Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Mpingo

110 Mau a m'Baibulo Okhudza Mphamvu ya Mpingo

Ndili wokhulupirira, ndikudziwa kuti pali maufumu awiri padziko lapansi: wachibadwa ndi wauzimu. Ndife otsatira a Khristu, ndipo tiyerekeze kuphunzira kukhala mu ufumu wauzimu m'njira yoti ukhudze bwino ufumu wachibadwa.

Ngakhale zingaoneke zovuta, koma tikafufuza Mawu a Mulungu, tingamvetse mauthenga auzimu omwe amapita patsogolo pa nzeru zathu zachibadwa, chifukwa Mzimu Woyera amatipatsa luntha lomvetsa uthenga wa Khristu kwa anthu.

Mphamvu ya Khristu imaperekedwa kwa wokhulupirira aliyense wokhulupirika kuti agonjetse Satana ndi mizimu yoipa yoyendayenda padziko lapansi. Mphamvu imene Khristu anapatsa mpingo imatithandiza kulamulira dziko lapansi pamodzi ndi kukhalapo kwake, ndi kutipatsa ulamuliro wokweza dzina la Ambuye.




Machitidwe a Atumwi 4:31

Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:16

Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:4-5

Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga, ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:20

Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:14-15

Kodi wina mwa inu akudwala? Aitanitse akulu a mpingo. Iwowo adzampempherere ndi kumdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye. Akampempherera ndi chikhulupiriro, wodwalayo adzapulumuka, Ambuye adzamuutsa, ndipo ngati anali atachimwa, Ambuye adzamkhululukira machimowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 12:5

Motero Petro ankasungidwa m'ndende. Koma Mpingo unkamupempherera kwa Mulungu kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:22

Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:18

“Ndithu ndikunenetsa kuti chilichonse chimene mudzamanga pansi pano, chidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo chilichonse chimene mudzamasula pansi pano, chidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 3:6-8

Koma Petro adamuuza kuti, “Ndalama ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: m'dzina la Yesu Khristu wa ku Nazarete, yenda!” Atatero adamgwira dzanja lamanja, namuimiritsa. Pompo mapazi ake ndi akakolo ake adalimba. Adalumpha, naimirira, nayamba kuyenda, ndipo adaloŵa nao m'Nyumba ya Mulungu akuyenda ndi kulumpha ndi kutamanda Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:58

Tsono abale anga okondedwa, limbikani, khalani osagwedezeka, gwirani ntchito ya Ambuye mwachangu masiku onse, podziŵa kuti ntchito zimene mumagwirira Ambuye sizili zopanda phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:18-20

Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano. Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:18

Ndipo Ine ndikuti, Ndiwe Petro, ndipo pa thanthwe limeneli ndidzamanga Mpingo wanga. Ndipo ngakhale mphamvu za imfa sizidzaugonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:31

Pamenepo Mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya unali pa mtendere. Udakhazikika, ndipo anthu ochuluka adaloŵamo chifukwa anthu ake ankayenda moopa Ambuye, ndipo Mzimu Woyera ankaŵalimbikitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:20-21

Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Mudzisunge m'chikondi cha Mulungu podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu Yesu Khristu adzakupatseni mwa chifundo chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:10

Abale, ndikukupemphani m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu, kuti muzivomerezana pa zimene munena. Pasakhale kupatulana pakati panu, koma muzimvana kwenikweni pokhala a mtima umodzi ndi a maganizo amodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:14-15

Tsono adasankhapo khumi ndi aŵiri, naŵatcha dzina loti, “Atumwi.” Adaŵauza kuti, “Ndasankha inu kuti muzikhala nane, ndidzakutumani kukalalika, ndipo mudzakhala ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:17-18

Okhulupirira azidzachita zozizwitsa izi: azidzatulutsa mizimu yoipa potchula dzina langa, azidzalankhula zilankhulo zachilendo, ndipo akagwira njoka kapena kumwa chakumwa chotha kuŵapha, sadzapwetekedwa. Akasanjika manja pa anthu odwala, anthuwo azidzachira.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:19

Ndakupatsanitu mphamvu kuti muziponda njoka ndi zinkhanira, ndi kumagonjetsa mphamvu zonse za mdani uja. Palibe kanthu kamene kangakupwetekeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:49

Ine ndidzakutumizirani mphatso imene Atate anga adalonjeza. Koma inu bakhalani mumzinda muno mpaka mutalandira mphamvu zochokera Kumwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 14:12

Ndithu ndikunenetsa kuti amene amandikhulupirira, ntchito zomwe ndimachita Ine, nayenso adzazichita. Ndipo adzachita zoposa pamenepa, chifukwa ndikupita kwa Atate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 15:16

Si ndinutu mudandisankha Ine ai, koma ndine ndidakusankhani inu. Ndipo ndidakupatulani kuti mukabereke zipatso, zipatso zake zokhalitsa. Motero chilichonse chimene mungapemphe Atate potchula dzina langa, adzakupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 16:13-15

