Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


65 Mau a Mulungu Okhudza Nyumba Yake Yopatulika

65 Mau a Mulungu Okhudza Nyumba Yake Yopatulika

Kuyambira kalekale, Mulungu walamula anthu ake kumanga Nyumba Yake Yopatulika, komwe tingachite miyambo Yake Yopatulika. Chifukwa Ambuye amabwera ku Nyumba Yake Yopatulika ndi ulemerero Wake, tiyenera kulemekeza nthawi zonse tikapezeka kutchalitchi, kaya tikupembedza kapena tikumvetsera mawu a Mulungu.

Mose ndi ana a Israeli anamanga chihema chopatulika chomwe chinali ngati kachisi koyenda nako paulendo wawo wotuluka mu Igupto. Kachisi wodziwika kwambiri m’Chipangano Chakale ndi uja womangidwa mu Yerusalemu nthawi ya Solomoni (2 Mbiri 2–5).

Masiku ano, kachisi waukulu kwambiri komwe Mulungu akufuna kukhala ndi mtima wako. Konzekeretsa malo okongola mkati mwako komwe Mzimu Woyera angakhalemo mosangalala ndipo asafune kuchoka.




1 Akorinto 6:19-20

Kodi simudziŵa kuti thupi lanu ndi nyumba ya Mzimu Woyera? Mulungu adakupatsani Mzimuyo kuti akhale mwa inu. Nchifukwa chake moyo umene muli nawo si wanunso. Kodi simukudziŵa kuti akhristu ndiwo adzaweruza anthu onse? Tsono ngati inu mudzaweruza anthu onse, kodi simungathe kuweruza ngakhale ndi timilandu tating'ono tomwe? Mulungu adakugulani ndi mtengo wapatali, tsono muzimlemekeza ndi matupi anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:16

Kodi Nyumba ya Mulungu nkufanana bwanji ndi mafano? Pajatu ife ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo, monga Mulungu mwini adanena kuti, “Ndidzakhazikika mwa iwo, ndi kukhala nawo. Ndidzakhala Mulungu wao, iwo adzakhala anthu angaanga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:10-11

Tsono pamene ansembewo adatulukamo m'malo opatulikawo, mtambo udadzaza Nyumba ya Chauta. Ndipo ansembe sankatha kutumikira chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta udaadzaza Nyumba yake ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:1-2

Solomoni atatha kupemphera, moto udatsika kuchokera kumwamba, nuwotcha nsembe zopsereza pamodzi ndi nsembe zina. Pomwepo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba ya Chauta ija. Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiŵiriwo, Solomoni adauza anthu aja kuti apite kwao. Anthuwo anali okondwa ndiponso a mtima wosangalala, chifukwa cha zokoma zimene Chauta adaachitira Davide ndi Solomoni ndiponso Aisraele, anthu ake. Motero Solomoni adamaliza kumanga Nyumba ya Chauta ndi nyumba ya mfumu ndipo zonse zimene adaaganiza kuti achite m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba yake adazimalizadi mokhoza kwambiri. Tsono Chauta adamuwonekera usiku namuuza kuti, “Ndamva pemphero lako, ndipo ndadzisankhira malo ano kuti akhale Nyumba yoperekera nsembe. Ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena ndikalamula dzombe kuti liwononge zomera zapadziko, kapena ndikatumiza mliri pakati pa anthu anga, ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao. Ndiye maso anga adzatsekuka, ndipo ndidzatchera khutu ku pemphero limene adzapemphere ku malo ano. Chifukwa tsopano ndaisankha ndipo ndapatula Nyumba ino kuti dzina langa lizikhala m'menemo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga, zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse. Tsono iweyo ukamayenda pamaso panga monga m'mene ankayendera Davide bambo wako, ukamachita zonse zimene ndidakulamula ndi kumvera mau anga ndi malangizo anga, ukatero Ine ndidzaukhazikitsa mpando wako waufumu, monga momwe ndidalonjezera Davide bambo wako kuti, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wolamulira Israele.’ “Koma inu mukapatuka ndi kusiya malamulo anga ndi malangizo anga amene ndidakupatsani, mukamatumikira milungu ina ndi kumaipembedza, Tsono ansembe sadathe kuloŵa m'Nyumbamo, popeza kuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 3:10-11

Tsono amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Chauta, ansembe adadza akuimba malipenga atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, adadza akuimba ziwaya zamalipenga ndi kutamanda Chauta, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraele. Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati, “Chauta ndi wabwino, chikondi chake pa Israele nchamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 84:10

Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:12-13

Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa onse amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndiponso mipando ya ogulitsa nkhunda. Adaŵauza kuti, “Malembo akuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo.’ Koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:19-21

Yesu adaŵayankha kuti, “Gwetsani nyumba ya Mulungu ino, Ine ndidzaimanganso masiku atatu.” Yesu nayenso pamodzi ndi ophunzira ake adaaitanidwa kuukwatiko. Apo iwo adati, “Nyumba ya Mulunguyi idatenga zaka 46 kuti aimange, tsono Inu nkuimanga masiku atatu chabe?” Koma Yesu ankanena za thupi lake mophiphiritsa, pamene adaatchula Nyumba ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:17

Ngati wina aliyense aononga nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo. Pakuti nyumba ya Mulungu ndi yopatulika, ndipo nyumbayo ndinu amene.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:6

Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 43:4-5

Ulemerero wa Chauta udakaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, kuloŵera chipata choyang'ana kuvuma. Mzimu wa Mulungu udandinyamula numandiloŵetsa m'bwalo lam'kati. Ndipo ulemerero wa Chauta udadzaza Nyumba yakeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:4

Ndapempha chinthu chimodzi chokha kwa Chauta, chinthu chofunika kwambiri, chakuti ndizikhala m'Nyumba ya Chauta masiku onse a moyo wanga, kuti ndizikondwera ndi kukoma kwake kwa Chauta ndi kuti ndizipembedza Iye m'Nyumba mwakemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 65:4

Ngwodala munthu amene Inu mumamsankha nkubwera naye kudzakhala m'mabwalo anu. Mutikhutitse ndi zinthu zabwino za m'Nyumba yanu, Nyumba yanu yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 25:8

Ndipo andipangire chihema chopatulika kuti Ine ndidzakhale pakati pao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:46-47

Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 9:3

Ndipo Chauta adamuuza kuti, “Ndamva pemphero lako ndi kupemba kwako kumene wachita pamaso panga. Ine ndaipatula Nyumba wamangayi, ndaikamo dzina langa kuti anthu azidzandipembedzeramo mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala m'menemo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:42

Tsono tsiku ndi tsiku ankaphunzitsabe ndi kulalika m'Nyumba ya Mulungu ndi m'nyumba za anthu, Uthenga Wabwino wakuti Yesu ndiye Mpulumutsi wolonjezedwa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:22

Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:12

Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, nayamba kutulutsa onse amene ankachita malonda m'menemo. Adagubudula matebulo a osinthitsa ndalama, ndiponso mipando ya ogulitsa nkhunda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:4

Koma Chauta ali m'Nyumba yake yoyera, Chauta mpando wake waufumu uli kumwamba. Maso ake amapenya anthu onse ndi kuŵayesa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:21-22

Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 7:2

Tsono ansembe sadathe kuloŵa m'Nyumbamo, popeza kuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'menemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 21:23

Yesu adaloŵa m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akulu a Ayuda adadzamufunsa kuti, “Kodi mphamvu zoti muzichita zimenezi mudazitenga kuti? Ndani adakupatsani mphamvu zimenezi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:7

Koma ine ndidzatha kuloŵa m'Nyumba mwanu chifukwa cha kukula kwa chikondi chanu. Ndidzaŵeramitsa mutu pansi, kupembedza Inu m'Nyumba yanu yoyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:8

Inu Chauta, ndimakonda Nyumba imene mumakhalamo, ndiye kuti malo amene kuli ulemerero wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:19-22

Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:12-13

“Kunena za Nyumba ukumangayi, iwe ukamamvera mau anga ndi malangizo anga ndi kutsata malamulo anga onse, Ine ndidzakuchitiradi zimene ndidalonjeza kwa Davide bambo wako. Ndiye kuti Ine ndidzakhala pakati pa Aisraele, Aisraele anthu anga sindidzaŵasiya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:27

“Kodi Mulungu angakhale nawodi pa dziko lapansi? Onani, kumwamba ndi kumwambamwamba komwe sikukukwanirani kukhala, nanji tsono nyumba imene ndakumangiraniyi!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 100:4

Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:4

Musamangodzinyenga ndi maganizo akuti muli pabwino ponena kuti, ‘Malo ano ndi Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta, Nyumba ya Chauta!’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:12

Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 6:40

Tsopano, Inu Mulungu wanga, tsekulani maso anu, ndipo makutu anu amve pemphero ili la ku malo ano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 6:16

Tsono Aisraele, ndiye kuti ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, adachita chikondwerero cha kupereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 37:26-28

Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya. Nyumba yanga idzakhala pakati pao. Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Apo anthu a mitundu ina adzadziŵa kuti Ine Chauta Aisraele ndimaŵasandutsa oyera, chifukwa chakuti Nyumba yanga ili pakati pao mpaka muyaya.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:48-49

Ngakhale zinali choncho Mulungu Wopambanazonse sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja, monga akunenera mneneri kuti, “Chauta akuti, ‘Kumwamba ndi mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga. Kodi mudzandimangira nyumba yotani? Kapena malo opumuliramo Inewo ngotani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:11

Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 9:24

Paja Khristu sadaloŵe m'malo opatulika omangidwa ndi anthu, malo ongofanizira malo enieni opatulika a Kumwamba. Iye adapita Kumwamba kwenikweniko, kuti tsopano aziwonekera pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 40:34-35

Mtambo udaphimba chihema chamsonkhanocho, ndipo ulemerero wa Chauta udachidzaza Mose sadathe kuloŵa m'chihema chamsonkhanocho chifukwa mtambo unali momwemo, ndipo ulemerero wa Chauta udaadzaza chihema chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 7:5

“Kamuuze mtumiki wanga Davide kuti Ine Chauta ndikuti, Kani wayesa udzandimangira ndiwe nyumba yoti ndizikhalamo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 22:19

Tsono ikani nzeru zanu ndi mtima wanu pa kutumikira Chauta Mulungu wanu. Muyambepo tsopano kumanga Nyumba ya Chauta kuti muikemo Bokosi lachipangano la Chauta ndiponso ziŵiya zonse zofunikira pa chipembedzo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 7:15

“Nchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndipo amampembedza m'Nyumba mwake usana ndi usiku. Wokhala pa mpando wachifumu uja adzakhala ngati hema lao loŵateteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 6:12-13

Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzamange Nyumba ya Chauta. Ndiye amene adzakhale ndi ukulu waufumu, ndi kumalamulira atakhala pa mpando wake waufumu. Pafupi ndi mpando wake padzakhala wansembe, ndipo aŵiriwo adzagwira ntchito mwamtendere ndi mogwirizana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:6

Ndipotu ndikunenetsa kuti pali wina pano woposa Nyumba ya Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 5:5

Choncho ndikufuna kumangira nyumba Chauta Mulungu wanga, monga momwe Iye adaauzira bambo wanga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando wako waufumu m'malo mwako, ndiye amene adzandimangire nyumba.’

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezara 1:2-3

“Kirusi, mfumu ya ku Persiya, akunena kuti, ‘Chauta, Mulungu Wakumwamba, wandipatsa ine maiko onse a pa dziko lonse lapansi, ndipo wandilamula kuti ndimmangire Nyumba ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda. Tsono inu nonse amene muli akeake, Mulungu wanuyo akhale nanu. Aliyense mwa inu apite ku Yerusalemu, ku dziko la Yuda, kuti akamange Nyumba ya Chauta, Mulungu wa Israele. Iyeyo ndiye Mulungu amene amampembedza ku Yerusalemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:9

Choncho ulemerero wa Nyumba yachiŵiriyi udzaposa ulemerero wa Nyumba yoyamba ija. Ndipo ndidzakhazikitsa ufulu ndi mtendere pa malo ano. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 4:23-24

Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 29:9

Liwu la Chauta likuzunguza miŵanga likupulula masamba a mitengo yonse m'dondo. Onse a m'nyumba mwake akufuula kuti, “Ulemererowo!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:33

Mulungu safuna chisokonezo ai, koma mtendere. Monga zimachitikira m'mipingo yonse ya anthu a Mulungu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:30

Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 5:13-14

Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo, ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 29:12-13

Nthaŵi imeneyo mudzandiitana ndi kumanditama mopemba, ndipo ine ndidzakumverani. Mudzandifunafuna, ndipo mudzandipeza. Mukadzandifunafuna ndi mtima wanu wonse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 6:1-4

Chaka chimene mfumu Uziya adamwalira, ndidaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu wautali ndi wokwezedwa. Mkanjo wao unali wautali kwambiri, kotero kuti udadzaza Nyumba yao yonse. Tsono anthu ameneŵa uŵaphe mtima, uŵagonthetse makutu, ndipo uŵatseke m'maso, kuti angaone ndi maso ao, angamve ndi makutu ao, angamvetse ndi mitima yao, kenaka nkutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.” Pamenepo ndidafunsa kuti, “Zimenezo ndi mpaka liti, Inu Ambuye?” Iwo adati: “Mpaka mizinda itasanduka mabwinja, mpaka nyumba zitasoŵa anthu okhalamo, mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu. Ine anthuŵa ndidzaŵasamutsira kutali, ndipo dziko lidzakhala thengo. Tsono ngakhale chigawo chachikhumi cha anthu chitsaleko m'dzikomo, nachonso chidzayatsidwa moto. Koma monga mitengo ya muŵanga ndi ya thundu imasiya chitsa akaidula, chonchonso mbeu yoyera ija idzatsalira ngati chitsa chotsala m'dziko.” Pamwamba pao padaaimirira Aserafi. Aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: aŵiri ophimbira kumaso, aŵiri ophimbira mapazi, aŵiri oulukira. Aserafiwo ankafuulirana kuti, “Ngwoyera, ngwoyera, ngwoyera Chauta Wamphamvuzonse, ulemerero wake wadzaza dziko lonse lapansi.” Chifukwa cha kufuulako maziko a zitseko ndi ziwundo adagwedezeka ndipo m'Nyumba ya Chautamo mudangoti utsi pha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:1

Chauta akunena kuti, “Thambo lam'mwamba ndiye mpando wanga waufumu, dziko lapansi ndiye chopondapo mapazi anga. Kodi ndi nyumba yotani imene mungathe kundimangira inu? Ndi malo otani amene inu mungandikonzere kuti Ine ndizipumulirapo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 28:6

Adandiwuza kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye amene adzamange nyumba yanga ndiponso mabwalo anga. Ndamsankha iyeyo kuti akhale mwana wanga, ndipo Ine ndidzakhala bambo wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 11:1

Pambuyo pake adandipatsa bango loyesera, longa ndodo, nandiwuza kuti, “Nyamuka, kayese Nyumba ya Mulungu ndi guwa lansembe, ndipo ukaŵerenge opembedza m'Nyumbamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:4

Ameneyu ndi mdani, ndipo adzadziika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza, kotero kuti mwiniwakeyo adzadzikhazika m'Nyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:1

Yesu adatuluka m'Nyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankachoka, ophunzira ake adabwera nkumamuwonetsa kamangidwe ka Nyumbayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:7

Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Samueli 3:3

Samuelenso anali gone m'Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthaŵiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 6:12

Tsono umuuze kuti, Zimene ndikunena Ine Chauta Wamphamvuzonse ndi izi: Ndi ameneyutu munthu wotchedwa ‘Nthambi’ uja. Adzaphuka ndi kukulira pomwe aliripo, ndipo adzamangapo Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 8:10

Tsono pamene ansembewo adatulukamo m'malo opatulikawo, mtambo udadzaza Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 6:1

Pakutha pa zaka 480 Aisraele atatuluka ku Ejipito, chaka chachinai cha ufumu wa Solomoni wolamulira Aisraele, pa mwezi wa Zivi, umene uli mwezi wachiŵiri, Solomoni adayambapo kumanga Nyumba ya Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Wamphamvuzonse! Ndimakulambirani, ndikuvomereza ukulu wanu ndi ulemerero wanu, ndaona kukoma mtima kwanu pa moyo wanga ndi chifundo chanu chachikulu. Atate, ndikufuna kukhala m'nyumba mwanu ndikhale ndi abale anga pamodzi mwamtendere, chifukwa kumeneko mumatumiza madalitso anu ndi moyo wosatha. Zikomo chifukwa kumeneko ndi komwe ndimakumana ndi ena komwe ndingalimangire ndikupeza chilakolako chotumikira ufumu wanu, komwe ndingakwaniritse cholinga chanu ndi masomphenya a moyo. Ndikupemphani kuti tsiku lililonse m'mtima mwanga mukhale chikhumbo ndi chilakolako chosonkhana ndikukupatsani nthawi zonse ulemerero wanga wabwino kwambiri. Ndikukuthokozani chifukwa cha nyumba yanu chifukwa kumeneko ndi komwe anthu aamuna, akazi ndi anthu amitundu yonse amapempherera. Mawu anu amati: "Ndidzawatenga kupita ku phiri langa lopatulika, ndipo ndidzawasangalatsa m'nyumba yanga yopempherera; nsembe zawo zopsereza ndi nsembe zawo zidzalandiridwa pa guwa langa la nsembe, chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopempherera anthu a mitundu yonse." Zikomo, Ambuye, chifukwa m'nyumba mwanu muli mphamvu yauzimu ndi chitetezo, chifukwa tsiku loipa mudzandibisira m'chihema chanu. M'dzina la Yesu. Ameni!
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa