M’mawu a Mulungu, nkhani ya cholowa imapezeka kale mu Chipangano Chakale, ponena za Mulungu akupatsa Aisraeli dziko lolonjezedwa. Popeza dzikolo linaperekedwa ndi Mulungu kwa mabanja osiyanasiyana, anthu sanaloledwe kugulitsa malo awo kwamuyasa.
Koma cholowa chenicheni, chomwe chimatikhudza ife lero, ndi madalitso auzimu omwe tili nawo monga ana a Mulungu. Aliyense amene akhulupirira Yesu Khristu ndi kumulandira ngati Mpulumutsi wake, amalandira cholowa mu Ufumu wa Kumwamba chomwe Atate akumwamba anakonzeratu onse amene amawalandira monga ana awo.
Lero, Mulungu akuika cholowa m’manja mwako kuti uchisangalale naye kosatha; ingokhulupirira mumtima mwako. Ngakhale utakumana ndi mavuto ovuta padziko lapansi, Mulungu wako sadzakusiya ndipo ali ndi zinthu zabwino zokukonzeratu, komwe sipadzakhala kuŵaŵa kapena kuvutika, ndipo palibe amene adzachoke nacho chimene chili chako.
kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba.
Chauta ndiye chuma changa ndi choloŵa changa. Tsogolo langa lili m'manja mwanu.
Malire a malo anga andikhalira mwabwino. Inde, ndalandira madalitso abwino ndithu.
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
Chauta amasamalira moyo wa anthu angwiro, ndipo choloŵa chao chidzakhalapo mpaka muyaya.
Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.
Tandipempha uwone, ndidzasandutsadi mitundu ya anthu kuti ikhale choloŵa chako, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala lako.
Koma masiku otsiriza ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana wake. Ndi mwa Iyeyu Mulungu adalenga zolengedwa zonse, namuika kuti alandire zinthu zonse ngati choloŵa chake.
Tsono mfumuyo ikuti, “Ndidzalalika zimene Chauta walengeza. Adandiwuza kuti, ‘Iwe ndiwe mwana wanga, Ine lero ndakubala.
Tandipempha uwone, ndidzasandutsadi mitundu ya anthu kuti ikhale choloŵa chako, ndipo dziko lonse lapansi lidzakhala lako.
Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ngwodala mtundu wa anthu amene Mulungu wao ndi Chauta, anthu amene Chauta waŵasankha akeake.
Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.
Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.
Nchifukwa chake pasakhale wina aliyense wonyadira anthu chabe. Zinthu zonse nzanu:
Paulo, Apolo ndi Kefa, dziko lapansi, moyo ndi imfa, zimene zilipo ndi zimene zilikudza. Koma ngakhale zonsezi nzanu,
inu ndinu ake a Khristu, ndipo Khristu ndi wake wa Mulungu.
Amatiyesa achisoni, komabe ndife okondwa masiku onse. Amatiyesa amphaŵi, komabe timalemeretsa anthu ambiri. Amatiyesa opanda kanthu, komabe tili ndi zonse.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Motero sindiwenso kapolo ai, koma mwana. Ndipo popeza kuti ndiwe mwana wake, Mulungu adakusandutsanso mloŵachuma wake.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu.
Adatisankhulira dzikoli kuti likhale choloŵa chathu, adatipatsa ife anthu a Yakobe dziko lokomali pakuti amatikonda.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Nyumba ndi chuma ndiye choloŵa chochokera kwa makolo, koma mkazi wanzeru ndi wochokera kwa Chauta.
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Koma inu ndinu anthu amene Mulungu adakutulutsani ku dziko la Ejipito, ng'anjo yotentha ija. Adakutulutsanimo kuti mukhale anthu akeake monga m'mene muliri leromu.
Uŵalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, oolowa manja, ndi okonda kugaŵana zinthu zao ndi anzao.
Pakutero adzadziwunjikira chuma chokoma ndi chokhalitsa chimene chidzaŵathandize kutsogoloko, kuti akalandire moyo umene uli moyo weniweni.
Abale, chimene ndikunena nchakuti munthu ndi thupi lake lamnofuli sangathe kuloŵa mu Ufumu wa Mulungu, ndipo zimene zimaola, sizingathe kuloŵa kumene zinthu siziwola.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Munthu ameneyo adzakhaladi pabwino, ana ake adzalandira dziko kuti likhale choloŵa chao.
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.
Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo adatipatsa madalitso aakulu ndi amtengowapatali amene Iye adatilonjeza. Adatero kuti mulandireko moyo wake wa Mulungu, mutapulumuka ku chivunde chimene chili pa dziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoipa.
Kumbukirani atumiki anu aja Abrahamu, Isaki ndi Israele ndiponso zija mudaŵalonjezazi molumbira pa dzina lanu, pamene mudaŵauza kuti, ‘Ndidzakupatsani zidzukulu zambiri, zochuluka ngati nyenyezi zakuthambo. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonse limene ndidalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lao mpaka muyaya.’ ”
Chauta akunena kuti, “Iwe Israele, ndikadakonda kukukhazika pakati pa ana anga, ndi kukupatsa dziko lokoma, choloŵa chokongola kwambiri kupambana maiko a mitundu ina ya anthu. Ndidaganiza kuti udzanditchula ‘Atate’, ndipo kuti sudzaleka kumanditsata.
Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero.
Sitifuna kuti mukhale aulesi, koma kuti mutsanzire anthu amene, pakukhulupirira ndi pakupirira, akulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Inu Mulungu, mwamva zimene ndalumbira popemphera. Inu mwandipatsa choloŵa chimene amalandira anthu oopa dzina lanu.
“Monga momwe dziko lapansi latsopano ndi dziko lakumwamba latsopano, zimene ndidzapange, zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, chonchonso zidzukulu zanu ndi dzina lanu zidzakhala mpaka muyaya.
Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.
Munthu wabwino amasiyira zidzukulu zake choloŵa, koma chuma cha munthu woipa amachilandira ndi anthu abwino.
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
Chilichonse chimene mungachite, muchichite ndi mtima wonse, ngati kuti mukuchitira Ambuye, osati anthu ai.
Paja mukudziŵa kuti Ambuye adzakupatsani mphotho. Mphothoyo ndi madalitso amene adalonjeza kudzapatsa anthu ake. Ambuye amene mukuŵatumikirawo ndi Khristu.
Anthu a Mulungu adzalandira dziko kuti likhale lao, ndipo adzakhala m'menemo mpaka muyaya.
Adachita zimenezi, kuti mwa kukoma mtima kwake tisanduke olungama pamaso pake, ndipo tikalandire moyo wosatha umene tikuuyembekeza.
“Choncho tsopano ndikukuikani m'manja mwa Mulungu, mau ake oonetsa kukoma mtima kwake akusungeni bwino. Mauwo ali ndi mphamvu zakukulitsa mpingo, ndi kukupatsani madalitso onse aja amene Mulungu akusungira anthu ake.
Ndipo uŵauze Aisraele kuti, ‘Munthu akafa opanda mwana wamwamuna, choloŵa chake chikhale cha mwana wake wamkazi.
M'dziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobe. Bambo wao adaŵapatsa choloŵa chimodzimodzi ngati alongo ao.
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Kalonga akapereka chigawo cha chuma chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo ndi ya ana akewodi, popeza kuti ndi chigawo cha choloŵa cha makolo.
Koma akapereka mphatso yotere kwa mmodzi mwa atumiki ake, idzakhala ya mtumikiyo mpaka pa chaka cha ufulu. Pamenepo mphatsoyo idzabwerera kwa kalonga uja, chifukwa chuma chake chonse ncha ana okha.
Pamenepo Mose adandilonjeza kuti, ‘Chifukwa choti wamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga, iweyo pamodzi ndi ana ako, udzalandiradi dziko limene walipondalo, kuti likhale choloŵa chako.’ ”
Koma Naboti adauza Ahabu kuti, “Ndithu, pali Chauta, sindingakupatseni choloŵa cha makolo anga.”
Ndi limenelitu dziko limene ndikulipereka kwa inu. Muloŵe ndi kukhazikika m'dzikoli limene Ine Chauta, Mulungu wanu, ndidalumbira kuti ndidzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, ndi zidzukulu zao zonse.”