Magazi a Khristu ali ndi mphamvu zosaneneka, akundipatsa ine moyo ndi moyo wosatha. Magazi akewa akunditsuka ku machimo onse ndi kundichiritsira matenda onse a thupi, a m'maganizo ndi a m'moyo wanga.
Palibe chomwe chingalepheretse mphamvu ya magazi a Yesu; palibe nsembe ina iliyonse yomwe ingandimasule ndi kundisintha monga kulengeza kuti Magazi a Yesu Khristu ali ndi mphamvu. Nsembe ya pa mtanda ikundiombola ku machimo anga; ndikamayang'ana magazi ake kuti anditsuke ndi kundichapa ku zoipa zanga, ndimamasulidwa ndipo ndimatha kuyandikira kwa Atate wanga wakumwamba mwaufulu.
Dontho lililonse la magazi lomwe linatuluka pa mtanda limasonyeza chikondi cha Yesu kwa ine. Ndiyenera kuyamikira lero chikondi chachikulu chimenechi ndi kusangalala nacho, chifukwa magazi ake andifikira ndipo ndine womasuka kuyenda m'chifuniro cha Ambuye.
Pakuti popanda kuthiridwa magazi palibe chikhululukiro. Aheberi 9:22 amandikumbutsa kuti malinga ndi chilamulo, pafupifupi chilichonse chimatsukidwa ndi magazi; ndipo popanda kuthiridwa magazi palibe chikhululukiro.
Koma tikamayenda m'kuŵala, monga Iye ali m'kuŵala, pamenepo tikuyanjana tonsefe. Ndipo magazi a Yesu, Mwana wake, amatitsuka ndi kutichotsera tchimo lililonse.
Nanji tsono magazi a Khristu, angathe kuchita zoposa. Mwa Mzimu wamuyaya Iye adadzipereka ngati nsembe yopanda chilema kwa Mulungu. Ndiye kuti magazi ake adzayeretsa mitima yathu pakuichotsera ntchito zosapindulitsa moyo, kuti tizitumikira Mulungu wamoyo.
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu.
Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Chifukwa cha chimenechi, Yesu nayenso adafera kunja kwa mzinda, kuti pakutero ayeretse anthu ndi magazi ake.
Magaziwo adzakhala chizindikiro pa nyumba zimene mumakhalamo. Ndikadzangoona magaziwo, ndidzakupitirirani inuyo, ndipo mliri wosakaza sudzakugwerani, pamene ndidzakanthe dziko la Ejipito.
Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Malinga ndi Malamulo a Mosewo pafupifupi zonse zimayeretsedwa ndi magazi, ndipo machimo sakhululukidwa popanda kukhetsa magazi.
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Mzimu Woyera adakuikani kuti muziyang'anira mpingo wonse. Tsono mudzisamale nokha, ndipo musamalenso mpingowo. Ŵetani nkhosa za mpingo wa Ambuye umene Iwo adauwombola ndi magazi aoao.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya. Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake.
Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu. Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen.
Yesu Khristu ndiye amene adabwera kudzera mwa madzi ndi mwa magazi. Sadabwere mwa madzi okha, koma mwa madzi ndi mwa magazi omwe. Ndipo Mzimu Woyera ndiye amene amachitirapo umboni, pakuti Mzimuyo ndiye choona.
Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Iyeyo ndiye nsembe yopepesera machimo athu, ndipo osati athu okha, komanso a anthu a pa dziko lonse lapansi.
Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu. Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Nchifukwa chake tsono, munthu akadya mkate umenewu, kapena kumwa chikho cha Ambuyechi mosayenera, apalamula mlandu wonyoza thupi la Ambuye ndiponso magazi ao.
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera. Ndiye popeza kuti tsopano chifukwa cha magazi ake tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, Iyeyo adzatipulumutsa koposa pamenepo ku mkwiyo wa Mulungu.
Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.” Pakuti nthaŵi zonse mukamadya mkate umenewu, ndi kumwa chikho chimenechi, mumalalika imfa ya Ambuye, mpaka adzabwerenso.
Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndipo Ine ndimakhala mwa iyeyo.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Mukudziŵa bwino chimene adakuwombola nachoni ku khalidwe lanu lachabe limene mudalandira kwa makolo anu. Sadakuwomboleni ndi ndalama zotha kuwonongeka zija, siliva kapena golide ai, adakuwombolani ndi magazi amtengowapatali a Khristu amene adakhala ngati mwanawankhosa wopanda banga kapena chilema.
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
Koma ine sindinganyadire kanthu kena kalikonse, koma mtanda wa Ambuye athu Yesu Khristu basi. Popeza kuti Iye adafa pa mtanda, tsopano zapansipano kwa ine zili ngati zakufa, ndipo inenso kwa zapansipano, ndili ngati wopachikidwa.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Yesu adati, “Ndithu ndikunenetsa kuti ngati simudya thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense wodya thupi langa ndi kumwa magazi anga, ali ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.
Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Adati, “Ndidachimwa pakupereka munthu wosalakwa kuti aphedwe.” Koma iwo adati, “Ife tilibe nazo kanthu. Izo nzako.”
Ankaimbira Mwanawankhosa uja nyimbo yatsopano iyi yakuti: “Ndinu oyenera kulandira bukuli ndi kumatula zimatiro zake. Pakuti mudaaphedwa, ndipo ndi imfa yanu mudaombolera Mulungu anthu a fuko lililonse, a chilankhulo chilichonse, ndi a mtundu uliwonse.
Ine ndidati, “Mbuyanga, mukudziŵa ndinu.” Ndipo iye adandiwuza kuti, “Ameneŵa ndi amene adapambana m'masautso aakulu aja. Adachapa mikanjo yao ndi kuiyeretsa m'magazi a Mwanawankhosa.
Kodi inu simukudziŵa kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa zonsezi kuti aloŵe mu ulemerero wake?”
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Tidziŵa kuti mkhalidwe wathu wakale udapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kuti khumbo lathu lokonda machimo liwonongeke, ndipo tisakhalenso akapolo a uchimo.
Iye sadaumire ngakhale Mwana wakewake, koma adampereka chifukwa cha ife tonse. Atatipatsa Mwana wakeyo, nanga Iye nkulephera kutipatsanso zonse mwaulere?
Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.
Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzakhala woyera. Mundisambitse, ndipo ndidzayera kupambana chisanu chambee.
Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Adapita patsogolo pang'ono, nadzigwetsa choŵeramitsa nkhope pansi nkuyamba kupemphera. Adati, “Atate, ngati nkotheka, chindichokere chikho chamasautsochi. Komabe chitani zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Adati, “Atate, ngati mukufuna, mundichotsere chikho chamasautsochi. Komabe muchite zimene mukufuna Inu, osati zimene ndikufuna Ine ai.”
Zikadatero, akadayenera kumamva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri chilengedwere cha dziko lapansi. Koma monga zilirimu, waoneka kamodzi kokha pakutha pake pa nthaŵi yotsiriza, kuti achotse uchimo pakudzipereka yekha nsembe.