Mawu a Mulungu ndi nyali yowunikira mtima wanga, yondiwongolera, yondipatsa nzeru kuchokera kumwamba. Ndiyo chinsinsi chotsegulira njira yolankhulirana ndi Atate wanga wakumwamba komanso Mwana wawo wokondedwa Yesu Khristu.
Ndikagwiritsa ntchito Malemba moyenera, mawu anga amakhala ndi mphamvu chifukwa Mawu a Mulungu ndi oona, okhulupirika, ndipo nthawi zonse amapezeka ndikawafuna.
Ndiyenera kuphunzira, kusinkhasinkha, kufufuza, ndi kusunga Malemba mumtima mwanga kuti ndidziwe choonadi ndi kumasulidwa ku mabodza onse a mdani.
"Malemba onse ndi ouziridwa ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kulangiza, ndi kulera m'chilungamo." (2 Timoteo 3:16)
Mau a Mulungu ankafalikira ponseponse, ndipo ophunzira ankachulukirachulukira ndithu ku Yerusalemu. Ansembe omwe ambirimbiri ankamvera chikhulupirirocho.
Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu.
Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu.
Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana.
Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena.
Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.
koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta, nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku. Munthuyo ali ngati mtengo wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi, ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake, umene masamba ake safota konse. Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.
Malonjezo a Chauta ndi angwiro, ali ngati siliva womkometsa m'ng'anjo yamoto, woyeretsedwa kasanunkaŵiri.
Mulungu wathuyo, zochita zake nzangwiro, mau ake sapita pachabe, Iye ndiye chishango choteteza onse othaŵira kwa Iye.
Mau a Chauta ngangwiro, amapatsa munthu moyo watsopano. Umboni wa Chauta ndi wokhulupirika, umaŵapatsa nzeru amene alibe. Malangizo a Chauta ndi olungama, amasangalatsa mtima. Malamulo a Chauta ndi olungama, amapatsa mtima womvetsa.
Chauta adalankhula ndipo zakumwamba zidalengedwa. Zonse zakumeneko zidalengedwa pamene Iye adalankhula mau ake.
Kodi mnyamata angathe bwanji kusunga makhalidwe ake kuti akhale angwiro? Akaŵasamala potsata mau anu.
Kufotokozera mau anu kumakhala ngati kuŵala, kumapatsa nzeru za kumvetsa kwa anthu opanda nzeru.
Mwana wanga, mvetsetsa mau anga. Tchera khutu ku zimene ndikunena. Zisachoke m'mutu mwakomu, uzisunge bwino mumtima mwako. Paja zimampatsa moyo amene wazipeza, zimachiritsa thupi lake lonse.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Ndalumbira dzina langa lomwe, pakamwa panga palankhula moona mau amene sadzasinthika konse, akuti, ‘Bondo lililonse lidzandigwadira, anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.’
Chauta, Mpulumutsi wako, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ine ndine Chauta, Mulungu wako, amene ndimakuphunzitsa, kuti zinthu zikuyendere bwino. Ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuitsata.
“Mvula ndi chisanu chambee zimatsika kuchokera kumwamba, ndipo sizibwerera komweko, koma zimathirira nthaka. Zimameretsa ndi kukulitsa zomera, kenaka nkupatsa alimi mbeu ndi chakudya. Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Tsono Chauta adatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga. Ndipo adandiwuza kuti, “Tamvera, ndikuika mau anga m'kamwa mwako.
Nchifukwa chake tsono Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, akuti, “Poti iwowo atero, mau anga ndidzaŵasandutsa moto m'kamwa mwako, anthuwo ndidzaŵasandutsa nkhuni, ndipo motowo udzaŵapserezeratu.”
Nditamva mau anu, ndidaŵalandira bwino, mauwo adandipatsa chimwemwe ndi chisangalalo. Paja Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndimadziŵika ndi dzina lanu.
“Kodi suja mau anga amatentha ngati moto? Kodi suja mau anga ali ngati nyundo imene imaphwanya thanthwe?
Tsono uŵauze kuti, Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso ai. Ndidzachitadi chilichonse chimene ndanena. Ndikutero Ine Chauta!”
Koma Yesu adati, “Malembo akuti, “ ‘Munthu sangakhale moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mau onse olankhula Mulungu.’ ”
“Munthu aliyense womva mau angaŵa nkumaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu wanzeru amene adaamanga nyumba yake pa thanthwe.
Zophunzitsa zake anthu zidaaŵagwira mtima kwambiri, chifukwa ankalankhula moonetsa ulamuliro ngati mwiniwake.
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Pachiyambi pa zonse Iye amene amatchedwa dzina loti Mau, anali alipo kale. Anali kwa Mulungu, ndipo anali Mulungu.
Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.
“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo.
Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo.
Yesu adauza anthu amene adamkhulupirirawo kuti, “Ngati mumvera mau anga nthaŵi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. Mudzadziŵa zoona zenizeni, ndipo zoonazo zidzakusandutsani aufulu.”
Pamenepo anthu amene adamvera mau akewo adabatizidwa, ndipo tsiku limenelo anthu ngati zikwi zitatu adaonjezedwa pa gulu lao.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Koma nanga akuti chiyani? Akuti, “Mau sali nawe kutali, ali pakamwa pako, ndiponso mumtima mwako.” (Ameneŵa ndiwo mau a chikhulupiriro amene timaŵalalika.)
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Ndinkachita zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisakhazikike pa nzeru za anthu, koma chikhazikike pa mphamvu za Mulungu.
Mulungu adzakupulumutsani ndi Uthenga Wabwinowu, ngati musunga bwino mau ake monga ndidakulalikirani. Popanda kutero, bwenzi mutangokhulupirira pachabe.
Ifetu sitili ngati anthu ena ambiri amene amangochita malonda ndi mau a Mulungu. Koma, popeza kuti tili mwa Khristu, ngati anthu otumidwa ndi Mulungu, timalankhula moona, molingana ndi kufuna kwake.
Takaniratu njira zonse zochititsa manyazi zimene anthu amatsata mobisika. Sitichita kanthu monyenga kapena kupotoza mau a Mulungu; koma pakulankhula zoona poyera pamaso pa Mulungu, tifuna kuti anthu onse ativomereze m'mitima mwao.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake.
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
pakuŵauza mau opatsa moyo. Motero ine ndidzakhala ndi chifukwa chonyadira pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu. Pakuti pamenepo padzadziŵika kuti sindidathamange pachabe pa mpikisano wa liŵiro, ndipo khama langa pa ntchito silidapite pachabe.
Gwero la zonsezi ndi chiyembekezo chimene muli nacho chodzalandira zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Mudamva za zimenezi pamene mau oona, adakufikani poyamba paja. Mau oonawo ndi Uthenga Wabwino.
Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu, ngati wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi, wolalika mau a choona mwachilungamo.
Ukudziŵanso kuti kuyambira ukali mwana waŵazoloŵera Malembo Oyera, amene angathe kukupatsa nzeru zopulumukira pakukhulupirira Khristu Yesu. Malembo Oyera onse ndi Mulungu amene adaŵalembetsa mochita ngati kuŵauzira, ndipo amathandiza pakuphunzitsa choona, pakutsutsa zolakwa, pakuwongola zokhota, ndi pakuphunzitsa anthu za kukhala olungama. Motero Malembo amathandiza munthu wa Mulungu kukhala wokhoza kwenikweni, ndi wokonzekeratu kuchita ntchito yabwino iliyonse.
Asunge mogwiritsa mau okhulupirika, amene ali ogwirizana ndi zimene tidaphunzitsidwa. Pakutero adzatha kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona, ndiponso kugonjetsa otsutsana nacho.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Paja mau a Mulungu ndi amoyo ndi ogwira ntchito mwamphamvu. Ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse. Amabaya mpaka molumikizirana mwa moyo ndi mzimu, ndiponso molumikizirana mfundo ndi mafuta a m'mafupa. Amaweruza ngakhale zimene anthu amalingalira ndi kulakalaka m'mitima mwao.
