjerani tsono! “Mbale wako akachimwa, umdzudzule. Akatembenuka mtima, umkhululukire. Zidzateronso pa tsiku limene Mwana wa munthu adzaoneke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:37-39

Kudza kwa Mwana wa Munthu kudzakhala monga momwe zinthu zidaayendera pa nthaŵi ya Nowa. Masiku amenewo, chisanafike chigumula, anthu ankangodya ndi kumwa, ankakwatira ndi kukwatiwa, mpaka tsiku limene Nowa adaloŵa m'chombo. Sadazindikire kanthu mpaka chigumula chidafika nkuŵaononga onse. Zidzateronso pamene Mwana wa Munthu adzabwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:7

Chidaloledwa kuŵathira nkhondo anthu a Mulungu ndi kuŵagonjetsa. Chidapatsidwanso mphamvu zolamulira anthu a fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi a chilankhulo chilichonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:4

Pambuyo pake ndidaona mipando yachifumu, ndipo okhala pamipandopo adapatsidwa mphamvu zoweruzira milandu. Ndidaonanso mizimu ya anthu amene adaŵadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mau a Mulungu. Iwowo sadapembedze nao chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo adakana kulembedwa chizindikiro chija pa mphumi kapena pa dzanja. Adakhalanso ndi moyo nkumalamulira pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:12-13

Inu okondedwa, musazizwe ndi chimoto cha masautso chimene chakugwerani kuti muyesedwe nacho. Musaganize kuti zimene zakuwonekeranizo nzachilendo. Koma kondwerani popeza kuti mulikumva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, kuti podzaoneka ulemerero wake, mudzasangalale kwakukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 13:24-25

“Masiku amenewo, mavutowo atatha, dzuŵa lidzada, mwezi udzaleka kuŵala. Nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo, ndipo mphamvu zamumlengalenga zidzagwedezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:30

Pamenepo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka ku thambo. Anthu a mitundu yonse ya pansi pano adzayamba kulira, ndipo adzaona Mwana wa Munthu akubwera pa mitambo ali ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yoweli 3:15-16

Dzuŵa ndi mwezi zada, ndipo nyenyezi zaleka kuŵala. Chauta akukhuluma ku Ziyoni, mau ake amveka ngati bingu kuchokera ku Yerusalemu. Ndipo thambo ndi dziko lapansi zikugwedezeka. Koma Chauta ndiye pothaŵirapo anthu ake, ndiye linga lotetezera a ku Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:19-20

Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:28

Zimenezi zikadzayamba kuchitika, mudzaimirire nkukweza mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chayandikira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:11-16

Pambuyo pake ndidaona Kumwamba kutatsekuka, kavalo woyera nkuwoneka. Wokwerapo wake dzina lake ndi “Wokhulupirika”, ndiponso “Woona.” Poweruza, ndi pomenya nkhondo, amachita molungama. Maso ake anali psuu ngati malaŵi a moto, ndipo pamutu pake panali zisoti zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lolidziŵa iye yekha, osati wina aliyense. Chovala chake chinali choviika m'magazi, ndipo ankatchedwa, “Mau a Mulungu.” Magulu a ankhondo a Kumwamba ankamutsatira atakwera akavalo oyera, ndipo iwowo atavala zabafuta, zoyera ndi zangwiro. M'kamwa mwake munali lupanga lakuthwa lotulukira kunja, loti adzalangire mitundu ya anthu. Adzaŵalamulira ndi ndodo yachitsulo, ndipo m'chopondera mphesa adzaponda mphesa za vinyo wa mkwiyo waukali wa Mulungu Mphambe. Pa mkanjo wake, ndi pantchafu pake padaalembedwa dzina loti, “Mfumu ya mafumu onse, ndi Mbuye wa ambuye onse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:15-16

“Pajatu Chauta adzabwera ndi moto. Ndipo magaleta ake adzafika ngati mkuntho. Iye adzaonetsa poyera ukali wake, ndipo adzalanga adani ake ndi malaŵi a moto. Adzalanga anthu onse a pa dziko lapansi ndi moto ndi lupanga. Alipo ambiri amene Chauta adzaŵapha.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 14:12

Pambuyo pake Chauta adzalanga ndi mliri adani onse amene ankamenyana nkhondo ndi Yerusalemu. Matenda ake adzakhala motere: matupi ao adzaola eni ake akuyendabe, maso ao adzaola ali chikhalire m'malo mwake, ndipo malilime ao adzaola m'kamwa mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 38:22

Ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ndi matalala ndiponso sulufure ndi miyala yamoto pa iye, pa magulu ake ankhondo ndiponso pa mitundu yonse ya anthu omperekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:20-22

“Pamene mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, dziŵani kuti chiwonongeko chake chafika. Pamenepo amene ali m'Yudeya athaŵire ku mapiri, amene ali mumzinda atulukemo, ndipo amene ali ku minda asadzaloŵenso mumzindamo. Chifukwa masiku amenewo adzakhala masiku akulipsira, kuti zonse zija zimene zidaalembedwa m'Malembo zipherezere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 30:7

Kalanga ine! Tsiku limenelo nlalikulu kwambiri, sipadzakhala lina lofanana nalo. Idzakhala nthaŵi yamavuto kwa Yakobe, komabe adzapulumuka ku mavutowo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:7

Mvetsetsani! Akubwera pa mitambo! Aliyense adzamuwona, amene adamubaya aja nawonso adzamuwona. Ndipo anthu a mitundu yonse pansi pano adzalira chifukwa cha Iye. Nzoonadi zimenezi. Ndithudi!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:15

Pambuyo pake mngelo wachisanu ndi chiŵiri adaliza lipenga lake. Atatero kumwamba kudamveka mau okweza. Mauwo adati, “Tsopano mphamvu zolamulira dziko lapansi zili m'manja mwa Ambuye athu ndi mwa Wodzozedwa wake uja, ndipo adzalamulira mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:1-3

Pambuyo pake ndidaona mngelo akutsika kuchokera Kumwamba. M'manja mwake anali ndi kiyi ya Chiphompho chija, ndiponso unyolo waukulu. Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya. Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo. Pamenepo nyanja idapereka onse amene adaferamo. Imfa ndi Malo a anthu akufa zidaperekanso akufa ake, ndipo aliyense adaweruzidwa potsata ntchito zake. Kenaka Imfa ija ndi Malo a anthu akufa aja zidaponyedwa m'nyanja yamoto. Nyanja yamoto imeneyi ndiyo imfa yachiŵiri. Aliyense wopezeka kuti dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo lija, adaponyedwa m'nyanja yamotoyo. Adagwira Chinjoka chija, ndiye kuti njoka yakale ija yotchedwa Mdyerekezi ndiponso Satana, nachimanga zaka chikwi chimodzi. Kenaka adachiponya m'Chiphompho muja, nachitsekera nkumatirira potsekerapo kuti chisadzanyengenso mitundu ya anthu mpaka zitatha zaka zija chikwi chimodzi. Zitatha zakazo ayenera kudzachimasulanso nthaŵi pang'ono.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:10

Pamenepo Satana amene adaaŵanyenga uja, adaponyedwa m'nyanja yamoto yodzaza ndi miyala ya sulufure yoyaka, m'mene munali kale chilombo chija ndi mneneri wonama uja. M'menemo adzazunzidwa usana ndi usiku mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:1

Pambuyo pake ndidaona chilombo chikuvuuka m'nyanja. Chinali ndi nyanga khumi ndi mitu isanu ndi iŵiri. Pa nyanga iliyonse chidaavala chisoti chaufumu, ndipo pa mutu uliwonse panali dzina lonyoza Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:7-9

Tsono kudabuka nkhondo Kumwamba, Mikaele ndi angelo ake kumenyana ndi chinjoka chija. Chinjokacho pamodzi ndi angelo ake chidatengana nawo, koma onsewo adagonjetsedwa, mwakuti adataya malo ao Kumwamba. Chinjoka chachikulu chija chidagwetsedwa pansi. Ichocho ndiye njoka yakale ija yotchedwa “Mdyerekezi” ndiponso “Satana”, wonyenga anthu a pa dziko lonse lapansi. Chidagwetsedwa pa dziko lapansi pamodzi ndi angelo ake onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:4-5

Yesu adaŵayankha kuti, “Chenjerani kuti wina aliyense asadzakusokezeni. Pa nthaŵi imeneyo anthu aŵiri adzakhala ali m'munda, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. Azimai aŵiri adzakhala akusinja, mmodzi adzamtenga, winayo nkumusiya. “Nanunso tsono, khalani maso, chifukwa simudziŵa tsiku limene Ambuye anu adzabwere. Koma dziŵani kuti mwini nyumba akadadziŵa nthaŵi yofika mbala, bwenzi atakhala maso, osalola kuti mbala imuthyolere nyumba. Choncho inunso muzikhala okonzeka, pakuti Mwana wa Munthu adzabwera pa nthaŵi imene inu simukuyembekeza.” “Tsono wantchito wokhulupirika ndi wanzeru ndani, amene mbuye wake adamuika kuti aziyang'anira onse a m'nyumba mwake, nkumaŵagaŵira chakudya chao pa nthaŵi yake? Ngwodala wantchito ameneyo, ngati mbuye wake pofika adzampeza akuchitadi zimenezi. Ndithu ndikunenetsa kuti adzamuika woyang'anira chuma chake chonse. Koma ngati ndi wantchito woipa, mumtima mwake azidzati, ‘Mbuye wanga akuchedwa.’ Ndiye adzayamba kumenya antchito anzake, ndiponso kumadya ndi kumamwa pamodzi ndi zidakwa. Chifukwa kudzafika anthu ambiri m'dzina langa namadzanena kuti, ‘Mpulumutsi wolonjezedwa uja ndine,’ ndipo adzasokeza anthu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:8-9

Tsono pamenepo Munthu Woipitsitsa uja adzaululuka. Ndipo Ambuye Yesu adzamthetsa ndi mpweya wa m'kamwa mwake, nkumuwonongeratu ndi maonekedwe ake aulemerero a kubwera kwake. Munthu Woipitsitsa uja adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzachita zamphamvu zosiyanasiyana, ndiponso zizindikiro ndi zozizwitsa zonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:3

Umodzi mwa mitu yake unkaoneka ngati uli ndi bala lofa nalo, koma balalo linali litapola. Pamenepo anthu onse ankachitsata chilombocho ali odabwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:5-6

Chilombo chija chidaloledwa kulankhula mau onyada ndi onyoza Mulungu mwachipongwe. Ndipo chidapatsidwa mphamvu zolamulira pa miyezi 42. Tsono chidayamba kunena mau achipongwe onyoza Mulungu, dzina lake, malo ake okhalamo, ndi onse okhala Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 18:4

Pambuyo pake ndidamva mau ena ochokera Kumwamba. Adati, “Inu anthu anga, tulukanimo mumzindamo, kuti mungachimwire nawo pamodzi, miliri yao ingakugwereniko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:15

“Mudzaona ‘Chosakaza chonyansa chija’ chimene mneneri Daniele adaanena, atachiimika m'Nyumba ya Mulungu. (Amene ukuŵerengawe, umvetse bwino.)

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:13-14

Chilombo chachiŵirichi chinkachita zozizwitsa kwambiri, mpaka kumadzetsa moto pa dziko lapansi kuchokera kumwamba, anthu akuwona. Chinkanyenganso anthu okhala pa dziko lapansi ndi zozizwitsa zimene chidaaloledwa kuchita pamaso pa chilombo choyamba chija. Chinkauza anthu okhala pa dziko lapansiwo kuti apange fano lolemekezera chilombo chimene chidaavulazidwa ndi lupanga, koma nkukhalabe moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 2:12-19

Chauta Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku, pamene adzatsitsa onse onyada ndi odzitama, ndipo adzagonjetsa onse amphamvu. Adzadula mikungudza yonse ya ku Lebanoni, italiitali kopambana ina yonse. Adzalikha mitengo yonse ya thundu ya ku Basani. Adzasalaza mapiri onse aatali. Adzafafaniza magomo onse okwera. Adzagwetsa nsanja zonse zazitali. Adzagumula malinga onse olimba. Adzamiza zombo zonse za ku Tarisisi. Adzaononga mabwato onse okongola. Kudzikuza kwa anthu kudzatha, kudzitama kwao konse kudzaonongedwa. Chauta yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo. Mafano onse adzatheratu. Anthu adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'maenje am'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:20-21

Abale anga, pitani mukaloŵe m'nyumba zanu, ndipo mukadzitsekere. Mubisale pang'ono mpaka mkwiyo wa Chauta utatha. Chauta akubwera kuchokera kumene amakhala, akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo ao. Magazi okhetsedwa pa dziko lapansi adzaululuka, mitembo ya anthu ophedwa sidzabisikanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:1-14

Mphamvu ya Chauta idandigwira, Mzimu wa Chauta udandinyamula nkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Motero ndidayamba kulalika monga adandilamulira. Tsono mpweya udaloŵa mwa iwo, ndipo akufa aja adakhala ndi moyo, naimirira. Linali gulu lalikulu kwambiri la ankhondo. Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa ameneŵa ndi Aisraele onse. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu ndi ouma, chiyembekezo chathu chidataika, taonongekeratu.’ Nchifukwa chake uŵalalikire ndi kuŵauza kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo. Ndidzakubwezerani ku dziko la Israele. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzafukula manda anu ndi kukutulutsanimo, inu anthu anga. Tsono ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo, pambuyo pake ndidzakukhazikani m'dziko lanu. Choncho mudzadziŵa kuti Ine Chauta ndalankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:11-12

Pambuyo pake ndidaona mpando wachifumu woyera, waukulu, ndiponso amene amakhalapo. Dziko lapansi ndi thambo zidathaŵa pamaso pake, ndipo sizidapezekenso konse. Ndidaonanso anthu akufa, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Adaimirira patsogolo pa mpando wachifumu uja, ndipo mabuku adafutukulidwa. Adafutukula buku linanso, limene lili buku la amoyo. Tsono anthu akufawo adaweruzidwa poyang'anira ntchito zao monga momwe zidaalembedwera m'mabukumo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:1

Pambuyo pake ndidaona thambo latsopano ndi dziko lapansi latsopano. Paja thambo loyamba lija ndi dziko lapansi loyamba lija zinali zitazimirira, ndipo nyanja panalibenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:12

Yesu akuti, “Mvetsetsani, ndikubwera posachedwa. Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense molingana ndi zimene adachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 22:20

Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye wanga, ndinu woyenera, wolungama, ndi wangwiro m'njira zanu zonse. Mwavala chiyero ndi ulemerero. Inu Mulungu, mukukhala mu nthawi yosatha, Alfa ndi Omega, chiyambi ndi chimaliziro. Mulungu Wamphamvuzonse, panthawi yovutayi ndi yosadziwika, ndikupemphani kuti munditeteze ndi kunditsogolera. Mundipatse mphamvu ndi nzeru pamaso panu, ndipo chikondi chanu ndi mtendere wanu zidzaze mtima wanga. Ndikupemphani kuti munditeteze ku masautso akulu akubwera padziko lapansi, ndithandizeni kukhala m'chiyero kuti moyo wanga upulumuke ku masautso akulu. Ndikudziwa kuti mwa Inu ndekha ndimapeza pothawirapo, ndipo ndikukhulupirira kuti muli nane pakati pa mavuto aliwonse. Ambuye, ndikupemphani kuti mundipatse luntha kuti ndisankhe zochita motsatira malamulo anu. Mundilimiritse ndi kundidzaza ndi Mzimu Woyera wanu kuti palibe chomwe chingandichotse pamaso panu, moyo wanga uli pamaso panu, wongolani mapazi anga ndi kundionetsa njira yoyenera kuyenda podziwa kuti ndinu thanthwe langa ndi mphamvu yanga. Dzanja lanu lamphamvu linditeteze ndi kunditeteza ku choipa chilichonse chofuna kusokoneza moyo wanga. Ndimayika tsogolo langa ndi chikhulupiriro changa m'manja mwanu, ndikudziwa kuti mumasamalira ubwino wanga. Mu dzina la Yesu, ndikukuthokozani chifukwa cha zonse, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa