Yesu ndiye kasupe wa chipulumutso changa, ufulu wanga ku ukapolo, machiritso anga ku matenda, ndi kubwezeretsedwa kwa moyo wanga. Kale, ndinali wakufa mu machimo anga, koma kudzera mu nsembe ya Khristu, chimene chinali cha imfa tsopano chakhala cha moyo.
Chikondi cha Mulungu pa ine n'chachikulu kwambiri moti, poona kuti sindingathe kudzipulumutsa ndekha chifukwa cha kuipa komwe kunali mwa ine, anatumiza Mwana wake yekhayo, amene anali wangwiro ndipo analibe choipa mwa Iye, kuti ine ndipulumuke. Ndi kudzera m'magazi a Yesu momwe ndatsukidwira kuipa kwanga.
Mbodzi uliwonse imene Yesu anavutika nayo inali yoti lero ndisangalale ndi ufulu, komwe kulibe chiweruzo kwa ine amene ndavomereza Khristu ngati Ambuye ndi Mpulumutsi wanga. Machitidwe 4:12¹ amati, "Palibe chipulumutso mwa wina aliyense; pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo lopatsidwa kwa anthu, limene tingapulumutsidwe nalo." Palibe aliyense amene ali ndi mphamvu yopulumutsa moyo wanga, koma Yesu wa ku Nazarete yekha.
Bwera lero ndi chikhulupiriro ku mpando wachifumu wa chisomo chake, vomereza kuti ndiwe wochimwa ndipo walakwa pamaso pake, ndipo udzalandira chikhululukiro cha machimo ako ndi chipulumutso cha moyo wako. Ambuye amakukonda kwambiri, ndipo kuyambira pachiyambi cha chilengedwe cha dziko lapansi wakhala akufuna kukhala pa ubwenzi ndi iwe.
Chifukwa chake, ndikukupempha kuti ubwere kumapazi a Yesu, ugwadire pamaso pake, ndipo uyanjane ndi Mulungu, kuti usatayike ku gehena, komwe chilango ndi kuzunzika kudzakhala kosatha. Chipulumutso ndi cha aliyense, koma ndi ochepa okha amene amayamikira mphatso yapaderayi. Usanyoze mwayi womwe uli nawo lero wotumikira Mulungu, choka pa choipa, yenda m'malamulo a Atate, yamikira chimene umalandira kudzera mu chipulumutso, ndipo yamikira chifukwa uli ndi mwayi wovomereza Khristu ngati Mpulumutsi wako yekhayo wokwanira. Aleluya!
¹ Machitidwe 4:12Mulungutu adaŵakonda kwambiri anthu a pa dziko lonse lapansi. Anali naye Mwana mmodzi yekha, komabe adampereka kuti aliyense wokhulupirira Iyeyo asatayike, koma akhale ndi moyo wosatha.
Tsiku limenelo aliyense mwa inu adzati: “Ndikukuthokozani Inu Chauta, pakuti ngakhale mudaandipsera mtima, mkwiyo wanu udaleka, ndipo mwandilimbitsa mtima.
Ndipo palibe wina aliyense amene angathe kupulumutsa anthu, pakuti pa dziko lonse lapansi palibe dzina lina limene Mulungu adapatsa anthu kuti tipulumuke nalo.”
Koma Mulungu adatsimikiza kuti amatikonda kwambiri, chifukwa pamene tinali ochimwabe, Khristu adatifera.
Iwo adamuyankha kuti, “Khulupirira Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka iwe ndi a m'nyumba mwako.”
Koma tikamavomera kuti ndife ochimwa, Mulungu amene ali wokhulupirika ndi wolungama, adzatikhululukira machimo athuwo. Adzatiyeretsa ndi kutichotsera kusalungama kwathu konse.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye.
Koma adambaya chifukwa cha machimo athu, ndipo adamtswanya chifukwa cha zoipa zathu. Chilango chimene chidamgwera iye chatipatsa ife mtendere, ndipo mabala ake atichiritsa.
Chikondi chanu chosasinthika ndi chamtengowapatali. Nchifukwa chake anthu anu amathaŵira m'munsi mwa mapiko anu.
Chifukwa munthu amati akakhulupirira ndi mtima wake, amapezeka wolungama pamaso pa Mulungu, ndipo amati akavomereza chikhulupiriro chakecho ndi pakamwa pake, amapulumuka.
Amene akakhulupirire ndi kubatizidwa, adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira, adzaweruzidwa kuti ngwolakwa.
Choncho ngati munthu ali mwa Khristu, ngwolengedwa kwatsopano. Zakale zapita, zimene zilipo nzatsopano.
Yesu adamuyankha kuti, “Ineyo ndine njira, ndine choona ndiponso moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate ngati sadzera mwa Ine.
Momwemonso Khristu adaperekedwa nsembe kamodzi kokha, kuti asenze ndi kuchotsa machimo a anthu ambiri. Adzaonekanso kachiŵiri, osati kuti adzachotsenso uchimo ai, koma kuti adzapulumutse anthu amene akumuyembekeza.
Paja Ambuye adatilamula kuti, “ ‘Ndakuika kuti uunikire anthu akunja, kuti mwa iwe ndipulumutse dziko lonse lapansi.’ ”
Ine sindichita manyazi ndi Uthenga Wabwino ai, chifukwa Uthengawo ndi mphamvu ya Mulungu yopulumutsa munthu aliyense wokhulupirira, poyamba Ayuda, pambuyo pake anthu a mitundu ina.
Mtima wanga umakhala chete kuyembekezera Mulungu yekha, pakuti chipulumutso changa chimafumira kwa Iye. Musakhulupirire kuti zachiwawa zingakuthandizeni. Musaganize kuti kuba kungakupindulitseni. Chuma chikachuluka musaikepo mtima. Mulungu adalankhula kamodzi, ine ndaphunzirapo zinthu ziŵiri, china ndi chakuti mphamvu ndi zanu, Inu Mulungu, chikondi chanu nchosasinthika, Inu Ambuye; china ndi chakuti Inu mumabwezera munthu molingana ndi ntchito zake. Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Ife tinali adani a Mulungu, koma imfa ya Mwana wake idatiyanjanitsa ndi Iye. Tsono popeza kuti imfa ya Khristu idatiyanjanitsa ndi Mulungu, nanji tsono moyo wake, ndiye udzatipulumutsa kwenikweni.
Adatilanditsa ku mphamvu za mdima wa zoipa, nkutiloŵetsa mu Ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu Mulungu adatiwombola, ndiye kuti adatikhululukira machimo athu.
Pakuti Chauta ndiye muweruzi wathu. Chauta ndiye wotilamula, Chauta ndiye mfumu yathu, ndiye amene adzatipulumutsa.
Mulungu adatuma Mwana wakeyo pansi pano, osati kuti adzazenge anthu mlandu, koma kuti adzaŵapulumutse.
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Iye mwa chifundo chake chachikulu adatibadwitsanso pakuukitsa Yesu Khristu kwa akufa. Motero timakhulupirira molimba mtima kuti tidzalandira ngati choloŵa zokoma zosaonongeka, zosaipitsidwa, ndi zosafota, zimene Mulungu akukusungirani Kumwamba. Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Choncho adatipulumutsa osati chifukwa cha ntchito zolungama zimene ife tidaachita, koma mwa chifundo chake pakutisambitsa. Adatisambitsa mwa Mzimu Woyera pakutibadwitsa kwatsopano ndi kutipatsa moyo watsopano.
Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima, ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe. Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga, ndipo ndimakukonda, ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Ndi monga momwe mau a Mulungu anenera kuti, “Aliyense amene adzatama dzina la Ambuye mopemba adzapulumuka.”
Chifukwa wofuna kupulumutsa moyo wake, adzautaya, koma wotaya moyo wake chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.
Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa.
Chipulumutso changa ndi ulemerero wanga, zonsezo zili kwa Mulungu. Mulungu ndiye thanthwe langa lamphamvu, ndiye kothaŵira kwanga.
Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga. Inu Aisraele, ndinu mboni zanga, ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani, kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira, ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha. Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina, ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina. Chauta ndi Ineyo, mpulumutsi wanu ndine ndekha. Ndine amene ndidaneneratu zimenezi, ndipo ndine ndidakupulumutsani. Si mulungu wina wachilendo amene adazichita pakati pa inu. Inu nomwe ndinu mboni zanga, ndikutero Ine Chauta. Ine ndine Mulungu ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse. Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga, palibe amene angathe kusintha zochita zanga.” Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele, akunena kuti, “Ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babiloni, kuti ndikupulumutseni. Ndidzagwetsa zipata za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira. Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja, Mlengi wa Israele. Ine ndekha ndine mfumu yanu.” Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja, njira pakati pa madzi amphamvu. Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo, ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu. Onsewo adagwa osadzukanso, adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale. Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale. Ndikuchita zinthu zatsopano. Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya? Ndikulambula mseu m'chipululu, ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma. Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.
Monga makanda obadwa chatsopano amalirira mkaka, inunso muzilakalaka mkaka weniweni wodyetsa mtima wanu, kuti ukukuzeni ndi kukufikitsani ku chipulumutso,
Chauta ali pafupi ndi onse amene amamutama mopemba. Ali pafupi ndi onse amene amamutama mokhulupirika.
Koma ine ndidzadalira Chauta. Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga. Mulungu wanga adzandimva.
Khomo ndine. Munthu akaloŵera pa Ine, adzapulumuka. Azidzaloŵa ndi kutuluka, ndipo adzapeza chakudya.
popeza kuti onse adachimwa, nalephera kufika ku ulemerero umene Mulungu adaŵakonzera. Koma mwa kukoma mtima kwake kwaulere, anthu amapezeka kuti ngolungama pamaso pa Mulungu, chifukwa cha Khristu Yesu amene adaŵaombola.
Mau onena za imfa ya Khristu pa mtanda ndi chinthu chopusa kwa anthu amene akutayika, koma kwa ife amene tili pa njira ya chipulumutso, mauwo ndi mphamvu ya Mulungu.
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale. Mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.
Ndidapachikidwa pa mtanda pamodzi ndi Khristu, kotero kuti sindinenso amene ndili ndi moyo, koma ndi Khristu amene ali ndi moyo mwa ine. Moyo umene ndili nawo tsopano m'thupi lino, ndi moyo wokhulupirira Mwana wa Mulungu, amene adandikonda napereka moyo wake chifukwa cha ine.
Tithandizeni, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, kuti dzina lanu likhale ndi ulemerero. Tipulumutseni, ndipo mutikhululukire zochimwa zathu, kuti dzina lanu lilemekezeke.
Nchifukwa chake angathe kuŵapulumutsa kwathunthu anthu amene akuyandikira kwa Mulungu kudzera mwa Iye, pakuti Iyeyo ali ndi moyo nthaŵi zonse kuti aziŵapempherera.
Chauta, mundikonde ndi chikondi chanu chosasinthika, mundipulumutse monga momwe mudalonjezera. Pamenepo ndidzakhala nchoŵayankha anthu ondinyodola, pakuti ndimakhulupirira mau anu.
Iye yekhayo ndiye thanthwe langa, chipulumutso changa, ndi linga langa. Sindidzagwedezeka konse.
Koma ife kwathu kwenikweni ndi Kumwamba, ndipo kumeneko kudzachokera Mpulumutsi amene tikumuyembekeza. Mpulumutsiyo ndi Ambuye Yesu Khristu.
Mulungu yekha ndiye wopanga Malamulo ndiponso woweruza. Ndiyenso wotha kupulumutsa ndi kuwononga. Nanga iwe ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
“Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu. “Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?” Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”
Inu Chauta, chiritseni ndipo ndidzachiradi. Pulumutseni ndipo ndidzapulumukadi. Ndinu amene ndimakutamandani.
Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.
Yang'aneni mtumiki wanune mwa kukoma mtima kwanu, pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
Paja chisoni chokomera Mulungu chimamtembenuza munthu ndi kumpulumutsa, kotero kuti chisoni chake chimathera pomwepo. Koma kumva chisoni monga m'mene amachitira anthu odalira zapansipano, kumadzetsa imfa.
Sindikayika konse kuti Mulungu, amene adayamba kuchita ntchito yabwinoyi mwa inu, adzaipitiriza mpaka itatsirizika pa Tsiku la Kubweranso kwa Khristu Yesu.
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
Ndimazipatsa moyo wosatha, ndipo sizidzatayika konse. Palibe munthu wodzazilanda m'manja mwanga. Atate anga amene adandipatsa nkhosazo amapambana onse, ndipo palibe amene angathe kuzilanda m'manja mwao.
Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.
Mzimu wa Ambuye Chauta wadzaza mwa ine, chifukwa Chauta wandidzoza. Wandituma kuti ndikalalike uthenga wabwino kwa anthu osauka, ndi kukasangalatsa a mtima wosweka, kukalengeza kwa akapolo kuti adzalandira ufulu, ndiponso kwa am'ndende kuti adzaŵamasula.
Tsono abale, popeza kuti Mulungu watichitira chifundo chachikulu chotere, ndikukupemphani kuti mupereke matupi anu omwe kuti akhale nsembe yamoyo, yopatulika, ndi yokondwetsa Mulungu. Imeneyi ikhale njira yanu yopembedzera Mulungu mwauzimu. Muzikondana kwenikweni monga abale, ndipo muzichita ngati kupikisana poonetsana ulemu. Potumikira Ambuye, changu chanu chisazilale, koma chikhalebe choyaka. Muzikhala okondwa chifukwa cha chiyembekezo chanu. Muzipirira pakati pa masautso, ndipo muzipemphera nthaŵi zonse. Muzipereka zothandiza akhristu anzanu osoŵa, ndipo muziyesetsa kulandira alendo mokondwa. Pemphani Mulungu kuti aŵadalitse amene amakuzunzani. Ndithu, pemphani kuti aŵadalitse, osaŵatemberera ai. Muzikondwa nawo amene akukondwa, muzilira nawo amene akulira. Muzimvana bwino, ndipo musamadzikweze, koma muziyanjana nawo anthu wamba. Musamadziyese anzeru. Munthu akakuchitani choipa, musamubwezere choipa. Yesani kuchita zimene anthu onse amaziwona kuti nzabwino. Ngati nkotheka, khalani ndi mtendere ndi anthu onse, monga momwe mungathere. Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.” Musamatsanzira makhalidwe a anthu odalira zapansipano, koma Mulungu asinthe moyo wanu wonse pakukupatsani mitima yatsopano. Pamenepo mudzatha kudziŵa zimene Mulungu afuna, ndipo mudzazindikira zimene zili zabwino, zangwiro ndi zomkondwetsa.
Ine ndidayembekeza Chauta ndi mtima wokhulupirira kuti adzandithandize. Adaŵeramira pansi kuyang'ana kwa ine, namva kulira kwanga. Sindidabise mumtima mwanga zoti ndinu wolungama. Ndalankhula za kukhulupirika kwanu ndi za chipulumutso chanu. Sindidaŵabisire a pa msonkhano waukulu za chikondi chanu chosasinthika ndi za kukhulupirika kwanu. Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse. Mavuto osaŵerengeka andizinga, machimo anga andigwira, kotero kuti sindingathe kuwona populumukira, ngambiri kupambana tsitsi la kumutu kwanga, ndipo ndataya mtima kotheratu. Inu Chauta, pulumutseni. Inu Chauta, fulumirani kudzandithandiza. Anthu ofunafuna moyo wanga, muŵachititse manyazi ndi kuŵasokoneza. Okhumba kundipweteka, abwezedwe m'mbuyo ndi kunyozedwa. Amene amandinyodola kuti, “Ha, Ha,” achoke ndi kuchita manyazi poona kuti alephera. Koma onse okufunafunani akondwe ndi kusangalala chifukwa cha Inu. Onse okondwerera chipulumutso chanu azinena kosalekeza kuti, “Chauta ndi wamkulu!” Inu Chauta, ine ndine wolefuka ndi wosoŵa, koma simunandiiŵale. Inu ndinu mthandizi wanga ndi Mpulumutsi wanga. Inu Mulungu wanga, musachedwe kudzandithandiza. Adanditulutsa m'dzenje la chiwonongeko, m'chithaphwi chamatope. Adapondetsa mapazi anga pa thanthwe, nandiyendetsa bwino lomwe. Mulungu waika nyimbo yatsopano m'kamwa mwanga, nyimbo yake yotamanda Iye. Anthu ambiri adzaona zimenezi ndipo adzaopa, nadzakhulupirira Chauta.
Tiyeni tsono, tiyandikire mopanda mantha ku mpando wachifumu wa Mulungu wokoma mtima. Kumeneko tidzalandira chifundo, ndipo mwa kukoma mtima kwa Mulungu tidzapeza thandizo pa nthaŵi yake yeniyeni.
Mkwiyo wake ndi wa kanthaŵi chabe, koma kukoma mtima kwake nkwa moyo wonse. Misozi ingachezere kugwa usiku, m'maŵa kumabwera chimwemwe chokhachokha.
Nonsenu ndinu ana a Mulungu chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu. Pajatu nonsenu amene mudasanduka amodzi ndi Khristu pakubatizidwa, mudachita ngati kuvala moyo wa Khristu.
Umboniwo tsono ndi wakuti Mulungu adatipatsa moyo wosatha, ndipo moyowo umapezeka mwa Mwana wake. Amene ali ndi Mwanayo, ali nawo moyo. Amene sali ndi Mwana wa Mulungu, alibe moyo.
Malipiro amene uchimo umalipira ndi imfa. Koma mphatso yaulere imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha mwa Khristu Yesu Ambuye athu.
Onse amene Atate andipatsa, adzabwera kwa Ine. Ndipo munthu aliyense wodza kwa Ine, sindidzamkana konse.
Iye adatipulumutsa, ndipo adatiitana kuti tikhale anthu ake. Sadachite zimenezi chifukwa choti ife tidaachita zabwino ai, koma chifukwa mwiniwakeyo adaazikonzeratu motero, ndiponso chifukwa mwa Khristu Yesu adatikomera mtima nthaŵi isanayambe.
Tsiku limenelo aliyense adzati, “Uyu ndiye Mulungu wathu! Tidamkhulupirira kuti adzatipulumutsa. Iyeyu ndiye Chauta. Tidamkhulupirira, tsopano tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa choti watipulumutsadi.”
Ngwodala amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake afafanizidwa. Anthu oipa amapeza zoŵaŵa zambiri, koma munthu wokhulupirira Chauta amazingidwa ndi chikondi chosasinthika. Sangalalani ndi kukondwa inu nonse okonda Mulungu, chifukwa cha zimene Chautayo adakuchitirani. Inu anthu ake onse, fuulani ndi chimwemwe. Ngwodala amene Chauta samuŵerengera mlandu wake, amene mumtima mwake mulibe zonyenga.
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu.
Akunenanso za ife amene tidzapezeka kuti ndife olungama pakukhulupirira Mulungu, amene adaukitsa Yesu Ambuye athu kwa akufa. Yesuyo adaperekedwa kuti aphedwe chifukwa cha zochimwa zathu, ndipo adauka kwa akufa kuti tipezeke olungama pamaso pa Mulungu.
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
Monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, ndi momwenso chidakulira chikondi chake chosasinthika kwa anthu oopa Chauta. Monga kuvuma kuli kutali ndi kuzambwe, ndi momwenso amachotsera zolakwa zathu kuti zikhale kutali ndi ife.
Adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo ao.”
Ngwodala munthu amene chithandizo chake chimafumira kwa Mulungu wa Yakobe, munthu amene amakhulupirira Chauta, Mulungu wake.
Ndipo zonse zimene Mulungu adalonjeza zidachitika ndi “Inde” ameneyu. Nchifukwa chake mwa Yesu Khristuyo timanena kuti, “Amen” kulemekeza Mulungu.
Koma nthaŵi itakwana, Mulungu adatuma Mwana wake. Mwanayo adabadwa mwa mkazi, adabadwa woyenera kumvera Malamulo a Mose. Adachita zimenezi kuti akaombole amene anali akapolo a Malamulowo, ndipo kuti potero tisanduke ana a Mulungu.
Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani.
Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.
Ngodala anthu amene akumva njala ndi ludzu lofuna chilungamo, pakuti Mulungu adzakwaniritsa zofuna zao.
Koma inu ndinu fuko losankhidwa, ansembe achifumu, mtundu wopatulika, anthu akeake a Mulungu. Adakusankhani kuti mukalalike ntchito zamphamvu za Iye amene adakuitanani kuti mutuluke mu mdima, mukaloŵe m'kuŵala kwake kodabwitsa.
Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?
Mulungu wanga ali ndi chuma chochuluka, ndipo mwa Khristu Yesu adzakupatsani zonse zimene mukusoŵa.
Munthu wokhulupirira Mwanayo, ali ndi moyo wosatha. Koma wokana kukhulupirira Mwanayo, sadzaona moyo, chifukwa chilango cha Mulungu chili pa iye.”
Tsono ngati mudaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mtima pa zinthu za Kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. ndipo mwavala moyo watsopano. Moyo umenewu, Mlengi wanu akuukonzabe kosalekeza, kuti mudzamdziŵe kwenikweni ndi kufanafana naye. M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse. Popeza kuti mudasankhidwa ndi Mulungu kuti mukhale akeake, ndipo Iye amakukondani, muzikhala a mtima wachifundo, okoma mtima, odzichepetsa, ofatsa ndi odziŵa kupirira. Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana. Kuwonjezera pa zonsezi muzikhala ndi chikondi, pakuti nchimene chimamanga zonse m'chigwirizano chathunthu. Mtendere wa Khristu uzikutsogolerani m'mitima mwanu. Mulungu adakuitanani kuti mukhale nawo mtendere umenewu, popeza kuti ndinu ziwalo za thupi limodzi. Muzikhala oyamika. Mau a Khristu akhazikike kwathunthu m'mitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana ndi nzeru zonse. Muziimbira Mulungu ndi chiyamiko m'mitima mwanu, pamene mukuimba masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndi nyimbo zina zauzimu. Chilichonse chimene mungachite, kaya nkulankhula, kaya nkugwira ntchito, muchichite m'dzina la Ambuye Yesu ndi kuthokoza Mulungu Atate kudzera mwa Iye. Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga ayenera kuchitira okhala mwa Ambuye. Inu amuna, muzikonda akazi anu, musamaŵavutitse ai. Muzifunafuna za Kumwamba, osati zapansipano.
adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”
Koma amene amakhulupirira Chauta adzalandira mphamvu zatsopano, adzauluka ngati ziwombankhanga. Adzathamanga koma osatopa, adzayenda koma osalefuka konse.
monga Malembo anenera kuti, “Inetu ndikuika m'Ziyoni mwala wodzakhumudwitsa anthu, thanthwe limene lidzaŵagwetsa. Koma wokhulupirira Iyeyo, sadzachita manyazi.”
Khristu adatimasula kuti tikhale mfulu ndithu. Muzichilimikira tsono, osalola kumangidwanso m'goli la ukapolo.
Sikuti akuzengereza kuchita zimene adalonjeza, monga m'mene ena amaganizira, koma akukulezerani mtima. Safuna kuti ena aonongedwe, koma afuna kuti onse atembenuke mtima.
Motero tsono, abale, timayembekeza mosakayika konse kuloŵa m'Malo Opatulika Kopambana chifukwa cha imfa ya Yesu. Anthu opembedza Mulungu aja akadayeretsedwa kwathunthu, sibwenzi mtima wao ukuŵatsutsabe, ndipo akadaleka kumapereka nsembe. Iye adatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo yobzola chochinga, chimene chili thupi lake. Ndiponso tili ndi Wansembe wamkulu woyang'anira nyumba ya Mulungu. Nchifukwa chake tsono, tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona, tili ndi chitsimikizo cha chikhulupiriro. Timuyandikire ndi mitima yoyeretsedwa, yopanda kalikonse koitsutsa, ndiponso ndi matupi osambitsidwa ndi madzi oyera.
Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.
“Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga, ndidzamkhulupirira Iye, ndipo sindidzaopa. Pakuti Chauta ndiye mphamvu zondilimbitsa, ndiye amene ndimamuimbira, ndiye Mpulumutsi wanga.”
Mulungu amene amatipatsa chikhulupiriro, adzaze mitima yanu ndi chimwemwe ndi mtendere pakumvera Iye, kuti chiyembekezo chanu chizikulirakulira ndi mphamvu za Mzimu Woyera.
Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?
Mavuto andigwera pamodzi ndi zoŵaŵa zomwe, koma malamulo anu amandisangalatsa. Malamulo anu ndi olungama mpaka muyaya, patseni nzeru zomvetsa kuti ndizikhala ndi moyo.
Nchifukwa chake inu pitani kwa anthu a mitundu yonse, mukaŵasandutse ophunzira anga. Muzikaŵabatiza m'dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Mwadzidzidzi kudachita chivomezi chachikulu. Ndiye kuti mngelo wa Ambuye adaatsika kuchokera Kumwamba, nadzagubuduza chimwala chija, nkukhalapo. Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”
Koma mutamva zoŵaŵa pa kanthaŵi, Mulungu mwini amene nthaŵi zonse amakukomerani mtima, adzakukonzaninso, nadzakukhazikitsani pa maziko olimba. Ndiye amene adakuitanani, kuti pokhala limodzi ndi Khristu, mukalandire ulemerero wake wosatha.
Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”
Tsono ngati ndife ana a Mulungu, tidzalandira nao madalitso amene Iye akusungira anthu ake. Pamodzi ndi Khristu ifenso tidzalandira madalitso amene Mulungu anali atamsungira. Pakuti ngati timva zoŵaŵa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Mapiri angathe kusuntha, magomo angathe kugwedezeka, koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha. Lonjezo langa losunga mtendere mpaka muyaya silidzatha,” akuterotu Chauta amene amakumvera chifundo.
Mulungu adaonetsa chikondi chake kwa ife motere: Iye nkukhala ndi Mwana mmodzi yekha, koma adamtuma pansi pano, kuti mwa Iye tikhale ndi moyo.
Iyeyo ndiye amene adatitsekulira njira kuti pakukhulupirira tilandire mwai uwu umene Mulungu amapatsa mwaulere, umene takhazikikamo tsopano. Motero timakondwerera chiyembekezo chathu chakuti tidzalandirako ulemerero wa Mulungu.
Koma inu, yambani mwafunafuna ufumu wa Mulungu ndi kumachita zimene Iye akufuna, ndipo zina zonsezi adzakupatsaninso.
Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.
Ndipo tikudziŵa kuti Mulungu amayendetsa zinthu mwa njira yoti zonse ziŵakomere anthu omukonda ndipo apindulepo. Anthuwo ndi amene Iye amaŵaitana monga momwe Iye adazikonzera.
Uzikhulupirira Chauta ndi mtima wako wonse, usadalire nzeru zako za kumvetsa zinthu. Pa ntchito zako zonse uzivomera kuti kuli Mulungu, choncho njira zako Iye adzazilungamitsa.
“Ine, Ineyo ndithu, ndine amene ndimafafaniza machimo anu, kuti ulemerero wanga uwoneke. Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu.
Ndi mphamvu zake Mulungu akukusungani inunso omkhulupirira, kuti mudzalandire chipulumutso chimene Iye ali wokonzeka kuchiwonetsa pa nthaŵi yotsiriza.
Njira yake imene anthu amapezekera kuti ngolungama pamaso pa Mulungu ndi yakuti anthuwo akhulupirire Yesu Khristu. Zimenezi Mulungu amachitira anthu onse okhulupirira Khristu. Paja palibe kusiyana pakati pa anthu ai,
Khristu sadachimwe konse, koma Mulungu adamsandutsa uchimo chifukwa cha ife, kuti mwa Iyeyo ife tisanduke olungama pamaso pa Mulungu.
Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?
“Mukatero, mudzaŵala ngati mbandakucha, ndipo mabala anu adzapola msanga. Ine, kulungama kwanu, ndidzakutsogolerani, ndipo ulemerero wanga udzakutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Chauta ndi wabwino kwa amene amamudalira, kwa onse amene amafuna kuchita zimene Iye afuna. Nkwabwino kumdikira Chauta mopirira kuti aonetse chipulumutso chake.
Komabe ena adaamlandira nakhulupirira dzina lake, ndipo ameneŵa Iye adaŵapatsa mphamvu zoti akhale ana a Mulungu. Kukhala ana a Mulungu kumeneku sikudachokere m'kubadwa kwao, kapena ku chifuniro cha thupi, kapena ku chifuniro cha munthu ai, koma kudachokera kwa Mulungu.
Ngati uvomereza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo ukhulupirira mumtima mwako kuti Mulungu adamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka.
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu. Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.