Pokhala ndi chikhulupiriro timamvetsa kuti zonse zimene zilipo zidalengedwa ndi mau a Mulungu, mwakuti zinthu zoonekazi zidachokera ku zinthu zosaoneka.
Muzikumbukira atsogoleri anu amene ankakulalikirani mau a Mulungu. Muzilingalira za moyo wao ndi m'mene adafera, ndipo muzitsanzira chikhulupiriro chao.
Mwa kufuna kwake mwiniwakeyo, adatipatsa moyo kudzera mwa mau ake oona, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, ife tikhale ngati zipatso zoyamba zimene Iye wadzipatulira.
Nchifukwa chake siyani chizoloŵezi chilichonse chonyansa, ndiponso kuipamtima kulikonse. Muŵalandire mofatsa mau amene Mulungu adabzala m'mitima mwanu, pakuti ndiwo angathe kukupulumutsani.
Chimodzimodzinso lilime: ndi kachiwalo kakang'ono, komabe limadzitama kuti nkuchita zazikulu. Tangoganizani kukula kwake kwa nkhalango imene ingayatsidwe ndi kalilaŵi kakang'ono ka moto. Tsonotu lilime limatentha ngati moto. Chifukwa chokhala pakati pa ziwalo zathu limawanditsa zoipa m'thupi monse. Limaipitsa khalidwe lonse la munthu. Limayatsa moto moyo wathu wonse kuyambira pobadwa mpaka imfa; ndipo moto wake ngwochokera ku Gehena.
Pakuti mwa mwachita kubadwanso, moyo wake si wochokera m'mbeu yotha kuwonongeka, koma m'mbeu yosatha kuwonongeka. Mbeuyi ndi mau a Mulungu, mau amoyo ndi okhala mpakampaka. Paja mau a Mulungu amanena kuti, “Anthu onse ali ngati udzu, ulemerero wao uli ngati duŵa lakuthengo. Udzu umauma, ndipo duŵa limathothoka, koma mau a Ambuye ngokhala mpaka muyaya.” Mau ameneŵa ndi Uthenga Wabwino umene walalikidwa kwa inu.
Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,
Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Motero tikudziŵa ndithu tsopano kuti mau aja a anereriŵa ngoona. Nkwabwino tsono kuti muŵayang'anitsitse ngati nyale yoŵala m'malo amdima, kufikira nthaŵi imene kudzayambe kucha, pamene nyenyezi yam'mamaŵa idzayambe kuŵala m'mitima mwanu. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wochuluka, pakumdziŵa Iyeyo ndiponso Yesu Ambuye athu. Koma choyamba mumvetse kuti munthu payekha sangathe kumasulira mau a aneneri olembedwa m'Malembo. Paja mau a aneneri sadadze konse ndi kufuna kwa munthu yekha, koma Mzimu Woyera adaŵalankhulitsa mau ochokera kwa Mulungu.
Apa akuiŵala dala kuti kalelo Mulungu atanena mau, zakuthambo zidalengedwa, ndipo dziko lapansi lidapangidwa ndi madzi kufumira m'madzi. Ndipo ndi madzi okhaokhawo dziko lapansi la masiku amenewo lidamizidwa ndi kuwonongedwa. Koma Mulungu ndi mau omwe aja adasunga zakuthambo ndi dziko lapansi la masiku ano kuti adzazitenthe ndi moto. Akuzisunga kufikira tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osasamala za Iye.
Tikukulemberani za Iye uja amene adaalipo kuyambira pa chiyambi, amene tidamumva ndipo tidamuwona ndi maso athu, amene tidampenya ndithu, ndipo tidamkhudza ndi manja athu: Iyeyo ndiye Mau opatsa moyo.
