Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


107 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Yesu

107 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Yesu

Ndili ndi uthenga wabwino kwambiri kwa inu lero. Mu Colose 2:13-15, tikuwona mphamvu ya Khristu pa zoipa zonse, machimo onse, ndi maufumu onse. Baibulo limati, "Inu amene munali akufa m’machimo anu ndi m’kusadulidwa kwa thupi lanu, Iye anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, anakhululukira machimo anu onse; anathetsa chikalata cha milandu chimene chinali chotitsutsana, nachichotsa pakati, nachikhomera pa mtanda; ndipo atavula maufumu ndi maulamuliro, anawaonetsa poyera, napambana pa iwo mwa mtanda."

Taganizirani zimenezi! Khristu anakhululukira machimo anu onse! Anagonjetsa mphamvu za mdima! Chifukwa cha nsembe yake pa mtanda, muli ndi ufulu ndi moyo. Tiyenera kukumbukira nthawi zonse mphamvu imeneyi ndi ulamuliro umene uli wa Khristu.

Mphamvu ndi ulamuliro umenewu umalemekeza Yesu Khristu, amene analemekeza Atate. Ndipo Atate amatiuza kuti tionetse mphamvu imeneyi pano padziko lapansi, m’mipingo yathu, ndi m’mitundu yonse. Tiyeni tipite ndi kulalikira uthenga wabwino wa chipulumutso kwa munthu aliyense. Mulungu akhale nanu.




Luka 6:19

Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:6

Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:27

Ophunzira aja adazizwa nati, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja yomwe zizimumvera?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 4:23-24

Yesu adayendera dziko lonse la Galileya akuphunzitsa m'nyumba zamapemphero ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za ufumu wakumwamba. Ankachiritsanso nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi. Mbiri yake idabuka m'dziko lonse la Siriya, kotero kuti anthu ankabwera kwa Iye ndi odwala onse ovutika ndi nthenda ndi zoŵaŵa zosiyanasiyana, ogwidwa ndi mizimu yoipa, akhunyu ndi opunduka, Iye nkumaŵachiritsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:18

Palibe munthu wondilanda moyo wangawu, koma ndikuupereka ndekha. Ndili nazo mphamvu zoutaya moyo wanga, ndili nazonso mphamvu zoutenganso. Udindo umenewu ndidaulandira kwa Atate anga.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 1:3

Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:28-29

Yesu atatsiriza kunena zimenezi, anthu onse aja adadabwa ndi kaphunzitsidwe kake, chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:29

chifukwa ankaŵaphunzitsa monga munthu waulamuliro osati monga m'mene ankachitira aphunzitsi a Malamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:17

Tsiku lina Yesu ankaphunzitsa. Pomwepo padaakhala Afarisi ena ndi aphunzitsi ena a Malamulo, ochokera ku midzi yonse ya ku Galileya, ndi ya ku Yudeya, ndiponso ku Yerusalemu. Mphamvu zochokera kwa Ambuye zinali mwa Iye kuti azichizira odwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:3

Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, ndipo palibe chilichonse chimene chidalengedwa popanda Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 63:1

“Ndaninso kodi akuchokera ku Edomuyu, atavala zofiira za ku Bozira? Ndani ameneyu wovala zovala zokongola, akuyenda monyadira mphamvu zake? Ndi Ineyo, wolankhula zachilungamo, ndiponso wa mphamvu zoti nkupulumutsa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:16-17

Madzulo amenewo, anthu adabwera kwa Yesu ndi anzao ambiri ogwidwa ndi mizimu yoipa. Yesu adaitulutsa mizimuyo ndi mau chabe, ndipo onse amene ankadwala adaŵachiritsa. Adachita zimenezi kuti zipherezere zimene mneneri Yesaya adaanena zakuti, “Iye adatenga zofooka zathu, adasenza nthenda zathu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 7:25

Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 8:26-27

Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha, inu anthu a chikhulupiriro chochepa?” Atatero adaimirira nkudzudzula mphepoyo ndi nyanjayo, kenaka padagwa bata lalikulu ndithu. Ophunzira aja adazizwa nati, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja yomwe zizimumvera?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:4

koma poyang'anira kuyera kwake kwaumulungu, kuuka kwake kwa akufa kukutsimikiza kuti Yesuyo ndi Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:31

Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:17

Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:24

Koma amene Mulungu adaŵaitana, kaya ndi Ayuda kaya ndi Agriki, onsewo amazindikira kuti Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndiponso nzeru ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:35

Yesu adayendera mizinda ndi midzi yonse. Adanka naphunzitsa m'nyumba zao zamapemphero, nkumalalika Uthenga Wabwino wonena za Ufumu wakumwamba. Ndiponso ankachiritsa nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 11:27

“Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:25-27

M'mamaŵa kukali mbuu, Yesu adadza kwa iwo Iye akuyenda pa madzi. Pamene ophunzira aja adamuwona akuyenda pa madzi, adaopsedwa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo adayamba kukuwa chifukwa cha mantha. Koma nthaŵi yomweyo Yesu adaŵauza kuti, “Khazikani mtima pansi, ndine; musaope.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 14:35-36

Anthu akumeneko adamzindikira Yesu, nakadziŵitsa anzao a ku dera lonse lozungulira pamenepo. Motero adadza kwa Yesu ndi anthu onse odwala. Adampempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:30-31

Anthu ambirimbiri adadza kwa Iye ndi anthu opunduka miyendo, akhungu, olumala, osalankhula, ndiponso ndi odwala ena ambiri. Adaŵakhazika pafupi ndi Yesu, Iye nkuŵachiritsa. Tsono anthu onse adadabwa poona kuti osalankhula aja akulankhula, olumala aja achira, opunduka miyendo aja akuyenda, ndipo akhungu aja akupenya. Choncho adatamanda Mulungu wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18-19

Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa. Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 17:20-21

Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [ “Koma mzimu wa mtundu umenewu, pokhapokha mutayamba mwapemphera ndi kusala zakudya mpamene mungautulutse.”]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:18-20

“Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe. “Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:27-28

Anthu onse aja adazizwa kwambiri, mpaka kumafunsana kuti, “Kodi zimenezi nzotani? Zophunzitsa zamtundutu zimenezi! Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu, ndipo ikumumveradi.” Mwamsanga mbiri yake idawanda ponseponse ku dera lonse la ku Galileya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:10-11

Pakuti anali atachiritsa anthu ambiri, ndipo onse amene adaali ndi matenda ankakankhana pofuna kuti amkhudze. Mizimu yoipa inkati ikamuwona, inkadzigwetsa pansi pafupi ndi Iye nkumafuula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:39-41

Yesu adadzuka, ndipo adadzudzula mphepoyo, nalamula nyanja kuti, “Tonthola! Khala bata!” Mphepo ija idalekadi, kenaka padagwa bata lalikulu. Akufesa choncho, mbeu zina zidagwera m'njira, ndipo mbalame zidabwera nkuzitolatola. Apo Yesu adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuchita mantha? Kani mulibe chikhulupiriro inu?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha kwambiri, nkumafunsana kuti, “Kodi Iyeyu ndi munthu wotani kuti ngakhale mphepo ndi nyanja zizimumvera?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:1-20

Tsono Yesu ndi ophunzira ake adafika ku tsidya la Nyanja ya Galileya, ku dera la Agerasa. Ndipo iye adadandaulira Yesu kwambiri kuti mizimuyo asaitulutsire kunja kwa dera limenelo. Pafupi pomwepo, pachitunda poteropo, pankadya gulu lalikulu la nkhumba. Tsono mizimu yoipa ija idapempha Yesu kuti, “Tipirikitsireni ku nkhumbazo, tiloleni tikaloŵe m'menemo.” Yesu adailoladi. Iyo idatuluka nkukaloŵadi m'nkhumbazo. Pomwepo gulu lonselo lidaguduka kutsika chitunda chija mwaliŵiro, nkukadziponya m'nyanja, mpaka kufera m'madzimo. Zonse zidaalipo ngati zikwi ziŵiri. Oŵeta nkhumbazo adathaŵa, nakasimbira anthu mu mzinda ndi ku midzi. Pamenepo anthu adatuluka kuti akaone zimene zidaachitikazo. Atafika kumene kunali Yesuko, adaona munthu adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja atakhala pansi, atavala, misala ija itatha, munthu woti adaloŵedwa ndi chigulu cha mizimu yoipa. Anthuwo adagwidwa ndi mantha. Anzao amene adaaonerera zonse zikuchitika, adaŵasimbira zimene zidaamuchitikira munthu wamizimuyo ndiponso nkhumba zija. Apo anthuwo adampempha Yesu kuti achoke ku dera laolo. Pamene Yesu ankakaloŵa m'chombo, munthu amene adaagwidwa ndi mizimu yoipa uja adampempha kuti apite nao. Koma Yesu adakana namuuza kuti, “Iyai, iwe pita kumudzi kwa anthu akwanu, ukaŵafotokozere zazikulu zimene Ambuye akuchitira mwa chifundo chao.” Yesu atangotuluka m'chombo, munthu wina wogwidwa ndi mzimu woipa adadzakumana naye kuchokera ku manda. Munthuyo adapitadi nakayamba kufalitsa ku dera lotchedwa Mizinda Khumi, zazikulu zimene Yesu adaamchitira. Atamva zimenezo anthu onse adazizwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:25-34

Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaazunzika zedi ndi asing'anga ochuluka amene ankayesa kumuchiza. Mwakuti adaamwaza chuma chake chonse, komabe osapeza bwino konse. M'malo mwake matendawo analikunka nakulirakulira. Maiyo anali atamva za Yesu. Tsono adaloŵa m'chinamtindi cha anthu chija, nkuphaphatiza mpaka kukafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza chovala chake. Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Ndikangokhudza ngakhale zovala zake zokhazo, ndichira.” Ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka, mwiniwakeyo nkumva m'thupi mwake kuti matenda ake aja atha. Munthuyo ankakhala kumandako, ndipo padaalibe wina wothanso kummanga, ngakhale ndi unyolo womwe. Pomwepo Yesu adazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Iye. Tsono adatembenuka nayang'ana anthu aja ndipo adafunsa kuti, “Kodi ndani wandikhudza zovala?” Ophunzira ake adati, “Ndi Inu nomwe mukuwona kuti anthu akukupanikizani, ndiye mungafunse bwanji kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ” Koma Yesu adayang'anayang'ana kuti aone yemwe wachita zimenezo. Apo mai uja adachita mantha nayamba kunjenjemera, chifukwa anali atazindikira zimene zidaamuwonekerazo. Adadza pafupi, nadzigwetsa pansi pamaso pa Yesu, nkumufotokozera zonse monga momwe zidaachitikira. Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere. Matenda anu atheretu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 5:41-42

Tsono adagwira mwanayo pa dzanja namuuza kuti, “Talita, kumi.” (Ndiye kuti, “Mtsikana iwe, ndikuti dzuka.”) Pomwepo mtsikanayo adadzukadi, nayamba kuyenda, pakuti adaali wa zaka khumi ndi ziŵiri. Pamenepo anthu aja adazizwa kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:7

Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵatuma aŵiriaŵiri. Adaŵapatsa mphamvu zotulutsira mizimu yoipitsa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 6:56

Kulikonse kumene Yesu ankapita, ku midzi ndi ku mizinda, anthu ankadzakhazika odwala pa mabwalo. Ankamupempha kuti aŵalole odwalawo kungokhudza ngakhale mphonje ya chovala chake. Mwakuti onse amene ankaikhudza, ankachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:6-9

Apo Yesu adalamula anthu aja kuti akhale pansi. Kenaka adatenga buledi msanu ndi muŵiri uja, adathokoza Mulungu, namunyemanyema nkumupereka kwa ophunzira ake kuti akagaŵire anthu aja. Ophunzira aja adaŵagaŵiradi anthuwo. Adaalinso ndi tinsomba toŵerengeka. Yesu adathokoza Mulungu chifukwa cha tinsombato, nalamula ophunzira ake kuti atiperekenso kwa anthu aja. Anthu adadya mpaka kukhuta. Adatola zotsala, nadzaza madengu asanu ndi aŵiri. Anthu amene adaali pamenepo, amuna okha adaalipo ngati zikwi zinai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 9:23

Yesu adati, “Bwanji mukuti, ‘Ngati mungathe?’ Zinthu zonse nzotheka kwa amene ali ndi chikhulupiriro.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 10:27

Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu nkosathekadi, koma ndi Mulungu ai, nkotheka. Paja ndi Mulungu zonse nzotheka.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17-18

Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:18-19

“Mzimu wa Chauta wadzaza mwa Ine. Wandidzoza kuti ndikalalikire amphaŵi Uthenga Wabwino. Wandituma kuti ndikalengeze kwa am'ndende kuti adzamasulidwa, ndi kwa akhungu kuti adzapenyanso. Wandituma kuti ndikaŵapatse ufulu anthu osautsidwa, ndi kukalalika za nthaŵi imene Ambuye adzapulumutsa anthu ao.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:36-37

Anthu onse aja adazizwa, mpaka kumafunsana kuti, “Mau ameneŵa ngotani? Ngakhale mizimu yoipitsa anthu yomwe akuilamula ndi mphamvu ndi ulamuliro, ndipo ikutulukadi.” Motero mbiri ya Yesu idawanda ku dera lonselo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:12-13

Pamene Yesu anali m'mudzi wina, kudabwera munthu wina wa khate thupi lonse. Pamene adaona Yesu, adadzigwetsa moŵerama pansi pamaso pake nayamba kumdandaulira. Adati, “Ambuye, mutafuna, mungathe kundichiritsa.” Yesu adatambalitsa dzanja nkumukhudza, nati, “Chabwino, ndikufuna, chira!” Pomwepo khate lake lija lidatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 5:24

Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti, “Iwe, ndikuti dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:17-19

Yesu adatsika phiri pamodzi ndi ophunzira ake, naima pa chidikha. Panali khamu lalikulu la ophunzira ake, ndi anthu ena ambirimbiri ochokera ku dera lonse la Yudeya ndi ku Yerusalemu, ndi ku mbali yakunyanja, ku Tiro, ndi ku Sidoni. Iwo adabwera kudzamva mau ake, ndiponso kuti Iye aŵachiritse. Anthu amene ankasautsidwa ndi mizimu yoipa, amenewonso Iye ankaŵachiritsa. Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:14-15

Tsono adafika pafupi nakhudza chithathacho. Anthu amene ankanyamula malirowo adaima, ndipo Yesu adati, “Mnyamata iwe, ndikukuuza kuti, Uka.” Pamenepo wakufayo adakhala tsonga nayamba kulankhula, Yesu nkumupereka kwa mai wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 7:21

Nthaŵi imeneyo nkuti Yesu akuchiritsa kumene nthenda zosiyanasiyana za anthu ambiri. Ankatulutsa mizimu yoipa, nkumapenyetsa anthu akhungu ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:25

Tsono Yesu adaŵafunsa kuti, “Kodi chikhulupiriro chanu chili kuti?” Koma iwo adaagwidwa ndi mantha nathedwa nzeru, nkumafunsana kuti, “Kodi ameneyu ndi munthu wotani? Angolamula mphepo ndi madzi omwe, izo nkumumveradi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:43-48

Tsono panali mai wina amene adakhala akuvutika ndi matenda a msambo pa zaka khumi ndi ziŵiri. Adaamwaza chuma chake chonse kulipira asing'anga, koma panalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumchiza. Iyeyu adafika cha kumbuyo kwa Yesu, nakhudza mphonje ya chovala chake, ndipodi nthaŵi yomweyo matenda a msambowo adaleka. Pompo Yesu adafunsa kuti, “Ndani wandikhudza?” Poti onse ankangoti, “Kaya,” Petro adati, “Aphunzitsi, anthu onseŵa akuzungulirani ndipo akukupanikizani.” Koma Yesu adati, “Iyai, wina wandikhudza ndithu. Ndazindikira kuti mphamvu zina zatuluka mwa Ine.” Pamene mai uja adaona kuti sangathenso kudzibisa, adadza monjenjemera nadzigwetsa ku mapazi a Yesu. Adafotokoza pamaso pa anthu onse aja chifukwa chimene adaakhudzira Yesu, ndiponso m'mene adachirira nthaŵi yomweyo. Apo Yesu adamuuza kuti, “Inu mwana wanga, chikhulupiriro chanu chakuchiritsani. Pitani ndi mtendere.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:1-2

Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja naŵapatsa ulamuliro ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa yonse ndi zochiritsira nthenda. Pamene atumwi aja adabwerako, adafotokozera Yesu zonse zimene adaachita. Tsono Iye adaŵatenga nakakhala nawo paokha ku mudzi wina, dzina lake Betsaida. Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.” Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?” Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Auzeni anthuŵa akhale pansi m'magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.” Ophunzira aja adaŵakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri. Nthaŵi ina pamene Yesu ankapemphera yekha, ophunzira ake adaali naye. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya. Koma enanso amati mneneri wina wakale wauka kwa akufa.” Adaŵatuma kuti akalalike za ufumu wa Mulungu, ndi kukachiritsa anthu odwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:11

Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:43

Apo anthu onse aja adazizwa nazo mphamvu za Mulunguzi. Pamene anthu onse aja ankazizwabe ndi zonse zimene Yesu adaachita, Iye adauza ophunzira ake kuti,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:17-19

Anthu 72 aja adabwerako ndi chimwemwe nati, “Ambuye, ngakhale mizimu yoipa yomwe imatigonjera tikamailamula m'dzina lanu.” Yesu adaŵauza kuti, “Ndidaona Satana alikugwa ngati mphezi kuchokera Kumwamba. Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:27

Yesu adati, “Zimene zili zosatheka ndi anthu, zimatheka ndi Mulungu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:49

Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 1:14

Wotchedwa Mau uja adasanduka munthu, nadzakhala pakati pathu. Anali wokoma mtima ndi wokhulupirika kwabasi. Ndipotu tidaona ulemerero wake, ndiye kuti ulemerero womwe Iye amalandira kwa Atate pokhala Mwana wao mmodzi yekha uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 2:7-9

Tsono Yesu adauza anyamata aja kuti, “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Ndipo adazidzaza mpaka m'milomo. Pambuyo pake adaŵauza kuti, “Tsopano tungani, kaperekeni kwa mkulu wa phwando,” Iwowo adakaperekadi. Mkulu wa phwandoyo adalaŵa madzi osanduka vinyowo osadziŵa kumene achokera. (Koma anyamata aja amene adaatunga madziwo ankadziŵa.) Tsono mkulu wa phwandoyo adaitana mkwati,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:35

Mulungu Atate amakonda Mwana wake, ndipo adaika zonse m'manja mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:21

Monga Atate amaukitsa akufa, naŵapatsa moyo, moteronso Mwana amapatsa moyo kwa amene Iye afuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 5:24-25

“Ndithu ndikunenetsa kuti munthu womva mau anga, nakhulupirira Iye amene adandituma, ameneyo ali ndi moyo wosatha. Iyeyo sazengedwa mlandu, koma watuluka kale mu imfa, ndipo waloŵa m'moyo. Ndikunenetsanso kuti ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu amene ali ngati akufa adzamva mau a Mwana wa Mulungu, ndipo amene adzaŵakhulupirira adzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:35

Yesu adaŵauza kuti, “Chakudya chopatsa moyocho ndine. Munthu aliyense wodza kwa Ine, sadzamva njala. Ndipo aliyense wokhulupirira Ine, sadzamva ludzu konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 6:63

Mzimu wa Mulungu ndiwo umapatsa moyo, mphamvu ya munthu siipindula konse. Mau amene ndalankhula nanu ndiwo amapatsa mzimu wa Mulungu ndiponso moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:12

Pambuyo pake Yesu adalankhulanso ndi Afarisi aja, adati, “Ine ndine kuŵala kounikira anthu onse. Munthu wotsata Ine, sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuŵala kotsogolera anthu ku moyo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:36

Tsono ngati Mwana akumasulani, mudzakhaladi mfulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:10

Wakuba amangodzera kuba, kupha ndi kuwononga. Koma Ine ndidabwera kuti nkhosazo zikhale ndi moyo, moyo wake wochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:28-30

Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao. Iyeyo mlonda amamtsekulira. Nkhosa zimamva mau ake, ndipo amaziitana maina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Ine ndi Atate ndife amodzi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 11:25-26

Yesu adamuuza kuti, “Woukitsa anthu kwa akufa ndiponso woŵapatsa moyo ndine. Munthu wokhulupirira Ine, ngakhale afe adzakhala ndi moyo. Ndipo aliyense amene ali ndi moyo nakhulupirira Ine, sadzafa konse. Kodi ukukhulupirira zimenezi?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:6

Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:12-14

Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate. Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:5

“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:33

Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 17:2

Pajatu mudampatsa mphamvu zolamulira anthu onse, kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mudampatsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:22

“Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:36

“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6

Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:10

Mudziŵetu tsono inu nonse, ndi Aisraele ena onse, kuti munthuyu akuima wamoyo pamaso panu chifukwa cha mphamvu ya dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete. Amene uja inu mudaampachika pa mtanda, koma Mulungu adamuukitsa kwa akufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:30

Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:12

Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:18

Mtsikanayo adachita zimenezi masiku ambiri. Koma Paulo zimenezo zidamunyansa, choncho adatembenuka nauza mzimu woipa uja kuti, “Iwe, m'dzina la Yesu Khristu ndikukulamula kuti utuluke mwa munthuyu.” Ndipo nthaŵi yomweyo udatulukadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:17

Chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi kuja, ulamuliro wa imfa udakhazikika ponseponse. Nanji tsono zotsatira za zimene adachita Munthu mmodzi wina uja, Yesu Khristu, nzazikulu kopambana. Pakuti onse olandira madalitso a Mulungu, pamodzi ndi chilungamo chimene chili mphatso yake, adzakhala ndi moyo ndi kusanduka mafumu, kudzera mwa iyeyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:11

Ndipo Mzimu wa Mulungu, amene adaukitsa Yesu kwa akufa, akamakhala mwa inu, pamenepo, mwa Mzimu wake yemweyo, Mulungu adzapatsanso moyo matupi anu otha kufaŵa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:34

Tsono palibe amene angaŵaweruze kuti ngopalamula. Khristu Yesu amene adafa, kaya tinene kuti amene adauka kwa akufa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndiye amene akutinenera kwa Mulunguyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:14

Mulungu adaukitsa Ambuye kwa akufa, ndipo mwa mphamvu yake adzatiwukitsa ifenso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:19-21

Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba. Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:16-17

Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu. Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:16-17

Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:19-20

Kudakomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristuyo. Tikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu okhala ku Kolose, abale athu okhulupirika mwa Khristu. Mulungu Atate athu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:5

Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:9

Chilango chao nchakuti adzaonongedwa kwamuyaya, sadzaona konse nkhope ya Ambuye kapena ulemerero wa mphamvu zake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:15-17

Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa. Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuŵalezera mtima onse amene adzamkhulupirire kuti alandire moyo wosatha. Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:10

Koma tsopano Mulungu watiwululira zimenezi kudzera m'kuwoneka kwa Mpulumutsi wathu, Khristu Yesu. Khristuyo adathetsa mphamvu za imfa, ndipo mwa Uthenga Wabwino adaonetsera poyera moyo umene sungafe konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:14-15

Tsono popeza kuti anawo ndi anthu, okhala ndi magazi ndi mnofu, Yesu yemwe adasanduka munthu wonga iwowo. Adachita zimenezi kuti ndi imfa yake aononge Satana amene anali ndi mphamvu yodzetsa imfa. Pakutero adafunanso kuti aŵamasule amene pa moyo wao wonse anali ngati akapolo chifukwa choopa imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 4:15-16

Sitili ndi Mkulu wa ansembe woti sangathe kutimvera chifundo chifukwa cha zofooka zathu. Wathu Mkulu wa ansembe onse adayesedwa pa zonse, monga momwe ife timayesedwera, koma Iye sadachimwe konse. Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:8

Yesu Khristu ndi yemweyo dzulo, lero ndi mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:18

Paja nayenso Khristu adafera machimo a anthu kamodzi kokha; munthu wolungama kufa m'malo mwa anthu ochimwafe, kuti atifikitse kwa Mulungu. Pa za thupi adaphedwa, koma pa za mzimu adapatsidwa moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4-5

Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:8

“Ine ndine Woyamba ndiponso Wotsiriza,” akutero Ambuye Mulungu, Mphambe, amene alipo, amene analipo kale, amene alikudza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Wamuyaya, Wapamwamba! Ndikukutamandani chifukwa ndinu Wolungama, Wabwino, Wachifundo ndipo mwakhululukira moyo wanga. Atate Woyera, ndikubwerera kwa Inu, chifukwa Inu nokha muli ndi Mphamvu yopulumutsa, kuchiritsa ndi kumasula. Ndikupemphani kuti mundidzaze ndi kukhalapo kwanu kwaulemerero ndipo Mphamvu yanu iwonekere pa moyo wanga ndi wa banja langa kuti tonse pamodzi tifunitsitse kukwaniritsa cholinga chimene munakonzeratu ife. Ndithandizeni kutsanzira chikhulupiriro chanu kulikonse kumene ndikupita ndipo kukhalapo ndi Mphamvu ya Mzimu Woyera wanu kuwonekere m'miyoyo ya achinyamata, achikulire, okalamba ndi onse amene ali pafupi ndi ine. Ndidziwitseni kuyenda monga momwe Inu munayendera, muchiritsa odwala, kumasula ogwidwa ndi kuchiritsa onse oponderezedwa. Ndithandizeni kukhala paubwenzi wolimba ndi Inu kuti ndiphunzire kugonjetsa mantha ndi kudzutsa mphamvu (dunamis) imene munaiika mwa ine. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa