Ndinapangidwa kuti ndimutamande ndi kumulemekeza Mulungu, ndipo pochita zimenezi, ndimapeza madalitso.
M’buku la Machitidwe 16:25-26, timawerenga kuti pakati pa usiku, Paulo ndi Sila ankapemphera ndi kuimba nyimbo zotamanda Mulungu m’ndende, ndipo mwadzidzidzi, chivomezi champhepo chinagwedeza maziko a ndendeyo, zitseko zinatseguka, ndipo maunyolo a akaidi anatuluka. Nkhani imeneyi ikuonetsa mphamvu ya kutamanda Mulungu.
Ngati ine ndikudziwa bwino mphamvu ya kutamanda Mulungu, ndikanayimba kwa Ambuye nthawi zonse. Zilibe kanthu kuti mawu anga ali bwanji; dzina la Yesu liyenera kukwezedwa nthawi zonse.
Pakuvomereza ukulu wake ndi kulengeza mphamvu yake, zitseko zidzatseguka ndipo maunyolo adzasweka m'moyo wanga. Zinthu zidzayenda bwino ngati ndingotamanda Mulungu nthawi zonse.
Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Chauta, ndani angathe kumtamanda kokwanira?
Ndidzapereka kwa Inu nsembe yothokozera, ndidzapemphera potchula dzina la Inu, Chauta.
Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Tipulumutseni Inu Chauta, Mulungu wathu, mutisonkhanitse kuchokera pakati pa anthu akunja, kuti tikuthokozeni potchula dzina lanu loyera, kuti tizinyadira pokutamandani.
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza.
Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, ndi mtima wanga wonse. Ndidzasimba za ntchito zanu zonse zodabwitsa. Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani. Imbani nyimbo zotamanda Chauta amene amakhala ku Ziyoni. Lalikani za ntchito zake kwa anthu a mitundu yonse. Paja Iye amachitira chifundo anthu ozunzika, salephera kumva kulira kwao ndipo amalanga anthu oŵazunzawo. Mundikomere mtima, Inu Chauta. Onani m'mene akundisautsira anthu ondida. Inu mumandipulumutsa ku imfa, kuti ndithe kuyamika ntchito zanu zonse, pakati pa anthu anu a mu Ziyoni. Zoonadi ndidzakondwa chifukwa mwandipulumutsa. Akunja agwera m'mbuna yokumba iwo omwe. Phazi lao lakodwa mu ukonde wobisika wotcha iwo omwe. Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe. Tsono anthu oipa adzapita ku dziko la anthu akufa, ndiye kuti anthu onse amene amakana Mulungu. Koma anthu aumphaŵi Mulungu saŵaiŵala nthaŵi zonse, anthu osauka Mulungu saŵagwiritsa mwala mpang'ono pomwe. Dzambatukani, Inu Chauta, munthu asakunyozeni. Azengeni mlandu anthu akunja. Ndidzakondwa ndi kusangalala chifukwa cha Inu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse.
Nchifukwa chake, kudzera mwa Yesu tiyeni tipereke kosalekeza mayamiko athu kwa Mulungu ngati nsembe. Ndiye kunena kuti tipereke ngati nsembe mau athu ovomereza dzina lake poyera.
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
Mtamandeni pakuti ndiye Mulungu wanu, ndipo mwadziwonera nokha zinthu zazikulu ndi zoopsa zimene adakuchitirani.
Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”
Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Ngodala anthu amene mumaŵaphunzitsa kuimba nyimbo zachikondwerero, amene amayenda m'chikondi chanu, Inu Chauta.
Komabe Inu ndinu oyera, mumakhala pa mpando wanu waufumu, ndipo anthu anu Aisraele amakutamandani.
Bwanji ukumva chisoni, iwe mtima wanga? Chifukwa chiyani ukuvutika choncho m'kati mwanga? Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamtamandanso, Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
Pomwepo ansembe adalizanso malipenga aja. Anthu atamva, adafuula kwambiri, ndipo linga la mzindawo lidagwa. Ndipo ankhondo onse adabwera nakaloŵa mu mzindawo, naulanda.
Tsono Mose pamodzi ndi Aisraele aja adaimba nyimbo iyi, kuimbira Chauta, adati, “Ndidzaimbira Chauta chifukwa choti wapambana, waponya m'nyanja akavalo pamodzi ndi okwerapo omwe.
Ombani m'manja inu anthu a mitundu yonse. Fuulani kwa Mulungu poimba nyimbo zachimwemwe. Paja Chauta Wopambanazonse, ndi woopsa, ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
Chauta ndi wamkulu, ndi woyenera kumutamanda kwambiri. Timuyamike mu mzinda wake, pa phiri lake loyera,
Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza, ndiye amene amandilemekeza. Woyenda m'njira zolungama, ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Inu Mulungu, mtima wanga wakonzeka, ndithu mtima wanga wakonzekadi. Ndidzaimba nyimbo, nyimbo yake yotamanda. Lumpha iwe mtima wanga. Inu zeze ndi pangwe, tiyeni lirani, Ndidzadzutsa dzuŵa ndi nyimbo zanga. Ndidzakuthokozani, Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu. Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa anthu a maiko onse,
Ndidzakutamandani chifukwa chikondi chanu nchabwino kupambana moyo. Choncho ndidzakutamandani masiku onse a moyo wanga. Ndidzakweza manja anga kwa Inu mopemphera.
Tamandani Mulungu ndi chimwemwe mokweza mau, inu anthu onse a pa dziko lapansi. Inu Mulungu, mwatiyesa, mwatiyeretsa monga m'mene amayeretsera siliva. Inu mudatiloŵetsa mu ukonde wa adani, mudatisenzetsa katundu wolemera pamsana pathu. Inu mudalola kuti adani atikwere pa mutu, tidaloŵa m'moto ndiponso m'madzi, komabe Inu mwatifikitsa ku malo opulumukirako. Ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzachitadi zimene ndidazilumbira kwa Inu, zimene ndidalankhula ndi pakamwa panga, ndiponso zimene ndidalonjeza pamene ndinali pa mavuto. Ndidzapereka kwa Inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa, utsi wa nsembe za nkhosa zamphongo udzafika kwa Inu. Ndidzaperekanso ngati nsembe ng'ombe zamphongo ndi mbuzi. Bwerani mudzamve, inu nonse amene opembedza Mulungu, ndidzakusimbireni zimene Iye wandichitira. Ndidafuula kwa Iye, ndipo ndidamtamanda ndi pakamwa panga. Ndikadazindikira choipa chilichonse mumtima mwanga ndi kuchibisa, Ambuye sakadandimvera. Koma zoonadi, Mulungu wandimvera, wasamala mau a pemphero langa. Imbani nyimbo zoyamika dzina lake laulemerero, mumtamande mwaulemu.
Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota. Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu,
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano! Imbirani Chauta, anthu a m'dziko lonse lapansi! Uzani mitundu ya anthu kuti, “Chauta ndiye Mfumu. Dziko lonse lidakhazikitsidwa molimba, silidzagwedezeka konse. Adzaweruza mitundu yonse ya anthu mwachilungamo.” Zakumwamba zisangalale, zapansi pano zikondwere, nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zam'menemo. Minda zikondwe pamodzi ndi zonse zam'menemo. Mitengo yam'nkhalango idzaimba mokondwa pamaso pa Chauta, pamene zabwera kudzalamulira dziko lapansi. Adzalamulira dziko lonse mwachilungamo, adzalamulira anthu a mitundu yonse moona. Imbirani Chauta, tamandani dzina lake! Lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
Loŵani pa zipata zake mukuthokoza, pitani m'mabwalo a Nyumba yake mukutamanda. Yamikani Chauta, lemekezani dzina lake!
Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, moyo wanga wonse umuyamike potchula dzina lake loyera. Satilanga moyenerera machimo athu, satibwezera molingana ndi zolakwa zathu. Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife. Monga bambo amachitira chifundo ana ake, ndi momwenso Chauta amaŵachitira chifundo omulemekeza. Amadziŵa m'mene adatipangira, amakumbukira kuti ife ndife fumbi. Kunena za munthu, masiku ake sakhalitsa, ali ngati a udzu, munthuyo amakondwa ngati duŵa lakuthengo. Koma mphepo ikaombapo, duŵalo pamakhala palibe, siliwonekanso pa malo ake. Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake. Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake. Tamanda Chauta, iwe mtima wanga, ndipo usaiŵale zabwino zake zonse.
Thokozani Chauta, tamandani dzina lake, lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya. Adati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani kuti likhale choloŵa chako chokhalira iweyo.” Pamene anali anthu oŵerengeka, anthu osatchuka, ongokhala nawo m'dzikomo, omangoyendayenda kuchokera ku mtundu wina wa anthu kupita ku mtundu wina, kuchokera ku ufumu wina kupita ku ufumu wina, sadalole ndi mmodzi yemwe kuti aŵapsinje, adalanga mafumu ena chifukwa cha anthu akewo. Adati, “Musakhudze odzozedwa anga, musaŵachite choipa aneneri anga.” Pamene Chauta adadzetsa njala m'dziko la Kanani ndi kuwononga chakudya chonse, Iye anali atatuma munthu patsogolo pa anthu ake, Yosefe uja amene adagulitsidwa ngati kapolo. Mapazi ake adapwetekedwa ndi matangadza, khosi lake lidavekedwa unyolo, mpaka zimene Yosefe adanena zija zidachitikadi. Mau a Chauta adatsimikiza kuti iye sadalakwe. Imbirani Chauta, muimbireni nyimbo zomtamanda, lalikani za ntchito zake zodabwitsa.
Tamandani Chauta. Thokozani Chauta chifukwa ngwabwino, pakuti chikondi chake nchamuyaya.
Kwa ife ai, Chauta, kwa ife ai, koma kwa dzina lanu lokha ndiye kukhale ulemerero. Chifukwa ndinu Mulungu wa chikondi chosasinthika ndi wokhulupirika.
Tamandani Chauta, inu mitundu yonse ya anthu. Mlemekezeni kwambiri, inu anthu a m'maiko onse. Pakuti chikondi chake kwa ife nchachikulu, kukhulupirika kwa Chauta nkwamuyaya. Tamandani Chauta!
Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Ndikukuthokozani Inu Chauta ndi mtima wanga wonse. Ndikuimba nyimbo zokutamandani pamaso pa milungu. Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Ndidzakuyamikani, Inu Mulungu wanga, mfumu yanga, ndidzalemekeza dzina lanu nthaŵi zonse mpaka muyaya. Zamoyo zonse zidzakuthokozani, Inu Chauta, anthu anu onse oyera mtima adzakutamandani. Adzalankhula za ulemerero wa ufumu wanu, adzasimba za mphamvu zanu, kuti adziŵitse anthu onse za ntchito zanu zamphamvu, kutinso asimbe za ulemerero ndi za ufumu wanu waukulu. Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya, ulamuliro wanu ndi wa pa mibadwo yonse. Chauta ndi wokhulupirika pa mau ake onse, ndi wokoma mtima pa zochita zake zonse. Chauta amachirikiza onse ogwa m'mavuto, amakweza onse otsitsidwa. Maso onse amayang'anira kwa Inu, ndipo mumaŵapatsa chakudya pa nthaŵi yake. Mumafumbatula dzanja lanu, ndipo mumapatsa chamoyo chilichonse zofuna zake. Chauta ndi wolungama m'zochita zake zonse, ndi wachifundo pa zonse zimene achita. Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa. Ndidzakuthokozani tsiku ndi tsiku, ndidzatamanda dzina lanu mpaka muyaya. Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse. Pakamwa panga padzayamika Chauta, zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka muyaya. Chauta ndi wamkulu ndi woyenera kumtamanda kwambiri, ndipo ukulu wake sitingathe kuumvetsa.
Tamandani Chauta! Tamanda Chauta, iwe mtima wanga. Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta! Ndidzatamanda Chauta pa moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthaŵi zonse pamene ndili moyo.
Tamandani Chauta! Nkwabwino kuimba nyimbo zotamanda Mulungu wathu, nkokondwetsa mtima kumtamanda moyenera.
Tamandani Chauta! Tamandani Mulungu m'malo ake opatulika. Mtamandeni ku thambo lake lamphamvu. Mtamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu, mtamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. Mtamandeni pomuimbira lipenga, mtamandeni ndi gitara ndi zeze. Mtamandeni poimba ng'oma ndi povina, mtamandeni ndi zipangizo zansambo ndi mngoli. Mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira, mtamandeni ndi ziwaya zamalipenga zolira kwambiri. Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Chauta. Tamandani Chauta!
Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamtamanda. Ndiye Mulungu wa atate anga, ndipo ndidzamuyamika kwakukulu.
“Chifukwa cha zimenezi ndidzakuyamikani Inu Chauta, pakati pa mitundu ya anthu, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.
Imbirani Chauta, inu anthu a dziko lonse lapansi. Lengezani tsiku ndi tsiku za m'mene Iye adapulumutsira anthu ake. Lalikani za ulemerero wake kwa anthu a mitundu yonse, simbani za ntchito zake zodabwitsa kwa anthu a m'maiko onse. Chauta ngwamkulu, ngwoyenera kumtamanda kwambiri, ngwoyenera kumuwopa kupambana milungu yonse.
Nchifukwa chake Davide adatamanda Chauta pamaso pa msonkhano wonse. Adati, “Mutamandike mpaka muyaya Inu Chauta, Mulungu wa Israele, kholo lathu. Inu Ambuye, ndinu aakulu, amphamvu, aulemerero, opambana pa nkhondo ndiponso oposa pa ulemu, pakuti zonse zakumwamba ndi za pansi pano nzanu. Mfumu ndinu nokha, Inu Chauta, ndipo wolamulira zonse ndinu. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu. Tsopano tikukuthokozani, Inu Mulungu wathu, ndi kutamanda dzina lanu laulemerero.
Ndipo ntchito ya anthu oimba malipengawo ndi ya anthu oimba nyimbo aja, inali yakuti azimveketsa mau amodzi potamanda ndi kuthokoza Chauta, ndipo ankaimba nyimboyo ndi kuliza malipenga, ziwaya zamalipenga ndiponso zoimbira zina, kutamanda Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Apo Nyumbayo, Nyumba ya Chauta, idadzaza ndi mtambo, ndipo ansembe sankatha kuimirira kuti agwire ntchito yao yotumikira, chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Chauta unali utadzaza m'Nyumba ya Chautayo.
Tsono ataŵafunsa anthuwo, adasankha ena oti aziimbira Chauta ndi kumtamanda, oimbawo atavala zovala zoyera, akutsogolera gulu lankhondo namanena kuti, “Thokozani Chauta, pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.” Iwo aja atayamba kuimba ndi kutamanda, Chauta adaŵatchera msampha Aamoni, Amowabu ndiponso anthu a ku phiri la Seiri, amene adaadzalimbana ndi anthu a ku Yuda, kotero kuti adaŵagonjetsa onse.
Ankaimba ndi mavume mopolokezana, motamanda ndi mothokoza Chauta. Ankati, “Chauta ndi wabwino, chikondi chake pa Israele nchamuyaya.” Ndipo anthu onse ankafuula kwambiri pamene ankatamanda Chauta chifukwa choti maziko a Nyumba ya Chauta anali akumangidwa.