Ndimakulemberani inu ana, chifukwa Atate mumaŵadziŵa. Ndimakulemberani inu atate, chifukwa mumamdziŵa Iye amene alipo kuyambira pa chiyambi. Ndimakulemberani inu achinyamata, chifukwa ndinu amphamvu, mau a Mulungu amakhala mwa inu, ndipo mwampambana Woipa uja.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Ngwodala munthu amene aŵerenga momveka mauŵa. Ngodalanso anthu amene amvera mau a m'buku limeneli loneneratu zam'tsogolo, ndi kutsata zimene zalembedwamo. Pakuti nthaŵi yoti zichitike zonsezi ili pafupi.
Akuti: Ntchito zanu zonse ndikuzidziŵa. Ndakutsekulirani pa khomo, ndipo palibe amene angatsekepo. Ndikudziŵa kuti mphamvu zanu nzochepa, komabe mwasunga mau anga, ndipo simudandikane.
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Mwana wanga, usaiŵale malangizo angaŵa, koma mtima wako usunge malamulo anga. Ukatero, nkhokwe zako zidzadzaza ndi dzinthu dzambiri, mbiya zako zidzachita kusefukira ndi vinyo. Mwana wanga, usanyoze malango a Chauta, usatope nako kudzudzula kwake. Paja Chauta amadzudzula yemwe amamkonda, monga momwe atate amamchitira mwana wokondwera naye. Ngwodala munthu amene wapeza nzeru, amene walandira nzeru zomvetsa zinthu, pakuti phindu la nzeru nloposa phindu la siliva, nloposanso ndi phindu la golide lomwe. Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali. Palibe chinthu chochilakalaka cholingana ndi nzeruyo. Ndi nzeru imene imakupatsa moyo wautali. Ndi nzeru imene imakuninkha chuma ndi ulemu. Nzeru imakudzeretsa m'njira za chisangalalo, nimakuyendetsa mumtendere mokhamokha. Nzeru ili ngati mtengo woŵapatsa moyo oigwiritsa. Ngodala amene amaikangamira molimbika. Pamene adakhazikitsa dziko lapansi, Chauta adaonetsa nzeru. Pamene adakhazikitsa zakumwamba, adaonetsa nzeru za kumvetsa bwino. Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka, ndipo udzakhala ndi moyo wabwino kwambiri.
Mwana wanga, uzitsata malamulo a atate ako, usasiye zimene adakuphunzitsa amai ako. Zimenezi uzimatirire pamtima pako masiku onse, uzimangirire m'khosi mwako. Pamene ukuyenda, zidzakulozera njira. Pamene ukukhala chogona, zidzakulonda. Pamene ukudzuka, zidzakulangiza.
Ndidaika mau anga m'kamwa mwanu, ndipo ndidakutetezani ndi dzanja langa. Ndidayalika zakuthambo, ndi kukhazika maziko a dziko lapansi. Ndidauza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
“Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ”
Koma mbeu zofesedwa pa nthaka yabwino zija zikutanthauza munthu amene amamva mau a Mulungu naŵamvetsa. Munthu wotere amaberekadi zipatso, mwina makumi khumi, mwina makumi asanu ndi limodzi, mwina makumi atatu.”
Munthu wochokera kwa Mulungu amatchera khutu ku mau a Mulungu. Koma inu simuchokera kwa Mulungu ai, nchifukwa chake simutchera khutu.”
Yesu adati, “Ngati munthu andikonda, adzatsata zimene ndanena Ine. Atate anga adzamkonda, ndipo Ife tidzabwera nkukhazikika mwa iye.
Motero mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira ndi kugwira ntchito mwamphamvu.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Ine Yohane, ndikuchenjeza aliyense womva mau a m'buku lino oneneratu zam'tsogolo. Wina akadzaonjezerapo kanthu pa mau ameneŵa, Mulungu adzamuwonjezera miliri ija yalembedwa m'buku munoyi. Ndipo wina akadzachotsapo kanthu pa mau a m'buku lino loneneratu zam'tsogolo, Mulungu adzamchotsera gawo lake la zipatso za mtengo wopatsa moyo uja, ndi malo ake omwe mu Mzinda Woyera uja, monga zalembedwera m'buku muno.