Zimene ndimalankhula zikusonyeza zomwe zili mumtima mwanga. Sindinganene kuti ndikutumikira Mulungu ngati mawu anga akunyoza chilengedwe chake. Pali mphamvu yayikulu m'mawu aliwonse amene ndimalankhula. Ambuye wapatsa lilime langa mphamvu, ndipo ndine amene ndingasankhe kugwiritsa ntchito bwino mphamvu imeneyi, ndipo nditha kuchita izi ndi chithandizo cha Mzimu Woyera. Iye anditsogolera kuti ndilankhule zokondweretsa mtima wa Atate wanga wakumwamba, osati zachabe, zosapindulitsa ndipo zodetsa mzimu, koma zochokera ku nzeru za Wam'mwambamwamba.
Tsiku lililonse ndiyenera kusamala ndi mawu anga kuti asatsutsane ndi malamulo a Ambuye. Ndiyenera kupewa miseche, ndewu, ndi mawu onenera anansi zoipa. M'malo mwake, ndiyenera kukhala mwamtendere ndi anthu onse, kuti mwa ine muziyenda chikondi cha Yesu, ndipo mawu anga akhale okoma. Ndimakumbukira kuti ndikangotchula dzina la Yesu, chilichonse chingasinthe. Ndingapulumutse moyo wa munthu ngati ndingololera kutsogoleredwa ndi Mzimu wa Mulungu nthawi zonse.
Ndiyenera kugwiritsa ntchito bwino zonse zomwe Mulungu wandipatsa ndi kutumikira anansi anga mwachikondi, kukhala woyimira Yesu padziko lapansi. Ndikakumana ndi mavuto, ndiyenera kuzindikira mphamvu ya mawu anga ndi kunena kuti, "Ndisamala ndi mawu otuluka mkamwa mwanga." Ili ndi nthawi yoti ndidzipereke ndekha ndi kukhala ndi moyo wa Yesu.
Mawu anga ayenera kusonyeza mphamvu ya chisomo cha Mulungu ndi moyo wa Mzimu Woyera mwa ine. Mulungu atithandize kugwiritsa ntchito lilime lathu ngati chida cha mphamvu yake ndi chisomo chopulumutsa.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.
Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru, ozama ngati nyanja yamchere yaikulu, omweka ngati a mu mtsinje wothamanga.
Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Koma lilime palibe munthu amene angathe kuliŵeta. Ndi loipa, silidziŵa kupumula, ndipo ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
Pakamwa pa munthu wabwino ndi kasupe wa moyo, koma pakamwa pa munthu woipa pamabisa zandeu.
Paja anthu amenewo amanena kuti, “Tidzapambana ndi mau athu, pakamwa tili napo, nanga angatigonjetse ndani?”
Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa chiwonongeko chake. Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.
mwa mau oona, ndiponso mwa mphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili m'dzanja lathu lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo.
Tsiku lonse umakhalira kusinkhasinkha za kuwononga ena, lilime lako lili ngati lumo lakuthwa, ntchito yako nkunyenga.
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto.
Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Akadzakutengerani ku milandu, musadzade nkhaŵa nkumanena kuti, ‘Kodi tikakambe bwanji?’ Kapena kuti, ‘Kodi tikanene chiyani?’ Mudzapatsidwa pa nthaŵi imeneyo mau oti munene.
Ngakhale nditamalankhula zilankhulo za anthu kapenanso za angelo, koma ngati ndilibe chikondi, ndili ngati chitsulo chongolira, kapena chinganga chosokosera.
Mtima wa munthu womvetsa zinthu umafunitsitsa ndithu kudziŵa zambiri, koma m'kamwa mwa anthu opusa zauchitsiru zili pha!
Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
Alewe zoipa, azichita zabwino. Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuupeza.
Kulankhula kwabwino sikuyenerana ndi chitsiru. Nanji kulankhula kwabodza, kodi kungayenerane ndi mfumu?
Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.
Wofulumira kulankhula, zonena zake zimalasa ngati mpeni, koma mau a munthu wanzeru amachiza anzake.
Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga.
Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola.
Tsono nanenso ndidzalalika za kulungama kwanu. Ndidzakutamandani masiku onse, Inu Chauta.
Ngati wina akudziyesa woika mtima pa zopembedza Mulungu, koma nkukhala wosasunga pakamwa, chipembedzo chakecho nchopanda pake, ndipo amangodzinyenga.
M'kamwa mwanu musatuluke mau aliwonse oipa, koma muzinena mau okhaokha abwino ndi olimbitsa mtima monga kungafunikire, kuti mupindulitse anzanu omva mau anuwo.
Ana a njoka inu, mungathe bwanji kulankhula zabwino pamene muli oipa? Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
Nthaŵi zonse mau anu akhale okoma, opindulitsa ena, kuti potero mudziŵe m'mene muyenera kuyankhira munthu aliyense.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.
Koma tsopano musachitenso zonsezi, monga kukalipa, kukwiya, kuipa mtima, ndi mijedu. Pakamwa panu pasamatulukenso mau otukwana kapena onyansa.
Abale anga okondedwa, gwiritsani mau aŵa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma kulankhula asamafulumira, ndipo kukwiya asamafulumiranso.
Abale anga, muzikondwa ndithu mukamayesedwa ndi mavuto amitundumitundu.
Paja munthu wokwiya safikapo pa chilungamo chimene amafuna Mulungu.
Ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo, anthu adzazengedwa mlandu chifukwa cha mau aliwonse opanda pake amene adaalankhula.
Mwakuti chifukwa cha mau ako omwe mlandu udzakukomera kapena kukuipira.”
Koma nanga akuti chiyani? Akuti, “Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.” (Ameneŵa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timaŵalalika.)
Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.
Munthu wabwino amatulutsa zabwino m'chuma chabwino cha mumtima mwake. Nayenso munthu woipa amatulutsa zoipa m'chuma choipa cha mumtima mwake. Pajatu pakamwa pamalankhula zimene zadzaza mu mtima.”
Paja mau a Mulungu akuti. “Yemwe afuna kukondwera ndi moyo, ndi kuwona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa, ndiponso milomo yake kunena mabodza.
Moto umazima pakasoŵa nkhuni, chonchonso kumene kulibe kazitape, kulibenso ndeu.
Monga momwe aliri makala pa moto wonyeka ndiponso nkhuni pa moto woyaka, ndimonso amakhalira munthu wandeu poutsa mikangano.
Ambuye Chauta andiphunzitsa zoyenera kunena, kuti ndidziŵe mau olimbitsa mtima anthu ofooka. M'maŵa mulimonse amandidzutsa, amathwetsa makutu anga kuti ndimve, monga amachitira amene akuphunzira.
Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba, ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi.
Si chinthu choloŵa m'kamwa mwa munthu chimene chimamuipitsa ai, koma chotuluka m'kamwa mwake ndiye chimene chimamuipitsa.”
Nchitsiru chomwe chikakhala chete, chimakhala ngati munthu wanzeru. Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
Ngakhale chitsiru chomwe nkuti ndiponi pali chikhulupiriro, koma osati munthu wodziyesa wanzeru pamene ali wopusa.
Nchifukwa chake tsono tizifunafuna zimene zingathandize kuti pakhale mtendere ndiponso kugwirizana pakati pathu.
Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.
Inu abale, Mulungu adakuitanani kuti mukhale mfulu. Koma chenjerani kuti ufulu wanu umenewu usapatse mpata khalidwe lanu lokonda zoipa. Kwenikweni muzitumikirana mwachikondi.
Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.
Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziŵa zinthu, munthu wodekha mtima ndiye womvetsa zinthu.
Nchitsiru chomwe chikakhala chete, chimakhala ngati munthu wanzeru. Chikasunga pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.
Paja Malamulo onse a Mulungu amaundidwa mkota pa lamulo limodzi lija lakuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”
Abale anga, musachuluke ofuna kukhala aphunzitsi, chifukwa monga mudziŵa, aphunzitsife tidzaweruzidwa mouma koposa anthu ena onse.
Pakamwa pomwe pamatuluka mayamiko pomweponso pamatuluka matemberero. Abale anga, zoterezi siziyenera kumachitika.
Kodi kasupe amatulutsa madzi omweka ndi oŵaŵa pa dzenje limodzimodzi?
Abale anga, kodi mkuyu ungathe kubala zipatso za olivi, kapena mpesa kubala nkhuyu? Momwemonso kasupe wa madzi amchere sangathe kupereka madzi omweka.
Ndani mwa inu ali wanzeru ndi womvetsa zinthu? Aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru zimaongoleradi zochita zake zofatsa.
Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi wodzikonda, musamanyada ndi kutsutsana ndi choona pakunena mabodza.
Nzeru zotere si zochokera Kumwamba, koma ndi nzapansipano, ndi za anthu chabe, ndiponso nzochokera ku mizimu yoipa.
Pajatu pamene pali kaduka ndi kudzikonda, pomweponso pali chisokonezo ndi ntchito yoipa ya mtundu uliwonse.
Koma nzeru zochokera Kumwamba, poyamba nzangwiro, kuwonjeza apo nzamtendere, zofatsa ndi zomvera bwino. Ndi za chifundo chambiri, ndipo zipatso zake zabwino nzochuluka. Nzeruzo sizikondera kapena kuchita chiphamaso.
Ndipo chilungamo ndiye chipatso cha mbeu zimene anthu odzetsa mtendere amafesa mu mtendere.
Paja tonsefe timalakwa pa zinthu zambiri. Ngati alipo amene salakwa pakulankhula, ndiye kuti ndi wangwirodi ameneyo, mwakuti angathe kulamuliranso thupi lake lonse.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Amene amakukonda, ngakhale akupweteke, chikondi chake chimakhalapobe, mdani wako ngakhale akumpsompsone, nkunyenga chabe kumeneko.