Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.
Pokhala ndi chikhulupiriro, Abele adapereka kwa Mulungu nsembe yopambana ya Kaini, navomerezedwa kuti ngwolungama, chifukwa Mulungu mwiniwake adaamchitira umboni pakulandira zopereka zake. Mwakuti ngakhale iye adafa, koma chifukwa cha chikhulupiriro chakecho, akulankhulabe mpaka pano.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Munthu asakupeputse poona kuti ndiwe wachinyamata, koma ukhale chitsanzo kwa akhristu onse pa mau, pa mayendedwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima.
Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzatamanda dzina lanu pa msonkhano wa anthu anu.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera.
Amene amakhulupirira Mwana wa Mulungu, ali nawo umboniwo mumtima mwake. Amene sakhulupirira Mulungu, amayesa kuti Mulungu ndi wonama, chifukwa sakhulupirira umboni umene Mulungu adachitira Mwana wake.
koma muzilemekeza Khristu m'mitima mwanu ngati Mbuye wanu. Khalani okonzeka nthaŵi iliyonse kuŵayankha mofatsa ndi mwaulemu anthu okufunsani za zimene mumayembekeza.
Pakamwa panga padzalankhula tsiku lonse za ntchito zanu zolungama ndi za chipulumutso chanu, popeza kuti sindidziŵa chiŵerengero chake. Ndidzabwera ndi uthenga wofotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta. Ndidzatamanda chilungamo chanu chokha.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Chomwechonso inuyo muziwonetsa kuŵala kwanu pamaso pa anthu, kuti ataona ntchito zanu zabwino azilemekeza Atate anu akumwamba.
Usachite manyazi tsono kuchitira umboni Ambuye athu. Usachitenso manyazi chifukwa cha ine amene ndili m'ndende chifukwa cha iye, koma umve nao zoŵaŵa chifukwa cha Uthenga Wabwino, ndi chithandizo cha mphamvu za Mulungu.
“Aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate anga amene ali Kumwamba.
Tsono adaŵauza kuti, “Pitani ku dziko lonse lapansi, kalalikireni anthu onse Uthenga Wabwino.
Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira.
Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa.
Musapereke chiwalo chilichonse cha thupi lanu ku uchimo, kuti chigwire ntchito zotsutsana ndi chilungamo. Inu mudzipereke kwa Mulungu, monga anthu amene anali akufa, koma tsopano ali amoyo. Ndipo mupereke ziwalo zanu zonse kwa Mulungu, kuti zigwire ntchito zachilungamo.
Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.
Tsopano ndili nawo mau akulu a mpingo amene ali pakati panu, ine mkulu mnzao. Ndinenso mboni ya zoŵaŵa za Khristu, ndipo ndikuyembekeza kudzalandira nao ulemerero umene uti udzaoneke.
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.
Ndimonso amachitira mau ochokera m'kamwa mwanga. Sadzabwerera kwa Ine popanda phindu lake, koma adzachita zonse zimene ndifuna, ndipo zimene ndidaŵatumira zidzayenda bwino.
Ine ndimadzichitira ndekha umboni, nawonso Atate amene adandituma amandichitira umboni.”
Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno,
Pa mbali yathu, timathokoza Mulungu kosalekeza. Timatero chifukwa chakuti pamene mudamva mau a Mulungu amene tidakulalikirani, mudaŵalandira osati ngati mau a anthu chabe, koma monga momwe aliri ndithu, mau a Mulungu. Mauwo ndi omwe akugwira ntchito mwa inu okhulupirira.
Mumaphunzira Malembo mozama, chifukwa mumaganiza kuti mupezamo moyo wosatha. Ndipotu ndi Malembo omwewo amene akundichitira umboni!
Ndipo adatilamula kuti tikalalikire anthu onse, ndi kuchita umboni kuti Iyeyo ndiye amene Mulungu adamsankha kukhala Woweruza anthu amoyo ndi akufa omwe.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake.
Ndine, Yohane, mbale wanu, ndipo ngati mnzanu wokhulupirira Yesu, ndili nanu limodzi mu ufumu wa Mulungu, komanso m'masautso ndi m'kupirira kosatepatepa. Ndidaponyedwa pa chilumba cha Patimosi, chifukwa cha kulalika mau a Mulungu ndi kuchitira Yesu umboni.
nchifukwa chake ndilikumva masautsoŵa. Koma sindichita manyazi, pakuti ndimamdziŵa Iye amene ndakhala ndikumkhulupirira, ndipo sindikayika kuti Iyeyo angathe kusunga bwino, mpaka tsiku la chiweruzo, zimene adandisungiza ine.
Malamulo anu ndiye madalitso anga mpaka muyaya, zoonadi, ndiwo amene amasangalatsa mtima wanga.
Komabe pamene ndikulalika Uthenga Wabwino, apo pokha palibe ponyadira ai, popeza kuti ndi Ambuye amene adachita kundilamula zimenezo. Tsoka kwa ine ngati sindiulalika Uthenga Wabwinowo.
Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi.
Koma chifukwa cha Khristu, zomwe kale ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziwona kuti nzosapindula. Zoonadi, zonse ndikuziwona kuti nzosapindulitsa poziyerekeza ndi phindu lopambana la kudziŵa Khristu Yesu, amene ndi Ambuye anga. Chifukwa cha Khristuyo ndidalolera kutaya zonse, nkumaziyesa zinyalala, kuti potero phindu langa likhale Khristu,
Koma dzuka, imirira. Pakuti ndakuwonekera kuti ndikuike kuti ukhale mtumiki wanga ndi mboni yanga. Ndifuna kuti ukhale mboni ya m'mene wandiwonera lero, ndiponso ya zimene ndidzakuwonetsa m'tsogolo.
Koma ngati mumva zoŵaŵa chifukwa chakuti ndinu akhristu, musachite manyazi, koma mulemekeze Mulungu chifukwa cha dzinalo.
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Amene akufotokoza zimenezi akuti, “Indedi, ndikubwera posachedwa.” Inde, bwerani, Ambuye Yesu.
Pakati pa anthu onse a Mulungu ine ndine wamng'ono koposa, komabe Mulungu adandipatsa ineyo ntchito iyi, yakuti ndilalikire anthu a mitundu ina za chuma chopanda malire, chimene Mulungu amatipatsa mwa Khristu.
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”
Moyowo udaoneka, ndipo ife tidauwona. Tikuuchitira umboni, ndipo tikukulalikirani za moyo wosatha, umene unali kwa Atate ndipo udatiwonekera.
Adzapita nanu kwa nduna ndi mafumu chifukwa cha Ine, mwakuti mudzandichitira umboni pamaso pao, ndi pa anthu a mitundu ina.
Ngodala amene amasunga malamulo a Chauta, amene amafunafuna Chauta ndi mtima wao wonse,
kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu.
Koma Petro ndi atumwi enawo adati, “Tiyenera kumvera Mulungu koposa kumvera anthu.
Simoni Petro adati “Ambuye, nanga tingapitenso kwa yani? Muli nawo ndinu mau opatsa moyo wosatha. Ife ndiye tikukhulupirira ndipo tikudziŵa kuti ndinu Woyera uja wochokera kwa Mulungu.”
Sikuti tikufuna kuchita ngati kukulamulirani pa zoti muzikhulupirira, pakuti pa mbali ya chikhulupiriro chanu, ndinu okhazikika ndithu. Makamaka tingofuna kugwirizana nanu kuti mukhale okondwa.
Okhulupirira amene adabalalika aja adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino.
Koma Yesu adati, “Iyai, odala ndi anthu amene amamva mau a Mulungu naŵagwiritsa ntchito.”
Motero munthu amakhulupirira chifukwa cha zimene wamva, ndipo zimene wamvazo zimachokera ku zolalika za Khristu.
Popeza kuti ponse pozungulira pali mboni zambirimbiri chotere, tiyeni tichotse kalikonse kotichedwetsa, makamaka tchimo limene limatikangamira, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu.
Inde kuchokera kwa inu mau a Ambuye adakafika ku Masedoniya ndi ku Akaiya, ndipo kuwonjezera apo mbiri yakuti mudakhulupirira Mulungu idawanda ponseponse. Motero palibe chifukwa chakuti ife nkunenapo kanthu.
“Iyai, iwe bwerera kwanu, ukafotokoze zazikulu zimene Mulungu wakuchitira.” Munthuyo adapitadi kwao nkumakalengeza mumzinda monse zazikulu zimene Yesu adaamchitira.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ife taona, ndipo tikuchita umboni, kuti Atate adatuma Mwana wake kuti adzakhale Mpulumutsi wa anthu a pa dziko lonse lapansi.
Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”
Lengezani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse.
Chachikulu nchakuti mayendedwe anu akhale oyenerana ndi Uthenga Wabwino wonena za Khristu. Ngakhale ndibwere kudzakuwonani, kapena ndikhale kutali, ndikufuna kumva kuti mukulimbika ndi mtima umodzi. Ndikufunanso kumva kuti momvana ndi mothandizana mukumenya nkhondo chifukwa chokhulupirira Uthenga Wabwino,
Tsono ndife akazembe oimirira Khristu, ndipo kudzera mwa ifeyo Mulungu mwini ndiye akulankhula nanu mokudandaulirani. Tikukupemphani m'dzina la Khristu kuti muvomere kuyanjananso ndi Mulungu.
Asamariya ambiri a m'mudzi muja adakhulupirira Yesu chifukwa cha umboni wa mai uja, wakuti, “Iye wandiwuza zonse zimene ndidachita.”
Iyeyu adaabwera ngati mboni, kudzachitira umboni kuŵala kuja, kuti anthu onse akhulupirire chifukwa cha umboni wakewo.
Anthu onse angathe kuwona kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, yolembedwa kudzera mwa ife, osati ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa zolembapo zamiyala koma m'mitima mwa anthu.
Chimene tidachiwona ndi kuchimva, tikukulalikirani, kuti inunso mukhale a mtima umodzi ndi ife. Kuyanjana kwathu tikuyanjana ndi Atate, ndiponso ndi Mwana wao, Yesu Khristu.
Koma Nkhoswe ija, Mzimu Woyera amene Atate adzamtuma m'dzina langa, ndiye adzakuphunzitseni zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndidakuuzani.
Mboni za zimenezi ndi ifeyo ndiponso Mzimu Woyera amene Mulungu adampereka ngati mphatso kwa anthu omvera Iye.”
Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu.
Abale, inetu pamene ndidafika kwanu kuti ndikulalikireni chinsinsi chimene Mulungu adatiwululira, sindidayese kulankhula mwaluso, ngati munthu wodziŵa zapatali. Ifeyo Mulungu adatiwululira zimenezi mwa Mzimu Woyera. Pajatu Mzimuyo amadziŵa zinthu zonse kotheratu, ngakhalenso maganizo ozama a Mulungu. Kodi za munthu angazidziŵe ndani, osakhala mzimu wa mwiniwake yemweyo umene uli mwa iyeyo? Momwemonso palibe munthu amene angadziŵe za Mulungu, koma Mzimu wa Mulungu Mwini. Ife sitidalandire mzimu wa dziko lino lapansi, koma tidalandira Mzimu Woyera wochokera kwa Mulungu, kuti adzatithandize kumvetsa zimene Mulunguyo adatipatsa mwaulere. Timalankhula zimenezi osati ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za anthu, koma ndi mau amene Mzimu Woyera amatiphunzitsa. Timaphunzitsa zoona zauzimu kwa anthu amene ali naye Mzimu Woyera. Munthu wodalira nzeru zake zokha sangalandire zimene zimachokera kwa Mzimu wa Mulungu. Amaziyesa zopusa, ndipo sangathe kuzimvetsa, popeza kuti zimalira kukhala ndi Mzimu Woyera kuti munthu azimvetse. Munthu amene ali ndi Mzimu Woyera angathe kuzindikira khalidwe la zonse, ndipo palibe wina amene angathe kutsutsapo ai. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Ndani adadziŵa maganizo a Ambuye, kuti athe kuŵalangiza?” Koma ife tili ndi maganizo a Khristu. Koma ndidaatsimikiza kuti pamene ndili pakati panu, ndiiŵale zina zonse, kupatula Yesu Khristu yekha, koma tsono amene adapachikidwa pa mtanda.
Ndithu ndikunenetsa kuti timalankhula zimene tikuzidziŵa, ndipo timachitira umboni zimene tidaziwona, koma inu simukukhulupirira mau athuŵa.
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
Chimene timanyadira nchakuti mtima wathu umatichitira umboni kuti ponseponse pamene tidapita, koma makamakanso pakati panu, mayendedwe athu anali oyera ndi opanda chinyengo. Zinali choncho osati chifukwa chotsata nzeru za anthu ai, koma chifukwa Mulungu adatikomera mtima.
Pajatu munthu akamakana Ine ndiponso mau anga, nanenso Mwana wa Munthune ndidzamkana pamene ndidzabwera ndili ndi ulemerero wanga ndi wa Atate anga, ndi wa angelo oyera.
Yohaneyo adaamchitira umboni. Ankauza anthu mwamphamvu kuti, “Uyu ndiye uja ndinkanenayu kuti amene akubwera pambuyo panga ngwoposa ine; pakuti ine ndisanabadwe, Iye alipo.”
Koma timalalika chifukwa Mulungu adativomereza natisungiza Uthenga Wabwino kuti tiulalike. Choncho tikamaphunzitsa sitifuna kukondweretsa anthu, koma timafuna kukondweretsa Mulungu, amene amapenyetsetsa mitima yathu.
kuti mukhale angwiro ndi osalakwa, ana a Mulungu opanda chilema chilichonse pakati pa anthu onyenga ndi osokeretsa anzao. Pakati pa anthu otere mumaŵala monga momwe zimaonekera nyenyezi pa dziko lapansi,
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala.
Khalani ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa, kotero kuti anthu ena akamasinjirira mayendedwe anu abwino pamene mukutsata Khristu, achite manyazi ndi chipongwe chao.
Nchifukwa chake ine, womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukupemphani kuti, chifukwa Mulungu adakuitanani, muziyenda moyenerana ndi kuitanidwako.
“Ndithu kunena zoona, aliyense wondivomereza pamaso pa anthu, Inenso Mwana wa Munthune ndidzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu.
Koma sindilabada konse za moyo wanga, ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malinga ndikatsirize ntchito yanga, ndi utumiki umene Ambuye Yesu adandipatsa, ndiye kuti kulalika poyera Uthenga Wabwino wonena za kukoma mtima kwa Mulungu.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene amakhala moyo chifukwa cha iye yekha, kapena kufa chifukwa cha iye yekha. Tikakhala ndi moyo, moyowo ndi wa Ambuye, tikafa, timafera Ambuye. Nchifukwa chake, ngakhale tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ao a Ambuye.
Sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, kuti nditsate malamulo anu.
Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”
uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.