Khalani amphamvu ndiponso mulimbe mtima. Musaŵaope anthu ameneŵa, musachite nawo mantha, chifukwa Chauta, Mulungu wanu, adzakhala nanu. Sadzalola kuti mulephere, ndipo sadzakusiyani.
Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”
Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.
Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse,
ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako.
Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Amene amadziŵa dzina lanu, Inu Chauta, amakukhulupirirani, pakuti Inu Chauta simuŵasiya anthu okufunitsitsani.
Ndakuuzani zimenezi kuti mukhale nawo mtendere pakukhulupirira Ine. M'dziko lapansi mudzaona masautso, koma limbikani, Ine ndagonjetsa mphamvu zoipa za dziko lapansi.”
Tikuwona masautso a mtundu uliwonse, koma osapsinjidwa. Tikuthedwa nzeru, koma osataya mtima.
Adani akutizunza, koma sitisoŵa wotithandiza. Akutigwetsa pansi, koma sitikugonja.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja.
Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
Musade nkhaŵa ndi kanthu kalikonse, koma m'mapemphero anu onse muzipempha Mulungu zimene zikusoŵani, ndipo nthaŵi zonse muzipemphe ndi mtima woyamika.
Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima.
Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu,
chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu.
Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Sindikukupatsani mtenderewo monga m'mene dziko lino lapansi limapatsira ai. Mtima wanu usavutike kapena kuda nkhaŵa.
Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”
Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.
Munthu amene ali ndi chikondi, alibe mantha, pakuti chikondi changwiro chimatulutsira mantha kunja. Munthu akamachita mantha, ndiye kuti akuwopa chilango, ndipo chikondi sichidafike pake penipeni mwa iye.
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?
Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu.
Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya.
Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.
Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe,
zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.
Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite.
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Mutichitire chifundo, Inu Chauta, tikukhulupirira Inu. Mutitchinjirize ndi dzanja lanu lamphamvu tsiku ndi tsiku, ndipo mutipulumutse pa nthaŵi yamavuto.
Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa.
Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.
Apo Chauta adafunsa kuti, “Kodi mkazi angathe kuiŵala mwana wake wapabere, osamumvera chifundo mwana wobala iye yemwe? Ndipotu angakhale aiŵale mwana wake, Ine ai, sindidzakuiŵalani konse.
Iwe Yerusalemu, ndidadinda chithunzi chako pa zikhatho zanga, zipupa zako ndimakhala ndikuziwona nthaŵi zonse.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.
Paja Mzimu amene Mulungu adatipatsa, si Mzimu wotipatsa mtima wa mantha ai, koma Mzimu wotipatsa mphamvu, chikondi ndi kudzigwira.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Ine wokhala ku mathero a dziko lapansi, ndataya mtima, ndipo ndikuitana Inu. Munditsogolere ku thanthwe lalitali.
Inutu ndinu kothaŵira kwanga, nsanja yolimba yonditeteza kwa adani.
Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Zonse zolembedwa m'Malembo kale, zidalembedwa kuti zitiphunzitse ife. Malembowo amatilimbikitsa ndi kutithuzitsa mtima, kuti tizikhala ndi chiyembekezo.
Mitima yathu ikuyembekeza Chauta, chifukwa Iye ndiye chithandizo ndi chishango chathu.
Mitima yathu imasangalala mwa Chauta, popeza kuti timadalira dzina lake loyera.
Inu mwakhala chithandizo changa, motero ndikuimba ndi chimwemwe pansi pa mapiko anu.
Mtima wanga ukukangamira Inu, dzanja lanu lamanja likundichirikiza.
Tsono Davide adauza mwana wake Solomoni kuti, “Khala wamphamvu ndipo uchite zimenezo molimba mtima. Usaope, usataye mtima, pakuti Chauta Mulungu wanga ali nawe. Sadzaleka kukusamala ndipo sadzakusiya pa ntchito zonse za Nyumba ya Chautazi.
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.
Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.
“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”
Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Pamene ndinkaganiza kuti, “Phazi langa likuterereka,” nkuti chikondi chanu chosasinthika chikundichirikiza.
Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.
Tsono Ambuye Chauta, Woyera uja wa Israele adati, “Ngati mutembenuka ndi kubwerera, mudzapulumuka. Ngati mudzinga ndi kukhulupirira, mudzakhala amphamvu.” Koma inu mudakana kutero.
Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama.
“Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi. Munthu wokhala mwa Ine, ndi Inenso mwa iye, amabereka zipatso zambiri. Pajatu popanda Ine simungathe kuchita kanthu.
Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.
Akunena kuti, “Ndidzayenda patsogolo pako, ndi kusalaza zitunda. Ndidzaphwanyaphwanya zitseko zamkuŵa, ndipo ndidzathyolathyola mipiringidzo yake yachitsulo.
Zoonadi, zokoma zanu ndi chikondi chanu zidzakhala ndi ine masiku onse a moyo wanga. Ndidzakhala m'Nyumba mwanu moyo wanga wonse.
Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.”
Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku.
Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto.
Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa.
Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga.
Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Tsono adani anga adzabwezedwa m'mbuyo pa tsiku lomwe ndidzaitana Mulungu. Ndikudziŵa kuti Mulungu ali pa mbali yanga.
Chauta ndi wokoma mtima ndi wolungama. Mulungu wathu ndi wachifundo.
Chauta amasunga a mtima wodzichepetsa. Pamene ndidagwa m'zoopsa, Iye adandipulumutsa.
Mulungu wopatsa mtendere, adaukitsa kwa akufa Ambuye athu Yesu, amene ndiye Mbusa wamkulu wa nkhosa, chifukwa cha imfa yake yotsimikizira Chipangano chamuyaya.
Mulunguyo akupatseni zabwino zonse zimene mukusoŵa kuti muzichita zimene Iye afuna. Ndipo mwa Yesu Khristu achite mwa ife zomkondweretsa, Khristuyo akhale ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Paja Mulungu ndiye amene amagwira ntchito mwa inu, muzifuna ndi kutha kuchita zimene zimkomera Iye.
Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.
Chauta mwafufuzafufuza, ndipo mwandidziŵa.
ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera, dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.
Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe, kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse, kwa Inu usiku umaŵala ngati usana, mdima uli ngati kuŵala.
Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga, mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa. Ntchito zanu zonse nzodabwitsa. Mumandidziŵa bwino kwambiri.
Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi, pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
Maso anu adandiwona ndisanabadwe. Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu, asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine, ndi osaŵerengeka konse.
Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga. Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu, ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.
Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi, pamenenso ndidzuka, mumazindikira maganizo anga muli kutali.
Anthuwo amakunenani zinthu zoipa, namakuukirani ndi mtima woipa.
Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta? Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?
Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni. Ndimaŵayesa adani anga.
Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga. Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.
Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse, ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona, mumadziŵa njira zanga zonse.
Yesu adauza ophunzira akewo kuti “Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu, khulupirirani Inenso.
Adavutika poona mavuto ao onse, Mngelo wochokera kwa Iye adaŵapulumutsa. Adaŵaombola mwa chikondi ndi chifundo chake. Wakhala akuŵasamala ngati ana kuyambira kale.
Ndipo Mulungu adati, “Ine ndemwe ndidzapita nawe pamodzi, ndipo ndidzakupatsa mtendere.”
Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.
Momwemonso Mzimu Woyera amatithandiza. Ndife ofooka, osadziŵa m'mene tiyenera kupempherera. Nchifukwa chake Mzimu Woyera mwiniwake amatipempherera ndi madandaulo osafotokozeka.
Mudzati, “Mulungu wathu ndi wotere, ndi Mulungu wathu kuyambira muyaya mpaka muyaya. Iye adzakhala wotitsogolera nthaŵi zonse.”
Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Ndidzatsogolera anthu akhungu m'miseu imene sadaidziŵe, ndidzaŵaperekeza pa njira zimene sadadzerepo konse. Ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwao kuti ukhale kuŵala, ndipo ndidzasalaza malo osasalala. Zimenezi ndidzazichitadi ndipo sindidzazilekera padera.
Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.
Nchifukwa chake sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifookerafookera, komabe mu mtima tikulandira mphamvu yatsopano tsiku ndi tsiku.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Mitima yathu siili pa zinthu zooneka, koma pa zinthu zosaoneka. Paja zooneka nzosakhalitsa, koma zosaoneka ndiye zamuyaya.
Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
Aliyense mwa iwo adzakhala ngati pothaŵirapo mphepo ndi malo obisalirapo namondwe. Adzakhala ngati mitsinje yoyenda m'dziko louma, ndipo ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m'chipululu.
“Kotero kuti dzanja langa lidzamchirikiza mpaka muyaya, mkono wanganso udzamulimbitsa.
“Adani sadzampambana, anthu oipa sadzamtsitsa.
Potsiriza, abale, muziika mtima pa zilizonse zabwino kwambiri ndi zotamandika, monga izi: zinthu zoona ndi zolemekezeka, zinthu zolungama, zoyera, zokongola, ndi zaulemu.
Muzichita zimene mudaphunzira ndi kulandira kwa ine, ndiponso zimene mudamva kwa ine ndi kuwonera kwa ine. Pamenepo Mulungu amene amapatsa mtendere adzakhala nanu.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!”
Mafumu oipa sadzalamulira nthaŵi yonse dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake, kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa.
Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.
Chauta akunena kuti, “Ineineyo ndine amene ndimakutonthozani mtima. Kodi ndinu yani kuti muziwopa munthu woti adzafa, mwanawamunthu amene angokhala nthaŵi yochepa ngati udzu?
Kodi ndinu yani kuti muziiŵala Chauta, Mlengi wanu, amene adayalika zakuthambo, ndi kuika maziko a dziko lapansi? Kodi ndinu yani kuti nthaŵi zonse muziwopa ukali wa anthu okuzunzani, amene angofuna kukuwonongani? Ukali wa anthu okuzunzaniwo tsopano uli kuti?
Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.
Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka.
Chauta amayang'ana anthu omumvera, ndi odalira chikondi chake chosasinthika.
Iye amachita izi kuti aŵapulumutse ku imfa ndi kuŵasungira moyo anthuwo pa nthaŵi ya njala.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.
Mbusa wabwino ndine. Nkhosa zanga ndimazidziŵa, ndipo izozo Ineyo zimandidziŵa,
monga momwe Atate amadziŵira Ine, nanenso nkuŵadziŵa Atatewo. Ndimatayirapo moyo wanga pa nkhosazo.
Chauta sadzataya anthu ake, kuti dzina lake lalikulu linganyozeke, poti chidamukondweretsa kuti akusandutseni anthu ake.
Tsono anthu aja adalira kwa Chauta pamene anali m'mavuto amenewo, ndipo Chauta adaŵapulumutsa ku mavuto aowo.
Chauta adatontholetsa namondwe, ndipo mafunde apanyanja adachita bata.
Waŵasonkhanitsa kuchokera ku maiko onse, kuchokera kuvuma ndi kuzambwe, kumpoto ndi kumwera.
Choncho anthuwo adasangalala chifukwa kudachita bata, ndipo Chauta adakaŵafikitsa kudooko kumene ankalinga.
Tsono ndidzakutsogolerani nthaŵi zonse, ndi kukupatsani zabwino. Matupi anu ndidzaŵalimbitsa. Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri, ngati kasupe wa madzi amene saaphwa.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Ambuye akulitsirekulitsire kukondana kwanu, ndiponso chikondi chanu cha pa anthu onse, monga momwe chikondi chathu cha pa inu chikukulirakulira.
Motero Iye adzalimbitsa mitima yanu kuti idzakhale yangwiro ndi yoyera pamaso pa Mulungu Atate athu, pamene Ambuye Yesu adzabwerenso pamodzi ndi oyera ake onse.
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama.
Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ndimakufunafunani. Mtima wanga ukumva ludzu lofuna Inu, thupi langa likulakalaka Inu ngati dziko louma, loguga ndi lopanda madzi.
Motero pali zinthu ziŵirizi, lonjezo ndi lumbiro, zimene sizingathe kusinthika, ndipo Mulungu sanganamirepo. Mwa zimenezi Mulungu adafuna kutilimbitsa mtima ife amene tidathaŵira kwa Iye, kuti tichigwiritse chiyembekezo chimene adatiikira pamaso pathu.
Chiyembekezo chimenechi tili nacho ngati nangula wa moyo wathu. Nchokhazikika, nchosagwedezeka konse, ndipo chimabzola chochinga cha Nyumba ya Mulungu ya Kumwamba, nkukaloŵa mpaka ku Malo Opatulika am'katikati.
Chauta adzaona kuti cholinga chake pa ine chichitikedi. Chikondi chanu, Inu Chauta, nchamuyaya. Muipitirize ntchito imene mwaiyambayo.
Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Pamene amphaŵi ndi osauka akufunafuna madzi, koma osaŵapeza, ndipo kum'mero kwao kwangoti gwa ndi ludzu, Ine Chauta ndidzayankha pemphero lao, Ine Mulungu wa Israele sindidzaŵasiya.
Ndidzayendetsa mitsinje pakati pa zitunda zouma, ndipo akasupe adzatumphuka m'zigwa. Ndidzasandutsa chipululu kukhala chidziŵe cha madzi, ndi dziko louma kukhala akasupe.
Abale anga, pitani mukaloŵe m'nyumba zanu, ndipo mukadzitsekere. Mubisale pang'ono mpaka mkwiyo wa Chauta utatha.
Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse, sadzaiŵalika mpaka muyaya.
Saopa akamva zoipa zimene zachitika. Mtima wake ndi wosasinthika, amakhulupirira Chauta.
Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.
Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.
Inu mwakhala ngati ngaka kwa anthu osauka, mwakhala ngati linga kwa anthu osoŵa pa nthaŵi yamavuto. Mwakhala ngati pobisalirapo namondwe, ndiponso ngati mthunzi wousirapo dzuŵa. Anthu ankhalwe ali ngati namondwe woomba pa khoma, ngati chitungu m'dziko louma.
Chauta ndiye amene ali kothaŵirako ndipo pa dziko lapansili amakusungani ndi mphamvu zosatha. Adathaŵitsa adani anu onse pamene munkayenda, ndipo adakuuzani kuti muŵaononge onse.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Ngati mukhala mwa Ine, ndipo mau anga akhala mwa inu, mupemphe chilichonse chimene mungachifune, ndipo mudzachilandiradi.
Mulungu angathe kukupatsani madalitso onse pakulu, kuti nthaŵi zonse mukhale ndi zokukwanirani inuyo, ndipo zinanso zochuluka kuti mukathandize pa ntchito zonse zabwino.