Chilichonse chili ndi nthawi yake, ndipo Mulungu yekha ndiye angakweze munthu. Sikuti ife tidzitamande tokha, koma Mlengi wa thambo ndi dziko lapansi, monga m’malemba m’buku la 2 Akorinto 10:17, “Iye amene adzitamande, adzitamande mwa Ambuye.”
Kudzitukumula, kunyada, ndi kudzikuza zimatsutsana ndi chipatso cha Mzimu Woyera, ndipo zimatulutsa Mzimu wa Mulungu, chifukwa iye amatsutsa odzikuza koma amapatsa chisomo odzichepetsa. Ngati ukufuna kukwezedwa, choyamba uzichepetse pamaso pa Yehova, ndipo ukadzichepetsa, iye adzafufuza mtima wako.
Ngati mumtima mwako mutuluka zabwino ndi zaukhristu, ndiye kuti iye adzakukweza ndi kukuika pakati pa anthu. Mulungu amafuna mitima yosalira zambiri yom’dziwa iye m’njira zake zonse ndipo sangathe kukhala popanda iye.
Usadzitamande ndi ntchito zako, koma tamanda kuti Yesu amakudziwa ndipo ntchito zako n’zoyera pamaso pake. Chenjera ndi kudzikuza ndipo ukhale wokonzeka kulandira chilango cha Wamphamvuyonse, monga m’malemba m’buku la Mateyu 23:12, “Aliyense wodzikweza adzachepetsedwa, ndipo wodzichepetsa adzakwezedwa.”
Sungani umunthu wako wamkati ndipo ulimbitse ubwenzi wako ndi Mulungu. Pemphero lachinsinsi lidzayankhidwa poyera. Mulungu amafuna ana omwe akufuna kukhala paubwenzi ndi iye, om’dziwa iye bwino osati ongooneka bwino, osafuna kudzionetsa kapena kuyang’ana phindu lawo, koma kuyang’ana kukhala naye.
Kagulu kochepa kameneka, kamene kadzakhala kokhulupirika ndi kudzisunga mwa Ambuye, iye adzakakweza pa nthawi yake.
Kugamula milandu sikuchokeratu kuvuma kapena kuzambwe, ndiponso sikuchokera ku chipululu. Koma ndi Mulungu yekha amene amagamula milandu, amatsitsa wina, nakweza wina.
Ndithu ndidzamsandutsa mwana wanga wachisamba, adzakhala wopambana mafumu a dziko lapansi.
Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse, amene alipo nthaŵi zonse, ndipo dzina lake ndi Woyera uja, akunena kuti, “Ndimakhala pa malo aulemu, oyera. Koma ndimakhalanso ndi anthu odzichepetsa ndi olapa mu mtima, kuti odzichepetsawo ndiŵachotse mantha, olapawo ndiŵalimbitse mtima.
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Chauta wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba, ndipo amalamulira zonse mu ufumu wake.
Iye amene adaatsika, ndi yemweyo amene adakwera, nabzola Kumwamba konse, kuti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye.
Ngakhale kabanja kakang'onong'ono kadzasanduka fuko, ndipo kafuko kakang'onong'ono kadzasanduka mtundu wamphamvu. Ndidzachita zimenezi mofulumira nthaŵi yake itafika. Ine ndine Chauta.”
Komatu tikuwona kuti Yesu, amene pa kanthaŵi pang'ono adaasanduka wochepera kwa angelo, adalandira mphotho ya ulemerero ndi ulemu chifukwa adamva zoŵaŵa za imfa. Zidatero chifukwa mwa kukoma mtima kwake Mulungu adaafuna kuti afere anthu onse.
Koma Inu Chauta, ndinu chishango changa chonditeteza, ndinu ulemerero wanga, mumalimbitsa mtima wanga ndinu.
Iye adakwezedwa kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, nalandira Mzimu Woyera, amene Atate adaalonjeza. Ndipo zimene mukuwona ndi kumvazi ndiye mphatso yake imene watitumizira.
Chifukwa cha chimenechi Mulungu adamkweza kopambana, nampatsa dzina lopambana dzina lina lililonse.
Chauta ndiye amene wachita zimenezi, zimenezi nzodabwitsa pamaso pathu. Lero ndiye tsiku limene Chauta adalipanga. Tiyeni tikondwe ndi kusangalala pa tsiku limeneli.
Ambuye Yesu atalankhula nawo, adatengedwa kupita Kumwamba, nakakhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
“Tsono Aisraele onse adziŵe ndithu kuti Yesu uja inu mudampachika pamtandayu, Mulungu adamsankhula kuti akhale Ambuye ndi Mpulumutsi.”
Ameneyo Mulungu adamkweza ku dzanja lake lamanja kuti akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi. Adachita zimenezi kuti apatse Aisraele mwai wotembenuka mtima kuti machimo ao akhululukidwe.
Masautso athu ndi opepuka, a nthaŵi yochepa, komabe akutitengera ulemerero umene uli waukulu kopambana, ndiponso wamuyaya.
Mudakonda chilungamo nkudana ndi zosalungama. Nchifukwa chake Ine, Mulungu wanu, ndakukwezani nkukudzozani ndi mafuta osonyeza chimwemwe, kupambana anzanu ena onse.”
Koma Chauta amakondwera ndi anthu omuwopa, amene amadalira chikondi chake chosasinthika.
amene adapita Kumwamba, ndipo ali ku dzanja lamanja la Mulungu. Kumeneko angelo ndi maulamuliro ndi zimphamvu zimamvera Iye.
Maso athu azipenyetsetsa Yesu amene ali woyambitsa chikhulupiriro chathu, ndiponso wochifikitsa pake penipeni. Chifukwa cha chimwemwe chimene chinkamudikira, Iyeyo adapirira zoŵaŵa zapamtanda. Adaŵanyoza manyazi a imfa yotere, ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.
Ndidamva angelowo akuimba mokweza mau kuti, “Mwanawankhosa amene adaaphedwayu, ngwoyenera kulandira mphamvu, chuma, nzeru, nyonga, ulemu, ulemerero ndi chiyamiko.”
Chauta amatsekula maso a anthu osapenya, Chauta amakweza anthu otsitsidwa. Chauta amakonda anthu ochita chilungamo.
“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”
Popeza kuti mudalandira manyazi, manyozo ndi zotukwana moŵirikiza, tsopano mudzalandira chigawo cha dziko lanu moŵirikizanso. Chimwemwe chanu chidzakhala chamuyaya.”
Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu kumwambamwamba, wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.
Inu Mulungu, onetsani ukulu wanu mumlengalenga monse. Wanditsani ulemerero wanu pa dziko lonse lapansi.
Komabe Chauta akufunitsitsa kuti akukomereni mtima. Ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo, chifukwa Chauta ndi Mulungu wachilungamo. Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Kuwopa Chauta kumaphunzitsa nzeru, ndipo ndi kudzichepetsa ndi ulemu, chili patsogolo nkudzichepetsa.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chikhulupiriro changa nchofumira kwa Iye. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa, ndiye linga langa ndipo sindidzagwedezeka.
Ndi mphatso ya Mulungu kwa anthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ntchito zao zolemetsa.
Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.
Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu zoti athe kupirira naŵalimbitsa mtima, akuthandizeni kumvana bwino, motsata chitsanzo cha Khristu Yesu, akuthandizeni kuti ndi mtima umodzi, nonse pamodzi mulemekeze Mulungu ndi Atate a Ambuye athu Yesu Khristu.
Ndidzayamika Chauta nthaŵi zonse, pakamwa panga padzatamanda Iye kosalekeza. Ngakhale anaamkango amasoŵa chakudya ndipo amakhala anjala, koma anthu amene amalakalaka Chauta, sasoŵa zinthu zabwino. Bwerani ana anga, mundimvere, ndidzakuphunzitsani kuwopa Chauta. Ndani mwa inu amakhumba moyo ndi kulakalaka kuti akhale masiku ambiri, kuti asangalale ndi zinthu zabwino? Ngati ufunadi moyo, usalankhule zoipa, pakamwa pako pasakambe zonyenga. Lewa zoipa, ndipo uchite zabwino. Funafuna mtendere ndi kuulondola. Ngati mumvera Chauta, adzakuyang'anirani ndipo adzayankha kupempha kwanu. Koma Chauta amaŵakwiyira anthu ochita zoipa, anthuwo sadzakumbukikanso pansi pano. Pamene anthu ake akulira kuti aŵathandize, Chauta amamva naŵapulumutsa m'mavuto ao onse. Chauta amakhala pafupi ndi anthu a mtima wosweka, amapulumutsa otaya mtima. Anthu a Mulungu amaona masautso ambiri. Komabe Chauta amawapulumutsa m'mavuto awo onse. Moyo wanga umanyadira Chauta. Anthu ozunzika amve ndipo akondwere. Chauta amasunga thupi la munthuyo, palibe fupa limene limasweka. Choipa chitsata mwini, anthu odana ndi munthu wa Mulungu adzalangidwa. Chauta amaombola moyo wa atumiki ake. Palibe wothaŵira kwa Iye amene adzalangidwe. Lalikani pamodzi nane ukulu wa Chauta, tiyeni limodzi tiyamike dzina lake.
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Ndani angalingane ndi Chauta, Mulungu wathu, amene akukhala kumwamba, wochita kuŵeramira pansi poyang'ana mlengalenga ndi dziko lapansi.
Koma monga zilirimu tikuwona kuti ankafuna dziko lina, lokoma kopambana, ndiye kuti dziko la Kumwamba. Nchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wao, popeza kuti Iye adaŵakonzera mzinda.
Chauta amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza. Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Zoonadi, mwaisandutsa yodala kopambana mpaka muyaya. Mwaisangalatsa ndi chimwemwe, chifukwa muli nayo.
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
Mtima wanga wadzaza ndi nkhani yokoma. Ndikuimbira mfumu nyimbo yangayi. Lilime langa lili ngati cholembera cha katswiri wodziŵa kulemba bwino.
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu.
Munthu amene amakongoza mosafuna phindu, amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo, zinthu zimamuyendera bwino.
Mukatero ndiye kuti mudzakondwa mwa Ine, Chauta, ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi. Mudzadyerera dziko limene ndidapatsa Yakobe kholo lanu. Ine Chauta ndalankhula zimenezi ndi pakamwa panga.”
Chauta atamandike, pakuti wamva liwu la kupempha kwanga. Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.
Anthu osasamala za Mulungu amandinyoza kwathunthu, komabe sindisiyana nawo malamulo anu.
Ngakhale Chauta ndi wamphamvu, amasamalira anthu otsika, koma anthu odzikuza amaŵadziŵira chapatali.
Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao. “Ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani ndi kukunyengezerani zoipa zamitundumitundu chifukwa cha Ine. Sangalalani, kondwerani, chifukwa mphotho yanu ndi yaikulu Kumwamba. Paja ndi m'menenso anthu ankazunzira aneneri amene analipo kale inu musanabadwe.
Anthu amene amafunafuna ulemerero, ulemu ndi moyo pakuchita ntchito zabwino molimbikira, Mulungu adzaŵapatsa moyo wosatha.
Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti? Chithandizo changa nchochokera kwa Chauta, amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Mafumu adzakhala ngati atate okulerani, akazi a mafumuwo adzakhala ngati amai okuyamwitsani. Adzagwetsa nkhope zao pansi ndi kukuŵeramirani. Adzaseteka fumbi la m'mapazi mwanu modzichepetsa. Pamenepo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndipo amene amakhulupirira Ine sadzachita manyazi.”
Ine ndikutsimikiza kuti masautso amene tikuŵamva tsopano salingana mpang'ono pomwe ndi ulemerero umene Mulungu adakonza kuti adzatiwonetse m'tsogolo muno.
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.
Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.
Onani m'mene ndimakondera malamulo anu, sungani moyo wanga chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika Ndidzakondwera ndi malamulo anu, ndipo mau anu sindidzaŵaiŵala. mau anu ndi oona okhaokha, malangizo anu onse olungama ngamuyaya.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Mumandiwonetsa njira ya ku moyo. Ndimapeza chimwemwe chachikulu kumene kuli Inu, ndidzasangalala mpaka muyaya ku dzanja lanu lamanja.
Koma tsono mudziŵe kuti Chauta wadzipatulira Iye yemwe anthu olungama. Chauta amamva ndikamuitana.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika. Amene amamvera Chauta, amaŵapatsa zofuna zao, amamvanso kulira kwao, naŵapulumutsa.
Si kukondwetsa kwake pamene mukuwona wamthenga akuyenda m'mapiri, akubwera ndi uthenga wabwino, akulengeza za mtendere, akudzetsa chisangalalo, akulengeza za chipulumutso, akuuza anthu a ku Ziyoni kuti, “Mulungu wanu ndi mfumu.”
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Pakamwa panga musapaletse mpang'ono pomwe kulankhula mau anu oona, pakuti ndimakhulupirira malangizo anu.
Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza, koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.
Tsono Farao adauzanso Yosefe kuti, “Tsopano ine ndakusankhula iweyo kuti ukhale nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.” Atatero, Farao adavula mphete yaufumu ku chala chake, naiveka ku chala cha Yosefe. Adamuvekanso zovala zabafuta ndi ukufu wagolide m'khosi mwake. Adamkweza pa galeta lake lachiŵiri laufumu, ndipo alonda ake a Farao adayamba kufuula patsogolo pa galetalo kuti, “Mgwadireni.” Motero Yosefe adalandira ulamuliro, ndipo adakhala nduna yaikulu ya dziko lonse la Ejipito.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
“Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza, gogodani, ndipo adzakutsekulirani. Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira; amene amafunafuna, ndiye amapeza; ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.
Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira,
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Choncho palibe kusiyana pakati pa Ayuda ndi anthu a mitundu ina, pakuti Mulungu ndiye Ambuye a onse, ndipo amadalitsa mooloŵa manja onse otama dzina lake mopemba.
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
Tsono khulupirira Chauta. Khala wamphamvu, ndipo ulimbe mtima. Ndithu, khulupirira Chauta.
Ndipo timalimba mtima pamaso pa Mulungu, popeza kuti amatimvera tikapempha kanthu kalikonse komukomera.
Tsono ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Chauta, mtima wanga ukukondwadi chifukwa cha Mulungu wanga. Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso. Wandiveka mkanjo wa chilungamo. Zinali ngati mkwati wamwamuna wavala nkhata ya maluŵa m'khosi, ndiponso ngati mkwati wamkazi wavala mikanda ya mtengo wapatali.
Ndikulira kwa Inu ndi mtima wanga wonse, mundiyankhe, Inu Chauta. Ndidzatsata malamulo anu. Ndikukulirirani, mundipulumutse, kuti ndizitsata malamulo anu.
Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.
Khala bata pamaso pa Chauta, ndipo umdikire mosadandaula. Usavutike ndi munthu amene zake zikumuyendera bwino, ndi munthu amene amatha kuchitadi zoipa zimene wakonza.
Tsono uchimo sudzakhalanso ndi mphamvu pa inu, pakuti chimene chimalamulira moyo wanu si Malamulo ai koma kukoma mtima kwa Mulungu.
Amakweza osauka kuŵachotsa pa fumbi, amachotsa anthu osoŵa pa dzala, amaŵakhazika pamodzi ndi akalonga, amaŵapatsa mpando waulemu. Nsanamira za dziko lapansi nzake za Chauta, adakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo.
Ndidakhala nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndidagonjetsa adani ako onse, iweyo ukupenya. Tsono ndidzamveketsa dzina lako, kuti lidzafanefane ndi dzina la anthu otchuka a pa dziko lapansi.
Ndidzakutamandani, Inu Chauta, pakuti mwanditulutsa m'dzenje la imfa. Simudalole kuti adani anga akondwere poona kuti ndikuvutika.
Khulupirira Chauta, ndipo usunge njira zake. Motero adzakukweza ndipo udzalandira dziko kuti likhale lako. Udzaona anthu oipa akuwonongeka.
Nchifukwa chake mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthaŵi yake adzakukwezeni.