Koma akadzafika Mzimu wodziŵitsa zoona uja adzakuphunzitsani zoona zonse. Pakuti sadzalankhula zochokera kwa Iye yekha ai, koma zilizonse zimene Atate adzamuuze, ndizo zimene adzalankhula. Ndipo adzakudziŵitsani zinthu zam'tsogolo. Adzandilemekeza, pakuti adzatenga zochokera kwa Ine nadzakudziŵitsani. Zonse za Atate nzanga. Nchifukwa chake ndanena kuti adzatenga zochokera kwa Ine, nadzakudziŵitsani inu.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 1:8

Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:1-4

Pamene tsiku la chikondwerero cha Pentekoste lidafika, iwo onse anali pamodzi m'nyumba imodzi. ku Frijiya ndi ku Pamfiliya, ku Ejipito, ndi ku madera a Libiya kufupi ndi ku Kirene, ena ndi alendo ochokera ku Roma, ndiye kuti Ayuda ndi ena otsata za Chiyuda. Enanso ndi Akrete ndi Aarabu, komabe tonse tikuŵamva anthuŵa akulankhula m'zilankhulo zathu za ntchito zazikulu za Mulungu.” Onse adazizwa ndi kuthedwa nzeru, ndipo adayamba kufunsana kuti, “Kodi chimenechi nchiyani?” Koma ena ankangoseka nkumati, “Aledzera vinyo watsopano.” Koma Petro adaimirira pamodzi ndi atumwi ena aja khumi ndi mmodzi, ndipo iye adanena mokweza mau kuti, “Inu Ayuda, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu kuno, tamverani ndipo mumvetsetse bwino mau anga. Anthuŵa sadaledzere ai, monga mukuganizira inu, pakuti nthaŵi idakali 9 koloko m'maŵa. Koma zimenezi ndi zomwe mneneri Yowele adalosa kuti, “ ‘Mulungu akuti, Pa masiku otsiriza ndidzaika Mzimu wanga mwa anthu onse, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi azidzalalika za Mulungu. Anyamata anu azidzaona zinthu m'masomphenya, ndipo nkhalamba zanu zizidzalota maloto. Ndithu, pa masiku amenewo ndidzaika Mzimu wanga ngakhale mwa akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndipo azidzalalika za Mulungu. Ndidzachita zozizwitsa ku thambo lakumwamba, ndipo pansi pano zizindikiro izi: magazi, moto ndi utsi watolotolo. Mwadzidzidzi kudamveka kuchokera kumwamba mkokomo ngati wa mphepo yaukali, nudzaza nyumba yonse imene ankakhalamo. Dzuŵa lidzangoti bii ngati mdima ndipo mwezi udzangoti psuu ngati magazi, lisanafike tsiku la Ambuye Mulungu lalikulu ndi laulemerero. Pamenepo aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba, adzapulumuka.’ “Inu Aisraele mverani mau aŵa. Yesu wa ku Nazarete anali munthu amene Mulungu adamtuma kwa inu. Mulungu adakutsimikizirani zimenezi ndi zamphamvu, zozizwitsa ndi zizindikiro zimene ankachita kudzera mwa Iyeyo pakati panu, monga mukudziŵa. Tsono Yesuyo adaperekedwa monga momwe Mulungu adaakonzeratu, ndi m'mene Iye amadziŵiratu zinthu. Ndipo inuyo mudamupha pakumpereka kwa anthu ochimwa kuti ampachike pa mtanda. Koma Mulungu adammasula ku zoŵaŵa za imfa, namuukitsa kwa akufa, chifukwa kunali kosatheka kuti agonjetsedwe ndi imfa. “Paja Davide ponena za Iye adati, ‘Ndinkaona Ambuye Mulungu pamaso panga nthaŵi zonse, pakuti amakhala ku dzanja langa lamanja kuti ndingagwedezeke. Nchifukwa chake mtima wanga udakondwa, ndipo ndinkalankhula mosangalala. Ndithu, ngakhale thupi langa lomwe lidzapumula m'manda, ndikhulupirira kuti simudzandisiya ku Malo a anthu akufa, kapena kulekerera Woyera wanu kuti aole. Mudandidziŵitsa njira zopita ku moyo, ndipo mudzandidzaza ndi chimwemwe pamaso panu.’ “Abale anga, ndingathe kulankhula nanu monenetsa za kholo lathu Davide. Iye adamwalira, naikidwa m'manda, ndipo manda ake alipo mpaka pano. Ndipo adaona ngati timalaŵi ta moto tooneka ngati malilime tikugaŵikana nkukhala pa iwo, aliyense kakekake. Paja iye anali mneneri, ndipo ankadziŵa zimene Mulungu adamlonjeza molumbira zakuti mmodzi mwa zidzukulu zake ndiye adzaloŵe ufumu wake. Ndiye kuti Davideyo adaaoneratu zimenezi, zakuti Khristu adzauka kwa akufa, ndipo pamenepo adanena mau aja akuti, “ ‘Iye sadasiyidwe ku Malo a anthu akufa, ndipo thupi lake silidaole.’ Yesu yemweyo Mulungu adamuukitsadi kwa akufa, ndipo tonsefe ndife mboni za zimenezi. Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira. Pajatu Davide sadakwere kupita Kumwamba, koma iye yemwe adati, “ ‘Ambuye adauza Mbuye wanga kuti, Khala ku dzanja langa lamanja mpaka ndisandutse adani ako kuti akhale ngati chopondapo mapazi ako.’ “Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.” Pamene anthu aja anamva zimenezi, zidaŵalasa mtima, ndipo adafunsa Petro ndi atumwi ena aja kuti, “Abale, tsono ifeyo tichite chiyani?” Petro adaŵauza kuti, “Tembenukani mtima, ndipo aliyense mwa inu abatizidwe m'dzina la Yesu Khristu. Mukatero machimo anu akhululukidwa, ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.” Onse aja adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo adayamba kulankhula zilankhulo zachilendo, monga Mzimuyo ankaŵalankhulitsira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:42

Anthuwo ankasonkhana modzipereka kuti amve zimene atumwi ankaphunzitsa. Ankayanjana, ndipo ankadya Mgonero wa Ambuye ndi kupemphera pamodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:43

Anthu onse ankaopa Mulungu poona zozizwitsa ndi zizindikiro zambiri zimene atumwi ankachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:29-31

Ndiye tsono Ambuye, onani zimene akutiwopsezazi, ndipo mutithandize atumiki anufe, kuti tilankhule mau anu molimba mtima ndithu. Tsono adaŵagwira, ndipo poti kunali kutada kale, adaŵaika m'ndende kufikira m'maŵa. Tambalitsani dzanja lanu kuti anthu achire, ndipo pachitike zizindikiro ndi zozizwitsa m'dzina la Mtumiki wanu wopatulika.” Atatha kupemphera, nyumba imene adasonkhanamo ija idayamba kugwedezeka. Onse adadzazidwa ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula mau a Mulungu molimba mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:33

Atumwi ankachita umboni ndi mphamvu yaikulu kuti Ambuye Yesu adaukadi kwa akufa, ndipo onse Mulungu ankaŵakomera mtima kwambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:12-16

Atumwi ankachita zizindikiro ndi zozizwitsa zambiri pakati pa anthu. Onse okhulupirira Khristu ankasonkhana ndi mtima umodzi m'Khonde la Solomoni. Mwa anthu enawo panalibe ndi mmodzi yemwe amene adaalimba mtima kuti azisonkhana nawo, komabe anthu onse ankaŵatama. Ndipo anthu okhulupirira Ambuye ankachulukirachulukira, mwakuti linali ndithu gulu lalikulu la amuna ndi akazi omwe. Tsono anthu ankatulutsira odwala ao m'miseu yamumzinda, nkumaŵagoneka pa mabedi ndi pa mphasa, kuti Petro podutsapo, chithunzithunzi chake chokha ena mwa iwo chiŵafike. Kunkasonkhananso anthu ochuluka ochokera ku midzi yozungulira Yerusalemu. Anali atanyamula anthu odwala, ndiponso ena osautsidwa ndi mizimu yoŵaipitsa. Onsewo ankachiritsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:8

Stefano anali munthu amene Mulungu adamkomera mtima kwambiri namdzaza ndi mphamvu, kotero kuti ankachita zizindikiro zozizwitsa pakati pa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:6-7

Makamu a anthu ndi mtima umodzi ankatchera makutu ku zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera mau ake nkumaona zozizwitsa zimene iye ankachita. Pakuti mizimu yonyansa inkatuluka mwa anthu ambiri amene anali atagwidwa nayo, nimafuula kwambiri. Ndipo ambiri amene anali akufa ziwalo kapena opunduka, ankachira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 10:38

Mukudziŵa za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu adaamudzoza ndi Mzimu Woyera nampatsa mphamvu. Tsono popeza kuti Mulungu anali naye, adapita ponseponse akuchita ntchito zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:2-3

Tsiku lina pamene iwo adasonkhana kuti apembedze Ambuye ndi kuti asale zakudya, Mzimu Woyera adaŵauza kuti, “Mundipatulire Barnabasi ndi Saulo kuti akagwire ntchito imene ndaŵaitanira.” “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele. Kenaka anthu adapempha kuti aŵapatse mfumu, ndipo Mulungu adaŵapatsa Saulo, mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, iye nkuŵalamulira pa zaka makumi anai. Pambuyo pake Mulungu adamchotsa Sauloyo, naika Davide kuti akhale mfumu yao. Za iyeyu Mulungu adanena kuti, ‘Ndapeza Davide, mwana wa Yese, ndiye munthu wanga wapamtima, amene adzachita zonse zimene Ine ndifuna.’ Mwa zidzukulu za Davideyo Mulungu adasankha Yesu kuti akhale Mpulumutsi wa Aisraele, monga momwe adaalonjezera kale. Iyeyo asanayambe ntchito, Yohane ankalalikira Aisraele onse kuti atembenuke mtima ndi kubatizidwa. Pamene Yohane anali pafupi kutsiriza ntchito yake, adafunsa anthu kuti, ‘Kodi inu mumayesa kuti ine ndine yani? Inetu sindine amene mukumuyembekezayo ai. Koma pakubwera wina pambuyo panga amene ine sindili woyenera ngakhale kumvula nsapato zake.’ “Ine abale, zidzukulu za Abrahamu, ndi ena nonse oopa Mulungu, uthenga wa chipulumutsowu Mulungu watumizira ife. Anthu okhala ku Yerusalemu ndi akulu ao sadamzindikire Yesu, ndipo sadamvetse mau a aneneri amene amaŵerengedwa tsiku la Sabata lililonse. Komabe pakumzenga mlandu Yesuyo kuti aphedwe, adachitadi zimene aneneri adaaneneratu. Ngakhale sadapeze konse chifukwa chomuphera, komabe adapempha Pilato kuti Yesuyo aphedwe. Ndipo atachita zonse zimene zidalembedwa za Iye, adamtsitsapo pa mtanda paja namuika m'manda. Tsono atasala zakudya ndi kupemphera adaŵasanjika manja naŵatuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:48-49

Pamene anthu a mitundu ina aja adamva zimenezi, adakondwa, nayamikira wawu a Ambuye. Ndipo onse amene Mulungu adaaŵasankha kuti alandira moyo wosatha, adakhulupirira. Mau a Ambuye adafalikira m'dziko monse muja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 16:5

Motero mipingo ya akhristu inkamangidwa pa chikhulupiriro cholima, ndipo oloŵamo ankachulukirachulukira tsiku ndi tsiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:11-12

Mulungu adachita zozizwitsa kwambiri kudzera kwa Paulo. Anthu ankati akatenga zitambaya kapena nsalu zina zimene Paulo ankagwiritsa ntchito, nakaziika pa anthu odwala, odwalawo ankachira, ndipo mizimu yoipa inkatuluka mwa iwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:37

Koma pa zonsezi tili opambana ndithu chifukwa cha Iye amene adatikonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:5

Momwemonso ife, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, olumikizana mwa Khristu, ndipo tonse, aliyense pa mbali yake, ndife ziwalo zolumikizana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:6-8

Tili ndi mphatso zosiyanasiyana malinga ndi m'mene Mulungu adatigaŵira mwa kukoma mtima kwake. Ngati mphatso yathu nkulalika mau a Mulungu, tiigwiritse ntchito molingana ndi chikhulupiriro chathu. Ngati mphatso yathu nkutumikira, titumikire ndithu. Ngati nkuphunzitsa, tiphunzitse ndithu. Ngati nkulimbikitsa ena, tiŵalimbikitse ndithu. Wogaŵana ndi anzake zimene ali nazo, azichita moolowa manja. Amene ali mtsogoleri, azigwira ntchito yake mwachangu. Wochitira ena chifundo, azichita mokondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 15:18-19

Sindidzalimba mtima kulankhula za kanthu kena ai, koma zokhazo zimene ndimachita kudzera mwa Khristu, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kumvera. Zimenezi ndidazichita ndi mau anga ndi ntchito zanga, ndi zizindikiro ndi zozizwitsa zamphamvu zochitika ndi mphamvu za Mzimu Woyera. Motero Uthenga Wabwino wonena za Khristu ndidaulalika kwathunthu ku Yerusalemu ndi ku dziko lozungulira mpaka ku Iliriko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 1:18

Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 3:16

Kodi inu simudziŵa kuti ndinu nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:20

Pakuti mu Ufumu wa Mulungu chachikulu si mau chabe, koma ntchito.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:4-5

Tsono mutasonkhana m'dzina la Ambuye Yesu, inenso m'maganizo ndili nanu pomwepo, ndi mphamvu ya Ambuye athu Yesu, munthuyo mumpereke kwa Satana, kuti thupi lake liwonongedwe, ndipo pakutero mzimu wake udzapulumutsidwe pa tsiku la Ambuye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:4-7

Tsonotu pali mphatso zamitundumitundu, koma wozipereka ndi Mzimu Woyera mmodzimodzi. Pali njira zosiyanasiyana zotumikira, koma Ambuye amene timaŵatumikira ndi amodzimodzi. Pali mphamvu zosiyanasiyana, koma Mulungu ndi mmodzimodzi amene amagwiritsa ntchito mphamvu zonsezo mwa munthu aliyense. Mzimu Woyera amapatsa munthu aliyense mphatso yakutiyakuti yoti aigwiritse ntchito yopindulitsa anthu onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 12:27-28

Tsono inuyo nonse pamodzi ndinu thupi la Khristu, ndipo aliyense mwa inu ndi chiwalo cha thupilo. Mulungu mu Mpingo wake adaika anthu aŵa: poyamba atumwi, kachiŵiri aneneri, kachitatu aphunzitsi. Adaikanso anthu amene ali ndi mphamvu za kuchita zozizwitsa, ena amene ali ndi mphamvu za kuchiritsa matenda, ena amene ali ndi mphatso ya kulongosola ntchito, ndiponso ena amene ali ndi mphatso ya kulankhula zilankhulo zosadziŵika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 14:12

Inunso chimodzimodzi: popeza kuti mwaika mtima pa mphatso za Mzimu Woyera, muziyesetsa kuzigwiritsa ntchito, makamaka mphatso zolimbikitsa mpingo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:57

Koma tiyamike Mulungu amene amatipambanitsa mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 4:7

Koma ife ndife mbiya zadothi chabe zosungiramo chumachi, kuti padziŵike kuti mphamvu zazikulu zoterezi ndi za Mulungu, osati zathu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 12:9

koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:18-20

Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake. Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa, Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere. imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 1:22-23

Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo. Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 2:19-22

Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu. Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu. Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya. Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye. Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:10-11

Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu. Mulungu adachita zimenezi kuti zichitikedi zimene Iye adakonzeratu mwa Khristu Yesu Ambuye athu chikhalire, nthaŵi isanayambe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 3:20-21

Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza. Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:11-13

Iyeyu ndiye amene “adapereka mphatso kwa anthu.” Mphatso zake zinali zakuti ena akhale atumwi, ena aneneri, ena alaliki, ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yao inali yakuti akonzeretu anthu a Mulungu kuti akagwire ntchito yotumikira, ndi kulimbitsa Mpingo umene uli thupi la Khristu. Motero potsiriza, tonse tidzafika ku umodzi umene umapezeka pakukhulupirira, ndiponso pakudziŵa Mwana wa Mulungu. Pamenepo tidzakhwima ndithu, ndi kufika pa msinkhu wathunthu wa Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:23

Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa Mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:10-11

Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu. Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:17-18

Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani. Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:13

Ndingathe kuchita zonse chifukwa Khristu amandipatsa mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 1:18

Iye ndiyenso mutu wa mpingo thupi lake. Ndiye chiyambi chake, Woyambirira mwa ouka kwa akufa, kuti pa zonse Iye akhale wopambana ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:15-16

Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 1:5

Paja Uthenga Wabwino umene tidadza nawo kwa inu sunali wapakamwa chabe, koma tinkaulalika ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndiponso mosakayika konse. Mukudziŵa m'mene tinkakhalira pakati panu pofuna kuti tikuthandizeni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 1:11-12

Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu. Motero dzina la Ambuye athu Yesu lidzalemekezedwa mwa inu, ndipo inu mudzalemekezedwa mwa Iye. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:15

Koma zina zikandichedwetsa, zimene ndanenazi zidzakudziŵitsa za m'mene anthu ayenera kukhalira m'banja la Mulungu, limene lili Mpingo wa Mulungu wamoyo, ndi mzati wochirikiza choona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 1:7

Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 2:21

Tsono munthu akadziyeretsa nkusiya zotsikazi, adzakhala ngati chiŵiya cha ntchito zolemerera. Adzakhala wopatulika ndi wofunika zedi kwa Ambuye ake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:2

uzilalika mau a Mulungu. Uziŵalalika molimbikira, pa nthaŵi imene anthu akuŵafuna, ngakhalenso pamene sakuŵafuna. Uziŵalozera zolakwa zao, uziŵadzudzula, uziŵalimbitsa mtima, osalephera kuŵaphunzitsa moleza mtima kwenikweni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 2:14-15

Paja Iye adadzipereka chifukwa cha ife, kuti atipulumutse ku zoipa zathu zonse, ndi kutiyeretsa kuti tikhale anthu ake achangu pa ntchito zonse zabwino. Zimenezi ndizo zimene uyenera kumaphunzitsa. Uziŵalimbikitsa anthu, ndi kuŵadzudzula komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 2:4

Mulungu yemwe ankachitira umboni pakuchita zizindikiro, zinthu zozizwitsa ndi ntchito zamphamvu zamitundumitundu, ndi pakuŵagaŵira mphatso za Mzimu Woyera monga momwe Iye ankafunira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:24-25

Tizikumbukirana kuti tilimbikitsane kukondana ndi kuchita ntchito zabwino. Tisamakhalakhala ku misonkhano yathu, monga adazoloŵera ena, koma ife tizilimbitsana mtima, makamaka poona kuti tsiku la Ambuye likuyandikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 12:28-29

Popeza kuti talandira ufumu wosagwedezeka, tizithokoza Mulungu, ndipo pakutero timpembedze moyenera, mwaulemu ndi mwamantha. Paja Mulungu wathu ndi moto wopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:5

Inunso mukhale ngati miyala yamoyo yoti Mulungu amangire nyumba yake. M'menemo muzitumikira ngati ansembe opatulika, pakupereka nsembe zochokera ku mtima, zokomera Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:9

Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10-11

Aliyense mphatso imene adalandira kwa Mulungu azitumikira nayo anzake. Mukhale ngati akapitao ogwiritsa bwino ntchito mphatso zamitundumitundu zochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amalankhula, mau ake akhaledi mau ochokera kwa Mulungu. Aliyense amene amatumikira, atumikire ndi mphamvu zimene Mulungu ampatsa, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-3

Mau angawo ndi aŵa: Ŵetani gulu la nkhosa za Mulungu zimene zili m'manja mwanu. Musaziyang'anire ngati kuti wina akuchita kukuumirizani, koma mofuna nokha, monga momwe afunira Mulungu. Musagwire ntchito yanuyo potsatira phindu lochititsa manyazi, koma ndi mtima wofunitsitsa kutumikira. Musakhale ngati mafumu odzikuza potsogolera anthu amene muyenera kuŵayang'anira, koma onetsani chitsanzo chabwino kwa nkhosazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 1:3

Mulungu mwa mphamvu zake adatipatsa zonse zotithandiza kukhala ndi moyo ndiponso opembedza, pakutidziŵitsa za Iyeyo amene adatiitana ku ulemerero ndi ubwino wake woposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:4-5

Chifukwa aliyense amene ali mwana wa Mulungu, amagonjetsa dziko lapansi. Chimene timagonjetsera dziko lapansilo ndi chikhulupiriro chathu. Ndani amagonjetsa dziko lapansi? Amaligonjetsa si wina ai, koma wokhulupirira kuti Yesu ndi Mwana wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 1:5-6

Akukomereninso mtima ndi kukupatsani mtendere Yesu Khristu, mboni yokhulupirika, amene ali woyambirira kulandira moyo waulemerero, amenenso ali Mfumu yolamula mafumu onse a pa dziko lapansi. Iyeyo amatikonda, ndipo ndi magazi ake adatimasula ku machimo athu. Iye adatisandutsa mafumu, kuti tizitumikira Mulungu Atate ake modzipereka ngati mtundu wa ansembe. Motero Yesu Khristuyo alandire ulemerero ndi mphamvu zolamulira mpaka muyaya. Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:7

“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsa mwai wodya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku Paradizo la Mulungu Kumwamba.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:17

“Amene ali ndi makutu, amvetsetse zimene Mzimu Woyera akuuza mipingozi. “Amene adzapambane, ndidzampatsako chakudya chobisika cha mana. Ndidzampatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziŵa iye yekha, osati wina aliyense.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:26-28

Amene adzapambane ndi kuchita mpaka potsiriza zimene ndamlamula, ndidzampatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. Adzailamulira ndi ndodo yachitsulo, nadzaiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi womwe Ine ndidaulandira kwa Atate. Ndidzampatsanso Nthanda, nyenyezi yoŵala m'mamaŵa ija.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:12

Amene adzapambane, ndidzamsandutsa mzati wokhazikika m'Nyumba ya Mulungu wanga. Sadzatulukamonso, ndipo pa iye ndidzalemba dzina la Mulungu wanga, ndi la mzinda wa Mulungu wanga. Mzindawo ndi Yerusalemu watsopano, wotsika Kumwamba kuchokera kwa Mulungu wanga. Pa iye ndidzalembanso dzina langa latsopano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:21

Amene adzapambane, ndidzamlola kukhala nane pamodzi pa mpando wanga wachifumu, monga momwe ndidachitira Ineyo: ndidapambana, ndipo ndikukhala pamodzi ndi Atate anga pa mpando wao wachifumu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 12:11

Abale athuwo adamgonjetsa ndi magazi a Mwanawankhosa uja, ndiponso ndi mau amene iwo ankaŵachitira umboni. Iwo adadzipereka kotheratu, kotero kuti sadaope ngakhale kufa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 19:7-8

Tikondwere ndi kusangalala, ndi kumtamanda, pakuti nthaŵi ya ukwati wa Mwanawankhosa uja yafika, mkwati wake wamkazi waukonzekera ukwatiwo. Iye waloledwa kuvala zovala za nsalu yabafuta, yoŵala, yoombedwa bwino.” (Zovala zabafutazo zikutanthauza ntchito zabwino za anthu a Mulungu.)

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 20:4-6

Pambuyo pake ndidaona mipando yachifumu, ndipo okhala pamipandopo adapatsidwa mphamvu zoweruzira milandu. Ndidaonanso mizimu ya anthu amene adaŵadula pakhosi chifukwa cha kuchitira Yesu umboni, ndiponso chifukwa cha kulalika mau a Mulungu. Iwowo sadapembedze nao chilombo chija kapena fano lake lija, ndipo adakana kulembedwa chizindikiro chija pa mphumi kapena pa dzanja. Adakhalanso ndi moyo nkumalamulira pamodzi ndi Khristu zaka chikwi chimodzi. (Akufa ena onse sadaukenso mpaka zitatha zaka zomwezo chikwi chimodzi.) Kumeneku ndiye kuuka koyamba. Ngodala anthu amene adzauke nao pa kuuka koyamba kumeneku. Ameneŵa ndiwo akeake a Mulungu. Imfa yachiŵiri ilibe mphamvu pa iwo, koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Yesu Khristu, ndipo azidzalamulira pamodzi naye zaka chikwi chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:2-3

Tsono ndidaona Mzinda Woyera, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera Kumwamba kwa Mulungu. Unali wokonzeka ngati mkwati wamkazi wokonzekera mwamuna wake. achisanu anali a mwala mwina mofiira mwina mwabrauni; achisanu ndi chimodzi anali a mwala wofiira; achisanu ndi chiŵiri anali a mwala wachikasu; achisanu ndi chitatu anali a mwala wobiriŵira modera; achisanu ndi chinai anali a mwala wakadzira; achikhumi anali a mwala wachisipu; achikhumi ndi chimodzi anali a mwala wabuluu ngati changululu; achikhumi ndi chiŵiri anali a mwala wofiirira. Zitseko za pa zipata khumi ndi ziŵiri zija zinali za miyala yamtengowapatali kwambiri. Chitseko chilichonse chinali cha mwala umodzi wa mtundu womwewo. Ndipo mseu wamumzindamo unali wa golide wangwiro, woonekera mpaka pansi, ngati galasi. Sindidaonenso Nyumba ya Mulungu mumzindamo, pakuti Nyumba yake ndi Ambuye Mulungu, Mphambe, mwini wake, ndiponso Mwanawankhosa uja. Palibe chifukwa choti dzuŵa kapena mwezi ziziŵala pamzindapo, pakuti ulemerero wa Mulungu ndiwo umaŵalapo, ndipo nyale yake ndi Mwanawankhosa uja. Anthu a mitundu yonse adzayenda m'kuŵala kwake kwa mzindawo, ndipo mafumu a pa dziko lonse lapansi adzabwera ndi ulemerero wao m'menemo. Zitseko za pa zipata zake zidzakhala zosatseka tsiku lonse, chifukwa kumeneko kudzakhala kulibe usiku. Ndipo m'menemo adzabwera ndi ulemerero wa anthu a mitundu yonse, pamodzi ndi chuma chao. Koma simudzaloŵa kanthu kalikonse kosayera, kapena munthu aliyense wochita zonyansa, kapenanso wabodza. Okhawo amene maina ao adalembedwa m'buku la amoyo la Mwanawankhosa uja ndiwo adzaloŵemo. Ndidamva mau amphamvu ochokera ku mpando wachifumu uja. Mauwo adati, “Tsopano malo okhalamo Mulungu ali pakati pa anthu. Iye adzakhala nawo pamodzi, ndipo iwo adzakhala anthu akeake. Mulungu mwini adzakhala nawo, ndipo adzakhala Mulungu wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 21:7

Aliyense amene adzapambane, adzalandira zimenezi, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wake, iye adzakhala mwana wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:1

Yesu adasonkhanitsa ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, naŵapatsa mphamvu pa mizimu yoipitsa anthu, kuti aziitulutsa mwa anthuwo, ndiponso mphamvu zochiritsira nthenda zonse za anthu ndi zofooka zao zam'thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 18:19-20

“Ndikunenetsanso kuti aŵiri mwa inu mutavomerezana pansi pano popempha kanthu kalikonse, Atate anga akumwamba adzakupatsani. Apo Yesu adaitana mwana namuimiritsa pakati pao, Pajatu pamene aŵiri kapena atatu asonkhana m'dzina langa, Ineyo ndili nao pomwepo.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 24:14

Ndipo Uthenga Wabwinowu wonena za ufumu wa Mulungu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, kuti anthu a mitundu yonse apezepo umboni. Pamenepo ndiye chimalizo chidzafike.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 1:39

Tsono adapita nalalika m'nyumba zamapemphero ku Galileya konseko, ndipo ankatulutsa mizimu yoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 16:20

Tsono ophunzira aja adanka nalalika ponseponse. Ambuye ankagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo ankatsimikiza mau ao ndi zozizwitsa zimene ankachita.]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:1-2

Yesu adaitana ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja naŵapatsa ulamuliro ndi mphamvu zotulutsira mizimu yoipa yonse ndi zochiritsira nthenda. Pamene atumwi aja adabwerako, adafotokozera Yesu zonse zimene adaachita. Tsono Iye adaŵatenga nakakhala nawo paokha ku mudzi wina, dzina lake Betsaida. Anthu ambirimbiri ataona zimenezi, adamtsatira. Iye adaŵalandira bwino nayamba kulankhula nawo za ufumu wa Mulungu, nkumachiritsa odwala. Dzuŵa lili pafupi kuloŵa, ophunzira khumi ndi aŵiri aja adadzauza Yesu kuti, “Bwanji anthuŵa azinyamuka tsopano, apite ku midzi ndi ku miraga ili pafupiyi, kuti akapeze malo ogona ndiponso chakudya, chifukwatu kuno nkuthengo.” Koma Yesu adaŵauza kuti, “Inuyo apatseni chakudya.” Iwo adati, “Tili ndi buledi msanu ndi nsomba ziŵiri zokha. Kaya kapena tipite tikaŵagulire anthu onseŵa chakudya?” Ndiye kuti amuna okha adaalipo ngati zikwi zisanu. Tsono Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Auzeni anthuŵa akhale pansi m'magulumagulu, gulu lililonse anthu ngati makumi asanu.” Ophunzira aja adaŵakhalitsadi anthu onse aja pansi. Pambuyo pake Yesu adatenga buledi msanu uja ndi nsomba ziŵiri zija, nayang'ana kumwamba, nkuthokoza Mulungu. Kenaka atanyemanyema bulediyo, adazipereka kwa ophunzira ake kuti agaŵire anthuwo. Anthu onse aja adadya nakhuta. Ndipo ophunzira aja adatola zotsala, nkudzaza madengu khumi ndi aŵiri. Nthaŵi ina pamene Yesu ankapemphera yekha, ophunzira ake adaali naye. Tsono Iye adaŵafunsa kuti, “Kodi anthu amati Ine ndine yani?” Iwo adati, “Ena amati ndinu Yohane Mbatizi, ena amati ndinu Eliya. Koma enanso amati mneneri wina wakale wauka kwa akufa.” Adaŵatuma kuti akalalike za ufumu wa Mulungu, ndi kukachiritsa anthu odwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:6

Ophunzira aja adapitadi, adanka nalalika Uthenga Wabwino ku midzi yonse, nkumachiritsa anthu ponseponse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 24:47

kuti m'dzina lake mau alalikidwe kwa anthu a mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu, mau akuti atembenuke mtima, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:15

Koma Ambuye adamuuza kuti, “Pita, pakuti iyeyu ndi mtumiki wanga amene ndidamsankha kuti akalalikire dzina langa anthu a mitundu ina, mafumu, ndiponso Aisraele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 12:24

Koma mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 14:3

Paulo ndi Barnabasi adakhala komweko kanthaŵi ndithu, akulalika molimba mtima za kukoma mtima kwa Ambuye. Ndipo Ambuye ankachitira umboni mau ao pakuŵapatsa mphamvu zochitira zizindikiro ndi zozizwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:1

Motero tsopano palibiretu mlandu wotsutsa anthu amene amakhala mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 10:14-15

Kodi anthu angatame Mulungu bwanji mopemba ngati sadamkhulupirire? Ndipo angamkhulupirire bwanji ngati sadamve za Iye? Ndipo angamve za Iye bwanji ngati palibe wina wolalika? Ndipo anthu angalalike bwanji ngati palibe oŵatuma? Paja mau a Mulungu akuti, “Nchokondweretsa zedi kuwona olalika Uthenga Wabwino akufika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:24

Khristu mwiniwake adasenza machimo athu m'thupi lake pa mtanda, kuti m'machimo tikhale ngati akufa, koma pakutsata chilungamo tikhale amoyo ndithu. Mudachiritsidwa ndi mabala ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, kukhalapo kwanu ndi mtendere ndi ufulu kwa mzimu wanga. Chikondi chanu chandilimbitsa ndipo chapatsa chakudya mzimu wanga. Zikomo chifukwa mwapatsa mpingo wanu mphamvu pa mdima. Ndife asilikali a gulu lankhondo lanu ndipo mwatipatsa mphamvu kudzera mwa Mzimu Woyera wanu. Mawu anu ndi pemphero ndi zida zamphamvu zolimbanirana ndi mdani. Inu munatiuza kuti zida zathu siziri za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu kuti zigwetse mipanda, zigonjetse nzeru zonse ndi kudzikuza kulikonse kumene kukutsutsana ndi kudzifuna kwa Mulungu, ndi kugonjetsa maganizo onse kukhala omvera kwa Khristu. Ndikupempha kuti mulimbitse chikhulcho cha mpingo wanu wokondedwa, awathandize kumvetsa kuti chipambano chenicheni chimapezeka kudzera muubwenzi wolimba nanu, kuti mpingo woima chilili ndi womvera ndipo uli ndi chida champhamvu chotchedwa pemphero ndi kusala kudya. Ndikupempha kuti athe kufalitsa kukhalapo kwanu kwamphamvu kwa onse ozungulira iwo, kudzera muzozizwitsa, zizindikiro, zodabwitsa, ndi zinthu zazikulu. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa