Mawu oti “pangano” amatanthauza mapangano, malonjezano, ndi zikalata zomwe Mulungu anachita ndi anthu ake. Mapanganowa amasonyeza chikondi chachikulu cha Mulungu kwa ife ndipo amasonyezanso kufunitsitsa kwake kutipulumutsa ndi kutibwezeretsa kwa Iye.
Limodzi mwa mapangano ofunika kwambiri m’Baibulo ndi pangano la Mulungu ndi Abrahamu. Mu Genesis 12, Mulungu anachita pangano ndi Abrahamu, kumulonjeza kuti adzamudalitsa ndi kumupanga kholo la mitundu yambiri. Ichi sichinali pangano pakati pa Mulungu ndi Abrahamu yekha, koma ndi pangano lomwe linaphatikizapo mbadwa zake zonse.
Koma ili siliri pangano lokhalo lomwe timapeza m’Baibulo. Mapangano ena ofunika kwambiri ndi monga pangano la Mulungu ndi Mose pa Phiri la Sinai, pomwe Mulungu anapereka Malamulo Khumi ndi kukhazikitsa malamulo omwe Aisraeli ayenera kutsatira. Palinso pangano la Mulungu ndi Davide, pomwe Mulungu analonjeza kuti m’mibadwo ya Davide mudzatuluka mfumu yamuyaya.
Mapanganowa pakati pa Mulungu ndi anthu amasonyeza umunthu wake, kukhulupirika kwake, ndi kufunitsitsa kwake kukhala paubwenzi wolimba ndi cholengedwa chake. Kudzera mwa mapanganowa, Mulungu amasonyeza kufunitsitsa kwake kukwaniritsa malonjezo ake ndi kudzipereka kwake kukhalapo pa moyo wa anthu ake. Koposa zonse, amatiphunzitsa kuti Iye saswa mawu ake. Mulungu nthawi zonse amakwaniritsa zonse zomwe wanena chifukwa sanganama.
Mapanganowa amatikumbutsa kuti Mulungu ndi Mulungu wa pangano, wokhulupirika ku malonjezo ake ndi wodzipereka kwa iwo omwe amasankha kuchita pangano ndi Iye. Choncho, ukachita pangano ndi Mulungu, usachedwe kukwaniritsa mawu ako chifukwa Iye amatenga zonse mozama ndipo ndiye woyamba kukwaniritsa zonse zomwe wanena kuti adzakuchitira iwe ndi banja lako.
Nchifukwa chake mudziŵe kuti Chauta, Mulungu wanu, ndiye yekha Mulungu, ndipo ndi Mulungu wokhulupirika. Iye adzasungadi chipangano chake ndipo adzaonetsa chifundo chake chosasinthika kwa anthu a mibadwo zikwi zambirimbiri amene amakonda Iye namamvera malamulo ake.
Ndikuika utawaleza m'mitambo, ndipo udzakhala chizindikiro cha chipangano pakati pa Ine ndi dziko lapansi.
Chauta mwini wake adzakutsogolera, ndipo adzakhala nawe. Sadzalola kuti ulephere, ndipo sadzakusiya. Motero usachite mantha kapena kutaya mtima.”
Koma chikondi cha Chauta nchamuyaya kwa anthu omumvera, zidzukulu zao zonse amazichitira zolungama. Anthuwo ndi amene amasunga chipangano chake, amene amakumbukira kusunga malamulo ake.
Nchifukwa chake Khristu ndi Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kuti amene Mulungu adaŵaitana, alandire madalitso osatha amene Mulunguyo adalonjeza. Izi zidatheka chifukwa cha imfa ya Khristu, imene imapulumutsa anthu ku zochimwa zozichita akali m'Chipangano choyamba chija.
Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.
Chauta adauzanso Mose kuti, “Lemba mauŵa, chifukwa potsata mau ameneŵa, ndikuchita chipangano ndi iwe ndi Aisraele onse.”
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija.
Mau onse a chipangano ichi muŵamvere mokhulupirika, kuti choncho mudzakhoze pa zonse zimene mudzachite.
mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Atatha kudya, adaŵapatsanso chikho, nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chimene magazi anga, omwe akukhetsedwa chifukwa cha inu, akuchitsimikizira.
Motero Yoswa adapangana nawo anthu pa tsiku limenelo, ndipo ku Sekemu komweko Yoswa adapatsa anthuwo malamulo ndi malangizo.
Chauta adakuuzani zimene muyenera kuchita, kuti musunge chipangano chimene adapangana ndi inu, ndicho malamulo khumi amene adaŵalemba pa miyala iŵiri.
Motero Mulungu adzadalitsa zidzukulu zanga chifukwa Iye adachita nane chipangano chosatha, chipangano cholongosoka bwino ndi chosasinthika. Izi nzimene ndikulakalaka, ndiponso zimene zidzandipulumutsa. Ndi Mulungu amene adzachita zonsezi.
Chipanganocho ndi ichi: ‘Ndikulonjeza kuti sindidzaononganso zamoyo zonse ndi chigumula. Ndithu chigumula sichidzaononganso dziko lapansi.’ ”
Tsono Mose adakhala pamodzi ndi Chauta kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, osadya kanthu. Ndipo Chautayo adalemba pa miyala iŵiri ija mau onse a chipanganocho, ndiye kuti Malamulo Khumi aja.
Amakumbikira chipangano adachita ndi Abrahamu chija, lonjezo lake limene adachita molumbira kwa Isaki.
Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu nkuchipereka kwa ophunzirawo. Adaŵauza kuti, “Imwani nonsenu. Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzachite chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda.
Amasunga chipangano chake nthaŵi zonse, sangaiŵale lamulo limene adalipereka ku mibadwo yonse. Amasunga chipangano chimene adachita ndi Abrahamu, lonjezo lake limene adapatsa Isaki molumbira.
Nthaŵi imeneyo ndidzachita chipangano ndi nyama zakuthengo, mbalame zamumlengalenga, ndi zokwaŵa pansi, kuti ziyanjane ndi anthu anga. Tsono ndidzathyola uta, lupanga, ndi zida zina zonse zankhondo, ndipo ndidzazichotsa m'dzikomo, kuti iwo apeze moyo wamtendere.
Amadziŵitsa Yakobe mau ake, amaphunzitsa Israele malamulo ake ndi malangizo ake. Chauta akumanga Yerusalemu, akusonkhanitsa Aisraele omwazika. Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta!
Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera. Adalonjezanso Abrahamu, kholo lathu, molumbira,
Komabe ndidzakumbukira chipangano chimene ndidachita nawe pa ubwana wako. Ndidzachita nawe chipangano china, chipangano chake chosatha.
“Ndidzakuŵerengani ndi ndodo ya mbusa, ndi kukuloŵetsani m'chigwirizano cha chipangano changa.
Chauta akunena kuti, “Akubwera masiku pamene ndidzachite chipangano chatsopano ndi anthu a ku Israele ndi a ku Yuda. Sichidzakhalanso ngati chipangano chija chimene ndidaachita ndi makolo ao, pamene ndidaŵagwira padzanja nkuŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Chipangano chimenecho iwo adaphwanya, ngakhale ndinali Mbuye wao. Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga. Nthaŵi imeneyo wina sazidzachitanso kuphunzitsa mnzake kapena mbale wake kuti adziŵe Chauta. Pakuti onsewo, ana ndi akulu omwe adzandidziŵa, Ndidzaŵakhululukira machimo ao, sindidzakumbukiranso machimo aowo,” akuterotu Chauta.
Tcherani makutu, ndipo mubwere kwa Ine. Mumvere Ine, kuti mukhale ndi moyo. Ndidzachita nanu chipangano chosatha, ndipo ndidzakuwonetsani chikondi chosasinthika ndi chosapeneka, chimene ndidaalonjeza Davide.
“Ine Chauta ndakuitana kuti ukhazikitse chilungamo. Ndakugwira padzanja ndi kukusunga. Ndakusankhula kuti ukhale chipangano kwa anthu, ukhale kuŵala kounikira anthu a mitundu ina.
Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kuloŵetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzakuchotserani mtima wanu wouma ngati mwalawo ndi kukupatsani mtima wofeŵa ngati mnofu. Ndidzaika mzimu wanga mwa inu, ndipo ndidzakutsatitsani malangizo anga, ndi kukusungitsani malamulo anga mosamala kwambiri.
Ndidzachita nawo chipangano chamtendere. Chipangano chimenechi chidzakhala chao mpaka muyaya. Ndidzaŵakhazikitsa ndi kuŵachulukitsa, ndipo ndidzaika Nyumba yanga pakati pao mpaka muyaya.
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi imene ndidakukomera mtima, ndidakuyankha, ndipo tsiku la chipulumutso ndidakuthandiza. Ndidakusunga ndipo ndidakusandutsa kuti ukhale chipangano kwa anthu, kuti ndilibwezere dziko mwakale ndi kuligaŵagaŵa dziko loonongekali.
Ndidapangana nawo chipangano chopatsa moyo ndi mtendere. Ndidaŵapatsa zimenezi kuti azindiwopa, ndipo adandiwopadi namalemekeza dzina langa.
Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa.
Apo Mose adatenga magazi am'mbale aja, nawaza anthuwo, ndipo adati, “Magazi ameneŵa ndiwo amene akutsimikiza chipangano chimene Chauta wapangana nanu pakukupatsani mau onseŵa.”
Pakuti aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka, kuti Mulungu aŵakhululukire machimo ao.
Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Zimene Mulungu adalonjeza kudzera mwa aneneri nzokhudza inuyo ana ao. Momwemonso chipangano chimene adachita ndi makolo anu chikukhudza inu ana ake. Paja adauza Abrahamu kuti, ‘Mwa chidzukulu chako china ndidzadalitsa mitundu yonse ya anthu a pa dziko lapansi.’
Momwemonso atatha kudya, Ambuye Yesu adatenga chikho nati, “Chikhochi ndi chipangano chatsopano chotsimikizika ndi magazi anga. Nthaŵi zonse mukamamwa chikho chimenechi, muzindikumbukira.”
Koma monga zilirimu, Yesu adalandira unsembe wopambana kutalitali unsembe wakale uja, monga momwe ndiyenso Nkhoswe ya chipangano chopambana, chifukwa malonjezo ake ngopambana malonjezo a chipangano chakale chija. Chipangano choyamba chija chikadakhala changwiro, sipakadafunikanso china m'malo mwake.
“Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.”
Pa tsiku limeneli mpamene Chauta adachita chipangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapatsa zidzukulu zako dziko lonseli kuyambira ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate.
Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako.
Aisraele azisunga tsiku la Sabatalo, ndipo mibadwo yonse yakutsogoloko izidzalisunga ngati pangano losatha.
Ndidzakukumbukirani, ndipo ndidzakubalitsani ana ambiri ndi kukuchulukitsani. Ndidzalimbitsa chipangano changa ndi inu.
Chauta, Mulungu wathu, adachita nafe chipangano pa phiri la Horebu. “Usamchitire mnzako umboni wonama. “Usasirire mkazi wa mnzako. Usasilire nyumba yake, munda wake, wantchito wake wamwamuna, wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzakoyo.” Chauta adaalankhula mau ameneŵa kwa inu nonse amene mudaasonkhana kuphiri kuja. Iye adanena mau ameneŵa osaonjezerapo kanthu, ndipo adalankhula mau amphamvu, kuchokera m'moto, m'mitambo ndiponso mu mdima wandiweyani. Pambuyo pake adalemba malamulo khumiwo pa miyala iŵiri, ndipo adandipatsa ine. Pamene mudamva mau ochokera mu mdima, phiri lonse likuyaka moto, atsogoleri anu pamodzi ndi mafumu a mabanja anu adabwera kwa ine, ndipo adati, “Chauta, Mulungu wathu, adatiwonetsa ukulu ndi ulemerero wake, ndipo tidamumva akulankhula m'moto muja. Lero taona kuti munthu angathe kukhalabe ndi moyo ndithu, ngakhale kuti Mulungu walankhula naye. Koma ife, tiferenji kuno? Moto woopsawo udzatiwononga. Tidzafa tikamva Chauta, Mulungu wathu, akulankhulanso. Kodi alipo wina aliyense amene adakhalapo ndi moyo atamva Mulungu wamoyo akulankhula m'moto monga momwe tidamvera ifeyo? Inu Mose, musendere, ndipo mukamvere zonse zimene Chauta, Mulungu wathu, adzanene. Kenaka mubwere, mudzatiwuze tonsefe zimene wakuuzani inuyo. Ife tidzamvera ndipo tidzachita.” Pamene mudalankhula ndi ine, Chauta adamva mau anu ndipo adandiwuza kuti, “Ndamva zimene akulankhula anthuzi, ndi zabwino zokhazokha zonsezo. Ine ndikufuna kuti aziganiza zimenezo masiku onse. Ndikufuna kuti azindiwopa nthaŵi zonse, ndipo kuti azimvera malamulo anga, kuti zinthu ziŵayendere bwino iwowo ndi zidzukulu zao mpaka muyaya. Sikuti chipangano chimenechi adangochita ndi makolo athu okha ai, komanso ndi ife tonse amene tili ndi moyo pano lero lino.
Ine ndidakwera phiri kukalandira miyala iŵiri imene padalembedwapo chipangano chimene Chauta adachita nanu. Ndidakhala kumeneko masiku makumi anai, usana ndi usiku, ndipo sindidadye kapena kumwa kanthu kalikonse.
Tsono inu Aisraele, tamvani zimene Chauta, Mulungu wanu, akukuuzani. Akufuna kuti muzimuwopa ndi kuchita zonse zimene amakulamulani. Muzikonda Chauta, ndipo muzimtumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, ndipo muzimvera malamulo ndi malangizo onse a Chauta amene ndikukulamulani lero lino, kuti zinthu zikukomereni.
Chauta, Mulungu wanu, akukulamulani lero lino kuti mumvere malangizo ndi malamulo ake. Tsono muŵamveredi ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani. Lero Chauta wakulandirani ngati anthu ake, monga momwe adakulonjezerani, malinga nkusunga malamulo ake onse. Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera.
Iye akuti, “Sonkhanitsani pamaso panga, anthu anga okhulupirika, amene adachita chipangano ndi Ine popereka nsembe.”
“Ndidzamkonda nthaŵi zonse ndi chikondi changa chosasinthika, chipangano changa ndi iye sichidzaphwanyika.
Lonjezolo adabwerezanso kwa Yakobe kuti likhale chipangano chokhazikika mu Israele mpaka muyaya.
Anthu aipitsa dziko lapansi posatsata malamulo a Mulungu, ponyoza mau ake, ndipo pophwanya chipangano chamuyaya chimene Iye adapangana nawo.
Munthu wotere adzakhala pa malo otetezedwa. Kothaŵirako iye kudzakhala ku malinga am'matanthwe. Chakudya azidzalandira, ndipo madzi sadzamsoŵa.
Adzafunsa njira ya ku Ziyoni, nkuyamba ulendo wobwerera kumeneko. Adzati, ‘Tiyeni tibwerere kwa Chauta, tikachite naye chipangano chamuyaya, chimene sichidzaiŵalika konse.’
“Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo.
Apo mudzadziŵa kuti ndakupatsani lamulo ili kuti chipangano changa ndi ansembe, zidzukulu za Levi, chisaphwanyike. Ndikutero Ine Chauta Wamphamvuzonse.
“Musamaganiza kuti ndidadzathetsa Malamulo a Mose ndiponso zophunzitsa za aneneri. Inetu sindidadzere kudzaŵathetsa, koma kudzaŵafikitsa pachimake penipeni. Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Ine ndine chakudya chamoyo chimene chidatsika kuchokera Kumwamba. Munthu wodya chakudyachi, adzakhala ndi moyo mpaka muyaya. Ndipo chakudyacho chimene Ine ndidzapereka ndi thupi langa, limene ndikulipereka kuti anthu a pa dziko lonse lapansi akhale ndi moyo.”
Uthengawutu umatiwululira m'mene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu. Njira yake kuyambira pa chiyambi mpaka potsiriza ndi yakuti anthu akhulupirire. Paja Malembo akuti, “Munthu wolungama pakukhulupirira adzakhala ndi moyo.”
Iwoŵa ndi Aisraele, amene Mulungu adaŵasankha kuti akhale ana ake, ndipo adaŵapatsa ulemerero. Mulungu adachita nawo mapangano, ndipo adaŵapatsa Malamulo ake. Adaŵaphunzitsa mwambo wachipembedzo, ndipo adaŵapatsa malonjezo ake.
Khristu adafikitsa Malamulo a Mose ku mapherezero, kotero kuti aliyense wokhulupirira, amapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu.
Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Mulungu adataya anthu ake?” Iyai, chosatheka! Inenso ndine Mwisraele, mmodzi mwa zidzukulu za Abrahamu, ndiponso wa fuko la Benjamini. Maso ao atsekedwe kuti asapenye, ndipo msana wao ukhale wopindika nthaŵi zonse.” Tsono ndikufunsa kuti, “Kodi Ayuda adaphunthwa kuti agweretu osadzukanso?” Mpang'ono pomwe. Koma chifukwa cha kuchimwa kwa Ayudawo, chipulumutso chidafikiranso anthu a mitundu ina, kuti Ayuda aŵachitire nsanje. Ngati kuchimwa kwa Ayuda kudapindulitsa anthu a pa dziko lonse lapansi, ndipo ngati kulephera kwao kudapindulitsa kwakukulu anthu a mitundu ina, nanji tsono onse akadzamvera Mulungu, ndiye kuti madalitso adzakula zedi. Tsopano ndifuna kukuuzani kanthu, inu amene simuli Ayuda. Malinga nkuti ndine wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndimaunyadira utumiki wanga umenewu. Koma ndimakhumba kuti ndichititse nsanje anthu a mtundu wanga, ndi kupulumutsa ena mwa iwo. Ngati anthu a pa dziko lonse lapansi adayanjanitsidwa ndi Mulungu chifukwa Iye adaŵaika pambali Ayuda, nanga kudzatani Iye akadzaŵalandiranso? Kudzakhala monga ngati anthu akufa akuuka! Ngati munthu apatulira Mulungu chigawo chimodzi cha buledi, ndiye kuti yenseyo ndi wopatulika. Ndipo ngati muzu wa mtengo ndi wopatulika, ndiye kuti ndi nthambi zake zomwe nzopatulika. Nthambi zina za mtengo wobzala wa olivi zidakadzuka, ndipo pamalo pa nthambi zimenezo adalumikizapo kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo. Ndiye kuti inu amene simuli Ayuda, muli ngati kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo uja, ndipo tsopano mukulandira nao mphamvu ya m'mizu ya mtengo wobzala wa olivi, ndiye kuti Ayuda. Nchifukwa chake musamaŵanyoze amene adakadzuka monga nthambi zija. Kodi inu mungadzitame bwanji? Inutu ndinu kanthambi chabe. Sindinu amene mumagwirizira muzu ai, koma muzu ndiwo umene umagwirizira inu. Tsono mudzati, “Koma nthambi zija zidakadzuka kuti andilumikizepo ineyo pamtengopo.” Mulungu sadaŵataye anthu ake amene Iye adaŵasankha kale. Monga simudziŵa mau aja a m'Malembo, pamene mneneri Eliya akudandaula kwa Mulungu kuti aŵalange Aisraele? Paja adati,
Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya? Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Ndiye amene adatipatsa mphamvu kuti tikhale otumikira chipangano chatsopano, osati mwa malamulo olembedwa, koma mwa Mzimu Woyera. Paja malamulo olembedwa amadzetsa imfa, koma Mzimu Woyera amapatsa moyo.
Abale, ndikufotokozereni zimenezi pokupatsani chitsanzo cha zimene zimachitika tsiku ndi tsiku. Anthu aŵiri akapangana natsimikiza chimodzi, palibe munthu angaphwanye panganolo kapena kuwonjezapo mau. Tsono Mulungu adapatsa malonjezo ake kwa Abrahamu ndi kwa mbeu yake. Sakunena kuti, “Ndi kwa mbeu zake” ai, ngati kuti akunena za anthu ambiri. Koma akunena kuti, “Ndi kwa mbeu yake”, popeza kuti akukamba za munthu mmodzi yekha. Ameneyu ndi Khristu. Chimene ndikunena ndi ichi: Mulungu adachita chipangano, nalonjeza kuchisunga. Malamulo a Mose, amene adadza patapita zaka 430, sangathe kuchiphwanya chipanganocho ndi kuwononga lonjezo la Mulungu lija. Mulungu akapatsa munthu madalitso chifukwa munthuyo ndi wotsata Malamulo, ndiye kuti madalitsowo sapatsidwanso chifukwa cha lonjezo ai. Koma Mulungu adadalitsa Abrahamu chifukwa adaalonjeza kutero.
Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo.
Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu. Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Ngati munthu alemba Chipangano chosiyira ena chuma, pafunika kutsimikiza kuti wolemba chipanganocho wamwaliradi. Paja chipangano chotere chilibe mphamvu, asanamwalire wochilemba. Chimakhala ndi mphamvu pokhapokha wochilembayo atamwalira.
Utawaleza ukamadzaoneka m'mitambo, Ine ndidzaupenya, ndipo ndizidzakumbukira chipangano chamuyaya cha pakati pa Ine ndi zamoyo zonse zokhala pa dziko lapansi.
Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena.
Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.
Ngakhale zitachitika zonsezo, pamene ali m'dziko la adani ao, sindidzaŵanyoza ndipo sindidzadana nawo mpaka kuŵaononga kwathunthu ndi kuphwanya chipangano changa ndi iwo, chifukwa Ine ndine Chauta, Mulungu wao.
Samalani bwino, musaiŵale chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, adachita nanu, ndipo musapange fano lofanizira chinthu chilichonse chimene Chauta, Mulungu wanu, adakuletsani. Paja Chauta, Mulungu wanu, ndi Mulungu wansanje, salola kuti wina apikisane naye. Ali ngati moto waukali.
Chimene Chauta akukulolerani kuŵalanda dziko anthuwo, si chifukwa chakuti ndinu abwino ndi angwiro ai. Akuŵapirikitsa chifukwa iwowo ngoipa, ndiponso chifukwa choti Mulungu ndi wosunga lonjezo limene adachita ndi makolo anu Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Ngati ana ako aamuna asunga chipangano changa ndi malamulo anga amene ndidzaŵaphunzitsa, ana aonso adzakhala pa mpando wako wachifumu mpaka muyaya.”
Koma chipangano chimene ndidzachite ndi anthu a ku Israele atatha masiku amenewo, ndi ichi: Ndidzaika malamulo anga mwa iwo, ndidzachita kuŵalemba m'mitima mwao. Tsono Ineyo ndidzakhala Mulungu wao, ndipo iwowo adzakhala anthu anga.
Ndidzaŵapatsa mtima watsopano, ndipo ndidzaika moyo watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wouma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzaŵapatsa mtima wofeŵa ngati mnofu. Chauta adandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu aŵiri ameneŵa ndiwo amene amapangana zoipa nkumalangiza anthu zoipa mumzinda muno. Motero adzatsata malamulo anga, adzasunga ndi kumvera malangizo anga. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.
Chauta akuti, “Tsono kunena za inu, chifukwa cha chipangano changa ndi inu, chimene nsembe zamagazi zidachitsimikiza, ndidzaŵatulutsa m'dzenje lopanda madzi anthu anu amene ali ngati akapolo.
Yesu Khristu, makolo ake anali Davide ndi Abrahamu. Motsatanatsatana maina a makolo ake onse ndi aŵa:
Kunena zoona, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa cha mtengo wamphesachi, mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano pamodzi nanu mu Ufumu wa Atate anga.”
Iwo alikudya choncho, Yesu adatenga mkate, nathokoza Mulungu, nkuunyemanyema, nagaŵira ophunzira aja, ndipo adati, “Kwayani, ili ndi thupi langa.” Kenaka adatenga chikho, nathokoza Mulungu, nkuchipereka kwa ophunzirawo, naamwa onse. Ndipo adaŵauza kuti, “Aŵa ndi magazi anga otsimikiza Chipangano cha Mulungu. Magazi ameneŵa ndiŵakhetsa chifukwa cha anthu ochuluka.
Choncho Iye waŵachitiradi chifundo makolo athu akale, ndipo wakumbukira chipangano chake choyera.
Paja zimene Mulungu adalonjeza zija, adalonjezera inuyo, ana anu ndiponso anthu onse okhala kutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaŵaitana.”
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Chipangano choyamba chija chinali nawo malamulo okhudza chipembedzo, chinalinso ndi malo opembedzeramo omangidwa ndi anthu.
Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa ndi kukusandutsa wotchuka, kotero kuti udzakhala ngati dalitso kwa anthu ena. Farao adalamula anthu ake, ndipo iwowo adatulutsa Abramu ndi mkazi wake m'dzikomo, pamodzi ndi zonse zimene anali nazo. “Ndidzadalitsa onse okudalitsa iwe, koma ndidzatemberera aliyense wokutemberera. Mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzapeza madalitso kudzera mwa iwe.”
Pambuyo pake adatenga buku lachipangano, naŵaŵerengera momveka anthuwo. Tsono anthuwo adati, “Tidzachita zonse zimene Chauta walamula. Tidzamumvera Iyeyo.”
Lero lino, nonse mukuimirira pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, atsogoleri anu, akuluakulu anu, akalonga anu, anthu aamuna a Aisraele, zidzukulu zanu, akazi anu ndiponso alendo amene amakhala m'mahema mwanu, amene amakudulirani nkhuni ndi kumakutungirani madzi. Muli pano lero kuti mulumbire ndi kuchita chipangano chimene Chauta, Mulungu wanu, akupangana nanu. Motero, mudzakhala anthu a Chauta, ndipo Iyeyo adzakhala Mulungu wanu, monga momwe adalonjezera kwa inu ndi kulumbira kwa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe. Sindinu nokha amene Chauta akupangana nanu chipangano ichi chochita ndi malumbiro. Chipangano chimenechi akupangana ndi munthu aliyense amene ali pano lero pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, ndiponso ndi ena onse amene sali nafe kuno lero.
Ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima, chifukwa udzatsogolera anthu ameneŵa pokalandira dziko limene ndidalonjeza kwa makolo ao. Komatu ukhale wamphamvu ndipo ulimbe mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti usunge malamulo onse amene Mose mtumiki wanga adakupatsa. Usatayepo ndi kagawo kamodzi komwe, ndipo kulikonse kumene udzapite, udzapambana. Uziŵerenga buku lamalamuloli, ndipo usana ndi usiku uzisinkhasinkha zolembedwa m'menemo, kuti uzisunge zonse. Tsono ukamatero, udzapeza bwino ndipo udzapambana. Paja ndidakulamula kuti ukhale wamphamvu. Usamaopa kapena kutaya mtima, poti Ine, Chauta, Mulungu wako, ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.”
Adapulumutsa anthu ake. Adakhazikitsa chipangano chake kuti chikhale chamuyaya. Dzina lake ndi loyera ndi loopsa.
“Ndipo ndidzapangana nawo chipangano chakuti, ‘Kuyambira tsopano mpaka muyaya, mzimu wanga umene uli pa iwe, ndiponso mau anga amene ndidaika m'kamwa mwako, sizidzachokeranso m'kamwa mwako kapena m'kamwa mwa ana ako kapena mwa adzukulu ako mpakampaka.’ ”
Mau a Chauta adamvekanso kwa Yeremiya. Nthaŵiyo nkuti mfumu Zedekiya atapangana nawo anthu onse a ku Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo ao adzaŵamasule.
Ndithu ndikunenetsa kuti thambo ndi dziko lapansi zisanathe, sipadzachoka kalemba nkakang'ono komwe kapena kankhodolera pa Malamulowo, mpaka zonse zitachitika.
Nchifukwa chake, monga Atate anga adandipatsa ufumu, Inenso ndikukupatsani ufumu. Tsono Satana adamuloŵa Yudasi wotchedwa Iskariote, amene anali mmodzi mwa ophunzira khumi ndi aŵiri aja a Yesu. Ndikadzaloŵa mu ufumu wanga, muzidzadya ndi kumwa pamodzi nane, ndipo mudzakhala pa mipando yachifumu nkumaweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israele.”
Abrahamu ndi zidzukulu zake adalandira kwa Mulungu lonjezo lakuti dziko lapansi lidzakhala lao. Adalandira lonjezolo osati chifukwa cha kusunga Malamulo, koma chifukwa cha chilungamo chofumira m'chikhulupiriro.
Paja Malembo akuti, “Munthu woyamba uja, Adamu, adachita kusanduka chinthu chamnofu chokhala ndi moyo.” Koma Adamu wotsiriza adakhala chinthu chauzimu chopatsa moyo.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Ngati ndinu ake a Khristu, ndiye kuti ndinu ana a Abrahamu, oyenera kulandira zimene Mulungu adalonjeza.
Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.
Adafafaniza kalata ya ngongole yathu, yonena za Malamulo a Mose. Kalatayo inali yotizenga mlandu, koma Iye adaichotsa pakuikhomera pa mtanda.
Koma Khristu wafika, ndipo ndiye Mkulu wa ansembe onse wa zokoma zimene zilikudza tsopano. Chihema chimene Iye amatumikiramo nchachikulu ndiponso changwiro kopambana. Nchosapangidwa ndi anthu, ndiye kuti si chapansipano. Pamene Khristu adabzola chihemachi, nkukaloŵa kamodzi kokhako m'malo Opatulika Kopambana, sadaloŵemo ndi magazi a atonde ndi a anaang'ombe amphongo ai. Adaloŵamo ndi magazi akeake. Potero adatikonzera chipulumutso chosatha.
Ndi msampha kwa munthu kupereka chinthu kwa Chauta mosaganiza bwino, chifukwa mwina atha kusintha maganizo atalumbira kale.
Udzasendeza malire ake uku ndi uku. Zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina, zidzadzaza mizinda imene idasiyidwa.
Ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba, kotero kuti zimene udzamange pansi pano, zidzamangidwa ndi Kumwamba komwe, ndipo zimene udzamasule pansi pano, zidzamasulidwa ndi Kumwamba komwe.”
Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja,
Zimenezi zili ngati fanizo. Akazi aŵiri aja akufanizira zipangano ziŵiri. Mmodzi (Hagara uja), ndi wochokera ku phiri la Sinai, ndipo ana ake amakhala akapolo. Hagarayo akufanizira phiri la Sinai la m'dziko la Arabiya, lofanizira Yerusalemu walero, amene ali m'ukapolo pamodzi ndi anthu ake onse. Koma Yerusalemu wakumwamba ndiye mfulu, ndipo ndiye mai wathu.
Mulungu Atate adakusankhani, monga Iye adaziganiziratu kuyambira pa chiyambi, kuti Mzimu Woyera akuyeretseni ndipo kuti mumvere Yesu Khristu, ndi kutsukidwa ndi magazi ake. Mulungu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere wonka nuchulukirachulukira.
“Ndidzapangana nazo chipangano chamtendere. Zilombo zonse zolusa ndidzazichotsa m'dziko, kuti nkhosa zanga zizidzakhala mwamtendere, ngakhale m'chipululu kapena m'thengo. Ndidzakhazika anthu anga kufupi ndi phiri langa, ndipo ndidzaŵagwetsera mvula pa nthaŵi yake, mvula yake ya madalitso.
Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzatuma wamthenga wanga kuti akandikonzere njira. Kenaka mwadzidzidzi Chauta amene mukumfunafuna adzafika ku Nyumba yake. Wamthenga wa chipangano, amene mukumuyembekeza, suuyu akubwera.
Wadzathandiza anthu ake Aisraele, pokumbukira chifundo chake. Izi ndi zomwe adaalonjeza kuti adzaŵachitira makolo athu akale aja, Abrahamu ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.”
Koma tsopano yaoneka njira yopezera chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo njira yake si kutsata Malamulo ai. Malamulowo ndi aneneri omwe amaichitira umboni. Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,
Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya?
Anthu onse angathe kuwona kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, yolembedwa kudzera mwa ife, osati ndi inki koma ndi mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa zolembapo zamiyala koma m'mitima mwa anthu.
Khristu adatiwombola ku temberero la Malamulo pakusanduka wotembereredwa m'malo mwathu. Paja Malembo akuti, “Ndi wotembereredwa aliyense wopachikidwa pa mtengo.” Khristu adachita zimenezi, kuti dalitso limene Mulungu adaalonjeza Abrahamu, lipatsidwe kwa anthu a mitundu yonse kudzera mwa Khristu Yesu, ndipo kuti pakukhulupirira tilandire Mzimu Woyera amene Mulungu adaatilonjeza.
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu.
Kale inu munali kutali ndi Mulungu, ndipo munkadana naye m'maganizo anu ndi m'ntchito zanu zoipa. Koma tsopano, kudzera mwa imfa ya Mwana wake m'thupi lake, Mulungu wakuyanjanitsaninso ndi Iye mwini. Adachita zimenezi kuti pamaso pake muthe kuwoneka muli oyera mtima, opanda banga kapena cholakwa chilichonse.
Mzimu Woyera nayenso amatitsimikizira zimenezi. Poyamba Iye akuti, “Nachi chipangano chimene ndidzachita nawo atapita masiku amenewo, akutero Ambuye: ndidzaika Malamulo anga m'mitima mwao, ndidzachita kuŵalemba m'maganizo ao.” Pambuyo pake akutinso, “Sindidzaŵakumbukiranso konse machimo ao ndi zolakwa zao.” Pamene Mulungu wakhululukira zonsezi, sipafunikanso nsembe yoperekera machimo.
Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Nthambi zina za mtengo wobzala wa olivi zidakadzuka, ndipo pamalo pa nthambi zimenezo adalumikizapo kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo. Ndiye kuti inu amene simuli Ayuda, muli ngati kanthambi ka mtengo wa olivi wakuthengo uja, ndipo tsopano mukulandira nao mphamvu ya m'mizu ya mtengo wobzala wa olivi, ndiye kuti Ayuda. Nchifukwa chake musamaŵanyoze amene adakadzuka monga nthambi zija. Kodi inu mungadzitame bwanji? Inutu ndinu kanthambi chabe. Sindinu amene mumagwirizira muzu ai, koma muzu ndiwo umene umagwirizira inu.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Njira zonse za Chauta ndi za chikondi chosasinthika, nzokhulupirika kwa anthu osunga chipangano chake ndi malamulo ake.
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera ku banja la Davide idzakhala chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Onse adzasonkhana kwa iye, ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
Mulungu adampereka Iyeyu kuti ndi imfa yake akhale nsembe yokhululukira machimo a anthu omkhulupirira Iye. Mulungu adachita zimenezi kuti aonetse njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pake. Zoonadi kale mwa kuleza mtima kwake sadalange kotheratu anthu ochimwa.
Sadachitepo zimenezi ndi mtundu wina uliwonse wa anthu, iwo sadziŵa malangizo ake. Tamandani Chauta!
Chipangano changachi ndidzachikhazikitsa pakati pa Ine ndi iwe ndi zidzukulu zako zam'tsogolo, ndipo chidzakhala chipangano chosatha. Ine ndidzakhala Mulungu wako ndi Mulungu wa zidzukulu zako. Dziko lino limene ukukhalamo ngati mlendoli, ndidzakupatsa iwe ndi zidzukulu zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala la zidzukulu zako mpaka muyaya, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao.”
Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa. Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ ”
Ndikugwada moŵerama kumaso kwa Nyumba yanu yoyera. Ndikutamanda dzina lanu chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika, chifukwanso cha kukhulupirika kwanu. Mwakweza dzina lanu ndiponso malonjezo anu kupambana chinthu china chilichonse.
Chauta amakonda chilungamo, sadzaŵasiya okha anthu ake okhulupirika. Iye adzawasunga mpaka muyaya, koma adzaononga ana a anthu oipa.
Pajatu Mzimu amene mudalandira, sakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha ai. Koma Mzimuyo amakusandutsani ana a Mulungu, ndipo mwa mphamvu yake, popemphera kwa Mulungu timati, “Abba! Atate!” Mzimu Woyera mwiniwakeyo ndi amene amavomerezana ndi mitima yathu kutsimikiza kuti ndife ana a Mulungu. Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Pamene Mulungu ankamulonjeza kanthu Abrahamu, adaalumbira kuti, “Pali Ine ndemwe, Mulungune.” Adaatero, popeza kuti panalibe wamkulu koposa Mwiniwakeyo amene akadamtchula polumbirapo. Ndiye Mulungu adati, “Ndithudi ndidzakudalitsa kwakukulu, ndipo ndidzachulukitsa kwambiri zidzukulu zako.”
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Kusiyana kokhudza lumbiroku kukutiwonetsa kuti Yesu ndi Nkhoswe yotsimikizira Chipangano choposa. Kusiyana kwina nkwakuti ansembe akale aja anali ambiri, chifukwa ankafa, sankatha kupitirira ndi udindo waowo. Koma Yesu ngwamuyaya, motero unsembe wake ngwosasinthika.
Chifukwa kunena zoona, Khristu adasanduka mtumiki wa Ayuda, kutsimikiza kuti Mulungu ndi wokhulupirika. Adatsimikiza kukhulupirikako pakuchita zimene Mulungu adaŵalonjeza makolo ao akale aja, ndiponso pakupatsa anthu amene sali Ayuda chifukwa cholemekezera Mulungu kaamba ka chifundo chake. Ndi monga Malembo anenera kuti, “Nchifukwa chake ndidzakuyamikani pakati pa anthu a mitundu ina, ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.