Tsono Alevi aŵa, Yesuwa, Kadimiyele, Bani, Hasabeniya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya adalengeza kuti, “Imirirani, mumtamande Chauta, Mulungu wanu, nthaŵi zonse. Litamandike dzina lake laulemerero limene anthu sangathe kulilemekeza ndi kulitamanda mokwanira.” Pamenepo Ezara adapemphera kuti, “Inu nokha ndiye Chauta. Inu mudalenga kumwamba, kumwambamwamba, ndiponso zonse zokhala komweko, dziko lapansi ndi zonse zokhala m'menemo. Mudalenga nyanja ndi zonse zam'menemo. Zonse zakumwamba zimakupembedzani.
Adati, “M'mimba mwa amai ndidatulukamo maliseche, namonso m'manda ndidzaloŵamo maliseche, Chauta ndiye adapatsa, Chauta ndiyenso walanda. Litamandike dzina la Chauta.”
Tsiku limenelo mudzati: “Thokozani Chauta, tamandani dzina lake. Mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu, mulalike kuti dzina lake ndi lopambana. “Imbirani Chauta nyimbo zotamanda, pakuti wachita zazikulu. Zimenezi zidziŵike pa dziko lonse lapansi.
Inu Chauta, ndinu Mulungu wanga. Ndidzakulemekezani ndi kutamanda dzina lanu. Pakuti mwachita zinthu zodabwitsa mokhulupirika ndi motsimikiza, zinthu zimene mudakonzeratu kalekale.
Imbirani Chauta nyimbo yatsopano. Mtamandeni, inu okhala m'dziko lonse lapansi! Mtamandeni, inu zolengedwa zonse zam'nyanja. Imbani, inu maiko akutali ndi onse okhala kumeneko.
Wandituma kuti ndiŵakonzere zofunika olira a ku Ziyoni, ndiye kuti ndiŵapatse maluŵa achisangalalo m'malo mwa phulusa lachisoni, ndiŵapatse mafuta osonyeza kukondwa m'malo mwa kulira, ndiŵapatse chovala cha chikondwerero m'malo mwa kutaya mtima. Tsono adzatchedwa mitengo yamphamvu yachilungamo, yoibzala Chauta, kuti Iye mwini apezepo ulemu.
Ndidzasimba za chikondi chosasinthika cha Chauta. Ndidzamtamanda chifukwa cha zonse zimene watichitira. Wadalitsa kwambiri anthu a ku Israele, potsata chifundo ndi kukula kwa chikondi chake chosasinthika.
Ngakhale mikuyu ipande kuchita maluŵa, mipesa ipande kukhala ndi mphesa, mitengo ya olivi ipande kubala zipatso, m'minda musatuluke kanthu, ndipo nkhosa ndi ng'ombe zithe m'khola, komabe kwanga nkukondwerera mwa Chauta, kwanga nkusangalala chifukwa cha Mulungu Mpulumutsi wanga.
Kondwani kwambiri, inu anthu a ku Ziyoni. Fuulani kwambiri, inu anthu a ku Yerusalemu. Onani, mfumu yanu ikudza kwa inu. Ikubwera ili yopambana ndi yogonjetsa adani. Ndi yodzichepetsa ndipo yakwera pa bulu, bulu wake kamwana tsono.
Anthu ochuluka amene anali patsogolo, ndi amene anali m'mbuyo, adayamba kufuula kuti, “Ulemu kwa Mwana wa Davide. Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye. Ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
nafunsa Yesu kuti, “Kodi mukumva zimene akunenazi?” Yesu adaŵayankha kuti, “Inde. Kani simudaŵerenge konse mau a Mulungu aja akuti, ‘Mudaphunzitsa ana ndi makanda omwe kukutamandani kotheratu?’ ”
Pamenepo Maria adati, “Mtima wanga ukutamanda Ambuye, ndipo mzimu wanga ukukondwera mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,
Mwadzidzidzi pamodzi ndi mngeloyo padaoneka gulu lalikulu la angelo ena. Ankatamanda Mulungu ndi mau akuti, “Ulemerero kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndipo pansi pano mtendere pakati pa anthu amene Iye amakondwera nawo.”
Pamene ankayandikira Yerusalemu, pa matsitso a Phiri la Olivi, gulu lonse la omutsatira aja lidayamba kukondwerera. Adakweza mau, natamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene iwo adaziwona. Adati, “Ndi yodala Mfumu imene ilikudza m'dzina la Ambuye. Mtendere Kumwamba, ulemu kwa Mulungu kumwambamwamba.”
Koma ikudza nthaŵi, ndipo yafika kale, pamene anthu opembedza kwenikweni adzapembedza Atate mwauzimu ndi moona. Atate amafuna anthu otere kuti ndiwo azimpembedza. Mulungu ndi mzimu, ndipo ompembedza Iye ayenera kumpembedza mwauzimu ndi moona.”
Tsiku ndi tsiku ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Nyumba ya Mulungu, ndipo ankadyera pamodzi kunyumba kwao. Ankadya chakudya chaocho mosangalala ndiponso ndi mtima waufulu. Ankatamanda Mulungu, ndipo anthu onse ankaŵakomera mtima. Ndipo tsiku ndi tsiku Ambuye ankaŵawonjezera ena olandira chipulumutso.
Koma pakati pa usiku Paulo ndi Silasi ankapemphera ndi kuimba nyimbo zolemekeza Mulungu, akaidi anzao nkumamvetsera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi champhamvu, kotero kuti maziko a ndende adagwedezeka. Nthaŵi yomweyo zitseko zonse zidatsekuka, maunyolo a mkaidi aliyense nkumasuka.
ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Ndiye titani tsono, abale? Pamene musonkhana pamodzi, aliyense angathe kukhala ndi nyimbo, kapena phunziro loti aphunzitse, kapena kanthu kena kamene Mulungu wamuululira, kapena mau oti alankhule m'chilankhulo chosadziŵika, ndipo wina afuna kutanthauzira mauwo. Komatu cholinga cha zonsezi chikhale kulimbikitsa mpingo.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Ndiwo Atate a chifundo ndi otilimbitsa mtima kwathunthu. Mulungu amatilimbitsa mtima m'masautso athu onse, kuti monga momwe Iye amalimbitsira ife mtima, nafenso tithe kuŵalimbitsa mtima anzathu amene ali pakati pa masautso amitundumitundu.
Adaafuna kuti tizitamanda ulemu wake chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere.
Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse. Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu. Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndipo moyo wanu udzakhala wodzaza ndi zipatso za chilungamo zimene mudzaonetsa mothandizidwa ndi Yesu Khristu, kuti anthu onse alemekeze ndi kutamanda Mulungu.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Ndipo timapemphera kuti muziyamika Atate, amene adakuyenerezani kuti mudzalandire nao madalitso onse amene amasungira anthu ao mu ufumu wa kuŵala.
Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Khalani okondwa nthaŵi zonse. Muzipemphera kosalekeza. Muzithokoza Mulungu pa zonse. Paja zimene Mulungu amafuna kuti muzichita mwa Khristu Yesu nzimenezi.
Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
ponena mau akuti, “Ndidzasimbira abale anga za dzina lanu. Ndidzakutamandani pa msonkhano wa anthu anu.”
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.
Koma mukule m'chifundo ndi m'nzeru za Yesu Khristu, Ambuye athu ndi Mpulumutsi wathu. Iye akhale ndi ulemerero tsopano ndi mpaka muyaya. Amen.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Akhale ndi ulemerero Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe m'machimo, amene angathenso kukufikitsani pamaso pa ulemerero wake, muli okondwa ndi opanda chilema konse. Mulungu, amene Iye yekha ndiye Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye athu, akhale ndi ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, isanayambe nthaŵi, tsopano, ndi mpaka muyaya. Amen.
Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen.
Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.” Ndidamvanso mau a cholengedwa chilichonse chakuthambo, cha pa dziko lapansi, cha kunsi kwa dziko, ndiponso cham'nyanja. Zolengedwa zonsezo zinkaimba mau akuti, “Wokhala pa mpando wachifumu uja, ndiponso Mwanawankhosa, alandire chiyamiko, ulemu, ulemerero ndi nyonga mpaka muyaya.”
Adati, “Ambuye Mulungu, Mphambe, Inu amene mulipo ndipo munaliponso kale, tikukuyamikani chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwayamba kukhazikitsa ufumu wanu.
Pamenepo ndidamva mau amphamvu Kumwamba akunena kuti, “Tsopano Mulungu wathu watipulumutsa. Waonetsa mphamvu zake ndi ufumu wake. Tsopano Wodzozedwa uja waonetsa ulamuliro wake. Woneneza abale athu uja wagwetsedwa pansi, amangokhalira kuŵaneneza kwa Mulungu wathu usana ndi usiku. Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.
Ankaimba nyimbo ya Mose, mtumiki wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa uja. Mau ake ankati, “Ambuye, Mulungu Mphambe, ntchito zanu nzazikulu ndi zododometsa. Inu, Mfumu ya anthu a mitundu yonse, njira zanu nzolungama ndi zoona. Ambuye, ndani angapande kukuwopani ndi kutamanda dzina lanu? Paja ndinu nokha oyera. Anthu a mitundu yonse adzabwera nkudzakupembedzani, popeza kuti ntchito zanu zolungama zaonekera poyera.”
Pambuyo pake ndidamva ngati mau amphamvu a chinamtindi cha anthu Kumwamba. Mauwo ankati, “Aleluya! Chipulumutso, ulemerero ndi mphamvu ndi zake za Mulungu wathu,
Pambuyo pake ku mpando wachifumu uja kudachoka mau akuti, “Tamandani Mulungu wathu, inu nonse atumiki ake, inu nonse omuwopa, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe.” Pamenepo ndidamva ngati mau a chinamtindi cha anthu, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ndiponso ngati kugunda kwamphamvu kwa bingu. Mauwo ankati, “Aleluya! Paja Ambuye Mulungu wathu Mphambe akulamulira.
Bwerani, timuimbire Chauta. Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye, thanthwe lotipulumutsa. Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo, choncho ndidati, “Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika, sasamalako njira zanga.” Choncho ndidakwiya nkulumbira kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo. Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze, tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe, timuimbire nyimbo zotamanda.
Fuulirani Chauta ndi chimwemwe, inu dziko lonse lapansi. Muimbireni mokondwa nyimbo zotamanda. Imbani nyimbo zoyamika Chauta ndi pangwe, lizani pangwe ndi nyimbo zokoma. Imbirani Chauta Mfumu, imbani molimbika ndi malipenga ndi mbetete.
Ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano, Inu Mulungu. Ndidzakuimbirani zeze wa nsambo khumi,
Chauta adzakhala mfumu mpaka muyaya, Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzalamulira ku mibadwo yonse. Tamandani Chauta!
Ndipo Aisraele onse ataona moto wotsika kumwambawo, pamodzi ndi ulemerero wa Chauta m'Nyumba ya Chauta ija, adaŵerama, nazyolikitsa nkhope zao pansi, ndipo adapembedza nathokoza Chauta ndi mau akuti, “Ndithu Chauta ndi wabwino pakuti chikondi chake chosasinthika chimakhala mpaka muyaya.”
Motero adatenga nthambi za kanjedza natuluka kukamchingamira. Ankafuula kuti, “Ulemu kwa Mulungu! Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye! Idalitsidwe Mfumu ya Israele!”
Tamandani Chauta! Imbirani Chauta nyimbo yatsopano, imbani nyimbo yomtamanda pa msonkhano wa anthu ake oyera mtima. Aisraele asangalale ndi Mlengi wao. Anthu a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yao. Atamande dzina lake povina, amuimbire nyimbo yokoma ndi ng'oma ndi pangwe.