Mphamvu ya Mulungu ndi yosayerekezeka, yosatheka kuifotokoza, yokhoza kusintha, kuwombola, kuyeretsa ndi kulungamitsa munthu aliyense wosankhidwa kukhala mwana wake. Baibulo limatiuza za mphamvu yake, Mulungu angathe zonse, palibe chosatheka kwa Iye, ndi wamkulu kuposa mavuto aliwonse ndipo ali ndi mphamvu yosintha zinthu zonse.
Iye ndi Ambuye wa moyo, amapitirira kuposa matenda aliwonse, angathe kuchiritsa matenda aliwonse ndi kukupatsa chimene ukufuna. Muimbire Iye ndipo ukhulupirire ndi mtima wako wonse, ndipo udzalandira chimene wakhala ukupempha. Mulungu amagwira ntchito pamene mphamvu zako zatha, amautsa wogwa ndi kusunga chimene chinali chitatayika.
Mulungu ndi wopambana zonse, wokwanira ndi wamphamvu zonse. Choncho, usaope, Atate wako akumwamba adzakupatsa njira yopulumukira ndipo adzakhala mtendere wako pakati pa mavuto. M'masautso adzasunga moyo wako, ndipo udzawona ubwino wake ndi chikondi chake chachikulu masiku onse a moyo wako.
Wakumasula kuti ulalitse zodabwitsa zake ndi mphamvu zake zopanda malire. Mulungu amene amasunga chilengedwe chonse amakusamalira ndipo ndi wamphamvu kuposa mdani wako wamkulu.
Deuteronomio 32:39: “Taonani tsopano kuti Ine, Ine ndine, ndipo palibe Mulungu wina koma Ine; Ine ndipha, ndi Ine ndipatsanso moyo; Ine ndivulaza, ndi Ine ndichirirsanso; ndipo palibe wopulumutsa m’dzanja langa.”
Pajatu chilengedwere cha dziko lapansi anthu akhala akuzindikira makhalidwe osaoneka a Mulungu, ndiye kuti mphamvu zake zosatha, ndiponso umulungu wake. Akhala akuzizindikira poona zimene Mulungu adalenga. Choncho alibe konse pozembera.
Chauta amapatsa anthu ake mphamvu. Amaŵadalitsa anthu ndi mtendere. Salmo la Davide. Nyimbo yoimba potsekula Nyumba ya Mulungu
Komabe Iye adaŵapulumutsa malinga ndi ulemerero wa dzina lake, kuti aonetse mphamvu zake zazikulu.
Pakuti mfumuyo ikuti, “Ndachita zimenezi ndi mphamvu zanga ndiponso ndi nzeru zanga, pakuti kumvetsa nkwanga. Ndachotsa malire a mitundu ya anthu, ndipo ndafunkha chuma chao. Ndaŵatsitsa amene anali pa mipando yaufumu.
Anthu onsewo ankafuna kumkhudza, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa Iye ndi kuŵachiritsa onse.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Chauta ndi wamphamvu zedi. Ndi wosakwiya msanga, komabe sadzalola kuti munthu wochimwa akhale wosalangidwa. Pamene amayenda pamachitika kamvulumvulu ndi mphepo yamkuntho, mitambo ndiye fumbi limene mapazi ake amachititsa.
Iye ndiye kuŵala koonetsa ulemerero wa Mulungu, ndipo ndiye chithunzi chenicheni chosonyeza khalidwe la Mulungu. Iyeyu amachirikiza zonse ndi mau ake amphamvu. Atayeretsa mtundu wa anthu pakuŵachotsa machimo, adakakhala Kumwamba, ku dzanja lamanja la Mulungu waulemerero.
Adati, “Ambuye Mulungu, Mphambe, Inu amene mulipo ndipo munaliponso kale, tikukuyamikani chifukwa mwaonetsa mphamvu yanu yaikulu, ndipo mwayamba kukhazikitsa ufumu wanu.
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, kodi ndani ali wamphamvu ngati Inu Chauta, amene muli okhulupirika pa zonse?
Popeza kuti Chauta adakonda makolo anu, adasankha inu zidzukulu zao nakutulutsani ku Ejipito pakuwonetsa ulemu ndi mphamvu zake zazikulu.
Koma ndakusungani ndi moyo kuti muwone mphamvu zanga, kuti mbiri yanga iwande pa dziko lonse lapansi.
Inu Chauta dzanja lanu lamanja ndi laulemerero, chifukwa cha nyonga zake, dzanja lanu lamanja limatswanya adani.
“Ha! Inu Chauta! Mudalenga ndinu dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Mudazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu kwambiri. Palibe chokukanikani.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu.
Muwone tsopano kuti Mulungu uja ndine, Ine ndekha, palibenso mulungu wina. Ndimapha, Ine ndemwe ndimapatsanso moyo, ndimapweteka, Ine ndemwe ndimachiritsanso, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene angathe kupulumutsa munthu m'manja mwanga.
“Inu Ambuye Chauta, mwangondiwonetsa chiyambi chake chokha cha ntchito za ukulu wanu ndi mphamvu zanu. Kumwambako, ngakhalenso pansi pano, palibe Mulungu wina amene angathe kuchita zinthu zamphamvu zonga zimene inu mumachita.
Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa,
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba.
Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza.
Inu muli ndi mphamvu zonse. Dzanja lanu ndi lamphamvu kwambiri, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.
Mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandisandutsa wolalika Uthenga Wabwino umenewu, ndipo pakutero adaonetsapo mphamvu yake.
Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”
Ali kuti Chautayo amene adachita zinthu zodabwitsa ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose? Adagaŵa madzi am'nyanja, anthu ake akuwona, kuti dzina lake limveke mpaka muyaya.
koma Iwo adandiwuza kuti, “Chithandizo changa nchokukwanira. Mphamvu zanga zimaoneka kwenikweni mwa munthu wofooka.” Nchifukwa chake makamaka ndidzanyadira kufooka kwanga, kuti mphamvu za Khristu zikhale mwa ine.
“Inu Chauta, kodi pali mulungu wina wofanafana nanu? Ndani amafanafana ndi Inu, amene muli aulemu chifukwa cha ungwiro wanu? Ndani amafanafana nanu, Inu amene muli oopsa chifukwa cha ntchito zanu zaulemu ndi zodabwitsa?
Mudatambalitsa dzanja lanu lamanja, ndipo nthaka idaŵameza.
Zimenezi ndi pang'ono chabe za makhalidwe ake. Tingomva pang'ono za Iye ngati kunong'ona. Koma ndani angadziŵe kukula kwa mphamvu zake?”
Inu anthu, mukhulupirire Chauta mpaka muyaya, chifukwa chakuti Chauta Mulungu ndiye thanthwe losatha.
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Choncho Inu Mulungu, musandisiye ndekha ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbu, mpaka nditalalika mphamvu zanu kwa mibadwo yonse yakutsogolo.
Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.
Kukumveka mau akuti, “Konzani njira ya Chauta m'thengo, lungamitsani mseu wa Mulungu wathu m'chipululu.
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufooka, ngakhale anyamata amaphunthwa ndi kugwa.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Amadziŵa chiŵerengero cha nyenyezi, zonse amazitcha maina ake.
Mbuye wathu ndi wamkulu, ndipo ndi wa mphamvu zambiri, nzeru zake nzopanda malire.
Zimene umanena zingathe kukuphetsa kapena kukukhalitsa moyo, munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.
Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi, ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani. Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe. Adzakubwezera m'chikondi chake. Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.
Yesu adaŵayang'ana nati, “Kwa anthu zimenezi nzosatheka, koma zonse nzotheka ndi Mulungu.”
Chimene ndikufuna nchakuti ndidziŵe Khristu, ndiponso mphamvu zimene zidamuukitsa kwa akufa. Ndikufunanso kumva zoŵaŵa pamodzi naye ndi kufanafana naye pa imfa yake.
Mphambe sitingathe kumufika pafupi, ndi woopsa pa ulamuliro ndi pa mphamvu. Ndi wolungamadi kwambiri, sangazunze anthu.
Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.
Anthu adzasimba za mphamvu zanu zoopsa, inenso ndidzalalika za ukulu wanu.
Adzasimba za ubwino wanu, adzaimba nyimbo zotamanda kulungama kwanu.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu ndipo mumalamulira zonse, chifukwa muli ndi mphamvu zonse. Inu nokha mutha kukweza munthu ndi kumpatsa mphamvu.
Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
Kodi chilipo china choti chingakanike Chauta? Tsono pa nthaŵi yake, ndidzachitadi zimene ndalonjezazi, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”
Kudzera mwa Iye Mulungu adalenga zonse zakumwamba ndi zapansipano, zooneka ndi zosaoneka, mafumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu ena onse. Mulungu adalenga zonse kudzera mwa Iye, zonsezo adalengera Iyeyo.
Iyeyo analipo zinthu zonse pakadalibe, mwa Iye zinthu zonse zimalunzana pamodzi.
Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera akadzabwera pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ku Yerusalemu, ku Yudeya ndi ku Samariya konse, mpaka ku malekezero a dziko lapansi.”
Pajatu chimene chimaoneka ngati kupusa kwa Mulungu, nchanzeru kupambana nzeru za anthu. Ndipo chimene chimaoneka ngati kufooka kwa Mulungu, nchamphamvu kupambana mphamvu za anthu.
Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.
Chauta si wosoŵa mphamvu, kuti angalephere kukupulumutsani, ndipo si gonthi, kuti nkupanda kumva zimene mukupempha.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Yesu adadza pafupi naŵauza kuti, “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi pansi pano.
Chauta wadziwulula yekha, pakuweruza molungama, koma anthu oipa akodwa mu msampha wotcha iwo omwe.
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Muuzeni Mulungu kuti, “Ntchito zanu nzodabwitsa kwambiri. Mphamvu zanu nzazikulu, kotero kuti adani anu amakuŵeramirani moopa.
“Inu aYobe, tamvani izi, imani, muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu.
Kodi mukudziŵa m'mene Mulungu amazichitira, ndi m'mene amang'anipitsira mphezi m'mitambo yake?
Kaya mukudziŵa m'mene Mulungu amayalira mitambo, ntchito yosonyeza nzeru zake zodabwitsa,
Kaŵirikaŵiri ankamuyesa, ankamputa Woyera wa Israele.
Sadakumbukire mphamvu zake kapena tsiku limene adaŵaombola kwa adani ao,
Nchifukwa chake timakupemphererani nthaŵi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera moyo umene Iye adakuitanirani. Timapemphanso kuti ndi mphamvu zake akulimbikitseni kuchita zabwino zonse zimene mumalakalaka kuzichita, ndiponso ntchito zotsimikizira chikhulupiriro chanu.
Motero dzina la Ambuye athu Yesu lidzalemekezedwa mwa inu, ndipo inu mudzalemekezedwa mwa Iye. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha kukoma mtima kwa Mulungu wathu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu.
Motero mwa Khristu Mulungu adaŵalanda zida maufumu ndi maulamuliro onse, ndipo pamaso pa onse, adaŵayendetsa ngati akaidi pa mdipiti wokondwerera kupambana kwake.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.