Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


67 Mau a m'Baibulo Okhudza Mtima

67 Mau a m'Baibulo Okhudza Mtima

Baibulo, makamaka m’buku la Miyambo, limandiuza kuti ndisamalire mtima wanga, chifukwa moyo wanga umachokera mmenemo. Ngakhale limatiuza kuti mtima ndi wonyenga, limandikakamiza kuti ndiipe mtima wanga kwa Mulungu kuti ndisagonjedwe ndi zilakolako zanga. M’malo mwake, ndiyenera kufunafuna chitsogozo cha Mzimu Woyera kuti ndikhale moona mtima ndi kukondweretsa Mulungu.

Mulungu akufuna kukhala mumtima mwanga, koma sayenera kukhala mumtima wosokonezeka kapena wopanduka, koma kwa iwo amene amamufunafuna modzichepetsa. Mmawa uliwonse, ndiyenera kudzaza mtima wanga ndi Mawu a Mulungu kuti mawu anga akhale odalitsa, osati otemberera.

Chofunika kwambiri si maonekedwe akunja, koma mkati mwanga. Ndiyenera kukhala woona mtima pa chilichonse chimene ndichita, chifukwa iwo amene ali ndi mtima woyera adzamuona Mulungu. Aleluya!




1 Samueli 16:7

Koma Chauta adauza Samuele kuti, “Usayang'ane maonekedwe ake, ngakhale kutalika kwa msinkhu wake, poti ndamkana ameneyo. Chauta sapenya monga m'mene apenyera anthu. Anthu amapenya zakunja, koma Chauta amapenya zamumtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:4

Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:26

Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:9

Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:21

Pajatu kumene kuli chuma chako, mtima wakonso kokhala nkomweko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga. Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:10

Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:2

Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5-6

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:11

Ndasunga mau anu mumtima mwanga, kuti ndisakuchimwireni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:19

Monga momwe nkhope imaonekera m'madzi, momwemonso mtima wa munthu umadziŵika ndi zochita zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:37

Yesu adamuyankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:13

Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:22

Mtima wosangalala umakhala ngati mankhwala abwino, koma mtima woziya umaumitsa thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 90:12

Tsono tiphunzitseni kuŵerenga masiku athu, kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:13

Mtima wosangalala umaonetsa nkhope yachimwemwe, koma mtima wachisoni umaphwanya moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:10

Choncho muchotseretu zokusautsani mu mtima mwanu, mupewe zokupwetekani m'thupi mwanu. Pajatu unyamata ndi ubwana, zonse nzopandapake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:2

Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:5

Chiyembekezo chimenechi munthu sichingamugwiritse fuwa lamoto ai, pakuti Mulungu mwa Mzimu Woyera amene Iye adatipatsa, adadzaza mitima yathu ndi chikondi chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:45

Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:8

Yandikirani kwa Mulungu, ndipo Iye adzayandikira kwa inu. Muzisamba m'manja, inu anthu ochimwa. Chotsani maganizo onyenga m'mitima mwanu, inu anthu okayikakayika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:22-23

Koma zipatso zimene Mzimu Woyera amabweretsa m'moyo wa munthu ndi izi: Chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, kukhulupirika, kufatsa ndiponso kudziletsa. Zimenezi palibe lamulo loziletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:20

nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:15

koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 6:5

Muzikonda Chauta, Mulungu wanu, ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse ndi mphamvu zanu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 112:7

Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:12

Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:22

Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:8

Munthu wa mtima wanzeru adzasamala malamulo, koma chitsiru chomangolongolola chidzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 126:5-6

Anthu amene amafesa akulira, adzakolola akufuula ndi chimwemwe. Munthu amene amapita akulira, atatenga mbeu zokafesa, adzabwerera kwao akufuula ndi chimwemwe, atatenga mitolo yake yambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:30

Mtima wodekha umapatsa thupi moyo, koma nsanje imaoletsa mafupa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:17

Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 66:18

Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:14

Ndi wodala munthu amene amaopa Chauta nthaŵi zonse, koma woumitsa mtima wake adzagwa m'tsoka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:20

Anthu a mtima woipa amamnyansa Chauta, koma anthu a makhalidwe abwino amamkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:17

Nsembe imene Inu Mulungu mumailandira, ndi mtima wotswanyika. Mtima wachisoni ndi wolapa, Inu Mulungu simudzaunyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:27

Iye adayankha kuti, “Uzikonda Chauta, Mulungu wako, ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi nzeru zako zonse, ndiponso mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:8

Ndimakonda kuchita zimene mumafuna, Inu Mulungu wanga, malamulo anu ali mumtima mwanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 29:13

Ambuye adati, “Anthu aŵa amati amapemphera kwa Ine, koma mau ao ndi opanda tanthauzo, ndipo mitima yao ili kutali ndi Ine. Chipembedzo chao ndi kungotsata chabe malamulo ongoŵaloŵeza pamtima, malamulo ochokera kwa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:1

Zolinga zamumtima ndi za munthu, koma zolankhula zake ndi zochokera kwa Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 147:3

Akuchiritsa a mtima wachisoni, ndipo akumanga mabala ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:27

“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:7

Aliyense apereke monga momwe adatsimikiziratu mumtima mwake, osati ndi chisoni kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:26

Mwana wanga, mtima wako ukhulupirire ine, maso ako apenyetsetse njira zanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:4

Koma kudzikongoletsa kwanu kukhale kwa moyo wam'kati, kukongola kosatha kwa mtima wofatsa ndi wachete. Moyo wotere ngwamtengowapatali pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:61

Nchifukwa chake inu Aisraele, mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Mulungu wathu, ndipo mumvere bwino mau ake, ndi kutsata malamulo ake monga lero lino.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 24:7

Ndidzaŵapatsa mtima woti azidziŵa kuti ndine Chauta. Iwowo adzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wao, pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:26

Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 51:10

Mundilengere mtima woyera, Inu Mulungu, muike mwa ine mtima watsopano ndi wokhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:9

Mtima wa munthu ndi chinthu chonyenga kwambiri kupambana zinthu zonse. Kuipa kwake nkosachizika. Kodi ndani angathe kuumvetsa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:10

“Koma Ine Chauta ndimafufuza maganizo ndi kuuyesa mtimawo. Ndimamchitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndiponso moyenerera ntchito zake.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 11:19

Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:23

Mtima wako uziwulonda bwino, pakuti m'menemo ndimo muli magwero a moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:8

Ngodala anthu oyera mtima, pakuti adzaona Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:12

Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:5

Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:2

Makhalidwe a munthu amakhala olungama pamaso pa mwiniwakeyo, koma Chauta ndiye amayesa mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:18

Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:5

Koma chifukwa ndiwe wa mtima wokanika ndi wosafuna kutembenuka, ukudzisungira chilango cha Mulungu. Chilangocho chidzakugwera pa tsiku limene adzaonetse mkwiyo wake ndiponso kuweruza kwake kolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:2

Mundiyang'anitsitse, Inu Chauta, ndi kundiyesa. Muwone mtima wanga pamodzi ndi maganizo anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Chifukwa m'kati mwa mitima ya anthu ndiye mumatuluka maganizo oipa, za kuphana, za chigololo, za chiwerewere, za kuba, maumboni onama, ndiponso zachipongwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Woyera ndi Wamphamvuyonse, Wamkulukulu, kasupe wosatha wa chikondi, ndikukwezani dzina lanu, Yesu wanga wabwino. Atate, ndithandizeni kuti ndizikhala maso kusamalira mtima wanga tsiku lililonse ndipo ndisungepo kanthu kalikonse koipa. Ndikupemphani kuti muufufuze ndi kuwunika zamkati mwake, ngakhale zomwe sindikuzidziwa. Ndipatseni chizolowezi chokhala nthawi yayitali pamaso panu, chifukwa ndi malo otetezeka kusungira mtima wanga ndi kuupereka tsiku lililonse kuunika kwa mawu anu, kuti Mzimu wanu Woyera ulamulire moyo wanga. Mawu anu amati: "Samala mtima wako kuposa zonse, chifukwa ndiwo chitsime cha moyo." Ambuye Yesu, ndinu mtsogoleri wanga, ndithandizeni kumvetsa kuti mtima wanga ndi chitsime cha moyo ndipo ndiyenera kuugwirizanitsa ndi cholinga chimene munandikonzera, ndithandizeni kumvetsa kuti sindiyenera kusunga malingaliro oipa monga nsanje, kaduka, mkwiyo, chidani, ndiponso mbewu ina iliyonse yomwe ingabale zipatso zoipa ndi kundipitsa. Atate, pangani mwa ine mtima woyera, ndipo mukonzenso mzimu wolungama mkati mwanga. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa