Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


118 Mau a Mulungu Oteteza Ku Zoipa

118 Mau a Mulungu Oteteza Ku Zoipa

Ine ndikudziwa kuti Yesu, munthu wolungama amene anakhala padziko lapansi, ndiye chitsanzo chabwino cha nzeru ndi ungwiro. Iye ndiye woweruza woona, wosanama, komanso wopanda.

Chikondi ndi chifundo chake pa anthufe chimamupangitsa kumva ululu wathu tsiku ndi tsiku. Ndiye M'busa wabwino, mphunzitsi, mnzanga, mbale, komanso loya wathu wamkulu.

Kudalira anthu sikungatithandize kupambana, koma Baibulo mu 1 Yohane 2:1 limatiuza kuti Yesu Khristu ndiye loya wathu kwa Atate. Kaya muli pamavuto otani, Yesu amadziwa ndipo akumvetsa.

Kupita kwa Iye kuti akutetezeni ndiye chisankho chanzeru kwambiri. Mulungu akamakuthandizani, muli otetezeka. Mtima wake ndi wolungama, sadzachita zoipa, ndipo maganizo ake onse ndi abwino.

Ngati mwakumana ndi chisalungamo kapena kugwera mumsampha, pitani kwa Woweruza wabwino, muuzeni mavuto anu, ndipo mulole agwire ntchito m'malo mwanu. Musamafune kubwezera choipa ndi choipa, koma dalirani Mulungu. Mukamuuza mavuto anu, adzakumverani ndipo adzakuthandizani.

Khalani paubwenzi wolimba ndi Iye ndipo sungani mtendere, ngakhale mutakumana ndi mavuto, chifukwa mawu omaliza ndi a Mulungu. Mukadziwa Yesu ngati loya wanu, mudzaona momwe adzakhazikirire adani anu.

Mau onse a mdierekezi okunenani kuti ndinu wolakwa adzatha ndi mphamvu ya magazi a Yesu. Chifukwa cha Iye, ndinu omasuka ndipo mulibe chiweruzo. Aleluya.




Masalimo 91:1-2

Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:17

Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:7-8

Chauta adzakuteteza ku zoipa zonse, adzasamala moyo wako. Chauta adzakusunga kulikonse kumene udzapita, kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ngokhulupirika, ndipo adzakulimbitsani mtima ndi kukutchinjirizani kwa Woipa uja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:31

Nanga tsono tinganenenso chiyani pa zonsezi? Ngati Mulungu ali pa mbali yathu, angatsutsane nafe ndani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 18:2

Chauta ndiye thanthwe langa, linga langa ndi mpulumutsi wanga. Ndiye Mulungu wanga, ndi thanthwe langa limene ndimathaŵirako. Ndiye chishango changa, ndiye mtetezi wanga ndi mpulumutsi wanga, ndiye linga langa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:10

Chauta ali ngati nsanja yolimba, munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:20

“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 19:20

Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Chauta Wamphamvuzonse alimo m'dziko la Ejipito. Aejipito akadzalira kwa Chauta pa zovuta zao, Iye adzatuma mpulumutsi kuti aŵateteze ndi kuŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:11-12

Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:18

Tikudziŵa kuti aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira. Yesu, Mwana wa Mulungu, amamsunga, ndipo Woipa uja sangamkhudze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 38:6

Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya, ndipo mzindawu ndidzautchinjiriza.’ ”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 48:3

Mulungu waonetsa kuti ndiye woteteza mzindawo, pakuti Iye amakhala m'kati mwa malinga ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:10

Usachite mantha chifukwa Ine ndili nawe, usataye mtima, poti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakupatsa mphamvu, ndidzakuthandiza, ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 31:5

Monga mbalame zouluka pamwamba pa zisa zake, Chauta Wamphamvuzonse adzatchinjiriza mzinda wa Yerusalemu. Adzauteteza ndi kuupulumutsa, adzausiya pambali ndi kuuwombola.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 23:4

Ngakhale ndiyende m'chigwa chamdima wabii, sindidzaopa choipa chilichonse, pakuti Inu Ambuye mumakhala nane. Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimanditeteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:11-12

Koma onse othaŵira kwa Inu akondwere, aziimba ndi chimwemwe nthaŵi zonse. Inu muŵatchinjirize, kuti okukondani akondwere chifukwa cha chitetezo chanu. Inu Chauta, mumadalitsa munthu wochita chilungamo. Kukoma mtima kwanu kuli ngati chishango chomuteteza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 25:20

Tchinjirizani moyo wanga ndi kundipulumutsa. Musalole kuti andichititse manyazi, pakuti ndikuthaŵira kwa Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 51:36

Nchifukwa chake Chauta akunena kuti, “Ndidzakumenyera nkhondo yako, ndipo ndidzakulipsirira. Ndidzaumitsa nyanja ya ku Babiloni, akasupe ake onse adzaphwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:11

Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 12:8

Tsiku limenelo Chauta adzakhala ngati chishango chotchinjiriza anthu a ku Yerusalemu, kotero kuti anthu ofooka kwambiri mwa iwo adzakhala amphamvu ngati mfumu Davide. Tsono banja la Davide lidzakhala lolamulira zonse ngati Mulungu, ngati mngelo wa Chauta woŵatsogolera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:6

Tiyeni tsono tilimbe mtima ndi kunena kuti, “Ambuye ndiwo Mthandizi wanga, sindidzachita mantha. Munthu angandichite chiyani?”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 9:8

Pamenepo Ine ndidzakhala mlonda wa dziko langalo, kuti wina asamadutsepo kapena kuloŵamo. Palibe adani amene adzaŵapambane, pakuti zimenezi ndikuzisamala Ine ndemwe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 16:8

Nthaŵi zonse ndimalingalira za Chauta. Popeza kuti ali ku dzanja langa lamanja, palibe amene angandiopse konse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:1

Chauta ndiye muuni wanga ndi chipulumutso changa. Ndidzaopa yani? Chauta ndiye linga la moyo wanga, nanga ndichitirenji mantha?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:7

Inu ndinu kobisalira kwanga. Inu mumanditchinjiriza nthaŵi yamavuto. Nchifukwa chake ndimaimba nyimbo zotamanda chipulumutso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musalole kuti tigwe m'zotiyesa, koma mutipulumutse kwa Woipa uja.” [Pakuti ufumu, mphamvu ndi ulemerero ndi zanu kwamuyaya. Amen.]

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 17:8

Mundisunge ngati mwana wa diso, munditeteze pansi pa mapiko anu,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:1

Mulungu ndiye kothaŵira kwathu, ndiye mphamvu zathu. Ali wokonzekeratu kutithandiza pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 27:5

Pa tsiku lamavuto adzandibisa ndi kunditchinjiriza. Adzandisunga m'kati mwa Nyumba yake, adzanditeteza pa thanthwe lalitali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 59:1-2

Pulumutseni kwa adani anga, Inu Mulungu wanga, tetezeni kwa anthu ondiwukira. Mulungu wanga adzandichingamira chifukwa ndi wa chikondi chosasinthika. Mulungu wanga adzandilola kuti ndisangalale poona adani anga atagonja. Musaŵaphe pomwepa, kuwopa kuti anthu anga angaiŵale, koma muŵabalalitse ndi mphamvu zanu, ndipo muŵagwetse, Inu Ambuye, Inu chishango changa. Akodwe ndi kunyada kwao, chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao, ndi mau a pakamwa pao. Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama, muŵakwiyire ndi kuŵaononga. Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso, anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe, mpaka ku mathero a dziko lapansi. Amabweranso madzulo aliwonse akuuwa ngati agalu, nkumangoyendayenda mu mzinda. Amanka nafunafuna chakudya ndipo amangofuula akapanda kukhuta. Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu, m'maŵa ndidzaimba mokweza nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika. Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga. Inu mphamvu zanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokuyamikani, pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa, ndinu Mulungu wondiwonetsa chikondi chosasinthika. Pulumutseni kwa anthu ochita zoipa, landitseni kwa anthu okhetsa magazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 35:23

Tiyeni, Inu Chauta, dzukani kuti munditchinjirize pa mlandu wanga, Inu Mulungu wanga ndi Ambuye anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:20

Mumaŵabisa pamalo pamene pali Inu, kuti muŵateteze ku ziwembu za adani ao. Mumaŵasunga bwino ndi kuŵatchinjiriza, kuti anthu angakangane nawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8-9

Khalani odziletsa, khalani maso. Mdani wanu Satana amakhala akuyenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, kufunafuna woti amudye. Mulimbane naye mutakhazikika m'chikhulupiriro, podziŵa kuti akhristu anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso alikumva zoŵaŵa zomwezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:2

Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe, pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola. Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa, malaŵi ake sadzakutentha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 86:2

Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu. Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:3

Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 68:5

Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 50:20

Inu mudaapangana kuti mundichite chiwembu, koma Mulungu adazisandutsa kuti zikhale zabwino ndipo kuti zipulumutse moyo wa anthu ambiri. Choncho onsewo ali moyo lero lino chifukwa cha zimenezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:26

Munthu woopa Chauta ali ndi chikhulupiriro cholimba, ndipo ana ake adzakhala napo pothaŵira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:19

Okondedwa anga, musabwezere choipa, koma alekeni, mkwiyo wa Mulungu ndiwo uŵalange. Paja Malembo akuti, “Kulipsira nkwanga. Ndidzaŵalanga ndine, akutero Chauta.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:14-15

Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:7

Ngakhale ndiyende pakati pa mavuto, Inu mumasunga moyo wanga. Mumatambasula dzanja lanu kuletsa adani anga okwiya, dzanja lanu lamanja limandipulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:4

Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:3

Pakuti kunena za moyo wakalewo mudafa, ndipo moyo wanu watsopano ndi wobisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 10:29-31

Suja amagulitsa atimba aŵiri kandalama kamodzi? Komabe palibe ndi m'modzi yemwe amene angagwe pansi, Atate anu osadziŵa. Filipo ndi Bartolomeo; Tomasi ndi Mateyo, wokhometsa msonkho uja; Yakobe, mwana wa Alifeyo, ndi Tadeyo; Inuyotu ngakhale tsitsi lomwe la kumutu kwanu adaliŵerenga lonse. Choncho musati muziwopa ai. Ndinu a mtengo woposa atimba ambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:6-7

Chauta akakhala pa mbali yanga, sindichita mantha. Munthu angandichite chiyani? Chauta ali pa mbali yanga kuti andithandize. Odana nane ndidzaŵayang'ana monyoza nditaŵapambana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:114

Inu ndinu malo anga obisalako ndiponso chishango changa, ndimakhulupirira mau anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 40:29

Amalimbitsa ofooka, ndipo otopa amaŵaonjezera mphamvu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:8

Ndiye mlonda wa njira zolungama, amatchinjiriza njira ya anthu ake oyera mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 145:20

Onse amene amakonda Chauta, amaŵasunga, koma Chauta adzaononga oipa onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:5-6

Chauta ndiye amene amakusunga, Chauta ndiye mtetezi wako ali ku dzanja lako lamanja. Dzuŵa silidzakupweteka masana, mwezi sudzakuvuta usiku.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:39-40

Chipulumutso cha anthu abwino chimachokera kwa Chauta. Chauta ndiye kothaŵirako anthuwo pa nthaŵi yamavuto. Kondwa mwa Chauta, ndipo adzakupatsa zimene mtima wako ukukhumba. Chauta amaŵathandiza ndi kuŵalanditsa. Amaŵachotsa m'manja mwa anthu oipa nkuŵapulumutsa, popeza kuti anthuwo amadalira Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:15

Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:20

Ndipo Mulungu amene amapatsa mtendere, posachedwa adzatswanya Satana pansi pa mapazi anu. Ambuye athu Yesu Khristu akudalitseni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 4:8

Choncho ndidzagona ndi kupeza tulo mwamtendere, pakuti Inu nokha Chauta ndinu amene mumandisunga bwino lomwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 28:7

Chauta ndiye mphamvu zanga, ndiyenso chishango changa chonditeteza. Ndaika mtima wanga wonse pa Iye. Wandithandiza, choncho mtima wanga ukusangalala, ndipo ndimamthokoza ndi nyimbo yanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:3

Inu Chauta, mumapatsa mtendere weniweni kwa amene ali ndi mtima wokhazikika, chifukwa chokhulupirira Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:5-6

Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana. Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:24

Ukamakhala pansi, sudzachita mantha, ukamagona, udzakhala ndi tulo tabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 40:11

Musandichotsere chifundo chanu, Inu Chauta, chikondi chanu chosasinthika ndi kukhulupirika kwanu zindisunge nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:4

Inu Chauta, tetezeni kwa anthu oipa, tchinjirizeni kwa anthu andeu, amene amaganiza zofuna kundigwetsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 26:12

Inu Chauta, mumatipatsa mtendere, chifukwa choti zonse zimene timakhoza, mumatichitira ndinu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 1:10

Ndiye amene adatipulumutsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatipulumutsanso. Taika ndithu chikhulupiriro chathu pa Iyeyo choti adzatipulumutsanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 121:1

Ndimakweza maso anga ku mapiri. Kodi chithandizo changa chimachokera kuti?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 138:3

Pa tsiku limene ndidakuitanani, Inu mudandiyankha, mumandilimbitsa mtima ndi mphamvu zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:5

Mau aliwonse a Mulungu ndi oona. Iye ndiye chishango choteteza amene amathaŵira kwa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:39

Chabwino, koma Ine ndikukuuzani kuti munthu woipa osalimbana naye. Ngati munthu akumenya pa tsaya la ku dzanja lamanja, upereke linalonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 50:7

Koma kunyoza kwao sindikuvutika nako, chifukwa Ambuye Chauta amandithandiza. Nchifukwa chake ndalimbitsa mtima wanga ngati mwala. Ndikudziŵa kuti sadzandichititsa manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 144:2

Ndiye thanthwe langa ndi tchemba langa londiteteza, ndiye linga langa londipulumutsa, ndiye chishango changa chothaŵirako. Amaika mitundu ya anthu mu ulamuliro wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:10

zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:7

Pamenepo mtendere wochokera kwa Mulungu, umene uli wopitirira nzeru zonse za anthu, udzasunga bwino mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:13-17

Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji. Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu. Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu. Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana. Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 12:7

Titetezeni, Inu Chauta, titchinjirizeni nthaŵi zonse kwa anthu ameneŵa,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:4

Koma inu, ana anga, ndinu ake a Mulungu, ndipo mwaŵapambana aneneri onamawo. Pakuti Iye amene ali mwa inu, ndi wopambana iye uja amene ali mwa anthu odalira zapansipano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:38-39

Ndithu ndikudziŵa mosakayika konse kuti palibe kanthu kangatilekanitse ndi chikondi chake. Ngakhale imfa kapena moyo, ngakhale angelo kapena olamulira, ngakhale zinthu zimene zilipo tsopano, kapena zimene zidzaoneke m'tsogolomo, kapena zamphamvu zina zilizonse, ngakhale zakumwamba kapena zapansi, kapenanso kanthu kena kalikonse kolengedwa, sikangadzatilekanitse ndi chikondi cha Mulungu, chimene tili nacho mwa Khristu Yesu Ambuye athu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 69:14

Pulumutseni kuti ndisamire m'matope, landitseni kwa adani anga ndi ku madzi ozama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:1-2

Anthu amene amakhulupirira Chauta ndi olimba ngati phiri la Ziyoni, limene silingathe kugwedezeka, koma ndi lokhala mpaka muyaya. Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 28:20

Muzikaŵaphunzitsa kusunga zonse zimene Ine ndidakulamulani. Ndipo Ineyo ndili nanu masiku onse, mpaka kutha kwa dziko lino lapansi.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 32:8

Chauta akuti, “Ndidzakudziŵitsa ndi kukuphunzitsa njira imene uyenera kuyendamo. Ndidzakulangiza ndi kukuyang'anira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:5

Udzipereke m'manja mwa Chauta, umukhulupirire ndipo Iye adzakusamalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:19

Motero anthu adzaopa Chauta kuyambira kuvuma mpaka kuzambwe. Iyeyo adzabwera ngati mtsinje waliŵiro, wokankhidwa ndi mphepo yamkuntho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:166

Ndimakhulupirira kuti mudzandipulumutsa, Inu Chauta, ndipo ndimatsata malamulo anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 16:11

Muzidalira Chauta ndi mphamvu zake. Muziyesetsa kukhala pamaso pake kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 20:15

Iyeyo adati, “Mverani Ayuda nonsenu, ndi inu nonse okhala ku Yerusalemu, ndi inunso mfumu Yehosafati. Chauta akukuuzani kuti, ‘Musaope, ndipo musataye nacho mtima chinamtindi cha anthuchi, pakuti nkhondo si yanu, nja Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:140

Malonjezo anu ndi otsimikizika, ndipo ine mtumiki wanu ndimaŵakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:23

Tilimbikire kuvomereza mosafookera zimene timaziyembekeza, pakuti Iye amene adatilonjeza zimenezi ngwokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:22

Koma Chauta wasanduka linga langa londiteteza, Mulungu ndiye thanthwe langa lothaŵirako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 1:4

Khristuyo adadzipereka chifukwa cha machimo athu, kuti atipulumutse ku njira za moyo woipa uno. Pakutero adachita zimene Mulungu Atate athu ankafuna.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:22

Tula kwa Chauta nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakuchirikiza. Sadzalola konse kuti wolungama wake agwedezeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:1-2

Pulumutseni, Inu Chauta, kwa anthu oipa. Tchinjirizeni kwa anthu ankhanza. Makala amoto aŵagwere, aponyedwe m'maenje ozama, asatulukemonso. Musalole kuti woononga mbiri ya mnzake akhazikike m'dziko. Choipa chimlondole munthu wankhanza mpaka kumuwononga. Ndimadziŵa kuti Inu Chauta mumateteza ozunzika, mumaweruza mwachilungamo anthu osoŵa. Zoonadi, anthu ochita zabwino adzatamanda dzina lanu. Anthu amenewo adzakhala pamaso panu. Iwo amalingalira mumtima mwao kuti achite zoipa, amautsa nkhondo nthaŵi zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 46:10

“Khalani chete, ndipo mudziŵe kuti ndine Mulungu. Mitundu ya anthu imanditamanda, a m'dziko lapansi amandiyamika.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:14

Udzakhazikika m'chilungamo chenicheni. Sudzakhalanso wopanikizika, chifukwa palibe choopa, sudzakhalanso ndi mantha, chifukwa manthawo sadzakufikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:11

Ndimadalira Mulungu, sindidzachita mantha konse. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:13

Ine, Chauta Mulungu wako, ndikukugwira dzanja, ndine amene ndikukuuza kuti, “Usachite mantha, ndidzakuthandiza.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:19

Pamene nkhaŵa zikundichulukira, Inu mumasangalatsa mtima wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:9

Kwa Chauta ndiye kothaŵirako anthu opsinjidwa, ndiyenso kopulumukira pa nthaŵi yamavuto.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 22:4

Makolo athu ankadalira Inu. Zoonadi, ankakhulupirira Inu, ndipo Inu munkaŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu usakangamire pa ndalama, ndipo zimene muli nazo, mukhutire nazo. Paja Mulungu adati, “Sindidzakusiyani kapena kukutayani konse.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 5:1

Tsono, popeza kuti pakukhulupirira tapezeka kuti ndife olungama pamaso pa Mulungu, ndiye kuti tili pa mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 56:3-4

Pamene ndichita mantha ndimadalira Inu. Ndimatamanda Mulungu chifukwa cha zimene wandilonjeza. Ndimakhulupirira Mulungu mopanda mantha. Kodi munthu angandichite chiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:17

Chifukwa anthu onse akamachita zachilungamo, m'dziko mudzakhala mtendere ndi bata mpaka muyaya.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:20

Chauta adatumiza mau ake, naŵachiritsa anthuwo, adaŵapulumutsa kuti asaonongeke.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 118:14

Chauta amene ndimamuimbira ndiye mphamvu zanga. Ndiye mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 19:14

Mau anga ndi maganizo anga avomerezeke pamaso panu, Inu Chauta, thanthwe langa ndi mpulumutsi wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 146:9

Chauta amateteza alendo, amachirikiza mkazi wamasiye ndiponso mwana wamasiye. Koma njira za anthu oipa amazipotoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:10

Ngodala anthu ozunzidwa chifukwa cha kuchita chilungamo, pakuti Ufumu wakumwamba ndi wao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:1

Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe, amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti, “Usaope, chifukwa ndidakuwombola, ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 115:11

Inu amene mumaopa Chauta, mkhulupirireni. Chauta ndiye mthandizi wanu ndi chishango chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 20:1

Chauta akuthandize pa tsiku lamavuto. Mulungu wa Yakobe akuteteze.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:7

Mngelo wa Chauta amatchinjiriza anthu omvera Iye, ndipo amaŵapulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:22

Usamanena kuti, “Ndidzabwezera choipa ndine.” Udikire Chauta, ndipo adzakuthandiza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:31

Kavalo amamkonzera tsiku la nkhondo, koma ndi Chauta amene amapambanitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:10-11

Usasendeza malire akalekale, kapena kukaloŵerera minda ya ana amasiye. Paja Momboli wao ndi wamphamvu, adzaŵateteza pa mlandu wao kuti akutsutse iweyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:25

Chauta akuyankha kuti, “Ndithudi, ankhondo adzaŵalanda akaidi ao, ndipo mfumu yankhalwe adzailanda zofunkha zake. Ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu, ndipo ndidzapulumutsa ana anu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 49:26

Ndidzaumiriza okuzunzani kuti adzadye mnofu wao womwe. Ndipo adzaledzera nawo magazi ao omwe, monga momwe adakachitira ndi vinyo watsopano. Motero anthu onse adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, Mpulumutsi wanu, ndine Momboli wanu, Wamphamvu uja wa Yakobe.”

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 54:15-17

Ngati wina autsa nkhondo, si ndine ndachititsa ai. Amene alimbana nawe adzalephera, poti udzaŵagonjetsa. Udziŵe kuti ndidalenga ndine munthu wosula, amene amakoleza moto wamakala kuti asulire zida. Ndidalenganso ndine munthu wosakaza kuti aononge. Koma iwe palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke. Onse okuneneza udzaŵatsutsa. Ndimo adzapezera atumiki anga, ndipo ndidzaŵapambanitsa ndine,” akuterotu Chauta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu wanga ndi wamkulu ndipo woyenera kutamandidwa kwambiri, Iye ndi woopsa, wamphamvu pa nkhondo, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. M'dzina lamphamvu la Yesu ndikufuna kukuthokozani chifukwa cha chisamaliro chanu chodzaza ndi chikondi ndi chikhulupiriro. Zoonadi Ambuye, chifundo chanu chimakhala chatsopano tsiku lililonse pa ine chifukwa mwanditeteza ku ziwembu za mdani ndipo mwapulumutsa banja langa ku mapulani obisika. Munditeteze ndi kundipulumutsa kuti nthawi zonse ndisangalale ndi mtendere wanu ndikukwaniritsa cholinga chimene mwandipatsa. Mawu anu amati: "Ngati wina aliyense akukukonzerani chiwembu, adzachita popanda ine; aliyense amene akukukonzerani chiwembu, adzagwa pamaso panu." Ndikukupemphani Mzimu Woyera kuti munditeteze ku zoyipa zonse, ku malingaliro onse ndi chiwembu chilichonse chimene mdani akundikonzera, mundisunge pansi pa mthunzi wa mapiko anu Ambuye, yeretsani maganizo anga, mtima wanga, thupi langa, moyo wanga ndi mzimu wanga, ndipo musalole chilichonse choipa kuwononga ubale wanga ndi inu. Ambuye, ndikukupemphani chifukwa ndinu chishango changa ndi chitetezo changa, ndimakhulupirira inu, mu mphamvu yanu ndi ulemerero wanu, ndimayembekezera mawu anu, pamene akunditsutsa, chifukwa ndiwo okha amene angandipatse mtendere. Ndikukupemphani kuti muchotse zonse zomwe zikundivutitsa ndi kundipweteka, chotsani m'moyo wanga ndi m'nyumba mwanga mphamvu zonse za mdierekezi ndi ziwanda zake, ndipulumutseni ku choipa chilichonse chomwe chikubwera pa ine ndipo sungani unyolo uliwonse womwe ukundimanga, ndikukupemphani kuti ndikusangalatseni ndikukutumikirani popanda choletsa chakuthupi kapena chauzimu. Kwalembedwa: "Mukundikonzera tebulo pamaso pa omwe akunditsutsa; mukundidzoza mutu wanga ndi mafuta; chikho changa chikusefukira." M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa