Ndikufuna ndikuuzeni anzanga, nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, yopangidwa kuti imusangalatse Iye. Inde, Mulungu watipatsa ife talente yoimba, koma gwero la zonse ndi mphamvu zake zazikulu zolenga. M'Mawu a Mulungu, timaona kuti nyimbo zimagwiritsidwa ntchito nthawi yapadera, monga potamanda dzina la Mulungu ndi kukweza ukulu wake, kuvina pamaso pake, kulandira mtendere pakati pa mavuto, ndi kulengeza kugonjetsedwa kwa adani ndi kulengeza chipambano.
Masalimo ambiri analembedwa ngati nyimbo, ena mwa iwo akukhudzana ndi zochitika zenizeni, monga kupambana adani (Eksodo 15.1-18; Oweruza 5.1-31), kutamanda Mulungu, kupempha thandizo kapena chitsogozo. Ndipo kumbukirani, angelo anaimba polengeza kubadwa kwa Yesu (Luka 2.13-14).
Timadziwa kuti mdierekezi wayesa kuwononga tanthauzo la nyimbo, polimbikitsa zoipa ndi chiwerewere, choncho ana a Mulungu ayenera kusunga chiyambi chake ndi kuchiteteza ku machitidwe a dziko lino, lopangidwa ndi Mulungu Wamuyaya.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.
Koma Inu mudangouzira ndi mphepo yanu, ndipo nyanja idaŵamiza. Adangomira ngati chitsulo mpaka pansi pa madzi.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja, ndipo nthaka idaŵameza.
“Koma anthu amene mudaŵaombola, mudaŵatsogolera ndi chikondi chanu chosasinthika. Mudaŵatsogolera ku malo anu oyera ndi mphamvu zanu.
Anthu a mitundu ina amva mbiriyi, ndipo anjenjemera ndi mantha. Mantha oopsa aŵagwira Afilisti.
Tsopano lino mafumu a ku Edomu ataya mtima. Atsogoleri a ku Mowabu ayambapo kunjenjemera. Onse a ku Kanani agooka m'nkhongono.
Onsewo agwidwa ndi mantha oopsa. Iwo akhala chete ngati mwala, chifukwa cha kuwopa mphamvu zanu zazikulu. Angokhala chete mpaka anthu anu, Inu Chauta, atabzola, anthu amene mudaŵaombola mu ukapolo.
Mudzaŵaloŵetsa ndi kuŵakhazika pa phiri lanu, pa malo amene Inu Chauta mudaŵapanga kuti akhale anu, m'nyumba yopembedzera imene Inu mudaimanga.
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya.”
Pamene akavalo a Farao, pamodzi ndi magaleta ndi okwerapo ake omwe, adaloŵa m'nyanja, Chauta adaŵabweza madziwo, ndipo adamiza onsewo. Koma Aisraele adayenda pouma m'kati mwa nyanjayo.
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.”
Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo.
Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa.
“Imvani, inu mafumu, tcherani khutu, inu olamulira. Ndidzaimba nyimbo yokoma, kuimbira Chauta, Mulungu wa Israele.
Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino.
Tsono nthaŵi zonse mzimu woipa uja ukamfikira Saulo, Davide ankatenga zeze namamuimba. Motero Saulo ankapeza bwino, ndipo mzimu woipawo unkamsiya.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Tsono Davide pamodzi ndi Aisraele onse anali ankakondwera kwambiri kulemekeza Mulungu poimba nyimbo ndi azeze, apangwe ndi ting'oma, ziwaya zamalipenga ndi malipenga amene.
Ndidzaimbira Chauta moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Chauta, nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu mtima wanga wakonzekadi. Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
Pambuyo pake Davide adalamulanso atsogoleri a Alevi kuti asankhe ena mwa abale ao, kuti aziimba ndi kuliza mwamphamvu zipangizo zoimbira monga azeze, apangwe, ndiponso ziwaya zamalipenga, kuti mau achimwemwe amveke bwino.
Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Muimbireni nyimbo yatsopano, kodolani nsambozo mwaluso ndi kufuula mosangalala.
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake.
anthu 4,000 adzakhale alonda apakhomo, ndipo anthu 4,000 enawo azidzatamanda Chauta ndi zipangizo zoimbira zimene ndazipereka kuti zikhale zotamandira Chauta.”
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake.
Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
“Chauta wandipulumutsa, ndipo tidzamtamanda poimba ndi azeze m'Nyumba mwa Chauta pa moyo wathu wonse.”
Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo,
Pamene anthu adati apereke kwa Mulungu khoma lozinga mzinda wa Yerusalemu, adaitana Alevi kuchokera konse kumene ankakhala, kuti abwere ku Yerusalemu kudzachita mwambo wopereka khomalo mokondwera, mothokoza ndiponso poimba pamodzi ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi mapangwe.
Kenaka mfumu Hezekiya, pamodzi ndi nduna zake, adalamula Alevi kuti aimbe nyimbo zotamanda Chauta potsata mau a Davide ndi a mneneri Asafu. Pomwepo adaimba mosangalala nyimbo zotamanda, ndipo adagwada naŵeramitsa mitu pansi.
Anthuwo adagwira ntchitoyo mokhulupirika. Amene ankaŵayang'anira anali Yahati ndi Obadiya, a m'banja la Alevi, ana a Merari. Zekariya ndi Mesulamu, ana aamuna a m'banja la Akohati, adaŵaikamo kuti aziyang'anira. Alevi onse amene anali ndi luso la kumaimba ndi zipangizo zoimbira,
Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati, “Chauta ndi wabwino, chikondi chake pa Israele nchamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu, mtima wanga wakonzekadi! Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha, iwe mtima wanga.
Ndani adzandifikitse ku mzinda wamalinga? Ndani adzanditsogolere ku Edomu?
Si wina ai koma ndinu Mulungu amene mwatitaya, ndinu Mulungu amene mwaleka kuperekeza ankhondo athu.
Tithandizeni kulimbana ndi adani athuwo, pakuti chithandizo cha munthu nchopandapake.
Mulungu akakhala nafe, tidzamenya nkhondo molimba mtima, pakuti ndiye amene adzapondereza adani athu.
Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani. Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a m'maiko onse,
Pali nthaŵi yomva chisoni ndi nthaŵi yosangalala, nthaŵi yolira maliro ndi nthaŵi yovina.
Kondwerani mwa Chauta, inu anthu ake. Zoonadi ochita zolungama azitamanda.
Zolinga za anthu akunja Chauta amazisandutsa zopandapake. Maganizo ao onse amaŵasandutsa achabechabe.
Koma zolinga za Chauta zimachitika nthaŵi zonse, maganizo a mumtima mwake amakhazikika mpaka muyaya.
Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha akeake.
Chauta ali kumwamba, amayang'ana pansi ndi kuwona anthu onse.
Kumene amakhala pa mpando wachifumuko, amapenya anthu onse okhala pa dziko lapansi
Amene amapanga mitima ya anthu onse, ndiye amene amapenya ntchito zao zonse.
Mfumu siipulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake la ankhondo. Wankhondo sapulumuka chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri.
Pa kavalo wankhondo sungaikepo mtima kuti upambane, chifukwa sangathe kupulumutsa munthu, ngakhale kavaloyo ali ndi mphamvu zambiri.
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika.
Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
Tamandani Chauta ndi pangwe. Muimbireni nyimbo ndi zeze wa nsambo khumi.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika chikhale pa ife, chifukwa timakhulupirira Inu.
Muimbireni nyimbo yatsopano, kodolani nsambozo mwaluso ndi kufuula mosangalala.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Mtima wanga umaŵawa ndikamakumbukira m'mene ndinkayendera ndi chinamtindi cha anthu, poŵatsogolera ku Nyumba ya Mulungu. Panali khwimbi la anthu ofuula mosangalala, akuimba nyimbo zothokoza ndipo akuchita chikondwerero.
Muimbireni Mulungu, imbani nyimbo zotamanda dzina lake. Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo. Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake.
Kwezani mau kuimbira Mulungu amene ali mphamvu zathu. Fuulani ndi chimwemwe kwa Mulungu wa Yakobe.
Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndidakutulutsani m'dziko la Ejipito. Yasamani kukamwa, Ine ndidzakudyetsani.
“Koma anthu anga sadamvere mau anga. Israele adandinyoza.
Choncho ndidaŵasiya ndi mitima yao yosamverayo, kuti atsate zimene ankafuna.
“Anthu anga akadandimvera, Aisraele akadayenda m'njira zanga,
bwenzi posachedwa nditagonjetsa adani ao, ndipo dzanja langa likadakantha amaliwongo ao.
“Anthu amene amadana ndi Chauta, akadakhwinyata pamaso pake, ndipo tsoka lao likadakhala mpaka muyaya.
Ndikadakudyetsani ndi ufa wosalala watirigu, ndipo ndikadakukhutitsani ndi uchi wam'thanthwe.”
Yambani nyimbo, imbani ng'oma, pamodzi ndi pangwe wolira bwino ndi zeze.
Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano.
Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira.
Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni.
Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu.
Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,
imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota.
Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,
poimba nyimbo zokoma ndi gitara, zeze ndi pangwe.
Tsono ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu, kwa Mulungu amene amandipatsa chimwemwe chopambana. Ndipo ndidzakutamandani ndi pangwe, Inu Mulungu, Mulungu wanga.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi!
Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.”
Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo.
Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa
pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona.
Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo,
ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo.
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda.
Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma.
Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Fuulani kwa Chauta ndi chimwemwe, inu maiko onse.
Tumikirani Chauta mosangalala. Bwerani pamaso pake mukuimba mokondwa.
Motero nthaŵi zonse ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, tsiku ndi tsiku ndidzachitadi zimene ndidalumbirazo.
Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Inu Mulungu. Ndidzakuimbirani zeze wa nsambo khumi,
Mwasandutsa kulira kwanga kuti kukhale kuvina, mwachotsa chisoni changa ndi kundipatsa chisangalalo.
Choncho ndisakhale chete, koma ndikutamandeni ndi mtima wonse. Choncho mtima wanga udzakuimbirani mosalekeza, Chauta, Mulungu wanga, ndidzakuthokozani mpaka muyaya.
Chifukwa chiyani mumaima kutali nafe, Inu Chauta? Chifukwa chiyani mumabisala pamene tili pa mavuto?
Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga.
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta!
Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima.
Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao.
Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.
Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu.
Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana.
Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze.
Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli.
Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri.
Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
“Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Amene Chauta adaŵaombola adzabwerera, ndipo adzafika ku Ziyoni akuimba mosangalala. Kumeneko adzakondwa mpaka muyaya, ndipo adzaona chimwemwe ndi chisangalalo. Chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Ndidzatonthoza mtima Ziyoni, ndidzaŵatonthoza mtima okhala ku mabwinja ake. Ngakhale dziko lake ndi chipululu, ndidzalisandutsa ngati Edeni. Ngakhale dziko lake ndi thengo, ndidzalisandutsa ngati munda wa Chauta. Kumeneko anthu adzakondwa ndi kusangalala, adzaimba nyimbo zondilemekeza ndi zondithokoza.
Mverani, alonda anu akukweza mau, akuimba pamodzi mokondwa, popeza kuti akuwona chamaso Chauta akubweranso ku Ziyoni.
Fuulani mokondwera inu mabwinja a Yerusalemu, pakuti Chauta waŵatonthoza mtima anthu ake, wapulumutsa Yerusalemu.
Anthuwo adzabwera akuimba mofuula pa mapiri a Ziyoni, adzakhala osangalala kwambiri chifukwa cha zabwino zochuluka zochokera kwa Chauta. Zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano, mafuta, anaankhosa ndi anaang'ombe. Moyo wao udzakhala ngati munda wothirira, ndipo sadzamvanso chisoni.
Anamwali adzavina mokondwa, achinyamata ndi okalamba omwe adzasangalala. Kulira kwao kuja ndidzakusandutsa chimwemwe. Ndidzaŵasangalatsa, ndidzaŵakondwetsa, nkuchotsa chisoni chao.
Ntchito nkumangoimba azeze ngati Davide, ndi kumangopeka nyimbo zoimbira pa zing'wenyeng'wenye.
“Koma mwana wake wamkulu uja anali ku munda. Pochokera kumundako, atafika pafupi ndi nyumba, adamva anthu akuimba ndi kuvina.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Nanga pamenepa nkutani? Ndidzapemphera ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga. Ndidzaimba ndi mtima wanga, komanso ndi nzeru zanga.
ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.”
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Pamene adalilandira, Zamoyo zinai zija, pamodzi ndi Akuluakulu 24 aja, zidagwa pansi pamaso pa Mwanawankhosayo. Aliyense mwa Akuluakuluwo anali ndi zeze ndiponso mikhate yagolide yodzaza ndi lubani. Lubaniyo ndi mapemphero a anthu a Mulungu.
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
Tsono ndidamva liwu lochokera kumwamba longa ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Liwu limene ndidaamvalo linkamveka ngati anthu akuimba azeze ao.
Mphesazo zidapondedwa m'chopondera mphesa kunja kwa mzinda. Ndipo m'chopondera mphesacho mudatuluka magazi nkumayenderera ngati mtsinje, kutalika kwake makilomita 300, kuzama kwake ngati mita ndi hafu.
Anthu aja ankaimba nyimbo yatsopano pamaso pa mpando wachifumu uja ndi pamaso pa Zamoyo zinai zija, ndi Akuluakulu aja. Panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kuiphunzira nyimboyo, kupatula anthu zikwi 144 aja amene anali ataomboledwa mu ukapolo wa dziko lapansi.
Kenaka ndidaona ngati nyanja ya galasi losanganiza ndi moto. Ndidaonanso anthu amene adapambana chilombo chija, fano lake lija, ndi nambala yotanthauza dzina lake. Anthuwo adaaimirira pamphepete pa nyanja yagalasi ija, m'manjamu ali ndi azeze oŵapatsa Mulungu.
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona.