Nsembe ya anthu oipa mtima imamuipira Chauta, koma pemphero la anthu olungama limamkondweretsa.
Pa tsiku limenelo simudzandifunsa kanthu. Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo. Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata. Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera. Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
Choncho Yobe ataŵapempherera abwenzi ake aja, Chauta adambwezera chuma chake. Adampatsa moŵirikiza kuposa zimene adaali nazo kale.
Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti muzikonda adani anu ndipo muziŵapempherera amene amakuzunzani.
“Bwerera, kamuuze Hezekiya, mfumu ya anthu anga, mau aŵa, ‘Ine Chauta, Mulungu wa Davide kholo lako, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Chabwino, ndidzakuchiritsa. Udzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha.
“Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga, ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Iye adayang'anitsitsa mngeloyo mantha atamgwira, ndipo adamufunsa kuti, “Nkwabwino, Ambuye?” Mngeloyo adati, “Mulungu wakondwera nawo mapemphero ako ndipo wakumbukira ntchito zako zachifundo zako.
Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Pemphero langa likwere kwa Inu ngati lubani, kukweza kwa manja anga kukhale ngati nsembe yamadzulo.
“Mukamapemphera ndidzakumverani, ndipo mukandiitana ndidzakuyankhani. Mukaleka kuzunza anzanu, mukasiya kulozana chala, mukaleka kunena zoipa za anzanu,
Ndidapemphera kwa Chauta ndipo adandiyankha. Adandipulumutsa kwa zonse zimene ndinkaziwopa.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Inu nomwe muthandizane nafe pakutipempherera. Pamenepo anthu ambiri adzathokoza Mulungu m'malo mwathu, chifukwa cha zimene Iye adatichitira mwa kukoma mtima kwake.
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Ndipo Chauta adamumvera Eliyayo. Pomwepo moyo wa mwana uja udabwereranso mwa iye natsitsimuka.
Ndimakonda Chauta chifukwa amamva mau anga omupemba. Ndidakhulupirirabe ngakhale pamene ndinkati, “Ndazunzika koopsa.” Pamene ndinkachita mantha, ndidati, “Anthu ndi osakhulupirika.” Ndidzambwezera chiyani Chauta pa zabwino zonse zimene adandichitira? Ndidzakweza chikho cha chipulumutso, ndidzapemphera potchula dzina la Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Imfa ya anthu oyera mtima a Chauta, ndi yamtengowapatali pamaso pake. Chauta, ine ndine mtumiki wanu, mtumiki wanu weniweni, mwana wa mdzakazi wanu. Inu mwamasula maunyolo anga. Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta. Ndidzachita zimene ndidalumbira kwa Chauta pamaso pa anthu ake onse. Ndidzazipereka m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu, mu mzinda wa Yerusalemu. Tamandani Chauta! Iye amatchera khutu kuti andimve, nchifukwa chake ndidzampempha nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Kodi wina mwa inu ali m'mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Aimbe nyimbo zotamanda Mulungu.
Ndikukuitanani, Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Tcherani khutu kuti mumve liwu langa pamene ndikupemphera kwa Inu.
“Pitanso kwa Hezekiya, ukamuuze kuti, ‘Ine Chauta, Mulungu wa kholo lako Davide, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Nchifukwa chake ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.
Yesu adaŵayankha kuti, “Chifukwa chake nchakuti chikhulupiriro chanu nchochepa. Ndithu ndikunenetsa kuti mutakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa ngati kambeu ka mpiru, mudzauza phiri ili kuti, ‘Choka apa, pita uko,’ ilo nkuchokadi. Mwakuti palibe kanthu kamene kadzakukanikeni.” [
Usamafulumira kulankhula, ndipo usamalumbira msanga kwa Mulungu mumtima mwako. Paja Mulungu ali Kumwamba, iwe uli pansi pano, tsono usamachulukitsa mau ai.
Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Komanso kunena za ine, sindifuna kuchimwira Chauta, pakuleka kukupemphererani. Ndidzakuphunzitsani zimene zili zabwino ndi zolungama kuti muzizichita.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
M'maŵa, Inu Chauta, mumamva mau anga. M'maŵa ndimapemphera kwa Inu, ndi kudikira kuti mundiyankhe.
Ndikulirira Mulungu Wopambanazonse, Mulungu amene amandichitiradi zonse zimene walonjeza.
Ine ndidzaŵafikitsa ku Ziyoni, phiri langa lopatulika. Ndidzaŵapatsa chimwemwe m'nyumba yanga yopemphereramo. Zopereka zao zootcha ndiponso nsembe zao zinanso ndidzazilandira pa guwa langa. Paja Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Muzipemphera mosafookera, ndipo pamene mukupemphera, muzikhala tcheru ndiponso oyamika Mulungu.
Tsono munthu amapemphera kwa Mulungu, Iyeyo nkumulandira. Amabwera pamaso pa Mulungu mokondwa, ndipo Mulungu amamchitira zolungama.
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Muzikhala maso tsono, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse, kuti mukhale ndi mphamvu zopulumukira ku zonsezi zimene ziti zidzachitike, ndiponso kuti mukaimirire pamaso pa Mwana wa Munthu.”
Komabe Chauta amaonetsa chikondi chake chosasinthika tsiku ndi tsiku, Nchifukwa chake nthaŵi zonse ndimamuimbira nyimbo, ndi kumpemphera Mulungu wondipatsa moyo.
Muziwululirana machimo anu, ndipo muzipemphererana kuti muchire. Pemphero la munthu wolungama limakhala lamphamvu, ndipo silipita pachabe.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Ndidaitana Chauta m'zovuta zanga. Ndidafuulira Mulungu wanga kuti andithandize. Iye ali m'Nyumba mwake, adamva liwu langa, kulira kwanga kofuna chithandizo kudamveka kwa iye.
Chauta amakhala kutali ndi anthu oipa mtima, koma amamva pemphero la anthu achilungamo.
Chilichonse chomwe mudzachipemphe potchula dzina langa ndidzachita, kuti Atate adzalemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzandipempha kanthu potchula dzina langa ndidzakachitadi.”
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Paja Ambuye amaŵayang'anira bwino anthu olungama amatchera khutu ku mapemphero ao. Koma ochita zoipa saŵayang'ana bwino.”
Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse.
Khalani maso inu ndi kumapemphera, kuti mungagwe m'zokuyesani. Mtima ndiye ukufunitsitsadi, koma langokhala lofooka ndi thupi.”
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera. Ndipo ngati tikudziŵa kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse, timadziŵanso kuti talandiradi zimene tampempha.
Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse.
Akuti: Unditame mopemba, ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziŵa.
ndipo anthu anga amene amatchedwa dzina langa akadzichepetsa, napemphera, ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zao zoipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwambako. Choncho ndidzaŵakhululukira zoipa zao ndi kupulumutsa dziko lao.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Koma iwe, pamene ukuti upemphere, loŵa m'chipinda chako, tseka chitseko, ndipo upemphere kwa Atate ako amene ali osaoneka. Tsono Atate ako amene amaona zobisika adzakupatsa mphotho.
Nchifukwa chake ndikukuuzani kuti, m'mapemphero mwanu mukapempha Mulungu chinthu chilichonse, muzikhulupirira kuti mwalandira, ndipo mudzachilandiradi.
Ndipotu popanda chikhulupiriro nkosatheka kukondweretsa Mulungu. Paja aliyense wofuna kuyandikira kwa Mulungu, ayenera kukhulupirira kuti Mulunguyo alipodi, ndipo kuti amaŵapatsa mphotho anthu omufunafuna.
Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.
“Motero ndikukuuzani kuti, Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani, ndipo adzakutsekulirani.
Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.
Yabezi adatama Mulungu wa Israele mopemba kuti, “Mundidalitse ine, ndipo dziko langa mulikuze. Dzanja lanu lamphamvu likhale nane, ndipo mundisunge ine, kuti choipa chisandigwere ndi kumandisautsa.” Motero Mulungu adampatsadi zimene adaapemphazo.
Masiku amenewo Yesu adapita ku phiri kukapemphera, ndipo adachezera usiku wonse akupemphera kwa Mulungu.
Tsono ndikukupemphani abale, kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ndiponso ndi chithandizo cha chikondi chimene Mzimu Woyera amapereka, kuti mugwirizane nane polimbikira kundipempherera kwa Mulungu.
Anthu inu, ikani mtima wanu pa Iye nthaŵi zonse. Muuzeni zonse za kukhosi kwanu. Mulungu ndiye kothaŵira kwathu.
Komabe Inu Chauta, Mulungu wanga, imvani pemphero la ine mtumiki wanu ndi kupemba kwanga. Mverani kulira kwanga ndiponso pemphero limene ine mtumiki wanu ndikupemphera pamaso panu lero lino.
Wina mwa inu akasoŵa nzeru, apemphe kwa Mulungu, ndipo adzalandira, pakuti Mulungu amapereka kwa onse mwaufulu ndi mosatonzera.
“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani.
Ukadzapemphera kwa Iye adzakumvera, udzapereka kwa Iye zija udalumbira kuti udzaperekazi.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto. Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”
Tsono choyamba ndikukupemphani kuti pakhale mapemphero opempherera anthu onse. Mapemphero ake akhale opemba, opempha ndi othokoza Mulungu.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera.
Imvani pemphero langa, Inu Chauta. Tcherani khutu kuti mumve kupemba kwanga. Mundiyankhe chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndi kulungama kwanu.
Ndipo sindidzaleka kukondwa podziŵa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndiponso chithandizo cha Mzimu wopatsidwa ndi Yesu Khristu ndidzamasulidwa.
Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.
Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.